Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 99

Yesu Anachiritsa Anthu Akhungu Komanso Anathandiza Zakeyu

Yesu Anachiritsa Anthu Akhungu Komanso Anathandiza Zakeyu

MATEYU 20:29-34 MALIKO 10:46-52 LUKA 18:35–19:10

  • YESU ANACHIRITSA ANTHU AKHUNGU KU YERIKO

  • ZAKEYU YEMWE ANALI WOKHOMETSA MSONKHO ANALAPA

Pamene Yesu anali pa ulendo wopita ku Yerusalemu anafika ku Yeriko pamodzi ndi anthu amene ankayenda nawo. Kuchoka ku Yeriko kupita ku Yerusalemu unali mtunda woti anthu ankayenda tsiku limodzi. Zikuoneka kuti panali mizinda iwiri yomwe inkadziwika ndi dzina lakuti Yeriko. Mzinda wa Yeriko watsopano, womwe unamangidwa ndi Aroma, unali pa mtunda wa makilomita pafupifupi 1.6 kuchokera ku mzinda wa Yeriko wakale. Pamene Yesu ankatuluka mu umodzi mwa mizindayi kuti akalowe winawo, anthu awiri omwe anali akhungu komanso opemphapempha anamva phokoso la anthu amene ankayenda naye. Mmodzi wa opemphapemphawo dzina lake anali Batimeyu.

Batimeyu ndi mnzakeyo atamva kuti Yesu akudutsa anayamba kufuula kuti: “Ambuye, Mwana wa Davide, tichitireni chifundo!” (Mateyu 20:30) Pamene anthu ena pagululo anayamba kuwakalipira kuti akhale chete m’pamenenso Batimeyu ndi mnzakeyo ankafuula kwambiri. Kenako Yesu anaima atamva phokosolo ndipo anafunsa anthu amene anali nawo kuti aitane anthu amene ankakuwawo. Anthuwo anapita pamene panali opemphapemphawo n’kuuza mmodzi kuti: “Limba mtima, nyamuka, akukuitana.” (Maliko 10:49) Chifukwa cha chisangalalo munthu wakhunguyo anavula malaya ake akunja n’kunyamuka mofulumira kupita kwa Yesu.

Yesu anafunsa kuti: “Mukufuna kuti ndikuchitireni chiyani?” Anthuwo anayankha kuti: “Ambuye, titseguleni maso athu.” (Mateyu 20:32, 33) Yesu anagwidwa ndi chisoni ndipo anakhudza maso awo n’kuuza mmodzi wa akhunguwo kuti: “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa.” (Maliko 10:52) Anthu awiriwo anayamba kuona ndipo mosakayikira anayamba kulemekeza Mulungu. Gululo litaona zimene zinachitikazo linayambanso kulemekeza Mulungu. Anthu omwe anachiritsidwawo anayamba kutsatira Yesu.

Pamene Yesu ankadutsa mumzinda wa Yeriko anthu ambiri anabwera kuti aone munthu amene anachiritsa anthu akhunguwo. Anthuwo anayamba kum’panikiza kwambiri Yesu moti ena sankatha kumuona. Mmodzi mwa anthu amene sanathe kuona Yesu anali Zakeyu. Zakeyu anali mkulu wa okhometsa misonkho ku Yeriko komanso m’madera ena ozungulira. Chifukwa chakuti Zakeyu anali wamfupi sankatha kuona zimene zinkachitika. Choncho anathamangira kutsogolo n’kukakwera mumtengo wa mkuyu womwe unali m’mbali mwa njira imene Yesu ankadutsa kuti azitha kuona bwinobwino zonse zimene zinkachitika. Yesu atayandikira n’kuona Zakeyu ali mumtengo ananena kuti: “Zakeyu, fulumira tsika, chifukwa lero ndiyenera kukakhala m’nyumba mwako.” (Luka 19:5) Zakeyu anatsika mumtengowo ndipo anathamangira kunyumba kwake kuti akakonzekere kulandira mlendo wapaderayu.

Anthu ataona kuti Yesu akupita kunyumba kwa Zakeyu anayamba kung’ung’udza. Iwo ankaona kuti Yesu sankayenera kupita kunyumba kwa munthu amene ankamuona kuti ndi wochimwa. Zakeyu analemera chifukwa chobera anthu mwachinyengo potolera ndalama za misonkho.

Pamene Yesu ankalowa m’nyumba ya Zakeyu, anthu ankanena kuti: “Akupita kukakhala ndi munthu  wochimwa.” Koma Yesu ankaona kuti Zakeyu akhoza kulapa ndipo sanakhumudwe ndi zimene anthuwo ankanena. Kenako Zakeyu anaimirira n’kuuza Yesu kuti: “Ambuye, ine ndipereka ndithu hafu ya chuma changa kwa osauka. Ndipo chilichonse chimene ndinalanda munthu aliyense pomunamizira mlandu ndibweza kuwirikiza kanayi.”—Luka 19:7, 8.

Zakeyu anasonyeza kuti analapa kuchokera pansi pamtima. Zimene Zakeyu ananenazi zikusonyeza kuti akanagwiritsa ntchito mabuku amene ankalembamo misonkho kuwerengetsera ndalama zimene Ayuda osiyanasiyana ankapereka ndipo analonjeza kuti abweza ndalamazo kuwirikiza ka 4. Ndipo zimene analonjezazi zinaposa zimene Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti munthu azichita akatenga zinthu za munthu wina mwachinyengo. (Ekisodo 22:1; Levitiko 6:2-5) Komanso Zakeyu analonjeza kuti apereka hafu ya chuma chake chonse kwa anthu osauka.

Yesu anasangalala ndi zimene Zakeyu ananena posonyeza kuti walapa ndipo anamuuza kuti: “Lero chipulumutso chafika panyumba ino, chifukwa nayenso ndi mwana wa Abulahamu. Pakuti Mwana wa munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa anthu osochera.”—Luka 19:9, 10.

Yesu anali atangothandiza kumene anthu kumvetsa za ‘kusochera’ pamene ananena fanizo la mwana wosochera. (Luka 15:11-24) Koma tsopano Yesu anawasonyeza anthuwo chitsanzo cha munthu amene anali ngati wosochera ndipo wapezeka. Atsogoleri achipembedzo komanso anthu amene ankawatsatira anadandaula komanso kuimba Yesu milandu chifukwa chocheza ndi anthu ngati Zakeyu. Koma Yesu anapitirizabe kufunafuna ndi kuthandiza ana a Abulahamu amene anali osochera.