Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yesu—Ndi Njira, Choonadi ndi Moyo

Werengani bukuli kuti mudziwe zonse zimene zinachitika pa moyo wa Yesu monga mmene Baibulo limafotokozera.

MAWU OYAMBA

Njira, Choonadi ndi Moyo

Zimene Yesu ankachita komanso kuphunzitsa zinalembedwa m’mabuku a Uthenga Wabwino ndipo zingasinthe moyo wanu.

MUTU 1

Mauthenga Awiri Ochokera kwa Mulungu

Mngelo Gabirieli anapereka mauthenga ovuta kuwakhulupirira.

MUTU 2

Yesu Analemekezedwa Asanabadwe

Kodi Elizabeti komanso mwana amene anali m’mimba mwake analemekeza bwanji Yesu?

MUTU 3

Kubadwa kwa Wokonza Njira

Zekariya atayambiranso kulankhula ananena ulosi wofunika kwambiri.

MUTU 4

Mariya Anakhala ndi Pakati Asanakwatiwe

Kodi Yosefe anakhulupirira zimene Mariya anamuuza kuti anali ndi pakati, chifukwa cha mzimu woyera osati chifukwa chakuti anagona ndi mwamuna wina?

MUTU 5

Kodi Yesu Anabadwa Liti Ndipo Anabadwira Kuti?

Kodi timadziwa bwanji kuti Yesu sanabadwe pa 25 December?

MUTU 6

Mwana Amene Mulungu Analonjeza

Yosefe ndi Mariya atapita ndi Yesu kukachisi, Aisiraeli awiri omwe anali achikulire ananeneratu zimene Yesu adzachite m’tsogolo.

MUTU 7

Okhulupirira Nyenyezi Anapita Kukaona Yesu

N’chifukwa chiyani nyenyezi imene inatsogolera anthu a kum’mawa inayamba kuwatsogolera kwa mfumu yankhanza Herode, m’malo mowatsogolera kwa Yesu?

MUTU 8

Anathawa Mfumu Yankhanza

Maulosi atatu a m’Baibulo onena za Mesiya anakwaniritsidwa Yesu akadali mwana.

MUTU 9

Yesu Anakulira Ku Nazareti

Kodi Yesu anali ndi achimwene ndi achemwali angati?

MUTU 10

Yosefe ndi Banja Lake Anapita ku Yerusalemu

Yosefe ndi Mariya anavutika kwambiri Yesu atasowa, pomwe Yesuyo anadabwa kwambiri kuti makolo ake samadziwa kumene akanamupeza.

MUTU 11

Yohane M’batizi Anakonza Njira

Afarisi ndi Asaduki atapita kwa Yohane, iye anawadzudzula. N’chifukwa chiyani anachita zimenezi?

MUTU 12

Zimene Zinachitika Pamene Yesu Ankabatizidwa

Popeza Yesu analibe uchimo, n’chifukwa chiyani anabatizidwa?

MUTU 13

Zimene Yesu Anachita Atayesedwa

Zimene Yesu anakumana nazo poyesedwa zimatithandiza kudziwa mfundo ziwiri zokhudza Mdyerekezi.

MUTU 14

Yesu Anayamba Kupeza Ophunzira

N’chiyani chinatsimikizira ophunzira 6 oyambirira a Yesu kuti apeza Mesiya?

MUTU 15

Chozizwitsa Choyamba Chimene Yesu Anachita

Zimene Yesu anayankha mayi ake zinasonyeza kuti cholinga chake chinali kuchita zimene Atate wake wakumwamba amuuza, osati zimene mayi akewo anamuuza.

MUTU 16

Yesu Anali Wodzipereka pa Kulambira Mulungu

Chilamulo cha Mulungu chinkalola anthu kugula nyama zoti apereke nsembe ku Yerusalemu, nanga n’chifukwa chiyani Yesu anakwiya ndi amalonda mu kachisi?

MUTU 17

Yesu Anaphunzitsa Nikodemo

Kodi “kubadwanso” kumatanthauza chiyani?

