Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 27

Yesu Anaitana Mateyu

Yesu Anaitana Mateyu

MATEYU 9:9-13 MALIKO 2:13-17 LUKA 5:27-32

  • YESU ANAITANA MATEYU YEMWE ANALI WOKHOMETSA MSONKHO

  • KHRISTU ANKACHEZA NDI ANTHU OCHIMWA NDI CHOLINGA CHOTI AWATHANDIZE

Yesu anakhalabe m’dera la Kaperenao lomwe linali m’mbali mwa nyanja ya Galileya. Anthu ambiri ankabwera kwa iye ndipo ankawaphunzitsa Mawu a Mulungu. Kenako anaona Mateyu, yemwe ankadziwikanso kuti Levi, atakhala mu ofesi ya okhometsa msonkho. Yesu anamupatsa mwayi wapadera kwambiri pomuuza kuti: “Ukhale wotsatira wanga.”—Mateyu 9:9.

Mateyu ayenera kuti anali atamvapo zimene Yesu ankaphunzitsa komanso zinthu zodabwitsa zimene anachita m’deralo ngati mmene zinalili ndi Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane. Mofanananso ndi ophunzira 4 oyambirirawa, nayenso Mateyu anavomera kukhala wophunzira wa Yesu nthawi yomweyo. M’buku la Uthenga Wabwino limene Mateyuyo analemba, ananena kuti: ‘Nthawi yomweyo [Mateyu] ananyamuka ndi kutsatira’ Yesu. (Mateyu 9:9) Choncho Mateyu anasiya ntchito yake monga wotolera msonkho n’kukhala wotsatira wa Yesu.

Kenako patapita nthawi, Mateyu anakonza phwando lalikulu kunyumba kwake. N’kutheka kuti anachita zimenezi chifukwa choyamikira mwayi waukulu woitanidwa kuti akhale wophunzira wa Yesu. Kodi kupatula pa Yesu ndi ophunzira ake, ndaninso ena amene anaitanidwa ku phwandoli? Panalinso anthu ena otolera misonkho omwe Mateyu ankagwira nawo ntchito asanakhale wotsatira wa Yesu. Anthu amenewa ankatolera misonkho m’malo mwa boma la Aroma lomwe anthu ankadana nalo. Ankatoleranso misonkho ya ngalawa zimene zinkafika padoko, misonkho ya ngolo zimene zinkayenda m’misewu ikuluikulu komanso misonkho ya katundu wochokera ku mayiko ena. Kodi Ayuda ankawaona bwanji anthu okhometsa msonkhowa? Ankadana nawo chifukwa nthawi zambiri ankawalipiritsa ndalama zambiri kuposa zimene ankayenera kupereka. Kuphwandoko kunalinso anthu ‘ochimwa,’ omwe ankadziwika kuti ankachita zinthu zoipa.—Luka 7:37-39.

Afarisi omwe ankadziona kuti ndi olungama ataona Yesu akudya ndi anthu amenewa, anafunsa ophunzira ake kuti: “N’chifukwa chiyani mphunzitsi wanu amadya limodzi ndi okhometsa msonkho ndi anthu ochimwa?” (Mateyu 9:11) Yesu atamva zimene anthuwa ankanena, anawayankha kuti: “Anthu abwinobwino safuna dokotala, koma odwala ndi amene amamufuna. Choncho pitani mukaphunzire tanthauzo la mawu akuti, ‘Ndikufuna chifundo, osati nsembe.’ Chifukwa ine sindinabwere kudzaitana anthu olungama, koma ochimwa.” (Mateyu 9:12, 13; Hoseya 6:6) Afarisi ankanena mwachiphamaso kuti Yesu ndi Mphunzitsi, koma anaphunzirapo kanthu pa zimene anawayankha.

Ndipotu Mateyu anaitana anthu okhometsa misonkho komanso anthu ochimwa ndi cholinga choti adzamvetsere uthenga wa Yesu komanso kuti adzachiritsidwe mwauzimu. Kuphwandoko ‘kunali anthu ambiri ndipo anayamba kutsatira’ Yesu. (Maliko 2:15) Yesu ankafuna kuthandiza anthu amenewa kuti akhale pa ubwenzi wabwino ndi Mulungu. Mosiyana ndi Afarisi omwe ankadziona ngati olungama, Yesu sankanyoza anthu amenewa. Iye ankamvera chisoni komanso chifundo anthu ngati amenewa ndipo ankawathandiza mwauzimu ngati mmene dokotala amathandizira munthu amene akudwala.

Yesu anachitira chifundo okhometsa msonkho komanso ochimwa, osati kuti ankasangalala ndi machimo awowo, koma ankafuna kuwathandiza mokoma mtima ngati mmene anathandizira anthu ena amene ankadwala. Mwachitsanzo, kumbukirani kuti pochiritsa munthu wina wakhate, Yesu anamukhudza chifukwa chomumvera chifundo ndipo anamuuza kuti: “Ndikufuna. Khala woyera.” (Mateyu 8:3) Nafenso tingachite bwino kuyesetsa kuchitira chifundo komanso kuthandiza anthu makamaka mwauzimu.