Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 GAWO 3

Yesu Analalikira Kwambiri ku Galileya

‘Yesu anayamba kulalikira kuti: “Ufumu wakumwamba wayandikira.”’—Mateyu 4:17

Yesu Analalikira Kwambiri ku Galileya

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 20

Chozizwitsa Chachiwiri Chimene Yesu Anachita Ku Kana

Yesu anachiritsa mwana yemwe anali pamtunda wa makilomita 26.

MUTU 21

Zimene Zinachitika Yesu Ali ku Sunagoge wa ku Nazareti

Kodi Yesu ananena chiyani kuti anthu a m’tauni ya kwawo afike pofuna kumupha?

MUTU 22

Yesu Anaitana Ophunzira Ake 4

Anawaitana kuti asiye mtundu wina wa usodzi n’kuyamba wina.

MUTU 23

Yesu Anachita Zozizwitsa Ali ku Kaperenao

Pamene Yesu ankatulutsa mizimu yoipa, n’chifukwa chiyani analetsa mizimuyo kuti isawuze anthu kuti iyeyo ndi Mwana wa Mulungu?

MUTU 24

Yesu Analalikira M’madera Ambiri a ku Galileya

Anthu anapita kwa Yesu kuti akachiritsidwe, komabe Yesu anafotokoza kuti utumiki wake unali ndi cholinga chinachake chapadera.

MUTU 25

Yesu Anachitira Chifundo Munthu Wakhate N’kumuchiritsa

Yesu analankhula mawu ochepa koma amphamvu kwambiri ndipo zimene analankhulazo zinasonyeza kuti ankaganizira anthu amene ankawachiritsa.

MUTU 26

“Machimo Ako Akhululukidwa”

Kodi Yesu anasonyeza kuti pali kugwirizana kotani pakati pa uchimo ndi matenda?

MUTU 27

Yesu Anaitana Mateyu

N’chifukwa chiyani Yesu anadya ndi anthu ochimwa?

MUTU 28

N’chifukwa Chiyani Ophunzira a Yesu Sankasala Kudya?

Poyankha Yesu anafotokoza fanizo la matumba a chikopa.

MUTU 29

Kodi Kunali Kulakwa Kugwira Ntchito Yabwino pa Sabata?

N’chifukwa chiyani Ayuda ankavutitsa Yesu atachiritsa munthu amene ankadwala kwa zaka 38?

MUTU 30

Kodi Pali Ubale Wotani Pakati pa Yesu ndi Mulungu?

Ayuda ankaganiza kuti Yesu ankadziona kuti ndi wofanana ndi Mulungu, koma Yesu anafotokoza kuti Mulungu ndi wamkulu kwa iyeyo.

MUTU 31

Anabudula Ngala za Tirigu pa Tsiku la Sabata

N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti iye ndi “Mbuye wa Sabata”?

MUTU 32

Kodi Malamulo Ankalola Munthu Kuchita Chiyani pa Sabata?

Nthawi zambiri Asaduki ndi Afarisi sankagwirizana koma anagwiriza n’cholinga choti atsutse Yesu.

MUTU 33

Ulosi wa Yesaya Unakwaniritsidwa

N’chifukwa chiyani Yesu ankauza anthu amene wawachiritsa kuti asamauze anthu ena zimene wachita komanso kuti iye ndi ndani?

MUTU 34

Yesu Anasankha Atumwi 12

Kodi panali kusiyana kotani pakati pa atumwi ndi ophunzira?

MUTU 35

Ulaliki Wotchuka wa Paphiri

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zofunika kwambiri zimene Yesu anaphunzitsa.

MUTU 36

Kapitawo wa Asilikali Anasonyeza Kuti Anali ndi Chikhulupiriro

Kodi kapitawo wa asilikali anachita chiyani chomwe chinadabwitsa Yesu?

MUTU 37

Yesu Anaukitsa Mwana Wamwamuna wa Mzimayi Wamasiye

Anthu amene anaona Yesu akuukitsa mnyamatayo anamvetsa tanthauzo lake.

MUTU 38

Yohane Yemwe Anali M’ndende Ankafuna Kumva Kuchokera kwa Yesu

N’chifukwa chiyani Yohane m’batizi anafunsa ngati Yesu analidi Mesiya? Kodi Yohane ankakayikira?

MUTU 39

Tsoka kwa M’badwo Umene Sunamvere

Yesu ananena kuti chilango cha Sodomu pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha Kaperenao. Ku Kaperenao n’kumene Yesu ankakhala nthawi zambiri.

MUTU 40

Anawaphunzitsa Kukhululukira Ena

Kodi pamene Yesu anauza mzimayi yemwe mwina anali hule kuti machimo ake akhululukidwa, ankatanthauza kuti palibe vuto lililonse ngati munthu atachita zinthu zosiyana ndi malamulo a Mulungu?

MUTU 41

Kodi Yesu Ankazitenga Kuti Mphamvu Zochitira Zozizwitsa?

Abale ake a Yesu ankaganiza kuti wachita misala.

MUTU 42

Yesu Anadzudzula Afarisi

Kodi “chizindikiro cha mneneri Yona” chinkatanthauza chiyani?

MUTU 43

Mafanizo Ofotokoza za Ufumu

Yesu ananena mafanizo okwana 8 ofotokoza za Ufumu wakumwamba.

