Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 39

Tsoka kwa M’badwo Umene Sunamvere

Tsoka kwa M’badwo Umene Sunamvere

MATEYU 11:16-30 LUKA 7:31-35

  • YESU ANADZUDZULA ANTHU A M’MIZINDA INA

  • YESU ANKALIMBIKITSA ANTHU

Yesu ankalemekeza kwambiri Yohane M’batizi, koma kodi anthu ena ankamuona bwanji Yohane? Yesu ananena kuti: “M’badwo uwu . . . uli ngati ana aang’ono amene amakhala pansi m’misika n’kumafuulira anzawo osewera nawo kuti, ‘Tinakuimbirani chitoliro, koma simunavine. Tinalira mofuula, koma inu simunadzigugude pachifuwa chifukwa cha chisoni.’”—Mateyu 11:16, 17.

Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Pofuna kuwathandiza kuti amvetse mfundo yake, Yesu ananena kuti: “Yohane anabwera ndipo sanali kudya kapena kumwa. Koma anthu ankanena kuti, ‘Ali ndi chiwanda.’ Kunabwera Mwana wa munthu ndipo anali kudya ndi kumwa, koma anthu akunenabe kuti, ‘Taonani! Munthu wosusuka ndi wokonda kwambiri vinyo, bwenzi la okhometsa msonkho ndi ochimwa.’” (Mateyu 11:18, 19) Yohane ankakhala ngati Mnaziri moti sankamwa vinyo koma anthu a m’nthawi yake ankanena kuti anali ndi chiwanda. (Numeri 6:2, 3; Luka 1:15) Pomwe Yesu anali ngati anthu ena onse. Iye ankadya komanso kumwa mosapitirira malire koma anthu ankamunena kuti ndi wosusuka. Zimenezi zikusonyeza kuti n’zovuta kusangalatsa wina aliyense.

Yesu anayerekezera anthu a m’nthawi yake ndi ‘ana aang’ono amene anali atakhala pansi m’misika’ omwe ana ena atawaimbira chitoliro sanaimirire kuti avine kapena kulira pamenenso anzawo ankalira. Kenako Yesu anati: “Mulimonsemo, nzeru imatsimikizirika kuti ndi yolungama chifukwa cha ntchito zake.” (Mateyu 11:16, 19) Choncho zimene Yesu ndi Yohane ankachita, kapena kuti “ntchito” zawo, zinasonyeza kuti zonse zimene anthu ankanena zokhudza Yesu ndi Yohane zinali zabodza.

Yesu atafotokoza za m’badwo wosamverawo, anadzudzula anthu a m’mizinda ya Korazini, Betsaida komanso Kaperenao. Yesu anachita zinthu zodabwitsa m’mizinda imeneyi. Iye ananena kuti ngati akanachitira zinthu zodabwitsazo anthu a mumzinda wa Turo ndi Sidoni, yomwe inali m’chigawo cha Foinike, anthuwo akanalapa. Anatchulanso mzinda wa Kaperenao komwe ankakhala nthawi zambiri. Kumenekonso anthu ambiri sanamvere uthenga wake. Pofotokoza za mzinda umenewu, Yesu anati: “Chilango cha Sodomu pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha Kaperenao.”—Mateyu 11:24.

Kenako Yesu analemekeza Atate ake, amene amabisira “anthu anzeru ndi ozindikira” zinthu zauzimu zomwe ndi zamtengo wapatali koma amaziulula kwa anthu otsika omwe ali ngati tiana. (Mateyu 11:25) Yesu anauza anthu omwe anali ngati tianawa kuti: “Bwerani kwa ine nonsenu ogwira ntchito yolemetsa ndi olemedwa, ndipo ndidzakutsitsimutsani. Senzani goli langa ndipo phunzirani kwa ine, chifukwa ndine wofatsa ndi wodzichepetsa, ndipo mudzatsitsimulidwa, pakuti goli langa ndi lofewa ndipo katundu wanga ndi wopepuka.”—Mateyu 11:28-30.

Kodi Yesu anatsitsimula bwanji anthuwo? Atsogoleri achipembedzo ankazunza anthu powakakamiza kuti azitsatira miyambo yomwe inali yopanikiza. Mwachitsanzo, ankawakakamiza kuti azitsatira malamulo okhudza Sabata omwe anawakhwimitsa kwambiri chifukwa cha miyambo imene ankatsatira. Koma Yesu anawatsitsimula powaphunzitsa zinthu zolondola zokhudza Mulungu, zomwe sizinasakanikirane ndi miyambo yawoyo. Analimbikitsa anthu amene ankavutika chifukwa cha machimo komanso amene ankaponderezedwa ndi olamulira andale. Yesu anafotokozera anthu amenewa zimene angachite kuti machimo awo akhululukidwe komanso kuti akhale pamtendere ndi Mulungu.

Aliyense amene angavomereze kunyamula goli la Yesu akhoza kudzipereka n’kuyamba kutumikira Mulungu yemwenso ndi Atate wathu wachifundo. Kuchita zimenezi si kovuta chifukwa malamulo a Mulungu ndi osalemetsa.—1 Yohane 5:3.