Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 82

Zimene Zinachitika Pamene Yesu Ankalalikira ku Pereya

Zimene Zinachitika Pamene Yesu Ankalalikira ku Pereya

LUKA 13:22–14:6

  • ANAWALIMBIKITSA KUTI AYESETSE MWAMPHAMVU KULOWA PAKHOMO LOPAPATIZA

  • YESU ANANENA ZOTI AKAFERA KU YERUSALEMU

JYesu atamaliza kuphunzitsa komanso kuchiritsa anthu ku Yudeya ndi ku Yerusalemu anawoloka mtsinje wa Yorodano n’kupita ku Pereya. Kumeneko anayamba kuphunzitsa anthu m’mizinda yosiyanasiyana. Koma pasanapite nthawi yaitali anabwereranso ku Yerusalemu.

Pamene anali ku Pereya munthu wina anamufunsa kuti: “Ambuye, kodi amene akupulumuka ndi owerengeka okha?” Munthuyu anafunsa funsoli chifukwa cha mikangano imene inkachitika pakati pa atsogoleri achipembedzo. Atsogoleriwa ankakangana chifukwa ena ankanena kuti anthu odzapulumuka adzakhala ambiri pomwe ena ankati adzakhala ochepa. Yesu sanafotokoze kuti ndi angati amene adzapulumuke, m’malomwake anafotokoza zimene munthu ayenera kuchita kuti adzapulumuke. Iye anati: “Yesetsani mwamphamvu kulowa pakhomo lopapatiza.” N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti m’pofunika kuyesetsa mwamphamvu? “Chifukwa ambiri ndikukuuzani, adzafunitsitsa kulowamo koma sadzatha.”—Luka 13:23, 24.

Yesu anapereka fanizo lofotokoza za kufunika kochita khama. Ananena kuti: “Mwininyumba akanyamuka ndi kukakhoma chitseko, ndiyeno inu n’kuima panja ndi kuyamba kugogoda pachitsekopo, n’kumanena kuti, ‘Titsegulireni ambuye,’ . . . Koma iye adzakuuzani kuti, ‘Sindikudziwa kumene mukuchokera. Ndichokereni pano, nonsenu ochita zinthu zosalungama!’”—Luka 13:25-27.

Fanizoli likunena za mavuto amene munthu wobwera mochedwa amakumana nawo. Munthuyu anafika mochedwa chifukwa anayamba ulendowu pa nthawi imene iyeyo ankaona kuti ndi yabwino ndipo anapeza kuti chitseko ndi chotseka komanso chokhoma. Iye ankafunika kubwera mofulumira ngakhale kuti anali ndi zochita zina pa nthawiyo. Ndi mmenenso zinalili ndi anthu ambiri amene akanatha kuphunzira zinthu pamene Yesu ankawaphunzitsa. Anthuwa sanaone kuti kulambira kumene Mulungu amavomereza kunali kofunika kwambiri pa moyo wawo. Ayuda ambiri amene Yesu anawaphunzitsa sanavomereze njira imene Mulungu anapereka yowathandiza kuti adzapulumuke. Yesu ananena kuti anthuwa adzaponyedwa kunja ndipo ‘kunjako n’kumene adzalira ndi kukukuta mano.’ Komabe iye ananena kuti: “Anthu adzabwera kuchokera kumbali za kum’mawa ndi kumadzulo, kumpoto ndi kum’mwera, ndipo adzadya patebulo mu ufumu wa Mulungu.”—Luka 13:28, 29.

Yesu ananena kuti: “Amene ali omalizira [anthu amene sanali Ayuda komanso Ayuda ena amene ankaponderezedwa] adzakhala oyamba, ndipo oyamba [Ayuda amene ankakonda zopembedza komanso amene ankanyadira kuti iwo ndi ana a Abulahamu] adzakhala omalizira.” (Luka 13:30) Pamene Yesu ananena kuti oyamba adzakhala “omalizira” ankatanthauza kuti anthu amenewa, omwe anali osayamika, sadzalowa mu Ufumu wa Mulungu.

