Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 29

Kodi Kunali Kulakwa Kugwira Ntchito Yabwino pa Sabata?

Kodi Kunali Kulakwa Kugwira Ntchito Yabwino pa Sabata?

YOHANE 5:1-16

  • YESU ANALALIKIRA KU YUDEYA

  • ANACHIRITSA MUNTHU WODWALA AMENE ANALI PAFUPI NDI DZIWE

Pamene Yesu anali ku Galileya anachita zambiri pa ntchito yake yolalikira. Komabe pamene ananena kuti: “Ndiyenera kukalengeza uthenga wabwino wa ufumu wa Mulungu kumizinda inanso,” anasonyeza kuti ankaganizira zokalalikira kumadera enanso, osati ku Galileya kokha. Choncho anapita “n’kumalalikira m’masunagoge a mu Yudeya.” (Luka 4:43, 44) Zinali zomveka kuti achite zimenezi chifukwa pa nthawiyi mwambo wa Pasika, womwe unkachitikira ku Yerusalemu, unali utayandikira.

Mauthenga Abwino safotokoza zambiri zokhudza zimene Yesu anachita ku Yudeya poyerekeza ndi zimene anachita ku Galileya. Ngakhale kuti anthu ambiri a ku Yudeya sankamvetsera uthenga wake, Yesu sanasiye kulalikira mwakhama komanso kuchitira anthu ena zinthu zabwino kulikonse kumene ankapita.

Kenako Yesu anayamba ulendo wopita ku mzinda wa Yerusalemu, womwe unali likulu la chigawo cha Yudeya, kuti akachite nawo mwambo wa Pasika wa mu 31 C.E. Polowa mumzindawu anadzera ku Chipata cha Nkhosa ndipo pafupi ndi chipatachi panali dziwe lomwe linkadziwika kuti Betesida. Anthu ambiri odwala, akhungu komanso olumala ankabwera ku dziwe limeneli chifukwa ankakhulupirira kuti atha kuchira ngati atalowa m’dziwelo pa nthawi imene madziwo awinduka.

Yesu atafika ku dziweli anaona munthu wina yemwe anatha zaka 38 akudwala, koma tsikuli linali la Sabata. Kenako Yesu anamufunsa munthuyo kuti: “Kodi ukufuna kuchira?” Munthuyo anayankha kuti: “Bambo, ndilibe munthu wondiviika m’dziwemu madzi akawinduka, ndipo ndikati ndikalowemo wina amandipitirira n’kulowamo.”—Yohane 5:6, 7.

Kenako Yesu ananena mawu amene anadabwitsa munthuyo komanso aliyense amene anamumva akulankhula. Iye anamuuza kuti: “Nyamuka, nyamula machira akowa ndi kuyamba kuyenda.” (Yohane 5:8) Munthuyo anachitadi zimene anauzidwazo. Nthawi yomweyo anachira ndipo ananyamula machira ake n’kuyamba kuyenda.

M’malo mosangalala ndi zinthu zabwino zimene zinachitikazo, Ayuda ataona munthuyo anayamba kulankhula momuweruza kuti: “Lero ndi Sabata, n’kosaloleka kuti unyamule machirawa.” Koma munthuyo anawayankha kuti: “Amene wandichiritsayo wandiuza kuti, ‘Nyamula machira akowa ndi kuyamba kuyenda.’” (Yohane 5:10, 11) Ayudawo ankafuna kupezera zifukwa munthu amene anachiritsa wodwala pa tsiku la Sabata.

Pofuna kudziwa munthu amene anachita zimenezi, anafunsa wodwalayo kuti: “Ndiye ndani amene wakuuza kuti, ‘Nyamula machira ndi kuyamba kuyenda’?” Iwo anamufunsa funsoli chifukwa pa nthawiyi Yesu anali “atalowa m’chikhamu cha anthu” komanso munthu amene anachiritsidwa uja sankadziwa dzina la munthu amene anamuchiritsayo. (Yohane 5:12, 13) Komabe munthuyo anakumananso ndi Yesu m’kachisi ndipo tsopano anadziwa bwino munthu amene anamuchiritsa pa dziwe paja.

Munthu uja atakumananso ndi Ayuda omwe anamufunsa za munthu amene anamuchiritsa, anawauza kuti anachiritsidwa ndi Yesu. Ayudawo atamva zimenezo anapita kwa Yesu. Koma sanapite kwa Yesu kuti akadziwe chimene chinkamuchititsa kuti azitha kuchita zinthu zodabwitsazo. M’malomwake, anapita kuti akangomupezera zifukwa chifukwa choti anachita zinthu zabwino pa tsiku la Sabata. Ndipo anayamba kumuvutitsa chifukwa cha nkhaniyi.

Onaninso

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi Akhristu Ayenera Kusunga Sabata?

Ngati Akhristu sakuyenera kusunga Sabata n’chifukwa chiyani Baibulo limati ndi lamulo losatha?