MUTU 18

Ntchito ya Yesu Inayamba Kuwonjezeka Kuposa ya Yohane

Ophunzira a Yohane M’batizi ankachita nsanje ngakhale kuti Yohane sankachita nsanje.

MUTU 19

Yesu Analalikira Mayi wa ku Samariya

Yesu anamuuza zinthu zimene anali asanauzepo munthu aliyense.

MUTU 20

Chozizwitsa Chachiwiri Chimene Yesu Anachita Ku Kana

Yesu anachiritsa mwana yemwe anali pamtunda wa makilomita 26.

MUTU 21

Zimene Zinachitika Yesu Ali ku Sunagoge wa ku Nazareti

Kodi Yesu ananena chiyani kuti anthu a m’tauni ya kwawo afike pofuna kumupha?

MUTU 22

Yesu Anaitana Ophunzira Ake 4

Anawaitana kuti asiye mtundu wina wa usodzi n’kuyamba wina.

MUTU 23

Yesu Anachita Zozizwitsa Ali ku Kaperenao

Pamene Yesu ankatulutsa mizimu yoipa, n’chifukwa chiyani analetsa mizimuyo kuti isawuze anthu kuti iyeyo ndi Mwana wa Mulungu?

MUTU 24

Yesu Analalikira M’madera Ambiri a ku Galileya

Anthu anapita kwa Yesu kuti akachiritsidwe, komabe Yesu anafotokoza kuti utumiki wake unali ndi cholinga chinachake chapadera.

MUTU 25

Yesu Anachitira Chifundo Munthu Wakhate N’kumuchiritsa

Yesu analankhula mawu ochepa koma amphamvu kwambiri ndipo zimene analankhulazo zinasonyeza kuti ankaganizira anthu amene ankawachiritsa.

MUTU 26

“Machimo Ako Akhululukidwa”

Kodi Yesu anasonyeza kuti pali kugwirizana kotani pakati pa uchimo ndi matenda?

MUTU 27

Yesu Anaitana Mateyu

N’chifukwa chiyani Yesu anadya ndi anthu ochimwa?

MUTU 28

N’chifukwa Chiyani Ophunzira a Yesu Sankasala Kudya?

Poyankha Yesu anafotokoza fanizo la matumba a chikopa.

MUTU 29

Kodi Kunali Kulakwa Kugwira Ntchito Yabwino pa Sabata?

N’chifukwa chiyani Ayuda ankavutitsa Yesu atachiritsa munthu amene ankadwala kwa zaka 38?

MUTU 30

Kodi Pali Ubale Wotani Pakati pa Yesu ndi Mulungu?

Ayuda ankaganiza kuti Yesu ankadziona kuti ndi wofanana ndi Mulungu, koma Yesu anafotokoza kuti Mulungu ndi wamkulu kwa iyeyo.

MUTU 31

Anabudula Ngala za Tirigu pa Tsiku la Sabata

N’chifukwa chiyani Yesu ananena kuti iye ndi “Mbuye wa Sabata”?

MUTU 32

Kodi Malamulo Ankalola Munthu Kuchita Chiyani pa Sabata?

Nthawi zambiri Asaduki ndi Afarisi sankagwirizana koma anagwiriza n’cholinga choti atsutse Yesu.

MUTU 33

Ulosi wa Yesaya Unakwaniritsidwa

N’chifukwa chiyani Yesu ankauza anthu amene wawachiritsa kuti asamauze anthu ena zimene wachita komanso kuti iye ndi ndani?

MUTU 34

Yesu Anasankha Atumwi 12

Kodi panali kusiyana kotani pakati pa atumwi ndi ophunzira?

MUTU 35

Ulaliki Wotchuka wa Paphiri

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe mfundo zofunika kwambiri zimene Yesu anaphunzitsa.

MUTU 36

Kapitawo wa Asilikali Anasonyeza Kuti Anali ndi Chikhulupiriro

Kodi kapitawo wa asilikali anachita chiyani chomwe chinadabwitsa Yesu?

