Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

 MUTU 72

Yesu Anatumiza Ophunzira 70 Kuti Akalalikire

Yesu Anatumiza Ophunzira 70 Kuti Akalalikire

LUKA 10:1-24

  • YESU ANASANKHA OPHUNZIRA 70 NDIPO ANAWATUMIZA KUTI AKALALIKIRE

Pofika chakumapeto kwa chaka cha 32 C.E., n’kuti patadutsa zaka zitatu kuchokera pamene Yesu anabatizidwa. Iye ndi ophunzira ake anali atangochoka kumene ku Chikondwerero cha Misasa ku Yerusalemu ndipo ayenera kuti anali chakufupi ndi ku Yerusalemuko. (Luka 10:38; Yohane 11:1) Pa nthawiyi kunali kutatsala miyezi 6 kuti Yesu aphedwe ndipo anathera nthawi yambiri akulalikira m’dera la Yudeya kapena m’chigawo cha Pereya, chomwe chinali kutsidya lina la mtsinje wa Yorodano. Iye analalikira kwambiri m’madera amenewa chifukwa ankafuna kuti anthu a kumenekonso amve uthenga wake.

Kumbukirani kuti mwambo wa Pasika wa mu 30 C.E. utatha, Yesu anakhala miyezi ingapo akulalikira ku Yudeya komanso m’madera a ku Samariya. Kenako Pasika wa mu 31 C.E. atayandikira, Ayuda omwe ankakhala ku Yerusalemu ankafuna kumupha. Kuchokera nthawi imeneyo, Yesu anatha chaka ndi hafu akulalikira chakumpoto ku Galileya ndipo anthu ambiri anakhala otsatira ake. Ali ku Galileya, Yesu anaphunzitsa atumwi ake mmene angalalikirire kenako anawapatsa malangizo akuti: “Pitani ndi kulalikira kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’” (Mateyu 10:5-7) Koma tsopano Yesu anakonza zoti agwire ntchito yapadera yolalikira m’dera la Yudeya.

Yesu anayamba ntchito yapaderayi posankha ophunzira 70 n’kuwatumiza kuti akalalikire ndipo anawagawa awiriawiri. Ndiye kuti panali magulu 35 a anthu olalikira za Ufumu m’dera lomwe zokolola zinali zochuluka koma antchito anali ochepa. (Luka 10:2) Ophunzirawo ndi amene anatsogola kukayamba kulalikira ndipo Yesu ankabwera m’mbuyo mwawo. Ophunzirawo ankachiritsa odwala komanso kulalikira za uthenga umenenso Yesu ankalalikira.

Chifukwa chakuti Yesu anawauza kuti azipita m’nyumba za anthu, ophunzirawo sankalalikira kwambiri m’masunagoge. Iye anawauza kuti: “Mukafika panyumba, choyamba muzinena kuti, ‘Mtendere ukhale panyumba pano.’ Ndipo ngati pakhomopo pali munthu wokonda mtendere, mtendere wanu udzakhala pa iye.” Kodi ankalalikira uthenga woti chiyani? Yesu anati: “Muziwauza kuti, ‘Ufumu wa Mulungu wakuyandikirani.’”—Luka 10:5-9.

Pamene Yesu ankatumiza ophunzirawa anawapatsanso malangizo ofanana ndi amene anapereka kwa atumwi ake 12 atawatuma kuti akalalikire kudakali chaka chimodzi zimenezi zisanachitike. Anawachenjeza kuti si onse amene akawalandire bwino. Koma ntchito imene ophunzirawo anagwira inakonzekeretsa mitima ya anthu ofuna kuphunzira choonadi moti pamene Yesu ankafika, anthuwo anali ofunitsitsa kumuona komanso kumvetsera uthenga wake.

Koma pasanapite nthawi yaitali, ophunzirawo omwe anagawidwa m’magulu 35, anabwerera kwa Yesu ali osangalala kwambiri. Atafika anamuuza kuti: “Ambuye, ngakhale ziwanda zinatigonjera pamene tinagwiritsa ntchito dzina lanu.” Yesu anasangalala kwambiri ndi lipoti limene ophunzirawa anabweretsa moti ananena kuti: “Ndinayamba kuona Satana atagwa  kale ngati mphezi kuchokera kumwamba. Taonani! Inetu ndakupatsani ulamuliro kuti muzitha kupondaponda njoka ndi zinkhanira.”—Luka 10:17-19.

Yesu anatsimikizira ophunzira akewo kuti adzakhala ndi mphamvu zotha kulimbana ndi zinthu zoopsa kwambiri, komwe kunali ngati kupondaponda njoka komanso zinkhanira. Zimenezi zinawatsimikiziranso kuti Satana adzagwetsedwadi kuchokera kumwamba. Yesu anathandizanso ophunzirawo kuti adziwe kufunika kogwira ntchitoyo. Iye anati: “Musakondwere ndi zimenezi, kuti mizimu yakugonjerani, koma kondwerani chifukwa mayina anu alembedwa kumwamba.”—Luka 10:20.

Yesu anasangalala kwambiri ndipo anthu onse akuona, iye analemekeza Atate wake chifukwa chopatsa mphamvu atumiki ake odzichepetsawo kuti agwire ntchito yapaderayi. Kenako Yesu anatembenukira kwa ophunzira ake n’kuwauza kuti: “Pakuti ndikukuuzani, Aneneri ndi mafumu ambiri analakalaka kuona zimene mukuzionazi, koma sanazione. Analakalaka kumva zimene mukumvazi koma sanazimve.”—Luka 10:23, 24.