MATEYU 8:5-13 LUKA 7:1-10

  • WOGWIRA NTCHITO KWA MKULU WA ASILIKALI ANACHIRITSIDWA

  • ANTHU AMENE ALI NDI CHIKHULUPIRIRO ADZADALITSIDWA

Yesu atamaliza ulaliki wake wa paphiri anapita ku mzinda wa Kaperenao. Atafika mumzindawo anakumana ndi akuluakulu a Ayuda omwe anatumidwa ndi kapitawo wa asilikali Achiroma. Kapitawo wa asilikaliyu ankayang’anira asilikali okwana 100.

Kapitawoyu anali ndi wantchito yemwe ankamukonda kwambiri koma pa nthawiyi wantchitoyo anali akudwala moti anali atatsala pang’ono kumwalira. Ngakhale kuti kapitawoyu sanali Myuda ankafuna kuti Yesu amuthandize. Akuluakulu a Ayudawo anauza Yesu kuti wantchito wa kapitawoyu “wafa ziwalo moti ali gone m’nyumba, ndipo akuzunzika koopsa” chifukwa chomva kupweteka kwambiri. (Mateyu 8:6) Akuluakulu a Ayudawo anapempha Yesu kuti athandize kapitawoyo. Iwo anati: “N’ngoyeneradi kuti mum’thandize, chifukwa amakonda anthu amtundu wathu ndipo anatimangira sunagoge.”—Luka 7:4, 5.

Kenako Yesu anatengana ndi akuluakuluwo n’kuyamba ulendo wopita kunyumba ya kapitawoyo. Koma atatsala pang’ono kufika, kapitawoyo anatuma anzake kuti akakumane ndi Yesu n’kumuuza kuti: “Mbuyanga, musavutike, pakuti ine sindili woyenera kuti inu mulowe m’nyumba mwanga. N’chifukwa chake inenso sindinabwere kwa inu, poona kuti ndine wosayenera kutero.” (Luka 7:6, 7) Apatu munthuyu anasonyeza kudzichepetsa kwambiri ngakhale kuti anali ndi udindo wapamwamba. Anasonyezanso kuti anali wosiyana kwambiri ndi Aroma ena omwe ankazunza antchito awo.—Mateyu 8:9.

Kapitawoyu ankadziwa kuti Ayuda sankacheza ndi anthu amitundu ina. (Machitidwe 10:28) Mwina poganizira zimenezi, n’chifukwa chake anauza anzake kuti amuuze Yesu kuti: “Mungonena mawu okha ndipo mtumiki wanga achira.”—Luka 7:7.

Yesu anadabwa kwambiri atamva zimenezi ndipo ananena kuti: “Kunena zoona, ngakhale mu Isiraeli sindinapezemo chikhulupiriro chachikulu ngati chimenechi.” (Luka 7:9) Anzake a kapitawoyu atabwerera kunyumba kwake anakapeza kuti wantchito uja wachira ndipo ali bwino.

Yesu atangochiritsa munthuyo anagwiritsa ntchito zimene zinachitikazo ngati umboni wakuti anthu amitundu ina omwe ali ndi chikhulupiriro adzadalitsidwa. Iye anati: “Ambiri ochokera kum’mawa ndi kumadzulo adzabwera ndi kukhala patebulo limodzi ndi Abulahamu, Isaki ndi Yakobo mu ufumu wakumwamba.” Nanga bwanji za Ayuda omwe analibe chikhulupiriro? Yesu ananena kuti “adzaponyedwa kunja kumdima. Kumeneko adzalira ndi kukukuta mano.”—Mateyu 8:11, 12.

Choncho Ayuda omwe anakana mwayi wodzalamulira mu Ufumu ndi Khristu, womwe poyamba unaperekedwa ku mtundu wa Ayuda, nawonso anakanidwa. Koma mwayiwu unaperekedwa kwa anthu amitundu ina, komwe kunali ngati kukakhala patebulo limodzi ndi Yesu “mu ufumu wakumwamba.”