MUTU 37

Yesu Anaukitsa Mwana Wamwamuna wa Mzimayi Wamasiye

Anthu amene anaona Yesu akuukitsa mnyamatayo anamvetsa tanthauzo lake.

MUTU 38

Yohane Yemwe Anali M’ndende Ankafuna Kumva Kuchokera kwa Yesu

N’chifukwa chiyani Yohane m’batizi anafunsa ngati Yesu analidi Mesiya? Kodi Yohane ankakayikira?

MUTU 39

Tsoka kwa M’badwo Umene Sunamvere

Yesu ananena kuti chilango cha Sodomu pa Tsiku la Chiweruzo chidzakhala chocheperako poyerekeza ndi cha Kaperenao. Ku Kaperenao n’kumene Yesu ankakhala nthawi zambiri.

MUTU 40

Anawaphunzitsa Kukhululukira Ena

Kodi pamene Yesu anauza mzimayi yemwe mwina anali hule kuti machimo ake akhululukidwa, ankatanthauza kuti palibe vuto lililonse ngati munthu atachita zinthu zosiyana ndi malamulo a Mulungu?

MUTU 41

Kodi Yesu Ankazitenga Kuti Mphamvu Zochitira Zozizwitsa?

Abale ake a Yesu ankaganiza kuti wachita misala.

MUTU 42

Yesu Anadzudzula Afarisi

Kodi “chizindikiro cha mneneri Yona” chinkatanthauza chiyani?

MUTU 43

Mafanizo Ofotokoza za Ufumu

Yesu ananena mafanizo okwana 8 ofotokoza za Ufumu wakumwamba.

MUTU 44

Yesu Analetsa Mphepo Yamphamvu Panyanja

Zimene Yesu anachita poletsa mphepo ndi mafunde pa nyanja zimasonyeza mmene moyo udzakhalire akadzayamba kulamulira monga Mfumu.

MUTU 45

Anatulutsa Ziwanda Zambiri

Kodi n’zotheka kuti munthu akhale ndi ziwanda zambiri?

MUTU 46

Anachira Atagwira Malaya a Yesu

Yesu anasonyeza kuti anali wachifundo komanso kuti anali ndi mphamvu pamene anachiritsa mzimayi wodwala matenda otaya magazi.

MUTU 47

Kamtsikana Kanakhalanso ndi Moyo

Yesu atanena kuti mtsikana womwalirayo akugona anthu anayamba kuseka kwambiri. Kodi anthuwo sankadziwa kuti Yesu akhoza kuchita chiyani?

MUTU 48

Yesu Anachita Zozizwitsa Koma Anakanidwa Ngakhale Kwawo ku Nazareti

Anthu a ku Nazareti anakana Yesu, osati chifukwa cha zozizwitsa kapena zimene ankaphunzitsa, koma anali ndi zifukwa zina.

MUTU 49

Analalikira ku Galileya Komanso Anaphunzitsa Atumwi

Kodi mawu akuti ‘Ufumu wakumwamba wayandikira’ ankatanthauza chiyani?

MUTU 50

Anawakonzekeretsa Kuti Azilalikira Ngakhale Pamene Akuzunzidwa

Popeza atumwi sankafunika kuopa imfa, n’chifukwa chiyani Yesu anawauza kuti adzathawe akamadzazunzidwa?

MUTU 51

Anaphedwa pa Tsiku Lokondwerera Kubadwa

Salome anasangalatsa Herode ndi mmene anavinira moti Herode anamulonjeza kuti amupatsa chilichonse chimene angapemphe. Kodi Salome anapempha chiyani?

MUTU 52

Anadyetsa Anthu Masauzande Ambiri ndi Mikate Komanso Nsomba Zochepa

Chozizwitsa chimene Yesu anachita pa nthawi imeneyi chinali chapadera kwambiri moti chinalembedwa m’Mauthenga onse 4.

