MATEYU 17:14-20 MALIKO 9:14-29 LUKA 9:37-43

  • CHIKHULUPIRIRO CHOLIMBA CHIKANAWATHANDIZA KUCHIRITSA MNYAMATA AMENE ANALI NDI CHIWANDA

Pamene Yesu, Petulo, Yakobo ndi Yohane ankatsika m’phiri muja anakumana ndi chigulu cha anthu. Chinachake chinali chitasokonekera chifukwa alembi anali ataunjirira ophunzira a Yesu ndipo ankakangana nawo. Gulu la anthulo linadabwa kwambiri litaona Yesu ndipo linamuthamangira n’kukamupatsa moni. Iye anafunsa anthuwo kuti: “Mukukangana nawo chiyani?”—Maliko 9:16.

Munthu wina amene anali m’chigulumo anagwada pamapazi a Yesu n’kuyamba kufotokoza kuti: “Mphunzitsi, ine ndabweretsa mwana wanga wamwamuna kwa inu chifukwa ali ndi mzimu womulepheretsa kulankhula. Mzimuwo umati ukamugwira, umamugwetsera pansi. Akatero amachita thovu ndi kukukuta mano, ndipo amatha mphamvu. Chotero, ndinauza ophunzira anu kuti autulutse, koma alephera.”—Maliko 9:17, 18.

Chifukwa choti ophunzira a Yesu analephera kuchiritsa mnyamatayo, alembi ankanyoza ophunzirawo ndipo mwina ankawanena kuti akungotaya nthawi poyenda ndi Yesu. M’malo moyankha zimene bambo wa mwanayo ananena, Yesu anauza gulu la anthulo kuti: “Inu a m’badwo wopanda chikhulupiriro ndi wopotoka maganizo, kodi ndikhala nanube mpaka liti?” Pamenepa Yesu ankanena za alembi omwe ankavutitsa ophunzira ake iye palibe. Kenako anatembenukira kwa bambo uja n’kumuuza kuti: “Bwera nayeni kuno.”—Mateyu 17:17.

Mnyamatayo atayandikira pamene panali Yesu, chiwanda chija chinamugwetsera pansi moti anayamba kutsalima mwamphamvu. Mnyamatayo ankangogubuduka ndipo ankatuluka thovu kukamwa. Kenako Yesu anafunsa bambo akewo kuti: “Izi zakhala zikumuchitikira kwa nthawi yaitali bwanji?” Bambowo anayankha kuti: “Kuyambira ali mwana, mwakuti nthawi zambiri wakhala ukum’gwetsera pamoto ndi m’madzi kuti umuwononge.” Bambowo anapempha Yesu kuti: “Ngati mungathe kuchitapo kanthu, tichitireni chifundo ndi kutithandiza.”—Maliko 9:21, 22.

 Bambowo ankafunitsitsa mwana wawo atathandizidwa chifukwa ophunzira a Yesu anali atalephera kumuchiritsa. Poyankha zimene bambowo anapempha, Yesu anawalimbikitsa powauza kuti: “Mukuti, ‘Ngati mungathe’? Chilichonsetu n’chotheka kwa aliyense ngati iyeyo ali ndi chikhulupiriro.” Nthawi yomweyo bambowo anafuula kuti: “Chikhulupiriro ndili nacho! Limbitsani chikhulupiriro changa!”—Maliko 9:23, 24.

Ndiyeno Yesu anaona gulu lina la anthu likumuthamangira. Kenako Yesu anadzudzula chiwandacho anthu onsewo akuona. Iye ananena kuti: “Mzimu wosalankhulitsa ndi wogonthetsa iwe, ndikukulamula, tuluka ndipo usadzalowenso mwa iye.” Pamene chiwandacho chinkatuluka chinachititsa kuti mnyamatayo afuule komanso kutsalima kwambiri. Kenako mnyamatayo anangogona pansi osachitanso kalikonse. Ataona zimenezi anthu ambiri ananena kuti: “Wamwalira!” (Maliko 9:25, 26) Koma Yesu atagwira dzanja lake, mnyamatayo anadzuka ndipo “nthawi yomweyo . . . anachira.” (Mateyu 17:18) Ataona zimenezi anthuwo anadabwa kwambiri.

Nthawi ina m’mbuyomo Yesu atatumiza ophunzira ake kuti akalalikire, anawapatsa mphamvu moti ankatulutsa ziwanda. Chifukwa chokumbukira zimenezi, ophunzirawo ali ndi Yesu m’nyumba anamufunsa kuti: “N’chifukwa chiyani ife tinalephera kuutulutsa?” Yesu anawauza kuti analephera kutulutsa chiwandacho chifukwa chakuti analibe chikhulupiriro. Iye anawauza kuti: “Mzimu wa mtundu umenewu sungathe kutuluka ndi chilichonse, koma pemphero basi.” (Maliko 9:28, 29) Ophunzirawo ankafunika kukhala ndi chikhulupiriro cholimba komanso ankafunika kupempha mphamvu zochokera kwa Mulungu kuti akwanitse kutulutsa chiwanda champhamvucho.

Kenako Yesu anamaliza n’kunena kuti: “Ndithu ndikukuuzani, ngati mutakhala ndi chikhulupiriro chofanana ndi kanjere ka mpiru kuchepa kwake, mudzatha kuuza phiri ili kuti, ‘Choka pano upite apo,’ ndipo lidzachokadi. Palibe chimene chidzakhala chosatheka kwa inu.” (Mateyu 17:20) Choncho munthu akhoza kuchita zinthu zamphamvu ngati ali ndi chikhulupiriro cholimba.

Nthawi zina zinthu zimene zimatisokoneza potumikira Yehova zingawoneke ngati zosatheka kuzichotsa komanso zingawoneke zazikulu ngati phiri. Koma tikakhala ndi chikhulupiriro cholimba tikhoza kulimbana nazo.