Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 51

Anaphedwa pa Tsiku Lokondwerera Kubadwa

Anaphedwa pa Tsiku Lokondwerera Kubadwa

MATEYU 14:1-12 MALIKO 6:14-29 LUKA 9:7-9

  • HERODE ANALAMULA KUTI YOHANE M’BATIZI ADULIDWE MUTU

Pa nthawi imene atumwi a Yesu ankagwira ntchito yolalikira ku Galileya n’kuti Yohane M’batizi, yemwe anali woyamba kulengeza za kubwera kwa Yesu, atakhala m’ndende kwa zaka pafupifupi ziwiri.

Yohane anadzudzula poyera Mfumu Herode Antipa chifukwa chokwatira Herodiya, yemwe anali mkazi wa mchimwene wake Filipo. Herode anathetsa banja ndi mkazi wake woyamba kuti akwatire Herodiya. Mogwirizana ndi Chilamulo cha Mose, chimene Herode ankanena kuti ankatsatira, ndiye kuti Herode ankachita chigololo komanso ukwati umenewu unali wosavomerezeka. Chifukwa chokwiya ndi zimene Yohane ananena, Herode anatsekera Yohane m’ndende ndipo mwina Herodiya ndi amene analimbikitsa Herode kuti achite zimenezi.

Herode sankadziwa chilango chimene akanapatsa Yohane chifukwa anthu “anali kukhulupirira kuti [Yohane] ndi mneneri.” (Mateyu 14:5) Koma Herodiya ankadziwa kale zoti achite ndi Yohane chifukwa “anam’sungira chidani mumtima” moti ankafuna kupeza njira yoti amuphere. (Maliko 6:19) Kenako panachitika zinthu zina zomwe zinamupatsa mpata Herodiya woti achite zimene ankafuna.

Chikondwerero cha Pasika wa mu 32 C.E. chitatsala pang’ono kuchitika, Herode anakonza phwando lalikulu lokondwerera tsiku lake lakubadwa. Ku phwandoli kunabwera nduna za boma la Herode, akuluakulu a asilikali ndi atsogoleri a mu Galileya. Phwandolo lili mkati, Salome mwana wamkazi wa Herodiya amene anabereka ndi mwamuna wake wakale Filipo, anauzidwa kuti akavine pofuna kusangalatsa alendo amene anabwera ku phwandolo. Alendowo anasangalala kwambiri ndi mmene Salome anavinira.

Nayenso Herode anasangalala kwambiri ndi mmene mwana wakeyo anavinira moti anamuuza kuti: “Upemphe kwa ine chilichonse chimene ukufuna, ndipo ndidzakupatsa.” Anachita kulumbira kuti: “Chilichonse chimene ungapemphe kwa ine, ndidzachipereka kwa iwe, ngakhale hafu ya ufumu wangawu.” Salome asanayankhe anapita kaye kwa mayi ake kukawafunsa kuti: “Ndikapemphe chiyani?”—Maliko 6:22-24.

Zimenezi zinamupatsa mpata Herodiya wochita zimene ankafuna. Herodiya anayankha Salome kuti: “Kapemphe mutu wa Yohane m’batizi.” Nthawi yomweyo Salome anapita kwa Herode ndipo anamuuza kuti: “Ndikufuna mundipatse mutu wa Yohane M’batizi m’mbale pompano.”—Maliko 6:24, 25.

Herode anasokonezeka maganizo ndi zimene mtsikanayu anapempha koma alendo onse pa phwandolo anali atamva kale zimene Herode anamulonjeza. Herode akanachita manyazi akanalephera kumupatsa mtsikanayo zimene anapempha ngakhale kuti zimenezi zinatanthauza kuti aphe munthu wosalakwa. Pasanapite nthawi yaitali msilikali wolondera mfumu anabwera ndi mutu wa Yohane m’mbale ndipo anaupereka kwa Salome amene kenako anapita nawo kwa mayi ake.

Ophunzira a Yohane atamva zimene zinachitikazo anapita kukatenga thupi lake n’kukaliika m’manda. Kenako ophunzirawo anakauza Yesu za nkhaniyi.

Ndiyeno Herode atamva kuti Yesu akuchiritsa anthu ndiponso kutulutsa ziwanda, anachita mantha kwambiri. Iye ankaganiza kuti Yesu ndi Yohane M’batizi ndipo ‘wauka kwa akufa.’ (Luka 9:7) Choncho Herode Antipa ankafunitsitsa kuona Yesu. Cholinga chake si chinali choti amve Yesu akulalikira koma ankangofuna kutsimikizira ngati zimene ankaganizazo zinalidi zoona.