MUTU 53

Wolamulira Amene Akhoza Kulamulira Mphepo Yamphamvu

Kodi atumwi anazindikira chiyani ataona Yesu akuyenda pamadzi komanso ataletsa mphepo yamphamvu?

MUTU 54

Yesu Ndiye “Chakudya Chopatsa Moyo”

N’chifukwa chiyani Yesu anadzudzula anthu ngakhale kuti anayesetsa kumufunafuna kuti amupeze?

MUTU 55

Kudya Mnofu wa Yesu ndi Kumwa Magazi Ake

Yesu anaphunzitsa zinthu zimene zinadabwitsa ophunzira ake moti ambiri anasiya kumutsatira.

MUTU 56

Kodi Chimaipitsa Munthu N’chiyani?

Kodi chimaipitsa munthu n’chiyani, kodi ndi zimene zimalowa m’kamwa kapena zimene zimatuluka m’kamwamo?

MUTU 57

Yesu Anachiritsa Mtsikana Komanso Munthu Wogontha

N’chifukwa chiyani mayiyu sanakhumudwe Yesu atayerekezera anthu a mtundu wake ngati tiagalu?

MUTU 58

Anachulukitsa Mikate Komanso Anachenjeza Ophunzira Ake za Zofufumitsa

Ophunzira a Yesu anamvetsa tanthauzo la zofufumitsa zimene Yesu ankawachenjeza nazo.

MUTU 59

Kodi Mwana wa Munthu Ndi Ndani?

Kodi makiyi a Ufumu n’chiyani? Ndani anawagwiritsa ntchito ndipo anawagwiritsa ntchito bwanji?

MUTU 60

Anaona Ulemelero wa Khristu Atasandulika

Kodi atumwi anaona chiyani m’masomphenya? Nanga zimenezi zinkatanthauza chiyani?

MUTU 61

Yesu Anachiritsa Mnyamata Amene Anali ndi Chiwanda

Yesu panafunika chikhulupiriro cholimba kuti mnyamata uja achiritsidwe n’chifukwa chake zinakanika poyamba paja. Koma kodi ndi ndani amene ankafunika kukhala ndi chikhulupirirocho, ndi mnyamatayo, bambo ake kapena ophunzira a Yesu?

MUTU 62

Kufunika Kokhala Wodzichepetsa

Anthu akuluakulu anaphunzira khalidwe lofunika kwambiri kwa kamwana kakang’ono.

MUTU 63

Yesu Anafotokoza Zoyenera Kuchita Anthu Akakhumudwitsana Komanso Ngati Wina Wachita Tchimo

Yesu anafotokoza malangizo amene abale ayenera kutsatira ngati wina wachita tchimo lalikulu.

MUTU 64

Anawaphunzitsa Kufunika Kokhululukira Ena

Yesu anagwiritsa ntchito fanizo la kapolo wopanda chifundo pofuna kusonyeza kuti Mulungu amatikhululukira ngati ifenso timayesetsa kukhululukira anzathu.

MUTU 65

Yesu Anaphunzitsa Anthu Ena Ali pa Ulendo Wopita ku Yerusalemu

Zimene Yesu anakambirana ndi anthu atatu omwe anakumana nawo m’njira, zingatithandize kudziwa zinthu zimene zingalepheretse munthu kuti akhale wotsatira wake.

MUTU 66

Zimene Zinachitika Yesu Atapita ku Chikondwerero cha Misasa ku Yerusalemu

N’chifukwa chiyani anthu ena ankaganiza kuti Yesu anali ndi chiwanda?

MUTU 67

“Palibe Munthu Amene Analankhulapo Ngati Iyeyo”

Ngakhale anthu onse a m’khoti lalikulu la Ayuda ankatsutsa Yesu, panapezeka munthu mmodzi amene analimba mtima n’kulankhula momuikira kumbuyo.

MUTU 68

Mwana wa Mulungu Ndiye “Kuwala kwa Dziko”

Yesu ananena kuti “choonadi chidzakumasulani.” Kodi ankatanthauza kumasulidwa ku chiyani?

