Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 GAWO 4

Yesu Anakalalikira ku Yudeya

“Pemphani mwini zokololazo kuti atumize antchito.”—Luka 10:2

Yesu Anakalalikira ku Yudeya

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 66

Zimene Zinachitika Yesu Atapita ku Chikondwerero cha Misasa ku Yerusalemu

N’chifukwa chiyani anthu ena ankaganiza kuti Yesu anali ndi chiwanda?

MUTU 67

“Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyo”

Ngakhale anthu onse a m’khoti lalikulu la Ayuda ankatsutsa Yesu, panapezeka munthu mmodzi amene analimba mtima n’kulankhula momuikira kumbuyo.

MUTU 68

Mwana wa Mulungu Ndiye “Kuwala kwa Dziko”

Yesu ananena kuti “choonadi chidzakumasulani.” Kodi ankatanthauza kumasulidwa ku chiyani?

MUTU 69

Kodi Atate Wawo Anali Abulahamu Kapena Mdyerekezi?

Yesu anafotokoza mmene munthu angadziwire ana a Abulahamu, komanso kuti Atate ake ndi ndani.

MUTU 70

Yesu Anachiritsa Munthu Amene Anabadwa Wosaona

Ophunzira anafunsa chifukwa chake munthuyo anali wakhungu. Kodi anachimwa? Kodi makolo ake ndi amene anachimwa? Anthu anasiyana maganizo Yesu atachiritsa munthuyu.

MUTU 71

Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu

Afarisi anakwiya ndi zimene munthu amene poyamba anali wakhungu anayankha. Afarisi anachotsa munthuyo m’sunagoge ndipo zimenezi n’zimene makolo ake ankaopa.

MUTU 72

Yesu Anatumiza Ophunzira 70 Kuti Akalalikire

Yesu ali ku Yudeya anatumiza ophunzira 70 ndipo anawauza kuti akalalikire za Ufumu. Kodi ophunzirawo anakalalikira ku sunagoge kapena kunyumba za anthu?

MUTU 73

Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu Weniweni

Kodi Yesu anagwiritsa ntchito fanizo liti pophunzitsa mfundo yofunika kwambiri?

MUTU 74

Zimene Tikuphunzira pa Nkhani Yochereza Alendo Komanso ya Pemphero

Yesu anapita kukacheza kunyumba kwa Marita ndi Mariya. Kodi anawaphunzitsa chiyani pa nkhani yochereza alendo? Kodi anawaphunzitsa bwanji ophunzira ake kudziwa zimene angatchule popemphera?

MUTU 75

Yesu Ananena Zimene Zimachititsa Munthu Kukhala Wodala

Yesu anayankha anthu amene ankamutsutsa ndipo anawauza za “chala cha Mulungu” komanso kuti Ufumu wa Mulungu unawafikira modzidzimutsa. Ananenanso zimene anthu angachite kuti akhale odala kapena kuti osangalala.

MUTU 76

Anakadya Kunyumba kwa Mfarisi

Yesu anaulula zinthu zachinyengo zimene Afarisi ndi alembi ankachita. Kodi ndi katundu wolemera uti amene ankakakamiza anthu kuti anyamule?

MUTU 77

Yesu Anapereka Malangizo pa Nkhani ya Chuma

Yesu ananena fanizo la munthu wachuma yemwe anamanga nkhokwe zikuluzikulu. Kodi Yesu anabwerezanso malangizo ati pofuna kuchenjeza anthu za kuopsa kofunafuna chuma?

MUTU 78

Woyang’anira Nyumba Wokhulupirika Ayenera Kukhala Wokonzeka

Yesu anasonyeza kuti ankaganizira za moyo wauzimu wa ophunzira ake. Kodi woyang’anira nyumba ali ndi udindo wotani posamalira moyo wauzimu wa ophunzira a Yesu? N’chifukwa chiyani kukhala wokonzeka kuli kofunika kwambiri?

MUTU 79

Ayuda Ankayembekezera Kuwonongedwa

Yesu ananena kuti anthu amene ankawathandiza ankayembekezera kuwonongedwa chifukwa choti sanalape. Kodi anthuwo anaphunzirapo kanthu pa zimene Yesu anawaphunzitsa zoti aziganizira kwambiri za ubwenzi wawo ndi Mulungu?

MUTU 80

M’busa Wabwino Komanso Makola Awiri a Nkhosa

Mmene m’busa amachitira zinthu ndi nkhosa zake ndi mmenenso Yesu amachitira ndi ophunzira ake. Kodi ophunzirawo amazindikira zimene Yesu amaphunzitsa ndiponso kumutsatira?

MUTU 81

Yesu si Mulungu Koma Iye ndi Atate Wake Ndi Amodzi

Ena mwa anthu amene ankatsutsa Yesu anamuimba mlandu woti ankadziyesa kuti ndi Mulungu. Kodi Yesu anakana bwanji mlanduwu?