MATEYU 10:16-42;11:1 MALIKO 6:12, 13 LUKA 9:6

  • YESU ANAPHUNZITSA ATUMWI AKE NDI KUWATUMIZA KUTI AKALALIKIRE

Yesu anapatsa atumwi ake, omwe anawagawa awiriawiri, malangizo abwino kwambiri ogwirira ntchito yolalikira. Koma atawapatsa malangizowo anawachenjezanso kuti pogwira ntchito yolalikirayo akakumana ndi anthu otsutsa. Iye anawachenjeza kuti: “Taonani! Ndikukutumizani monga nkhosa pakati pa mimbulu. . . . Chenjerani ndi anthu, pakuti adzakuperekani kumakhoti aang’ono, ndipo adzakukwapulani m’masunagoge awo. Inde, adzakutengerani kwa abwanamkubwa ndi mafumu chifukwa cha ine, kuti ukhale umboni kwa iwo ndi kwa anthu a mitundu ina.”—Mateyu 10:16-18.

Ngakhale kuti otsatira a Yesu ankayembekezera kukumana ndi mavuto oopsa, iye anawalonjeza kuti: “Akakuperekani kumeneko, musade nkhawa za mmene mukalankhulire kapena zimene mukanene. Mudzapatsidwa nthawi yomweyo zoti mulankhule, pakuti wolankhula simudzakhala inu panokha, koma mzimu wa Atate wanu udzalankhula kudzera mwa inu.” Yesu ananenanso kuti: “Munthu adzapereka m’bale wake ku imfa, ndipo bambo adzapereka mwana wake. Ana adzaukira makolo awo ndipo adzawaphetsa. Anthu onse adzadana nanu chifukwa cha dzina langa, koma yekhayo amene adzapirire mpaka pa mapeto ndi amene adzapulumuke.”—Mateyu 10:19-22.

Chifukwa chakuti ntchito yolalikira inali yofunika kwambiri, Yesu anauza otsatira akewo kuti ayenera kukhala osamala kuti akwanitse kugwira ntchitoyi. Iye ananena kuti: “Akakuzunzani mumzinda wina, muthawire mumzinda wina, pakuti ndithu ndikukuuzani, simudzamaliza kuzungulira mizinda yonse ya Isiraeli Mwana wa munthu asanafike.”—Mateyu 10:23.

Kunena zoona Yesu anachenjeza, kulimbikitsa komanso kupereka malangizo abwino kwambiri kwa atumwi ake 12. Malangizo amene Yesu anapereka nthawi imeneyi anali othandizanso kwa anthu amene anali kudzagwira ntchito yolalikirayi Yesu atafa komanso ataukitsidwa. Tikutero chifukwa Yesu anauza ophunzira ake kuti “anthu onse adzadana nanu” osati anthu okhawo amene atumwiwa ankawalalikira. Ndipotu Baibulo silifotokoza zoti pa nthawi imene atumwiwa ankalalikira ku Galileya anthu anawatengera kwa mabwanamkubwa ndi mafumu kapena kuti anaperekedwa ndi achibale awo kuti aphedwe.

Choncho, n’zoonekeratu kuti pamene Yesu ankapereka malangizo amenewa kwa atumwi ake ankanena zimene zidzachitike m’tsogolo. Kumbukiraninso kuti anauza ophunzira ake kuti sadzamaliza kuzungulira mizinda yonse akugwira ntchito yolalikirayi “Mwana wa munthu asanafike.” Ponena mawu amenewa Yesu ankatanthauza kuti ophunzira ake sadzamaliza kulalikira za Ufumu wa Mulungu, Yesu Khristu yemwe ndi Mfumu asanabwere monga woweruza.

Pogwira ntchito yolalikira atumwiwo sanafunike kudabwa ngati akanakumana ndi anthu otsutsa  chifukwa Yesu ananena kuti: “Wophunzira saposa mphunzitsi wake, ndipo kapolo saposa mbuye wake.” Pamenepa Yesu ankatanthauza kuti anthu sankamuchitira zinthu zabwino komanso ankamuzunza chifukwa cholalikira za Ufumu wa Mulungu, choncho ophunzirawo ankayenera kukumananso ndi zomwezo. Koma Yesu anawalimbikitsa kuti: “Musachite mantha ndi amene amapha thupi koma sangaphe moyo, m’malomwake, muziopa iye amene angathe kuwononga zonse ziwiri, moyo ndi thupi lomwe m’Gehena.”—Mateyu 10:24, 28.

Yesu anasonyeza chitsanzo chabwino potsatira zimene ananenazi. Iye anapirira molimba mtima mpaka imfa moti sanalole kuti mavuto amulepheretse kusonyeza kuti ndi wokhulupirika kwa Yehova, yemwe ndi wamphamvu zonse. Mulungu Wamphamvuzonse ndi yekhayo amene angawononge moyo wa munthu (kutanthauza chiyembekezo chodzakhalanso ndi moyo m’tsogolo) kapena amene angamuukitse kuti adzasangalale ndi moyo wosatha. Zimenezi zinali zolimbikitsa kwambiri kwa atumwiwo.

Pofuna kusonyeza mmene Mulungu amakondera otsatira ake, Yesu ananena kuti: “Kodi mpheta ziwiri si paja amazigulitsa kakhobidi kamodzi kochepa mphamvu? Komatu palibe ngakhale imodzi imene idzagwa pansi Atate wanu osadziwa. . . . Choncho musachite mantha: Ndinu ofunika kwambiri kuposa mpheta zochuluka.”—Mateyu 10:29, 31.

Uthenga umene ophunzira a Yesu ankalalikira unkachititsa kuti anthu a m’banja limodzi asiye kugwirizana chifukwa chakuti ena ankalandira uthengawu pomwe ena ankaukana. Yesu ananena kuti: “Musaganize kuti ndinabweretsa mtendere padziko lapansi.” Choncho munthu amene achibale ake akumutsutsa amafunika kulimba mtima kuti aphunzire choonadi cha m’Baibulo. N’chifukwa chake Yesu ananena kuti: “Amene amakonda kwambiri bambo ake kapena mayi ake kuposa ine sali woyenera ine. Komanso amene amakonda kwambiri mwana wake wamwamuna kapena wamkazi kuposa ine sali woyenera ine.”—Mateyu 10:34, 37.

Komabe, panali anthu ena amene akanalandira ophunzira a Yesu. N’chifukwa chake iye ananena kuti: “Aliyense wopatsa mmodzi wa tiana iti ngakhale madzi ozizira okha m’kapu kuti amwe chifukwa ndi wophunzira, ndithu ndikukuuzani, ameneyo mphoto yake sidzatayika ngakhale pang’ono.”—Mateyu 10:42.

Yesu atangomaliza kuwalangiza, kuwachenjeza komanso kuwalimbikitsa, atumwiwo anali okonzeka ndipo “ananyamuka ndi kulowa m’deralo m’mudzi ndi mudzi. Iwo anali kulengeza uthenga wabwino ndi kuchiritsa anthu kwina kulikonse.”—Luka 9:6.