Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 60

Anaona Ulemelero wa Khristu Atasandulika

Anaona Ulemelero wa Khristu Atasandulika

MATEYU 16:28–17:13 MALIKO 9:1-13 LUKA 9:27-36

  • ANAONA YESU ATASANDULIKA

  • ATUMWI ANAMVA MAWU A MULUNGU

Pamene Yesu ankaphunzitsa anthu m’dera la Kaisareya wa Filipi ananena zinthu zomwe zinadabwitsa kwambiri atumwi ake. Derali linali pamtunda wa makilomita 25 kuchokera ku phiri la Herimoni. Iye anauza atumwiwo kuti: “Ndithu ndikukuuzani kuti pali ena mwa amene aimirira pano amene sadzalawa imfa m’pang’ono pomwe kufikira choyamba ataona Mwana wa munthu akubwera monga mfumu.”—Mateyu 16:28.

Ophunzirawo ayenera kuti anadabwa kuti Yesu ankatanthauza chiyani. Patatha mlungu umodzi, Yesu anatenga atumwi ake atatu omwe mayina awo anali Petulo, Yakobo ndi Yohane ndipo anakwera nawo m’phiri lalitali. Zikuoneka kuti anakwera m’phirili usiku. Tikutero chifukwa pa nthawiyi ophunzira atatuwo anali ndi tulo. Pamene Yesu ankapemphera, anasandulika iwo akuona. Atumwiwo anaona nkhope ya Yesu ikuwala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinali zoyera kwambiri komanso zinkanyezimira.

Kenako panaonekera anthu awiri ndipo anawazindikira kuti anali “Mose ndi Eliya.” Anthuwa anayamba kukambirana ndi Yesu za “mmene adzachokere m’dzikoli, ku Yerusalemu.” (Luka 9:30, 31) Mawu akuti mmene Yesu adzachokere m’dzikoli ankatanthauza za imfa ya Yesu komanso kuukitsidwa kwake, zimene anali atangofotokozera ophunzira akewo. (Mateyu 16:21) Zimene Mose ndi Eliya ankakambirana ndi Yesuzo zinasonyezeratu kuti zinali zosatheka kuti Yesu apewe imfa yochititsa manyazi ngati mmene Petulo ankaganizira pamene anauza Yesu kuti adzimvere chisoni.

Pa nthawiyi atumwi atatuwo anaona komanso kumvetsera zinthu zodabwitsazi chifukwa tulo tija tinali titawathera. Atumwiwa ankaona masomphenya koma zimene zinkachitikazo zinkaoneka ngati zenizeni moti Petulo anauza Yesu kuti: “Rabi, ndi bwino ife tizikhala pano, choncho timange mahema atatu pano, limodzi lanu, limodzi la Mose, ndi lina la Eliya.” (Maliko 9:5) N’kutheka kuti Petulo ankafuna kumanga mahemawo kuti masomphenyawo asathere pomwepo.

Petulo ali mkati molankhula, mtambo wowala kwambiri unawaphimba ndipo mumtambomo munamveka mawu akuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, amene ndikukondwera naye, muzimumvera.” Atumwiwo atamva mawu a Mulungu anagwada mpaka nkhope zawo pansi koma Yesu anawauza kuti: “Dzukani, musaope.” (Mateyu 17:5-7) Pamene atumwiwo ankadzuka sanaone munthu aliyense koma Yesu yekha chifukwa masomphenyawo anali atatha. Pamene ankatsika m’phirimo kutacha, Yesu anawalamula kuti: “Musauze wina aliyense za masomphenya amenewa kufikira Mwana wa munthu ataukitsidwa kwa akufa.”—Mateyu 17:9.

Atumwi aja ataona Eliya m’masomphenya anadabwa kwambiri moti anafunsa Yesu kuti: “Nanga n’chifukwa chiyani alembi amanena kuti Eliya ayenera kubwera choyamba?” Yesu anawayankha kuti: “Eliya anabwera kale ndipo iwo sanamuzindikire.” (Mateyu 17:10-12) Pamenepa Yesu ankanena za Yohane M’batizi yemwe anagwira ntchito yofanana ndi ya Eliya. Eliya anakonza njira ya Elisa ndipo Yohane anakonza njira ya Khristu.

Masomphenya amenewa analimbikitsa kwambiri Yesu komanso atumwiwo. Anasonyeza ulemelero umene Khristu adzakhale nawo mu Ufumu wake. Choncho ophunzirawo anaona “Mwana wa munthu akubwera monga mfumu” ngati mmene Yesu anawalonjezera. (Mateyu 16:28) Pa nthawi imene atumwiwo anali m’phiri muja ‘anaona ndi maso awo ulemerero wake.’ Ngakhale kuti Afarisi ankafuna kuti Yesu awaonetse chizindikiro chosonyeza kuti iye ndi Mfumu yosankhidwa ndi Mulungu, Yesu sanawaonetse chizindikiro chilichonse. Koma ophunzira a Yesu anapatsidwa mwayi woona Yesu akusandulika, zomwe zinawathandiza kutsimikizira kuti malonjezo onena za Ufumu adzakwaniritsidwa. Moti patapita nthawi Petulo analemba kuti: “Mawu aulosiwa ndi odalirika kwambiri.”—2 Petulo 1:16-19.