Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 96

Yesu Anayankha Wolamulira Wachinyamata Amene Anali Wolemera

Yesu Anayankha Wolamulira Wachinyamata Amene Anali Wolemera

MATEYU 19:16-30 MALIKO 10:17-31 LUKA 18:18-30

  • MUNTHU WOLEMERA ANAFUNSA ZIMENE ANGACHITE KUTI ADZAPEZE MOYO WOSATHA

Yesu anadutsa m’chigawo cha Pereya popita ku Yerusalemu. Ali m’njira anakumana ndi wachinyamata wina amene anali wolemera. Mnyamatayo anamuthamangira n’kukagwada pamapazi a Yesu. Munthu ameneyu anali mmodzi wa ‘olamulira’ ndipo mwina anali mtsogoleri wa pa sunagoge kapena anali woweruza m’khoti la Sanihedirini. Iye anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi Wabwino, ndizichita chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”—Luka 8:41; 18:18; 24:20.

Poyankha, Yesu anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ukunditchula kuti wabwino? Palibe wabwino, koma Mulungu yekha.” Munthuyo anatchula Yesu kuti “wabwino” mwamwambo chabe. Iye anachita zimenezi potengera aphunzitsi achiyuda omwe ankaitanana pogwiritsa ntchito mayina a udindo. Ngakhale kuti Yesu analidi mphunzitsi wabwino, iye ankafuna kuti munthuyo adziwe kuti Mulungu yekha ndi amene ayenera kutchulidwa kuti “Wabwino.”

Yesu anauza munthuyo kuti: “Chotero ngati ukufuna kukapeza moyo, uzisunga malamulo nthawi zonse.” Ndiyeno munthuyo anafunsa Yesu kuti: “Malamulo ati?” Poyankha munthuyo, Yesu anatchula malamulo 5 omwe ankapezeka pa Malamulo Khumi. Malamulowo ankanena za kupha, kuchita chigololo, kuba, kupereka umboni wabodza komanso kulemekeza makolo. Anamuuzanso lamulo lina lofunika kwambiri lakuti: “Uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.”—Mateyu 19:17-19.

Munthuyo anayankha kuti: “Ndakhala ndikutsatira zonsezi, n’chiyaninso chimene ndikupereweza?” (Mateyu 19:20) N’kutheka kuti munthuyu ankaganiza kuti afunika kuchita zinthu zinazake zabwino komanso zapamwamba kuti adzapeze moyo wosatha. Yesu ataona kuti munthuyu ankafunsa zimenezi kuchokera pansi pamtima, “anam’konda” kwambiri munthuyo. (Maliko 10:21) Komabe panali chinthu china chomwe chinkamusokoneza.

Munthuyo ankakonda kwambiri katundu wake choncho Yesu anamuuza kuti: “Chinthu chimodzi chikusowekabe mwa iwe: Pita kagulitse zilizonse zimene uli nazo ndipo ndalama zake upatse osauka. Ukatero udzakhala ndi chuma kumwamba, ndiyeno ubwere udzakhale wotsatira wanga.” Iye akanatha kugawa ndalama zake kwa anthu asauka, omwe sakanamubwezera, n’kukhala wotsatira wa Yesu. Munthuyo  anachoka ali wachisoni. Chifukwa chakuti munthuyu ankakonda kwambiri chuma komanso “katundu wambiri” amene anali naye, analephera kuona chuma chamtengo wapatali. (Maliko 10:21, 22) Yesu ananena kuti: “Zidzakhalatu zovuta kwambiri kuti anthu a ndalama adzalowe mu ufumu wa Mulungu!”—Luka 18:24.

Ophunzira a Yesu anadabwa kwambiri atamva mawu amenewa komanso zimene Yesu ananena kuti: “Kunena zoona, n’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu.” Zimenezi zinachititsa ophunzirawo kufunsa kuti: “Ndiye angapulumuke ndani?” Kodi zimenezi zikutanthauza kuti palibe munthu amene angapulumukedi? Yesu anayang’ana ophunzira ake n’kuwayankha kuti: “Zinthu zosatheka ndi anthu n’zotheka ndi Mulungu.”—Luka 18:25-27.

Kenako Petulo anauza Yesu kuti iye ndi ophunzira enawo anachita zosiyana ndi zimene munthu wolemera uja anachita. Iye anati: “Taonani! Ife tasiya zinthu zonse ndi kukutsatirani, kodi tidzapeza chiyani?” Yesu anawauza madalitso amene adzapeze chifukwa chosankha kukhala otsatira ake powauza kuti: “Pa nthawi ya kulenganso zinthu, pamene Mwana wa munthu adzakhala pampando wachifumu waulemerero, inu amene mwatsatira ine mudzakhalanso m’mipando yachifumu 12, kuweruza mafuko 12 a Isiraeli.”—Mateyu 19:27, 28.

Pamenepatu Yesu ankaganizira za m’tsogolo pa nthawi ya kulenganso zinthu padziko lapansi kuti zidzakhale mmene zinalili m’munda wa Edeni. Pa nthawi imeneyo Petulo ndi ophunzira enawo adzapatsidwa mwayi wolamulira dziko lapansi la Paradaiso limenelo pamodzi ndi Yesu. Umenewu unalidi mwayi wamtengo wapatali poyerekezera ndi zinthu zonse zimene anasiya.

Koma sikuti ophunzirawo ankayembekezera kuti adzalandira madalitso onse m’tsogolo. Iwo anayamba kulandira madalitso ena nthawi yomweyo. Yesu ananena kuti: “Palibe amene wasiya nyumba, mkazi, abale, makolo kapena ana, chifukwa cha ufumu wa Mulungu amene sadzapeza zochuluka kwambiri kuposa zimenezi m’nthawi ino, ndipo m’nthawi ikubwerayo moyo wosatha.”—Luka 18:29, 30.

Kulikonse komwe ophunzira a Yesuwo ankapita ankasangalala ndi ubale womwe anali nawo ndi okhulupirira anzawo. Ubale umenewu unkawachititsa kukhala ogwirizana kwambiri kuposa mmene zimakhalira ndi anthu a m’banja limodzi. N’zomvetsa chisoni kuti wolamulira wachinyamata amene anali wolemera uja anataya mwayi umenewu komanso mwayi wokalamulira nawo mu Ufumu wa Mulungu.

Yesu ananenanso kuti: “Koma ambiri amene ali oyamba adzakhala omaliza, ndipo omaliza adzakhala oyamba.” (Mateyu 19:30) Kodi Yesu ankatanthauza chiyani ponena mawu amenewa?

Wolamulira wachinyamata uja anali m’gulu la anthu “oyamba” chifukwa anali mmodzi wa atsogoleri achiyuda. Iye ankayembekezera kulandira madalitso ambiri komanso ankayembekezeredwa kuchita zinthu zambiri chifukwa chakuti ankatsatira malamulo a Mulungu. Koma munthuyu ankakonda kwambiri chuma ndiponso katundu wake kuposa china chilichonse pa moyo wake. Mosiyana ndi munthu ameneyu, anthu wamba ankaona kuti zimene Yesu ankaphunzitsa zinali zoona komanso zidzawathandiza kupeza moyo wosatha. Tinganene kuti anthuwa anali “omaliza” koma kenako anadzakhala “oyamba,” moti ankayembekezera kudzakhala pamipando yachifumu kumwamba pamodzi ndi Yesu n’kumalamulira dziko lapansi la Paradaiso.