MUTU 44

Yesu Analetsa Mphepo Yamphamvu Panyanja

Zimene Yesu anachita poletsa mphepo ndi mafunde pa nyanja zimasonyeza mmene moyo udzakhalire akadzayamba kulamulira monga Mfumu.

MUTU 45

Anatulutsa Ziwanda Zambiri

Kodi n’zotheka kuti munthu akhale ndi ziwanda zambiri?

MUTU 46

Anachira Atagwira Malaya a Yesu

Yesu anasonyeza kuti anali wachifundo komanso kuti anali ndi mphamvu pamene anachiritsa mzimayi wodwala matenda otaya magazi.

MUTU 47

Kamtsikana Kanakhalanso ndi Moyo

Yesu atanena kuti mtsikana womwalirayo akugona anthu anayamba kuseka kwambiri. Kodi anthuwo sankadziwa kuti Yesu akhoza kuchita chiyani?

MUTU 48

Yesu Anachita Zozizwitsa Koma Anakanidwa Ngakhale Kwawo ku Nazareti

Anthu a ku Nazareti anakana Yesu, osati chifukwa cha zozizwitsa kapena zimene ankaphunzitsa, koma anali ndi zifukwa zina.

MUTU 49

Analalikira ku Galileya Komanso Anaphunzitsa Atumwi

Kodi mawu akuti ‘Ufumu wakumwamba wayandikira’ ankatanthauza chiyani?

MUTU 50

Anawakonzekeretsa Kuti Azilalikira Ngakhale Pamene Akuzunzidwa

Popeza atumwi sankafunika kuopa imfa, n’chifukwa chiyani Yesu anawauza kuti adzathawe akamadzazunzidwa?

MUTU 51

Anaphedwa pa Tsiku Lokondwerera Kubadwa

Salome anasangalatsa Herode ndi mmene anavinira moti Herode anamulonjeza kuti amupatsa chilichonse chimene angapemphe. Kodi Salome anapempha chiyani?

MUTU 52

Anadyetsa Anthu Masauzande Ambiri ndi Mikate Komanso Nsomba Zochepa

Chozizwitsa chimene Yesu anachita pa nthawi imeneyi chinali chapadera kwambiri moti chinalembedwa m’Mauthenga onse 4.

MUTU 53

Wolamulira Amene Akhoza Kulamulira Mphepo Yamphamvu

Kodi atumwi anazindikira chiyani ataona Yesu akuyenda pamadzi komanso ataletsa mphepo yamphamvu?

MUTU 54

Yesu Ndiye “Chakudya Chopatsa Moyo”

N’chifukwa chiyani Yesu anadzudzula anthu ngakhale kuti anayesetsa kumufunafuna kuti amupeze?

MUTU 55

Kudya Mnofu wa Yesu ndi Kumwa Magazi Ake

Yesu anaphunzitsa zinthu zimene zinadabwitsa ophunzira ake moti ambiri anasiya kumutsatira.

MUTU 56

Kodi Chimaipitsa Munthu N’chiyani?

Kodi chimaipitsa munthu n’chiyani, kodi ndi zimene zimalowa m’kamwa kapena zimene zimatuluka m’kamwamo?

MUTU 57

Yesu Anachiritsa Mtsikana Komanso Munthu Wogontha

N’chifukwa chiyani mayiyu sanakhumudwe Yesu atayerekezera anthu a mtundu wake ngati tiagalu?

MUTU 58

Anachulukitsa Mikate Komanso Anachenjeza Ophunzira Ake za Zofufumitsa

Ophunzira a Yesu anamvetsa tanthauzo la zofufumitsa zimene Yesu ankawachenjeza nazo.

MUTU 59

Kodi Mwana wa Munthu Ndi Ndani?

Kodi makiyi a Ufumu n’chiyani? Ndani anawagwiritsa ntchito ndipo anawagwiritsa ntchito bwanji?

MUTU 60

Anaona Ulemelero wa Khristu Atasandulika

Kodi atumwi anaona chiyani m’masomphenya? Nanga zimenezi zinkatanthauza chiyani?

MUTU 61

Yesu Anachiritsa Mnyamata Amene Anali ndi Chiwanda

Yesu panafunika chikhulupiriro cholimba kuti mnyamata uja achiritsidwe n’chifukwa chake zinakanika poyamba paja. Koma kodi ndi ndani amene ankafunika kukhala ndi chikhulupirirocho, ndi mnyamatayo, bambo ake kapena ophunzira a Yesu?

MUTU 62

Kufunika Kokhala Wodzichepetsa

Anthu akuluakulu anaphunzira khalidwe lofunika kwambiri kwa kamwana kakang’ono.

MUTU 63

Yesu Anafotokoza Zoyenera Kuchita Anthu Akakhumudwitsana Komanso Ngati Wina Wachita Tchimo

Yesu anafotokoza malangizo amene abale ayenera kutsatira ngati wina wachita tchimo lalikulu.

MUTU 64

Anawaphunzitsa Kufunika Kokhululukira Ena

Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la kapolo wopanda chifundo pofuna kusonyeza kuti Mulungu amatikhululukira ngati ifenso timayesetsa kukhululukira anzathu.

MUTU 65

Yesu Anaphunzitsa Anthu Ena Ali pa Ulendo Wopita ku Yerusalemu

Zimene Yesu anakambirana ndi anthu atatu omwe anakumana nawo m’njira, zingatithandize kudziwa zinthu zimene zingalepheretse munthu kuti akhale wotsatira wake.