YOHANE 10:22-42

  • “INE NDI ATATE NDIFE AMODZI”

  • YESU ANAKANA MLANDU WOTI NDI MULUNGU

Yesu anapita ku Yerusalemu ku chikondwerero chopatulira kachisi (kapena kuti cha Hanuka). Chikondwererochi chinkachitika pokumbukira kupatulidwa kwa kachisi. Zaka zoposa 100 m’mbuyomo Mfumu Antiyokasi Epifinasi IV inamanga guwa lake la nsembe pamwamba pa guwa lansembe lalikulu lomwe linali pa kachisi wa Mulungu. Koma patadutsa nthawi, ana a wansembe wina wachiyuda analanda mzinda wa Yerusalemu ndipo anapatuliranso kachisi uja kwa Yehova. Kuyambira nthawi imeneyo chikondwerero cha pachaka chinkachitika pa 25 m’mwezi wa Kisilevi. Mwezi wa Kisilevi unkayambira chakumapeto kwa mwezi wa November ndipo unkatha chakumayambiriro kwa mwezi wa December.

Nthawiyi inali nyengo yozizira ndipo Yesu ankayenda m’mbali mwa zipilala zomwe zinali m’khonde la kachisi wa Solomo. Pa nthawiyi Ayuda anabwera n’kumuzungulira ndipo anamufunsa kuti: “Utivutitsa maganizo mpaka liti? Ngati ndiwedi Khristu, tiuze mosapita m’mbali.” (Yohane 10:22-24) Kodi Yesu anawayankha bwanji? Anawauza kuti: “Ndakuuzani kale, koma inu simukukhulupirira.” Yesu sanawauze mwachindunji kuti iye ndi Khristu ngati mmene anauzira mzimayi wachisamariya amene anakumana naye pachitsime uja. (Yohane 4:25, 26) Komabe ananena zinthu zimene zikanathandiza anthuwo kuti amuzindikire. Iye anawauza kuti: “Abulahamu asanakhaleko, ine n’kuti ndilipo kale.”—Yohane 8:58.

Yesu ankafuna kuti anthu azidziwa paokha kuti iye ndi Khristu pogwirizanitsa zochita zake ndi zomwe zinalembedwa zofotokoza zimene Khristu adzachite akadzabwera. N’chifukwa chake nthawi zina ankaletsa ophunzira ake kuti asauze anthu kuti iye ndi Mesiya. Koma tsopano Yesu anauza Ayuda omwe anali ovuta aja mosapita m’mbali kuti: “Ntchito zimene ine ndikuchita m’dzina la Atate wanga, zikundichitira umboni. Koma inu simukukhulupirira.”—Yohane 10:25, 26.

N’chifukwa chiyani anthuwo sankakhulupirira kuti Yesu ndi Khristu? Yesuyo ananena kuti: “Koma inu simukukhulupirira, chifukwa si inu nkhosa zanga. Nkhosa zanga zimamva mawu anga. Ine ndimazidziwa, ndipo izo zimanditsatira. Ndidzazipatsa moyo wosatha, moti sizidzawonongeka, komanso palibe amene adzazitsomphole m’dzanja langa. Chimene Atate wanga wandipatsa n’chofunika kuposa zinthu zonse, ndipo palibe amene angazitsomphole m’dzanja la Atate.” Kenako Yesu anafotokoza za ubale wake ndi Mulungu kuti: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” (Yohane 10:26-30) Pa nthawiyi Yesu anali padziko lapansi ndipo Atate wake anali kumwamba. Choncho Yesu sankatanthauza kuti iyeyo ndi Atate wake ndi munthu mmodzi. Yesu ndi Atate wake ndi amodzi chifukwa zolinga zawo ndi zofanana.

Zimene Yesu ananenazi zinakwiyitsa kwambiri Ayudawo moti anatolanso miyala kuti amuphe. Yesu sanachite mantha ndi zimenezi. Iye anati: “Ndakuonetsani ntchito zambiri zabwino zochokera kwa Atate. Tsopano mukundiponya miyala chifukwa cha ntchito iti mwa zimenezi?” Ayudawo anamuyankha kuti: “Sitikukuponya miyala chifukwa cha ntchito yabwino ayi, koma chifukwa chonyoza Mulungu. . . . Ukudziyesa mulungu.” (Yohane 10:31-33) Yesu sananene kuti iye ndi Mulungu. Nanga n’chifukwa chiyani anthuwo ankamuimba mlandu umenewu?

Yesu ankanena kuti anali ndi mphamvu zochokera kwa Mulungu koma Ayudawo ankatsutsa ponena kuti mphamvu zimenezo sizingapezeke ndi munthu aliyense koma Mulungu yekha. Mwachitsanzo, ponena za “nkhosa” zake, Yesu ananena zinthu zimene munthu wina aliyense sangachite. Iye anati: “Ndidzazipatsa moyo wosatha.” (Yohane 10:28) Koma Ayudawo anakana kuvomereza zimene Yesu anawauza zoti analandira mphamvu kuchokera kwa Atate wake.

Pokana mlandu umene ankamuimbawo, Yesu anawafunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo chanu sanalembemo [pa Salimo 82:6] kuti, ‘Ine ndinati “Inu ndinu milungu”’? Ngati anthu amene anatsutsidwa ndi mawu a Mulungu anawatcha ‘milungu,’. . . kodi inu mukundiuza ine woyeretsedwa ndi Atate ndi kutumizidwa m’dziko kuti, ‘Ukunyoza Mulungu,’ chifukwa ndanena kuti, Ndine Mwana wa Mulungu?”—Yohane 10:34-36.

Malemba amatchula za oweruza milandu amene sachita zachilungamo kuti ndi “milungu.” Ndiye n’chifukwa chiyani Ayudawa ankaimba Yesu mlandu chifukwa chonena kuti ndi “Mwana wa Mulungu?” Pofuna kuwathandiza kuti amukhulupirire, Yesu anawauza  kuti: “Ngati sindikuchita ntchito za Atate wanga, musandikhulupirire. Koma ngati ndikuzichita, ngakhale simukundikhulupirira, khulupirirani ntchitozo, kuti mudziwe ndi kupitirizabe kudziwa kuti Atate ndi ine ndife ogwirizana.”—Yohane 10:37, 38.

Ayudawo anakwiya ndi zimenezi ndipo anaganiza zoti amugwire koma Yesu anathawa. Ndiyeno Yesu anachoka ku Yerusalemu n’kupita ku tsidya lina la mtsinje wa Yorodano, dera lomwe Yohane anayambira kubatiza anthu zaka pafupifupi 4 m’mbuyomo. Dera limeneli linali chakufupi ndi kumwera kwa nyanja ya Galileya.

Gulu la anthu linabwera kumene kunali Yesu ndipo linanena kuti: “Yohane sanachite chizindikiro chilichonse, koma zonse zimene Yohane ananena zokhudza munthu uyu zinali zoona.” (Yohane 10:41) Pamenepo Ayuda ambiri anayamba kukhulupirira Yesu.