Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 73

Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu Weniweni

Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu Weniweni

LUKA 10:25-37

  • KODI MUNTHU AYENERA KUCHITA CHIYANI KUTI ADZAPEZE MOYO WOSATHA?

  • MSAMARIYA WACHIFUNDO

Yesu anali adakali chakufupi ndi ku Yerusalemu ndipo Ayuda ena anakamupeza kumeneko. Ena mwa Ayudawo ankafuna kumva uthenga wake pomwe ena ankangofuna kumuyesa. Myuda wina yemwe ankadziwa kwambiri Chilamulo anafunsa Yesu kuti: “Mphunzitsi, ndizichita chiyani kuti ndikapeze moyo wosatha?”—Luka 10:25.

Yesu anazindikira kuti munthuyo anafunsa funsoli osati ndi cholinga choti aphunzirepo kanthu koma mwina ankafuna kuti Yesu anene zinthu zimene zikanakhumudwitsa Ayuda enawo. Yesu ankadziwa mmene munthuyo ankaganizira, choncho anamufunsa funso lomwe linachititsa munthuyo kufotokoza yekha zimene ankaganiza.

Anamufunsa kuti: “Kodi m’Chilamulo analembamo chiyani? Umawerengamo zotani?” Munthuyo ankachidziwa bwino Chilamulo cha Mulungu, choncho anayankha mogwirizana ndi zimene Chilamulocho chinkanena. Ananena mawu opezeka pa Deuteronomo 6:5 ndi pa Levitiko 19:18, amene amati: “‘Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse, moyo wako wonse, mphamvu zako zonse, ndi maganizo ako onse.’ Komanso, ‘uzikonda mnzako mmene umadzikondera wekha.’” (Luka 10:26, 27) Kodi anayankha molondola?

Inde, chifukwa Yesu anamuuza kuti: “Wayankha molondola. ‘Uzichita zimenezo, ndipo udzapeza moyo.” Koma nkhaniyi siinathere pomwepo. Munthuyo ankangofuna “kudzionetsa kuti ndi wolungama” choncho sankafuna kuti Yesu angomuuza yankho lolondola. Ankafuna kuti zimene Yesu angamuyankhe zisonyeze kuti maganizo ake ndi olondola n’cholinga choti aoneke kuti ankachita zinthu mwachilungamo ndi anthu ena. Ndiyeno anafunsa Yesu kuti: “Nanga mnzanga amene ndikuyenera kumukonda ndani kwenikweni?” (Luka 10:28, 29) Yankho la funsoli silinali lophweka. N’chifukwa chiyani tikutero?

Tikutero chifukwa Ayuda ankakhulupirira kuti mawu akuti “mnzanga” ankatanthauza munthu yekhayo amene ankasunga miyambo yachiyuda. Ndipo n’kutheka kuti ankaganiza kuti ndi zimene mawu opezeka pa Levitiko 19:18 ankatanthauza. Ayuda ankanena kuti kugwirizana ndi anthu omwe sanali Ayuda “n’kosaloleka.” (Machitidwe 10:28) Choncho munthu ameneyu ankadziona kuti ndi wolungama chifukwa chochitira chifundo Ayuda anzake ndipo mwina ophunzira ena a Yesu analinso ndi maganizo amenewa. Anthuwa ankaona kuti akhoza kuchitira nkhanza munthu yemwe sanali Myuda ndipo ankadzikhululukira ponena kuti munthuyo si ‘mnzawo.’

Kodi Yesu akanathandiza bwanji munthuyo komanso Ayuda ena kusintha maganizo olakwikawo popanda kuwakhumudwitsa? Anachita zimenezi powafotokozera fanizo. Iye anati: “Munthu wina anali kuyenda kuchokera ku Yerusalemu kupita ku Yeriko. Ndipo anakumana ndi achifwamba amene anam’vula ndi kumumenya koopsa. Kenako anapita, n’kumusiya ali pafupi kufa.” Anapitiriza kufotokoza kuti: “Ndiye zinangochitika kuti wansembe wina anali kuyenda mumsewu womwewo, koma atamuona, anangomulambalala. Chimodzimodzinso Mlevi, atadutsa msewuwo n’kufika pamalo amenewo ndi kumuona, anangomulambalala. Koma panafika Msamariya wina amene anali kudutsanso msewu umenewo. Ndipo atamuona, anagwidwa chifundo.”—Luka 10:30-33.

Munthu amene Yesu ankamufotokozera nkhaniyi ankadziwa kuti ansembe ambiri komanso Alevi omwe ankathandiza ntchito za pakachisi ankakhala ku Yeriko. Kachisi wa ku Yerusalemu anali kumtunda choncho ansembe komanso Alevi ankatsetsereka pobwerera kwawo ku Yeriko. Ulendowu unali wa makilomita pafupifupi 23 ndipo msewuwu unali woopsa chifukwa munkakhala achifwamba ambiri. Ngati wansembe kapena Mlevi atapeza Myuda mnzawo atavutika munsewuwo ankafunika kumuthandiza. Koma m’fanizo limene Yesu ananenali ansembe komanso Alevi sanachite zimenezi. Amene anathandiza Myuda wovulalayo anali Msamariya ndipo pa nthawiyi Ayuda ankadana kwambiri ndi Asamariya.—Yohane 8:48.

Kodi Msamariyayo anathandiza bwanji Myuda amene anavulalayo? Yesu anapitiriza kufotokoza kuti: “Anam’yandikira ndi kumanga mabala ake. Anathira mafuta ndi vinyo m’mabalamo. Kenako anam’kweza pachiweto chake n’kupita naye kunyumba ya alendo kumene anam’samalira. Tsiku lotsatira anatulutsa madinari awiri ndi kupereka kwa mwini nyumba ya alendoyo. Ndiyeno anamuuza kuti, ‘Musamalireni bwino,  mukawononga ndalama zina zowonjezera, ndidzakubwezerani ndikadzabwera.’”—Luka 10:34, 35.

Yesu, yemwe anali Mphunzitsi Waluso, atamaliza kufotokoza fanizolo anafunsa munthu uja funso lomuchititsa kuganiza. Anamufunsa kuti: “Ndani mwa atatuwa amene iweyo ukuona kuti anakonda munthu amene anakumana ndi achifwambayu?” N’kutheka kuti munthuyo sankafuna kuyankha kuti “Msamariya,” choncho anangoyankha kuti: “Ndi amene anam’chitira chifundoyo.” Kenako Yesu anathandiza munthuyo kumvetsa mfundo yaikulu ya fanizoli pomuuza kuti: “Pita, iwenso uzikachita zomwezo.”—Luka 10:36, 37.

Imeneyi inali njira yabwino kwambiri yophunzitsira. Ngati Yesu akanangouza munthuyo kuti azionanso anthu ena omwe sanali Ayuda kuti ndi anzake, munthuyo komanso Ayuda ena amene ankamvetsera sakanavomereza zimenezi. Koma chifukwa chakuti Yesu ananena fanizo losavuta kumva komanso anafotokoza zinthu zomwe anthuwo ankazidziwa bwino, zinali zosavuta kuti anthuwo adziwe kuti mnzawo weniweni anali ndani. Choncho tinganene kuti mnzathu weniweni ndi munthu amene amatikonda komanso kutichitira chifundo mogwirizana ndi zimene Malemba amanena.