Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 95

Anawafotokozera Chifukwa Chothetsera Banja Komanso Kuti Azikonda Ana

Anawafotokozera Chifukwa Chothetsera Banja Komanso Kuti Azikonda Ana

MATEYU 19:1-15 MALIKO 10:1-16 LUKA 18:15-17

  • YESU ANAFOTOKOZA MMENE MULUNGU AMAONERA NKHANI YOTHETSA BANJA

  • MPHATSO YOKHALA OSAKWATIRA

  • TIZIKHALA NGATI ANA AANG’ONO

Yesu ndi ophunzira ake atachoka ku Galileya, anawoloka mtsinje wa Yorodano n’kulowera chakumwera ndipo anadutsa m’chigawo cha Pereya. Nthawi ina Yesu ali ku Pereya anauza Afarisi mmene Mulungu amaonera nkhani yothetsa banja. (Luka 16:18) Koma tsopano Afarisi anayambitsanso nkhaniyi ndi cholinga chofuna kuyesa Yesu.

Mose analemba kuti mwamuna akhoza kuthetsa banja ngati mkazi wake ali “ndi vuto linalake.” (Deuteronomo 24:1) Choncho anthu anali ndi maganizo osiyanasiyana pa zifukwa zothetsera banja. Anthu ena ankaganiza kuti zifukwa zing’onozing’ono zikanachititsanso kuti banja lithe. Chifukwa cha zimenezi, Afarisi anafunsa Yesu kuti: “Kodi n’kololeka kuti mwamuna asiye mkazi wake pa chifukwa chilichonse?”—Mateyu 19:3.

M’malo mofotokoza zimene anthu ankaganiza, Yesu anawakumbutsa zimene Mulungu anachita pamene ankayambitsa banja. Iye ananena kuti: “Kodi simunawerenge kuti amene analenga anthu pa chiyambi pomwe anawalenga mwamuna ndi mkazi n’kunena kuti, ‘Pa chifukwa chimenechi mwamuna adzasiya bambo ake ndi mayi ake n’kudziphatika kwa mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi’? Chotero salinso awiri, koma thupi limodzi. Choncho chimene Mulungu wachimanga pamodzi, munthu asachilekanitse.” (Mateyu 19:4-6) Pamene Mulungu ankayambitsa banja la Adamu ndi Hava sananene kuti banjalo lidzathe.

Pofuna kutsutsana ndi Yesu, Afarisiwo anamufunsa kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipereka kalata yothetsa ukwati kwa mkazi ndi kum’siya?” (Mateyu 19:7) Yesu anawauza kuti: “Chifukwa cha kuuma mtima kwanu, Mose anakulolezani kuti muzithetsa ukwati, koma kuyambira pa chiyambi sizinali choncho ayi.” (Mateyu 19:8) Pamene Yesu ananena kuti “pa chiyambi” sankanena za nthawi ya Mose koma ankanena za nthawi imene Mulungu anayambitsa banja mu Edeni.

Kenako Yesu ananena mfundo yofunika kwambiri kuti: “Ine ndikukuuzani kuti aliyense wosiya mkazi wake n’kukwatira wina wachita chigololo [por·neiʹa mu Chigiriki], kupatulapo ngati wamusiya chifukwa cha dama.” (Mateyu 19:9) Choncho chigololo ndi chifukwa chimodzi chokha chomveka chopezeka m’Malemba chomwe chingachititse munthu kuthetsa banja.

Zimenezi zinachititsa kuti ophunzira a Yesu anene kuti: “Ngati zili choncho kwa munthu ndi mkazi wake, ndiyetu ndi bwino kusakwatira.” (Mateyu 19:10) Pamenepatu n’zoonekeratu kuti ngati munthu wina akufuna kukwatira kapena kukwatiwa ayenera kudziwa kuti banja siliyenera kutha.

Ponena za anthu osakwatira, Yesu ananena kuti ena mwa anthu amenewa anabadwa choncho moti sangathe kugona ndi mkazi. Ananenanso kuti ena sakwatira chifukwa anachita kufulidwa. Pomwe ena amachita kudziletsa kuti asakwatire n’cholinga choti aziganizira komanso kuchita zinthu zambiri zokhudza Ufumu. Kenako Yesu analimbikitsa anthu amene ankamumvetserawo kuti: “Amene angathe [kukhala wosakwatira] achite” zimenezi.—Mateyu 19:12.

Kenako anthu anayamba kubweretsa ana awo aang’ono kwa Yesu. Koma ophunzira ake ankaletsa anthuwo kuchita zimenezi mwina pofuna kuti anawo asamuvutitse Yesu. Yesu ataona zimene ophunzira akewo ankachita, anakwiya ndipo anawauza kuti: “Alekeni anawo abwere kwa ine, musawaletse ayi. Pakuti ufumu wa Mulungu ndi wa anthu amene ali ngati ana amenewa. Ndithu ndikukuuzani, Aliyense wosalandira ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono sadzalowa n’komwe mu ufumuwo.”—Maliko 10:14, 15; Luka 18:15.

Imeneyitu ndi mfundo yofunika kwambiri. Kuti tikalowe mu Ufumu wa Mulungu, tiyenera kukhala odzichepetsa komanso ofunitsitsa kuphunzira zinthu ngati ana. Ndiyeno posonyeza kuti Yesu ankakonda ana anawanyamula n’kuwadalitsa. Amachitanso zimenezi ndi anthu onse amene amalandira “Ufumu wa Mulungu ngati mwana wamng’ono.”—Luka 18:17.