Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 45

Anatulutsa Ziwanda Zambiri

Anatulutsa Ziwanda Zambiri

MATEYU 8:28-34 MALIKO 5:1-20 LUKA 8:26-39

  • ANATULUTSA ZIWANDA NDIPO ZINAKALOWA MU NKHUMBA

Pambuyo pokumana ndi zinthu zoopsa panyanja ophunzira a Yesu anafika kumtunda. Atangofika anakumana ndi amuna awiri oopsa ogwidwa ndi ziwanda. Anthuwa anatuluka m’manda ena omwe anali pafupi akuthamanga kuti akakumane ndi Yesu. Koma nkhaniyi imanena kwambiri za munthu m’modzi mwa anthu awiriwo, mwina chifukwa chakuti anali wachiwawa kwambiri komanso chifukwa chakuti anagwidwa ndi ziwanda kwa nthawi yaitali.

Munthu ameneyo anali womvetsa chisoni ndipo nthawi zambiri ankayenda maliseche. “Nthawi zonse, usiku ndi usana, anali kufuula m’manda ndi m’mapiri ndi kudzitematema ndi miyala.” (Maliko 5:5) Munthuyo anali waukali kwambiri moti anthu ankachita mantha kudutsa njira yakumandayo. Anthu anali atayesapo kumumanga koma ankadula maunyolo ndi zinthu zina zonse zimene ankamumanga nazo ndipo panalibe munthu amene akanamugonjetsa.

Choncho munthuyo atayandikira pamene panali Yesu, anagwada pamapazi ake ndipo ziwanda zija zinamuchititsa kukuwa kuti: “Kodi ndili nanu chiyani, Yesu, Mwana wa Mulungu Wam’mwambamwamba? Ndikukulumbiritsani pali Mulungu kuti musandizunze.” Zimene Yesu anachita zinasonyeza kuti ali ndi mphamvu yolamulira ngakhale ziwanda. Iye ananena kuti: “Tuluka mwa munthuyu, mzimu wonyansa iwe.”—Maliko 5:7, 8.

Munthuyu anali ndi ziwanda zambiri. Tikutero chifukwa Yesu atafunsa kuti: “Dzina lako ndani?” yankho lake linali lakuti: “Dzina langa ndine Khamu, chifukwa tilipo ambiri.” (Maliko 5:9) Kenako ziwandazo zinapempha Yesu kuti “asazilamule kuti zipite kuphompho.” Mosakayikira ziwandazo zinkadziwa zimene zidzachitikire mtsogoleri wawo Satana komanso zimene zidzachitike kwa izozo m’tsogolo.—Luka 8:31.

Pafupi ndi pamalowa panalinso nkhumba pafupifupi 2,000 zomwe zinkadya. Malinga ndi Chilamulo, nyama zimenezi zinali zodetsedwa ndipo Ayuda sankaloledwa kuweta nyamazi. Ndiyeno ziwanda zija zinauza Yesu kuti: “Titumizeni ku nkhumbazo, kuti tikalowe mwa zimenezo.” (Maliko 5:12) Yesu anauza ziwandazo kuti zikalowe mu nkhumba zija. Zitatero, nkhumba zonse zija zinathamangira kuphedi n’kudumphira m’nyanja ndipo zinamira.

 Amene ankayang’anira nkhumbazo ataona zimenezi anathamanga n’kukauza anthu a mumzinda ndi m’midzi zimene zinachitikazo. Ndipo anthu ambiri anabwera kuti adzaone zimene zinachitika. Anthuwa atafika anapeza munthu uja ali bwinobwino, atavala komanso atakhala pansi pafupi ndi Yesu.

Anthu amene anamva za nkhani imeneyi komanso amene anaona munthuyo, anachita mantha kwambiri ndipo sanamvetse kuti zimenezi zinkatanthauza chiyani. Ndiyeno anthuwa anauza Yesu kuti achoke m’dera lawolo. Pamene Yesu ankakwera boti kuti azipita, munthu uja anamuchonderera kuti apite nawo. Koma Yesu anamuuza kuti: “Pita kunyumba kwa achibale ako, ndipo ukawauze zonse zimene Yehova wakuchitira ndi chifundo chimene wakusonyeza.”—Maliko 5:19.

Nthawi zambiri Yesu ankauza anthu amene waachiritsa kuti asauze munthu aliyense zimene waachitira, chifukwa sankafuna kuti anthu azingotengeka maganizo ndi zimene amva zokhudza iyeyo. Koma pa nthawiyi, munthu amene Yesu anamutulutsa ziwandayu anali mboni yooneka ndi maso kuti Yesu anali ndi mphamvu pa ziwanda, ndipo munthuyu analalikira kwa anthu amene Yesu sakanatha kukumana nawo. Umboni umene munthuyu anapereka unathandiza kuti anthu amene anamva nkhani ya kufa kwa nkhumba zija asakhumudwe kwambiri. Choncho munthu uja anapita kukalalikira zimene Yesu anamuchitira kwa anthu okhala m’madera a ku Dekapole.