MATEYU 12:9-14 MALIKO 3:1-6 LUKA 6:6-11

  • YESU ANACHIRITSA MUNTHU WOPUWALA DZANJA PA TSIKU LA SABATA

Pa tsiku lina la Sabata, Yesu anapita ku sunagoge ndipo n’kutheka kuti sunagogeyo anali wa ku Galileya. Ali kumeneko anapeza munthu yemwe anali wopuwala dzanja lamanja. (Luka 6:6) Pa nthawiyi alembi ndi Afarisi ankangoyang’anitsitsa kuti aone zimene Yesu achite. Kodi n’chifukwa chiyani ankachita zimenezi? Zimene ankaganiza zinadziwika bwino atamufunsa kuti: “Kodi n’kololeka kuchiritsa odwala tsiku la sabata?”—Mateyu 12:10.

Atsogoleri achipembedzo achiyuda ankakhulupirira kuti kuchiritsa pa tsiku la Sabata kunali kovomerezeka pokhapokha ngati moyo unali pangozi. Mwachitsanzo, sikunali kololeka kubwezeretsa fupa limene lachoka m’malo mwake kapena kumanga pamene wabinya, chifukwa sizinali zinthu zoika moyo wa munthu pangozi. Sikuti alembi ndi Afarisi ankamufunsa Yesu chifukwa choti ankadera nkhawa munthu wopuwala dzanja uja, ayi. Iwo ankangofuna kuti amupezere Yesu chifukwa chomuimbira milandu.

Komabe Yesu anadziwa maganizo olakwika amene anthuwa anali nawo. Anadziwanso kuti anthuwa ankakhwimitsa kwambiri malamulo okhudza ntchito zimene anthu ayenera kugwira pa tsiku la Sabata, zomwe zinali zosagwirizana ndi Malemba. (Ekisodo 20:8-10) Pa nthawiyi n’kutinso anthu ena atamuimbapo kale milandu chifukwa cha zinthu zabwino zimene ankachita. Koma nkhaniyo inakula pamene Yesu anauza munthu amene anali wopuwala dzanja uja kuti: “Nyamuka, bwera pakatipa.”—Maliko 3:3.

Kenako Yesu anayang’ana alembi ndi Afarisi aja n’kuwafunsa kuti: “Ndani wa inu amene atakhala ndi nkhosa imodzi, ndiyeno nkhosayo n’kugwera m’dzenje tsiku la sabata, sangaigwire ndi kuitulutsa?” (Mateyu 12:11) Pa nthawiyo nkhosa inkaonedwa kuti ndi chiweto chobweretsa ndalama. Ndiye ngati nkhosayo yagwera m’dzenje, mwiniwake sakanaisiya m’dzenjemo kufikira tsiku lotsatira chifukwa ikanatha kufa ndipo akanaluza zambiri. Ndipotu Malemba amanena kuti: “Wolungama amasamalira moyo wa chiweto chake.”—Miyambo 12:10.

Pofuna kuthandiza anthuwo kumvetsa mfundo yake, Yesu anawauza kuti: “Komatu munthu ndi wofunika kwambiri kuposa nkhosa. Choncho, n’kololeka inde kuchita chinthu chabwino pa tsiku la sabata.” (Mateyu 12:12) Izi zikusonyeza kuti Yesu sanaphwanye Sabata pochiritsa munthu uja pa tsiku la Sabata. Atsogoleri achipembedzowo analephera kutsutsa mfundo yomveka bwino komanso yosonyeza chifundo imene Yesu anafotokozayi, moti anangokhala chete.

Yesu atakwiya komanso atagwidwa ndi chisoni chifukwa chodziwa maganizo awo olakwika, anayang’ana uku ndi uku n’kuuza munthu wopuwala dzanja uja kuti: “Tambasula dzanja lako.” (Mateyu 12:13) Atangolitambasula, nthawi yomweyo dzanjalo linakhala bwinobwino. Munthuyo anasangalala kwambiri, koma kodi Afarisi aja anatani?

M’malo moti asangalale kuti munthu uja wachira, Afarisi anatuluka m’sunagogemo ndipo nthawi yomweyo “anapita kukakonza chiwembu limodzi ndi a chipani cha Herode kuti amuphe.” (Maliko 3:6) Anthu ena omwe anali m’chipanichi, anali ochokera m’gulu la chipembedzo la Asaduki. Nthawi zambiri Asaduki ndi Afarisi sankagwirizana koma pa nthawi imeneyi anagwirizana n’cholinga choti atsutsane ndi Yesu.