MATEYU 17:22–18:5 MALIKO 9:30-37 LUKA 9:43-48

  • YESU ANANENANSO ZA IMFA YAKE

  • ANALIPIRA MSONKHO NDI NDALAMA IMENE ANAIPEZA M’KAMWA MWA NSOMBA

  • KODI NDANI ADZAKHALE WAMKULU MU UFUMU?

Yesu atachoka m’dera la Kaisareya wa Filipi komwe anasandulika komanso kuchiritsa mnyamata yemwe anali ndi chiwanda uja, analowera ku Kaperenao. Pa ulendowu anali ndi ophunzira ake okha ndipo analowa m’deralo mobisa chifukwa ‘sankafuna kuti aliyense adziwe zoti ali kumeneko.’ (Maliko 9:30) Zimenezi zinachititsa kuti Yesu akhale ndi nthawi yokwanira yoti akonzekeretse ophunzira ake za imfa yake komanso za ntchito imene ophunzirawo adzagwire iye akadzachoka. Iye anawauza kuti: “Mwana wa munthu adzaperekedwa m’manja mwa anthu, ndipo adzamupha. Koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.”—Mateyu 17:22, 23.

Aka sikanali koyamba kuti Yesu auze ophunzira ake za nkhani imeneyi. Nthawi ina Yesu anawauza kuti ayenera kuphedwa koma Petulo sankafuna kuti zimenezi zichitike. (Mateyu 16:21, 22) Ndipo atumwi atatu anaona Yesu akusandulika komanso anamva Mose ndi Eliya akukambirana ndi Yesu mmene “adzachokere m’dzikoli.” (Luka 9:31) Ophunzirawo “anamva chisoni kwambiri” ndi zimene Yesu anawauzazo ngakhale kuti sanamvetse bwinobwino zimene ankatanthauza. (Mateyu 17:23) Koma sanamufunse zambiri pa nkhaniyi chifukwa ankachita mantha.

Kenako Yesu anafika ku Kaperenao, kumene ankakhala nthawi zambiri komanso komwe atumwi ake angapo ankachokera. Ali kumeneko, anthu amene ankatolera msonkho wapakachisi anakumana ndi Petulo n’kumufunsa kuti: “Kodi mphunzitsi wanu amapereka madalakima awiri a msonkho [wapakachisi]?” Iwo anachita zimenezi mwina pofuna kumuimba Yesu mlandu wosalipira msonkho.—Mateyu 17:24.

Petulo anayankha kuti: “Inde amapereka.” Yesu ali kunyumba imene ankakhala anali atadziwa kale zimene zinachitika. Choncho m’malo modikira kuti Petulo afotokoze zimene zinachitikazo, Yesu anamufunsa kuti: “Simoni, ukuganiza bwanji? Kodi mafumu a dziko lapansi amalandira ndalama za ziphaso kapena za msonkho kuchokera kwa ndani? Kuchokera kwa ana awo kapena kwa anthu achilendo?” Petulo anayankha kuti: “Kuchokera kwa anthu achilendo.” Ndiyeno Yesu anamuuza kuti: “Choterotu ana sayenera kukhoma msonkho.”—Mateyu 17:25, 26.

Atate ake a Yesu ndi Mfumu ya chilengedwe chonse ndipo ndi Amene anthu ankalambira akapita kukachisi. Choncho mwalamulo Mwana wa Mulungu sankafunika kupereka msonkho wapakachisi. Koma Yesu ananena kuti: “Kuti tisawakhumudwitse, pita kunyanja, ukaponye mbedza, ndipo ukatenge nsomba yoyambirira kuwedza. Ukakaikanula kukamwa kwake, ukapezako khobidi limodzi lasiliva [kapena kuti khobidi la siteta, lomwe linali lofanana ndi madalakima 4]. Ukalitenge n’kukhomera msonkho wako ndi wanga.”—Mateyu 17:27.

Kenako ophunzira onse atakumana pamodzi ankafuna kufunsa Yesu kuti ndi “ndani adzakhale wamkulu mu ufumu. Ophunzirawa ankachita mantha kufunsa Yesu za imfa yake koma chodabwitsa n’choti pa nthawiyi anamufunsa za tsogolo lawo. Yesu ankadziwa chimene chinawachititsa kufunsa funso limeneli. Pa ulendo wawo wobwerera ku Kaperenao, Yesu anamva ophunzirawo akukangana za nkhani imeneyi ngakhale kuti ankabwera m’mbuyo mwake. Choncho anawafunsa kuti: “Munali kukangana chiyani m’njira?” (Maliko 9:33) Ophunzirawo anachita manyazi moti sanayankhe chilichonse chifukwa ankakangana kuti wamkulu ndani pakati pawo. Koma kenako atumwiwo anafunsa Yesu nkhani yomwe ankakambirana ija kuti: “Ndani kwenikweni amene adzakhala wamkulu kwambiri mu ufumu wakumwamba?”—Mateyu 18:1.

Zinali zodabwitsa kuti ophunzirawo ankakangana za nkhani imeneyi ngakhale kuti anali ataona  komanso kuphunzira zinthu zambiri kuchokera kwa Yesu kwa zaka pafupifupi zitatu. Komabe, ophunzirawo anali ochimwa komanso anakulira m’dera limene anthu ambiri ankaona kuti kukhala ndi udindo wapamwamba n’kofunika kwambiri. Komanso Yesu anali atangolonjeza kumene Petulo kuti adzamupatsa makiyi a Ufumu. Mwina chifukwa cha zimenezi Petulo ankadziona kuti anali wapamwamba kuposa anzakewo. N’kuthekanso kuti Yakobo ndi Yohane anali ndi maganizo ngati a Petulo chifukwa anaona Yesu akusandulika.

Kaya panali zifukwa zina zimene zinkawachititsa kuganiza zimenezi, koma Yesu anachita zinthu zomwe zinawathandiza kusintha mmene ankaganizira. Iye anaitana kamwana n’kukaimika pakati pawo kenako anauza ophunzirawo kuti: “Mukapanda kutembenuka n’kukhala ngati ana aang’ono, simudzalowa mu ufumu wakumwamba. Chotero, aliyense amene adzadzichepetsa ngati mwana wamng’ono uyu ndi amene adzakhala wamkulu kwambiri mu ufumu wakumwamba. Ndiponso aliyense wolandira mwana wamng’ono ngati ameneyu m’dzina langa walandiranso ine.”—Mateyu 18:3-5.

Imeneyitu inali njira yabwino yophunzitsira. Yesu sanakwiyire ophunzira akewo komanso sanawanene kuti anali odzikonda kapena ofuna zinthu zapamwamba. M’malomwake anapezerapo mwayi woti awaphunzitse khalidwe lofunika kwambiri. Ana sakhala ndi udindo uliwonse ndipo samadziona kuti ndi apamwamba kuposa ana ena. Pamenepa Yesu ankalimbikitsa ophunzira ake kuti nawonso azidziona choncho. Kenako anamaliza n’kuwauza kuti: “Aliyense wokhala ngati wamng’ono pakati pa nonsenu ndi amene ali wamkulu.”—Luka 9:48.