Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 87

Muzichita Zinthu Mwanzeru Pokonzekera Zakutsogolo

Muzichita Zinthu Mwanzeru Pokonzekera Zakutsogolo

LUKA 16:1-13

  • FANIZO LA WANTCHITO WOSALUNGAMA

  • MUZIGWIRITSA NTCHITO CHUMA CHANU KUTI MUKHALE NDI “MABWENZI”

Fanizo la mwana wotayika limene Yesu anafotokoza lija liyenera kuti linathandiza okhometsa msonkho, alembi komanso Afarisi amene ankamumvetsera, kudziwa kuti Mulungu ndi wokonzeka komanso wofunitsitsa kukhululukira anthu ochimwa omwe alapa. (Luka 15:1-7, 11) Kenako Yesu anayamba kulankhula ndi ophunzira ake ndipo anawauza fanizo lina. Fanizoli linali lonena za munthu wolemera yemwe anazindikira kuti wantchito wake wina, yemwe ankayang’anira katundu wa m’nyumba yake, sankachita zinthu mokhulupirika.

Yesu anafotokoza kuti wantchitoyo sanayendetse bwino chuma cha bwana wake. Choncho bwanayo anamuuza kuti amuchotsa ntchito. Ndiyeno wantchitoyo anayamba kuganiza kuti: “Nditani ine, pakuti bwana wanga andichotsa ntchito? Sindingathe kulima chifukwa ndilibe mphamvu, ndipo ndikuchita manyazi kukhala wopemphapempha.” Pokonzekera zam’tsogolo iye ananena kuti: “Ndadziwa chochita kuti akandichotsa ntchito, anthu akandilandire bwino m’nyumba zawo.” Ndiyeno anaitana amene anali ndi ngongole kwa bwana wake mmodzi ndi mmodzi, ndipo anafunsa woyamba kuti: “Uli ndi ngongole yochuluka bwanji kwa bwana wanga?”—Luka 16:3-5.

Munthu woyamba anayankha kuti: “Mitsuko 100 ya mafuta a maolivi.” Mitsuko imeneyi inali yokwana malita 2,200. Munthu amene anatenga ngongoleyu ayenera kuti anali ndi munda waukulu wa maolivi kapena ankagulitsa mafuta. Wantchitoyo anauza munthuyo kuti: “Nayi kalata yako ya ngongole, khala pansi ulembe mitsuko 50 mwamsanga.”—Luka 16:6.

Wantchitoyo anafunsanso munthu wina kuti: “Nanga iwe, ngongole yako ndi yaikulu bwanji?” Munthuyo anayankha kuti: “Madengu 100 a tirigu.” Madengu onsewa anali okwana malita 22,000. Wantchitoyo anauza munthu amene anali ndi ngongoleyo kuti: “Nayi kalata yako ya ngongole ulembepo madengu 80.” Choncho anamuchotsera madengu 20 pa ngongole yakeyo.—Luka 16:7.

Nthawi imene wantchitoyu ankachita zimenezi, n’kuti akuyang’anirabe chuma cha bwana wake. Choncho anali adakali ndi mphamvu zochotsera anthu ngongole zomwe anali nazo kwa bwana wake. Zimenezi zinamuthandiza wantchitoyo kuti akhale ndi anzake amene akanamuthandiza ngati ntchito yake itatha.

Koma patapita nthawi bwana uja anadziwa zimene wantchito wake anachita. Ngakhale kuti zimene anachitazo zinachititsa kuti bwana wake aluze chuma, bwanayo anasangalala komanso anayamikira wantchitoyu chifukwa “anachita mwanzeru” “ngakhale kuti anali wosalungama.” Yesu ananenanso kuti: “Ana a m’dziko lino amachita mwanzeru pochita zinthu ndi anthu a m’badwo wawo kuposa ana a kuwala.”—Luka 16:8.

Sikuti Yesu ankalimbikitsa kuti anthu azichita zimene wantchitoyu anachita kapena kuti anthu azichita zinthu zachinyengo popanga bizinezi. Nanga Yesu ananeneranji zimenezi? Iye analimbikitsa ophunzira ake kuti: “Dzipezereni mabwenzi ndi chuma chosalungama, kuti chumacho chikatha, akakulandireni m’malo okhala amuyaya.” (Luka 16:9) Pamenepa tikuphunzirapo kuti tiyenera kuoneratu zinthu zili patali komanso kuchita zinthu mwanzeru. Atumiki a  Mulungu omwe ndi “ana a kuwala” ayenera kugwiritsa ntchito chuma chawo mwanzeru kuti adzapeze moyo wosatha.

Yehova Mulungu komanso Mwana wake ndi okhawo amene angalandire munthu kuti alowe mu Ufumu wakumwamba kapena m’Paradaiso padziko lapansi. Choncho tingachite bwino kuyesetsa kukhala nawo pa ubwenzi pogwiritsira ntchito chuma chathu kuti chithandizire pa ntchito za Ufumu. Tikachita zimenezi tidzakhala otsimikiza kuti tidzapeza moyo wosatha ngakhale zinthu ngati golide, siliva kapena zinthu zina zapamwamba zitatithera kapena kuwonongeka.

Yesu ananenanso kuti amene amakhala wokhulupirika poyang’anira komanso pogwiritsa ntchito chuma kapena zinthu zimene ali nazo, adzakhalanso wokhulupirika ngati atapatsidwa udindo woyang’anira zinthu zofunika kwambiri. Yesu ananena kuti: “Choncho, ngati simunakhale wokhulupirika pa chuma chosalungama, ndani adzakupatseni ntchito yoyang’anira chuma chenicheni [monga ntchito za Ufumu]?”—Luka 16:11.

Pamenepa Yesu anasonyeza ophunzira ake kuti ayenera kuchita zinthu zambiri kuti adzalandiridwe “m’malo okhala amuyaya.” Ndiyetu munthu sangathe kukhala mtumiki wokhulupirika wa Mulungu pa nthawi imodzimodziyo n’kukhalanso kapolo wachuma cha m’dzikoli. Kenako Yesu anamaliza kupereka malangizowa ponena kuti: “Wantchito wa panyumba sangatumikire ambuye awiri, chifukwa adzadana ndi mmodzi ndi kukonda wina, kapena adzakhulupirika kwa mmodzi ndi kunyoza winayo. Simungathe kutumikira Mulungu ndi Chuma nthawi imodzi.”—Luka 16:9, 13.