MUTU 69

Kodi Atate Wawo Anali Abulahamu Kapena Mdyerekezi?

Yesu anafotokoza mmene munthu angadziwire ana a Abulahamu, komanso kuti Atate ake ndi ndani.

MUTU 70

Yesu Anachiritsa Munthu Amene Anabadwa Wosaona

Ophunzira anafunsa chifukwa chake munthuyo anali wakhungu. Kodi anachimwa? Kodi makolo ake ndi amene anachimwa? Anthu anasiyana maganizo Yesu atachiritsa munthuyu.

MUTU 71

Afarisi Anatsutsana ndi Munthu Amene Anali Wakhungu

Afarisi anakwiya ndi zimene munthu amene poyamba anali wakhungu anayankha. Afarisi anachotsa munthuyo m’sunagoge ndipo zimenezi n’zimene makolo ake ankaopa.

MUTU 72

Yesu Anatumiza Ophunzira 70 Kuti Akalalikire

Yesu ali ku Yudeya anatumiza ophunzira 70 ndipo anawauza kuti akalalikire za Ufumu. Kodi ophunzirawo anakalalikira ku sunagoge kapena kunyumba za anthu?

MUTU 73

Nkhani ya Msamariya Imatithandiza Kudziwa Mnzathu Weniweni

Kodi Yesu anagwiritsa ntchito fanizo liti pophunzitsa mfundo yofunika kwambiri?

MUTU 74

Zimene Tikuphunzira pa Nkhani Yochereza Alendo Komanso ya Pemphero

Yesu anapita kukacheza kunyumba kwa Marita ndi Mariya. Kodi anawaphunzitsa chiyani pa nkhani yochereza alendo? Kodi anawaphunzitsa bwanji ophunzira ake kudziwa zimene angatchule popemphera?

MUTU 75

Yesu Ananena Zimene Zimachititsa Munthu Kukhala Wodala

Yesu anayankha anthu amene ankamutsutsa ndipo anawauza za “chala cha Mulungu” komanso kuti Ufumu wa Mulungu unawafikira modzidzimutsa. Ananenanso zimene anthu angachite kuti akhale odala kapena kuti osangalala.

MUTU 76

Anakadya Kunyumba kwa Mfarisi

Yesu anaulula zinthu zachinyengo zimene Afarisi ndi alembi ankachita. Kodi ndi katundu wolemera uti amene ankakakamiza anthu kuti anyamule?

MUTU 77

Yesu Anapereka Malangizo pa Nkhani ya Chuma

Yesu ananena fanizo la munthu wachuma yemwe anamanga nkhokwe zikuluzikulu. Kodi Yesu anabwerezanso malangizo ati pofuna kuchenjeza anthu za kuopsa kofunafuna chuma?

MUTU 78

Woyang’anira Nyumba Wokhulupirika Ayenera Kukhala Wokonzeka

Yesu anasonyeza kuti ankaganizira za moyo wauzimu wa ophunzira ake. Kodi woyang’anira nyumba ali ndi udindo wotani posamalira moyo wauzimu wa ophunzira a Yesu? N’chifukwa chiyani kukhala wokonzeka kuli kofunika kwambiri?

MUTU 79

Ayuda Ankayembekezera Kuwonongedwa

Yesu ananena kuti anthu amene ankawathandiza ankayembekezera kuwonongedwa chifukwa choti sanalape. Kodi anthuwo anaphunzirapo kanthu pa zimene Yesu anawaphunzitsa zoti aziganizira kwambiri za ubwenzi wawo ndi Mulungu?

MUTU 80

M’busa Wabwino Komanso Makola Awiri a Nkhosa

Mmene m’busa amachitira zinthu ndi nkhosa zake ndi mmenenso Yesu amachitira ndi ophunzira ake. Kodi ophunzirawo amazindikira zimene Yesu amaphunzitsa ndiponso kumutsatira?

