Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 63

Yesu Anafotokoza Zoyenera Kuchita Anthu Akakhumudwitsana Komanso Ngati Wina Wachita Tchimo

Yesu Anafotokoza Zoyenera Kuchita Anthu Akakhumudwitsana Komanso Ngati Wina Wachita Tchimo

MATEYU 18:6-20 MALIKO 9:38-50 LUKA 9:49, 50

  • ZIMENE ANTHU AYENERA KUCHITA AKAKHUMUDWITSANA

  • NGATI M’BALE WAKO WACHITA TCHIMO

Yesu anagwiritsa ntchito fanizo lonena za ana pofuna kuphunzitsa otsatira ake kuti akhale odzichepetsa. Anapereka fanizoli pofuna kuwathandiza kuti azidziona ngati ana omwe amakhala odzichepetsa komanso omwe safuna kukhala apamwamba kuposa anzawo. Iye analimbikitsa ophunzira akewo kuti ‘azilandira ana aang’ono m’dzina lake zomwe zikanakhala ngati akulandiranso Yesu.’—Mateyu 18:5.

Atumwiwo anali atangokangana zoti wamkulu ndani, choncho Yesu atanena fanizoli ophunzirawo anaona ngati akuwadzudzula. Ndiyeno mtumwi Yohane anayambitsa nkhani ina yomwe inali itangochitika. Iye anati: “Tinaona munthu wina akutulutsa ziwanda m’dzina lanu, choncho ife tinamuletsa chifukwa sakukutsatirani pamodzi ndi ife.”—Luka 9:49.

Kodi Yohane ankaona kuti ndi atumwi okha omwe ankayenera kuchiritsa anthu komanso kutulutsa ziwanda? Ngati zinali choncho, nanga zinatheka bwanji kuti Myuda ameneyu azikwanitsa kutulutsa mizimu yoipa? Yohane ankaona kuti munthu ameneyu sankayenera kuchita zinthu zamphamvu chifukwa sankayenda limodzi ndi Yesu komanso atumwi.

Yohane anadabwa Yesu atamuuza kuti: “Musamuletse, chifukwa palibe amene adzachita ntchito zamphamvu m’dzina langa, ndi kundinenera zachipongwe mwamsanga. Pakuti amene sakutsutsana ndi ife ali kumbali yathu. Chifukwa aliyense wokupatsani kapu ya madzi akumwa chifukwa chakuti ndinu ake a Khristu, ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika ayi.”—Maliko 9:39-41.

Munthuyo sankafunika kuchita kuyenda ndi atumwiwo kuti asonyeze kuti ali kumbali ya Yesu. Tikutero chifukwa pa nthawiyi mpingo wachikhristu unali utatsala pang’ono kukhazikitsidwa choncho chifukwa chakuti munthuyu sankayenda ndi Yesu, sizikutanthauza kuti ankamutsutsa kapena kulimbikitsa chipembedzo chonyenga. Munthuyo anasonyeza kuti ankakhulupirira Yesu ndipo zimene Yesu ananena zinasonyeza kuti munthuyo sadzalephera kulandira mphoto yake.

Koma zikanakhala zoopsa kwambiri ngati munthuyo akanakhumudwa ndi zimene atumwiwo ankachita kapena kulankhula. Yesu ananena kuti: “Aliyense wokhumudwitsa mmodzi wa tiana tokhulupirirati, zingakhale bwino kwambiri kuti amumangirire chimwala champhero m’khosi mwake, ngati chimene bulu amayendetsa, ndi kumuponya m’nyanja.” (Maliko 9:42) Kenako Yesu ananena kuti otsatira ake ayenera kusiya zinthu zimene zingawapunthwitse ngakhale zitakhala zofunika kwambiri ngati dzanja, phazi kapena diso. Kulibwino kukhala opanda zinthu zimenezi n’kukalowa mu Ufumu wa Mulungu kusiyana n’kukhala ndi zinthu zimenezi koma n’kukawonongedwa ku Gehena (Chigwa cha Hinomu). Atumwiwo ayenera kuti ankachidziwa bwino chigwa chimenechi, chomwe chinali pafupi ndi mzinda wa Yerusalemu ndipo kumalo amenewa ankawotcherako zinyalala. Choncho atumwiwo anamvetsa kuti Yesu ankatanthauza kuti munthuyo akadzawonongedwa sadzakhalanso ndi moyo.

