Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 52

Anadyetsa Anthu Masauzande Ambiri ndi Mikate Komanso Nsomba Zochepa

Anadyetsa Anthu Masauzande Ambiri ndi Mikate Komanso Nsomba Zochepa

Atumwi 12 a Yesu anasangalala kwambiri kugwira ntchito yolalikira m’madera onse a ku Galileya. Atakumananso ndi Yesu anamufotokozera “zonse zimene iwo anachita ndi kuphunzitsa.” N’zoona kuti atumwiwa anali atatopa koma sanapeze nthawi yoti n’kudya chifukwa zimene zinkachitika n’zakuti, anthu ena akamachoka ena ankabwera kudzakumana ndi Yesu. Ndiyeno Yesu anauza atumwiwo kuti: “Inuyo bwerani kuno, tipite kwatokha kopanda anthu kuti mupumule pang’ono.”—Maliko 6:30, 31.

Iwo anakwera boti mwina chakufupi ndi ku Kaperenao ndipo analowera chakum’mawa kwa mtsinje wa Yorodano. Anapitirira ku Betsaida n’kupita kumalo kopanda anthu. Komabe anthu ambiri anamva ndipo ena anawaona pamene ankanyamuka. Anthuwo ankawathamangira m’mbali mwa nyanjayo ndipo pamene botilo linkafika, n’kuti anthuwo atafika kale pamalowo.

Yesu atatsika m’botilo n’kuona gulu la anthu, anamva chisoni kwambiri chifukwa anthuwo anali ngati nkhosa zopanda m’busa. Choncho anayamba “kuwaphunzitsa zinthu zambiri” zokhudza Ufumu. (Maliko 6:34) Komanso anachiritsa “amene anafunika kuchiritsidwa.” (Luka 9:11) Ndiyeno chakumadzulo ophunzirawo anauza Yesu kuti: “Kuno n’kopanda anthu ndipo nthawi yatha, auzeni anthuwa kuti anyamuke, apite m’midzimo kuti akagule chakudya.”—Mateyu 14:15.

Yesu anawayankha kuti: “Palibe chifukwa choti apitire. Inuyo muwapatse chakudya.” (Mateyu 14:16) Ngakhale kuti Yesu ankadziwa zimene achite komabe anafunsa Filipo kuti: “Kodi mitanda ya mkate yodyetsa anthu onsewa tikaigula kuti?” Yesu anafunsa Filipo chifukwa kwawo kunali pafupi ndi ku Betsaida. Komabe ngakhale akanagula chakudyacho sichikanakwanira chifukwa panali amuna pafupifupi 5,000. Komanso n’kutheka kuti chiwerengero cha anthu onse amene anasonkhanawo chikanawonjezeka kawiri akanawerenga akazi ndi ana. Poganizira zimenezi, Filipo anayankha kuti: “Ngakhale mitanda ya mkate ya ndalama zokwana madinari 200 [dinari imodzi inali malipiro a tsiku limodzi] singawakwanire amenewa. Singawakwanire ngakhale titati aliyense angolandirako pang’ono.”—Yohane 6:5-7.

Mwina pofuna kusonyeza kuti sizikanatheka kudyetsa anthu onsewo, Andireya ananena kuti: “Pali kamnyamata pano kamene kali ndi mitanda isanu ya mkate wa balere ndi tinsomba tiwiri. Koma nanga zimenezi zingakwanire, poyerekeza ndi chikhamu chonse cha anthuchi?”—Yohane 6:9.

Mwina zimenezi zinkachitika m’miyezi ya March kapena April, mwambo wa Pasika wa mu 32 C.E. utatsala pang’ono kuchitika. Pa nthawiyi n’kuti udzu ukadali wobiriwira m’mbali mwa phiri. Choncho Yesu anatuma ophunzira ake kuti auze anthuwo kuti akhale pansi pa udzu m’magulu a anthu 50 komanso m’magulu a anthu 100. Kenako Yesu anatenga mikate 5 ndi nsomba ziwiri zija n’kupemphera kwa Mulungu. Ndiyeno ananyemanyema mikateyo n’kugawanso nsombazo. Atatero anapereka zakudyazo kwa ophunzira ake kuti agawire anthuwo. Zinali zodabwitsa chifukwa anthu onsewo anadya n’kukhuta.

Anthuwo atamaliza kudya, Yesu anauza ophunzira akewo kuti: “Sonkhanitsani zotsala zonse, kuti pasawonongeke chilichonse.” (Yohane 6:12) Zimene anatolerazo zinakwana madengu 12.

Onaninso

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA)

Yesu Amadyetsa Anthu Ambiri Kudzera mwa Anthu Ochepa

Kodi Yesu ankapereka bwanji chakudya chauzimu ku mipingo ya Akhristu oyambirira? Kodi amatsatira njira yomweyo masiku ano?