MUTU 81

Yesu si Mulungu Koma Iye ndi Atate Wake Ndi Amodzi

Ena mwa anthu amene ankatsutsa Yesu anamuimba mlandu woti ankadziyesa kuti ndi Mulungu. Kodi Yesu anakana bwanji mlanduwu?

MUTU 82

Zimene Zinachitika Pamene Yesu Ankalalikira ku Pereya

Yesu anauza anthu amene ankamumvetsera kudziwa zoyenera kuchita kuti akapulumuke komanso zimene zidzalepheretse anthu ena kupulumuka. Zimene Yesu ananena zinali zothandiza nthawi imeneyo. Kodi zimene ananenazo ndi zothandizanso masiku ano?

MUTU 83

Kuitanira Anthu ku Chakudya

Yesu atapita kukadya chakudya chamadzulo kunyumba kwa Mfarisi, ananena fanizo la phwando lalikulu la chakudya chamadzulo. Anagwiritsa ntchito fanizoli pophunzitsa mfundo yofunika kwambiri kwa anthu onse a Mulungu. Kodi mfundo yake inali yoti chiyani?

MUTU 84

Kukhala Wophunzira wa Yesu Ndi Udindo Waukulu

Kukhala wophunzira wa Khristu ndi udindo waukulu kwambiri. Yesu anafotokoza zimene munthu ayenera kuchita kuti akhale wotsatira wake ndipo anthu ena, omwe anadzakhala otsatira ake, anadabwa ndi zimene ananenazo.

MUTU 85

Pamakhala Chisangalalo Munthu Wochimwa Akalapa

Afarisi ndi alembi anadzudzula Yesu chifukwa chochita zinthu ndi anthu. Koma powayankha Yesu anagwiritsa ntchito mafanizo pofuna kuwathandiza kudziwa mmene Mulungu amaonera anthu ochimwa.

MUTU 86

Mwana Wotayika Anabwerera

Kodi tikuphunzira chiyani m’fanizo la Yesu la mwana wotayika?

MUTU 87

Muzichita Zinthu Mwanzeru Pokonzekera Zakutsogolo

Yesu ananena fanizo la woyang’anira amene anachita zinthu mwachinyengo pofuna kuphunzitsa mfundo yofunika kwambiri ya choonadi.

MUTU 88

Mmene Zinthu Zinasinthira kwa Munthu Wachuma Komanso kwa Lazaro

Kuti munthu amvetse fanizo la Yesuli ayenera kudziwa kuti anthu a m’fanizoli akuimira ndani.

MUTU 89

Anaphunzitsa ku Pereya Ali pa Ulendo Wopita ku Yudeya

Anafotokoza za khalidwe lomwe lingatithandize kuti tizikhululukira anthu ena ngakhale amene amatilakwira mobwerezabwereza.

MUTU 90

Yesu Ndi “Kuuka ndi Moyo”

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti onse omukhulupirira “sadzafa”?

MUTU 91

Yesu Anaukitsa Lazaro

Panali zinthu ziwiri zimene zinachititsa anthu amene ankatsutsa Yesu kuti alephere kukana zoti Yesu anaukitsa Lazaro.

MUTU 92

Pa Anthu 10 Akhate, Mmodzi Anathokoza Yesu

Munthu amene anachiritsidwa anasonyeza kuti anayamikira Yesu komanso winawake.

MUTU  93

Mwana wa Munthu Adzaonekera

Kodi kukhalapo kwa Khristu kudzaonekera bwanji ngati mphezi?

MUTU 94

Kupemphera Komanso Kudzichepetsa Ndi Zinthu Ziwiri Zofunika Kwambiri

Yesu anaphunzitsa khalidwe lina lofunika kwambiri pamene ananena fanizo la mkazi wamasiye ndi woweruza woipa.

MUTU 95

Anawafotokozera Chifukwa Chothetsera Banja Komanso Kuti Azikonda Ana

N’chifukwa chiyani Yesu ankaona ana mosiyana kwambiri ndi ophunzira ake?