Kenako Afarisi ena anabwera kwa Yesu n’kumuuza kuti: “Nyamukani muchoke kuno, chifukwa Herode [Antipa] akufuna kukuphani.” N’kutheka kuti Mfumu Herode inanena dala zimenezi pofuna kuti Yesu achoke m’deralo. Mwina Herode ankawopa kukhudzidwa ndi imfa ya mneneri wina ngati mmene zinakhalira ndi kuphedwa kwa Yohane M’batizi. Koma Yesu anauza Afarisiwo kuti: “Pitani mukaiuze nkhandwe imeneyo  kuti, ‘Ine ndikutulutsa ziwanda ndi kuchita ntchito yochiritsa lero ndi mawa, tsiku lachitatu ndidzamaliza.’” (Luka 13:31, 32) Zikuoneka kuti Yesu anatchula Herode kuti “nkhandwe” chifukwa nkhandwe imachita zinthu mochenjera komanso mwachinyengo. Koma Yesu sanachite zinthu mwaphuma chifukwa cha Herode kapena munthu wina. Iye anagwira ntchito yonse imene Atate wake anamutuma komanso pa nthawi imene Atate wake anamuuza ndipo sanasokonezedwe ndi munthu.

Yesu anapitirizabe ulendo wake wolowera ku Yerusalemu chifukwa iye ananena kuti: “N’kosayenera kuti mneneri amuphere kunja kwa Yerusalemu.” (Luka 13:33) Popeza palibe ulosi uliwonse m’Baibulo umene unanena kuti Mesiya adzafera mumzinda umenewo, nanga n’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti akafera kumeneko? Mzinda wa Yerusalemu unali likulu la Yudeya ndipo khoti lalikulu la Sanihedirini lomwe linkakhala ndi oweruza 71 linali kumeneko. Khotili ndi limene linkaweruza milandu ya anthu amene ankawaganizira kuti ndi aneneri onyenga. Kuwonjezera pamenepo, ku Yerusalemu n’kumene ankaperekerako nsembe za nyama. Choncho Yesu ankadziwa kuti zinali zosavomerezeka kuti akafere kumalo ena.

Kenako Yesu ananena kuti: “Yerusalemu, Yerusalemu! wakupha aneneri ndi kuponya miyala anthu otumidwa kwa iwe . . . mobwerezabwereza ndinafuna kusonkhanitsa ana ako monga mmene nkhuku yathadzi imasonkhanitsira anapiye ake m’mapiko ake, koma anthu inu simunafune zimenezo. Tsopano tamverani! Mulungu wachoka ndi kukusiyirani nyumba yanuyi.” (Luka 13:34, 35) Mtunduwu unayenera kulangidwa chifukwa unakana Mwana wa Mulungu.

Yesu asananyamuke ulendo wake wopita ku Yerusalemu, mtsogoleri wa Afarisi anamuitanira kunyumba kwake kuti akadye chakudya pa tsiku la Sabata. Anthu ena amene anaitanidwanso ankayang’anitsitsa kuti aone zimene Yesu achite ndi munthu wina wotupa manja ndi miyendo amene anabweranso kunyumbako. Kenako Yesu anafunsa Afarisi komanso anthu ena odziwa Chilamulo kuti: “Kodi n’kololeka kuchiritsa pa sabata kapena ayi?”—Luka 14:3.

Palibe aliyense amene anamuyankha. Zitatero Yesu anachiritsa munthuyo kenako anafunsa anthuwo kuti: “Ndani wa inu, amene mwana wake kapena ng’ombe yake itagwera m’chitsime pa tsiku la sabata, sangaitulutse nthawi yomweyo?” (Luka 14:5) Apanso anthuwo sanamuyankhe chifukwa Yesu ananena mfundo yosatsutsika.