Yesu anachenjezanso kuti: “Samalani anthu inu kuti musanyoze mmodzi wa tianati, chifukwa ndikukutsimikizirani kuti angelo awo kumwamba amaona nkhope ya Atate wanga wakumwamba nthawi zonse.” Kodi tiana timeneti tinali tofunika bwanji kwa Atate ake? Pofuna kuthandiza ophunzira ake kumvetsa  mmene Atate ake amaonera tianati, Yesu anafotokoza za munthu wina amene anali ndi nkhosa 100 koma kenako nkhosa imodzi inasowa. Munthuyo anasiya nkhosa 99 n’kukafunafuna imodzi yomwe inasowayo. Ataipeza anasangalala kwambiri ndi nkhosa imeneyo kusiyana ndi nkhosa 99 zomwe sizinasochere zija. Ndiyeno Yesu ananenanso kuti: “Atate wanga wakumwamba sakufuna kuti mmodzi wa tianati akawonongeke.”—Mateyu 18:10, 14.

Chifukwa choganizira atumwi ake omwe ankakangana kuti ndani adzakhale wamkulu, Yesu anawalimbikitsa kuti: “Khalani ndi mchere mwa inu nokha, ndipo sungani mtendere pakati panu.” (Maliko 9:50) Mchere umathandiza kuti chakudya chikhale chokoma. Mchere wophiphiritsa umathandiza kuti munthu asavutike kuvomereza zimene mnzake akunena zomwe zimachititsa kuti akhale pamtendere. Ndipotu anthu sakhala pamtendere ngati akukangana.—Akolose 4:6.

Kenako Yesu anafotokoza zimene munthu angachite ngati munthu wina wachita tchimo lalikulu. Iye ananena kuti: “Ngati m’bale wako wachimwa, upite kukam’fotokozera cholakwacho panokha iwe ndi iyeyo. Ngati wakumvera, ndiye kuti wabweza m’bale wakoyo.” Koma bwanji ngati munthuyo sanamvere? Yesu ananena kuti: “Upiteko ndi munthu wina mmodzi kapena awiri, kuti nkhani yonse ikatsimikizike ndi pakamwa pa mboni ziwiri kapena zitatu.” Ngati munthuyo sakusintha uuze “mpingo,” kutanthauza akulu a mumpingo omwe ali ndi udindo wodziwa zoyenera kuchita pa nkhaniyo. Koma bwanji ngati munthuyo sanamverenso akuluwo? “Kwa iwe akhale ngati munthu wochokera mu mtundu wina komanso ngati wokhometsa msonkho.” Yesu anatchula za anthu amitundu ina komanso okhometsa misonkho chifukwa Ayuda sankagwirizana ndi anthu amenewa.—Mateyu 18:15-17.

Akulu amafunika kutsatira kwambiri zimene Mawu a Mulungu amanena. Ngati akuluwo atapeza kuti munthuyo ndi wolakwa, zimene angasankhe kuchita pa nkhaniyo ‘zidzakhala zitamangidwanso kumwamba.’ Koma ngati akuluwo atapeza kuti munthuyo ndi wosalakwa, ndiye kuti ‘zidzakhalanso zomasulidwa kumwamba.’ Malangizo amenewa anayamba kugwira ntchito mpingo wachikhristu utakhazikitsidwa. Yesu anafotokozanso zimene zimachitika akulu akamakambirana nkhani zikuluzikulu ngati zimenezi. Iye ananena kuti: “Pakuti kulikonse kumene awiri kapena atatu asonkhana m’dzina langa, ine ndidzakhala pakati pawo.”—Mateyu 18:18-20.