MUTU 96

Yesu Anayankha Wolamulira Wachinyamata Amene Anali Wolemera

N’chiyani chinachititsa Yesu kunena kuti n’chapafupi kuti ngamila ilowe padiso la singano kusiyana n’kuti munthu wolemera alowe mu ufumu wa Mulungu?

MUTU 97

Fanizo la Anthu Ogwira Ntchito M’munda wa Mpesa

Kodi oyamba anakhala bwanji omaliza, nanga omaliza anakhala bwanji oyamba?

MUTU 98

Atumwi Anasonyezanso Kuti Ankafuna Udindo Wapamwamba

Yakobo ndi Yohane anapempha kuti akakhale ndi malo apadera kumwamba koma panali atumwi enanso omwe ankafuna malo apaderawa.

MUTU 99

Yesu Anachiritsa Anthu Akhungu Komanso Anathandiza Zakeyu

Kodi tingagwirizanitse bwanji nkhani za m’Baibulo zimene zimaoneka ngati zimatsutsana zomwe zimanena kuti Yesu anachiritsa munthu wakhungu pafupi ndi mzinda wa Yeriko?

CHAPTER 100

Fanizo la Ndalama 10 za Mina

Kodi Yesu ankatanthauza chiyani pamene ananena kuti: “Aliyense amene ali nazo, adzamuwonjezera zochuluka, koma amene alibe adzalandidwa ngakhalenso zimene ali nazo”?

MUTU 101

Yesu Anakadya Chakudya ku Nyumba kwa Simoni ku Betaniya

Mariya, yemwe anali mlongo wake wa Lazaro, anachita zinthu zomwe zinayambitsa mkangano koma Yesu anamuikira kumbuyo.

MUTU 102

Mfumu Inalowa mu Yerusalemu Itakwera pa Bulu

Anakwaniritsa ulosi womwe unanenedwa zaka 500 m’mbuyomo.

MUTU 103

Yesu Anayeretsanso Kachisi

Amalonda a ku Yerusalemu ankaoneka kuti sakuphwanya malamulo pochita malonda awo pakachisi, nanga n’chifukwa chiyani Yesu anawanena kuti ndi achifwamba?

MUTU 104

Kodi Ayuda Anakhulupirira Yesu Atamva Mulungu Akulankhula?

Kodi kukhulupirira Yesu ndi kuchita zinthu zosonyeza kuti umakhulupirira Yesu ndi zinthu ziwiri zosiyana?

MUTU 105

Yesu Anagwiritsa Ntchito Mtengo wa Mkuyu Pophunzitsa Anthu za Chikhulupiriro

Yesu anathandiza ophunzira ake kumvetsa zimene munthu angachite ngati ali ndi chikhulupiriro champhamvu komanso anafotokoza chifukwa chimene Mulungu anakanira mtundu wa Isiraeli.

MUTU 106

Mafanizo Awiri Onena za Munda wa Mpesa

Werengani nkhaniyi kuti mudziwe zimene fanizo la munthu amene anapempha ana ake kuti akagwire ntchito m’munda wake komanso zimene fanizo la munthu amene anasiyira antchito oipa munda wake wampesa limatanthauza.

MUTU 107

Mfumu Inaitanira Anthu ku Phwando la Ukwati

Fanizo limene Yesu ananena linkasonyeza zimene zidzachitike m’tsogolo.

MUTU 108

Yesu Analepheretsa Afarisi Kuti Amugwire

Yesu anasowetsa chonena Afarisi, Asaduki komanso gulu la anthu omwe ankamutsutsa.

MUTU 109

Anadzudzula Atsogoleri Achipembedzo Omwe Ankamutsutsa

N’chifukwa chiyani sanalekere zinthu zolakwika zimene atsogoleri achipembedzo ankachita?

MUTU 110

Tsiku Lomaliza Limene Yesu Anapezeka pa Kachisi

Anawaphunzitsa mfundo yofunika kwambiri pogwiritsa ntchito chitsanzo cha mkazi wamasiye wosauka.

