MALIKO 1:14, 15 LUKA 4:14, 15 YOHANE 4:43-54

  • YESU ANKALALIKIRA KUTI “UFUMU WA MULUNGU WAYANDIKIRA”

  • ANACHIRITSA MNYAMATA AMENE ANALI KUTALI

Yesu atakhala ku Samariya kwa masiku awiri, anayamba ulendo wobwerera kwawo. Ngakhale kuti anagwira ntchito yolalikira ku Yudeya kwa masiku ambiri kuposa mmene ankaganizira, iye sanabwerere kwawo ku Galileya kuti akapume. M’malomwake anayamba kugwira ntchito yolalikira mwakhama m’dera limene anakulira. Yesu sanayembekezere kuti alandiridwa bwino chifukwa anachita kunena yekha kuti: “Mneneri salemekezedwa kwawo.” (Yohane 4:44) Pa nthawiyi ophunzira ake anabwerera n’kumakakhala ndi mabanja awo komanso anapitiriza ntchito zawo zakale m’malo mokhala ndi Yesu.

Kodi uthenga umene Yesu anayamba kulalikira unali woti chiyani? Unali wakuti: “Ufumu wa Mulungu wayandikira! Lapani anthu inu! Khulupirirani uthenga wabwino!” (Maliko 1:15) Kodi anthu anatani atamva uthengawo? Anthu ambiri anamulandira komanso ankamupatsa ulemu. Iwo ankachita zimenezo osati chifukwa cha uthenga wokhawo, koma chifukwa chakuti ena mwa anthuwo anaona zinthu zodabwitsa zimene Yesu anachita ku Yerusalemu, atapita kukachita nawo mwambo wa Pasika.—Yohane 2:23.

Kodi Yesu atafika ku Galileya anayambira kuti kulalikira? Anayambira ku Kana, komwe pa nthawi ina anasandutsa madzi kukhala vinyo pa phwando la ukwati. Pa ulendo wachiwiriwu ali ku Kana komweko, Yesu anamva kuti mnyamata wina akudwala moti watsala pang’ono kumwalira. Mnyamatayu anali mwana wa munthu wina wokhala ndi udindo m’boma la mfumu Herodi Antipa. Mfumu imeneyi ndi yomwe inadzalamula kuti Yohane M’batizi adulidwe mutu. Bambo wa mwanayu anamva kuti Yesu wachoka ku Yudeya ndipo ali ku Kana. Choncho iye anachoka kwawo ku Kaperenao n’kupita ku Kana kuti akaonane ndi Yesu. Bamboyu yemwe anali ndi chisoni chachikulu, anapempha Yesu kuti: “Ambuye, tiyeni mwana wanga asanafe.”—Yohane 4:49.

Zimene Yesu anayankha ziyenera kuti zinadabwitsa bamboyo, chifukwa iye anati: “Pita, mwana wako ali moyo.” (Yohane 4:50) Bamboyo anakhulupirira zimene Yesu anamuuza ndipo anayamba ulendo wobwerera kwawo. Ali m’njira, anakumana ndi antchito ake omwe ankabwera kudzamuuza nkhani yabwino yakuti mwana wake uja wachira ndipo ali bwino. Pofuna kugwirizanitsa ndi zimene Yesu anamuuza, anafunsa kuti: ‘Wachira nthawi yanji?’

Iwo anamuyankha kuti: “Malungo ake anatha dzulo cha m’ma 1 koloko masana.”—Yohane 4:52.

Zitatero, anazindikira kuti nthawiyi inali yofanana ndendende ndi nthawi imene Yesu anamuuza kuti: “Mwana wako ali moyo.” Kenako bamboyu, yemwe anali wolemera moti anali ndi antchito, komanso banja lake lonse anakhala ophunzira a Khristu.

Choncho Yesu anachita zozizwitsa ziwiri ku Kana. Anasandutsa madzi kukhala vinyo kenako anachiritsa mnyamata amene anali pamtunda wa makilomita 26 kuchokera kumene iye anali. Yesu anachitanso zozizwitsa zina, komabe kuchiritsidwa kwa mnyamatayu kunali kosaiwalika kwa anthu a ku Galileya. Zimene Yesu anachitazi, zinasonyeza kuti anali mneneri wovomerezeka ndi Mulungu. Koma kodi anthu anamulemekeza atabwerera kwawo?

Tiyeni tione zimene zinachitika atabwerera kwawo ku Nazareti.