MATEYU 16:13-27 MALIKO 8:22-38 LUKA 9:18-26

  • YESU ANACHIRITSA MUNTHU WAKHUNGU

  • PETULO ANALANDIRA MAKIYI A UFUMU

  • YESU ANANENERATU ZA IMFA NDI KUUKITSIDWA KWAKE

Yesu ndi ophunzira ake anafika ku Betsaida. Ali kumeneko anthu anamubweretsera munthu wakhungu ndipo anamupempha kuti amukhudze kuti ayambe kuona.

Yesu anagwira dzanja la munthuyo n’kupita naye kunja kwa mudziwo. Atamulavulira m’maso anamufunsa kuti: “Kodi ukuona chilichonse?” Munthuyo anayankha kuti: “Ndikuona anthu, chifukwa ndikuona zinthu zooneka ngati mitengo, koma zikuyendayenda.” (Maliko 8:23, 24) Yesu anamugwira m’maso ndipo munthuyo anayamba kuona. Kenako anamuuza kuti azipita kwawo n’kumulamula kuti asalowenso m’mudziwo.

Ndiyeno Yesu ndi ophunzira ake analowera kumpoto m’dera la Kaisareya wa Filipi. Derali linali lokwera ndipo ulendowo unali wautali makilomita pafupifupi 40. Munthu akakhala m’derali ankatha kuona phiri la Herimoni lomwe linali kumpoto chakum’mawa. Pamwamba pa phirili pankagwa chipale chofewa kapena kuti sinoo. Ndipo ulendo wopita ku Kaisareya uyenera kuti unkatenga masiku angapo.

Ali pa ulendowu Yesu anapita kumalo a yekha kuti akapemphere. Pa nthawiyi n’kuti kutatsala miyezi 9 kapena 10 kuti aphedwe koma Yesu ankadera nkhawa kwambiri ophunzira ake. Ophunzira ambiri anali atasiya kuyenda naye ndipo ena anali atakhumudwa kapena atasokonezeka maganizo. Iwo sankamvetsa kuti n’chifukwa chiyani Yesu anakana kuti anthu amuveke ufumu kapena mwina sankamvetsa chifukwa chimene Yesu sanachitire zizindikiro kuti anthu amudziwe kuti iye ndi ndani.

Ophunzirawo atafika pamalo pamene Yesu ankapemphera, anawafunsa kuti: “Kodi anthu akumanena kuti Mwana wa munthu ndani?” Iwo anayankha kuti: “Ena akumanena kuti Yohane M’batizi, ena akumati Eliya, koma ena akuti Yeremiya kapena mmodzi wa aneneri.” Anthu ankaganiza kuti mwina Yesu ndi mmodzi mwa anthu amenewa ndipo wauka kwa akufa. Pofuna kudziwa maganizo a ophunzira akewo Yesu anawafunsa kuti: “Nanga inuyo mumati ndine ndani?” Petulo anayankha mwamsanga kuti: “Ndinu Khristu, Mwana wa Mulungu wamoyo.”—Mateyu 16:13-16.

Yesu ananena kuti Petulo anali wodala chifukwa Mulungu ndi amene anamuululira zimenezi. Ananenanso kuti: “Ndikukuuza kuti, Iwe ndiwe Petulo, ndipo pathanthwe ili ndidzamangapo mpingo wanga. Zipata za Manda sizidzaugonjetsa.” Ponena mawu amenewa Yesu ankatanthauza kuti iyeyo adzayambitsa mpingo ndipo anthu omwe adzakhale mumpingomo sadzakhala m’manda mpaka kalekale ngati atakhala okhulupirika pa nthawi imene ali ndi moyo. Analonjezanso Petulo kuti: “Ine ndidzakupatsa makiyi a ufumu wakumwamba.”—Mateyu 16:18, 19.

Sikuti Yesu ponena mawu amenewa anapatsa Petulo malo apamwamba kuposa atumwi enawo kapena kuti anakhala maziko a mpingo. Yesu ndiye anali Thanthwe limene panamangidwa mpingo. (1 Akorinto 3:11; Aefeso 2:20) Koma Petulo ankayembekezera kupatsidwa makiyi atatu. Iye anapatsidwa makiyi otsegulira magulu a anthu mwayi woti alowe mu Ufumu wakumwamba.

 Petulo anagwiritsa ntchito kiyi woyamba pa Pentekosite wa mu 33 C.E., posonyeza Ayuda olapa komanso anthu otembenukira kuchiyuda zimene akanachita kuti apulumuke. Anagwiritsa ntchito kiyi wachiwiri pothandiza Asamariya kuti nawonso akhale ndi mwayi wolowa mu Ufumu wa Mulungu. Kenako, mu 36 C.E., Petulo anagwiritsa ntchito kiyi wachitatu pothandiza anthu omwe sanali Ayuda komanso osadulidwa kuti alowe mu Ufumuwu. Pa nthawiyi Petulo anathandiza Koneliyo ndi anthu ena.—Machitidwe 2:37, 38; 8:14-17; 10:44-48.

Kenako Yesu ananeneratu za mavuto komanso za imfa yake zimene ankayembekezera kukumana nazo ku Yerusalemu ndipo atumwi ake anavutika maganizo atamva zimenezi. Chifukwa chosamvetsa kuti Yesu adzaukitsidwa n’kukhalanso ndi moyo kumwamba, Petulo anatengera Yesu pambali n’kumudzudzula. Iye anati: “Dzikomereni mtima Ambuye. Musalole kuti zimenezi zikuchitikireni ngakhale pang’ono.” Koma Yesu anatembenuka n’kumuuza kuti: “Pita kumbuyo kwanga, Satana! Ndiwe chopunthwitsa kwa ine, chifukwa zimene umaganiza si maganizo a Mulungu, koma maganizo a anthu.”—Mateyu 16:22, 23.

Ndiyeno Yesu anaitana anthu ena kuwonjezera pa atumwi ake aja ndipo anafotokoza kuti sizidzakhala zophweka kuti munthu akhale wotsatira wake. Iye anati: “Ngati munthu akufuna kunditsatira, adzikane yekha ndi kunyamula mtengo wake wozunzikirapo, ndi kunditsatira mosalekeza. Pakuti aliyense wofuna kupulumutsa moyo wake adzautaya. Koma aliyense wotaya moyo wake chifukwa cha ine ndi uthenga wabwino, adzaupulumutsa.”—Maliko 8:34, 35.

Choncho kuti azikondedwa ndi Yesu, otsatira akewo ayenera kukhala olimba mtima komanso odzipereka kwambiri. Yesu ananena kuti: “Aliyense wochita manyazi ndi ine, komanso ndi mawu anga mu m’badwo wachigololo ndi wochimwa uno, Mwana wa munthu adzachitanso naye manyazi akadzafika mu ulemerero wa Atate wake limodzi ndi angelo oyera.” (Maliko 8:38) Choncho Yesu akadzabwera “adzapatsa aliyense mphoto malinga ndi makhalidwe ake.”—Mateyu 16:27.