Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 28

N’chifukwa Chiyani Ophunzira a Yesu Sankasala Kudya?

N’chifukwa Chiyani Ophunzira a Yesu Sankasala Kudya?

MATEYU 9:14-17 MALIKO 2:18-22 LUKA 5:33-39

  • OPHUNZIRA A YOHANE ANAFUNSA YESU ZA KUSALA KUDYA

Yohane M’batizi anaponyedwa m’ndende patangopita nthawi yochepa Yesu atakapezeka ku mwambo wa Pasika wa mu 30 C.E. Yohane ankafuna kuti ophunzira ake akhale otsatira a Yesu. Pa miyezi yonse imene Yohane anali kundendeyi si ophunzira ake onse amene anakhala otsatira a Yesu.

Pamene Pasika wa mu 31 C.E. ankayandikira, ena mwa ophunzira a Yohane anapita kwa Yesu n’kukamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ife ndi Afarisi timasala kudya koma ophunzira anu sasala kudya?” (Mateyu 9:14) Afarisi ankaona kuti kusala kudya ndi mwambo wachipembedzo. Pa nthawi ina, Yesu anapereka fanizo la Mfarisi yemwe ankadziona kuti ndi wolungama. Popemphera Mfarisiyo ananena kuti: “Mulungu wanga, ndikukuyamikani chifukwa ine sindili ngati anthu enawa ayi. . . . Ine ndimasala kudya kawiri pa mlungu.” (Luka 18:11, 12) N’kutheka kuti ophunzira a Yohane ankasalanso kudya mwamwambo kapena ankasala kudya chifukwa cha chisoni poganizira kuti Yohane wamangidwa. Anthu ambiri anadabwa kuona kuti ophunzira a Yesu sankasala nawo kudya. Iwo ankaganiza kuti ophunzirawo sakukhudzidwa ndi zimene zamuchitikira Yohane.

Yesu anayankha pogwiritsa ntchito chitsanzo. Iye ananena kuti: “Anzake a mkwati samva chisoni ngati mkwatiyo ali nawo limodzi, si choncho kodi? Koma masiku adzafika pamene mkwatiyo adzachotsedwa pakati pawo, ndipo pa nthawiyo adzasala kudya.”—Mateyu 9:15.

Yohane anatchula Yesu ngati mkwati. (Yohane 3:28, 29) Pa nthawi imene Yesu anali ndi moyo ophunzira ake sankasala kudya. Koma Yesu ataphedwa, zinali zomveka kuti ophunzira ake akhale ndi chisoni komanso kuti asafune kudya. Komabe zinthu zinasintha Yesu ataukitsidwa. Ophunzirawo analibenso chifukwa chokhalira ndi chisoni kapena kusala kudya.

Kenako Yesu anafotokoza mafanizo awiri awa: “Palibe amene amasokerera chigamba cha nsalu yatsopano pamalaya akunja akale. Pakuti mphamvu yonse ya chigambacho ingakoke ndi kung’amba malayawo ndipo kung’ambikako kungawonjezeke kwambiri. Ndiponso anthu sathira vinyo watsopano m’matumba achikopa akale. Akachita zimenezo, matumba achikopawo amaphulika ndipo vinyoyo amatayika moti matumbawo amawonongeka. Koma anthu amathira vinyo watsopano m’matumba achikopa atsopano.” (Mateyu 9:16, 17) Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani?

Yesu ankafuna kuti ophunzira a Yohane amvetse chifukwa chimene ophunzira ake sankatsatira miyambo yakale ya Chiyuda monga kusala kudya. Yesu sanabwere kudzawonjezera miyambo yatsopano pa miyambo yakale, kapena kudzalimbikitsa anthu kutsatira miyambo yomwe inali itatsala pang’ono kusiya kugwira ntchito. Kupembedza kumene Yesu ankalimbikitsa kunali kosiyana ndi kumene Ayuda ankatsatira pa nthawiyo chifukwa iwo ankaphatikiza malamulo a Mulungu ndi zikhulupiriro za anthu. Ngati iye akanachita zimenezi, akanakhala ngati akusokerera chigamba chatsopano pamalaya akale kapena kuthira vinyo watsopano m’thumba lachikopa lakale.