MUTU 111

Atumwi Anapempha Chizindikiro

Ulosi umene Yesu ananena unakwaniritsidwa koyamba m’nthawi ya atumwi. Kodi n’kutheka kuti ulosiwu udzakwaniritsidwanso m’tsogolo kuposa poyamba paja?

MUTU 112

Fanizo la Anamwali Limatiphunzitsa Kufunika Kokhala Tcheru

Kodi Yesu ankatanthauza kuti hafu ya ophunzira ake ndi opusa ndipo enawo ndi ochenjera?

MUTU 113

Fanizo la Matalente Limatiphunzitsa Kufunika Kochita Zinthu Mwakhama

Fanizo la Yesu limatithandiza kumvetsa mawu akuti: “Amene ali nazo, adzawonjezeredwa zambiri.”

MUTU 114

Khristu Akadzayamba Kulamulira Adzaweruza Nkhosa ndi Mbuzi

Yesu anagwiritsa ntchito fanizo logwira mtima pofuna kutithandiza kudziwa chimene chidzachititse kuti anthu ena aweruzidwe ngati nkhosa, ena ngati mbuzi.

MUTU 115

Yesu Anachita Mwambo Womaliza wa Pasika

N’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo anagwirizana zoti amupatse Yudasi ndalama 30 za siliva kuti amupereke Yesu?

MUTU 116

Anawaphunzitsa Kudzichepetsa pa Pasika Womaliza

Yesu anadabwitsa ophunzira ake chifukwa anagwira ntchito yomwe ankayenera kugwira ndi antchito apakhomo.

MUTU 117

Chakudya Chamadzulo Cha Ambuye

Yesu anayambitsa mwambo wokumbukira imfa yake ndipo otsatira ake ayenera kuchita mwambo umenewu chaka chilichonse pa Nisani 14.

MUTU 118

Anakangananso Kuti Wamkulu Ndani

Yesu anali atangowaphunzitsa atumwi za kudzichepetsa koma usiku womwewu iwo sanachedwe kuiwala.

CHAPTER 119

Jesus—The Way, the Truth, the Life

Jesus teaches a powerful truth about how to approach God.

CHAPTER 120

Bearing Fruit as Branches and Being Jesus’ Friends

In what way do Jesus’ disciples “bear fruit”?

MUTU 121

“Limbani Mtima Ndaligonjetsa Dziko”

Kodi Yesu anagonjetsa bwanji dziko popeza anthu a m’dzikoli anamupha?

MUTU 122

Pemphero Lomaliza la Yesu Ali M’chipinda Chapamwamba

Ananena kuti anachita zinthu zina zofunika kwambiri kuposa kuthandiza anthu kuti adzapulumuke.

MUTU 123

Anapemphera Pamene Anali ndi Chisoni Kwambiri

N’chifukwa chiyani Yesu anapemphera kuti, ‘Ndichotsereni kapu iyi’? Kodi ankafuna kuzemba zimene Mulungu anamutumizira padzikoli, zoti adzapereke moyo wake dipo?

MUTU 124

Khristu Anaperekedwa Kenako Anamangidwa

Yudasi anadziwa kumene Yesu anali ngakhale kuti panali pakati pa usiku.

MUTU 125

Atamugwira Anapita Naye kwa Anasi Kenako kwa Kayafa

Mlandu wa Yesu unaweruzidwa mopanda chilungamo.

MUTU 126

Petulo Anakana Yesu Kunyumba kwa Kayafa

N’chifukwa chiyani Petulo, munthu amene anali ndi chikhulupiriro komanso wodzipereka, anakana Yesu?

MUTU 127

Khoti la Sanihedirini Linaweruza Mlandu wa Yesu Kenako Anapita Naye kwa Pilato

Atsogoleri achipembedzo achiyuda anasonyeza kuti anali ndi maganizo olakwika.

MUTU 128

Pilato Komanso Herode Sanamupeze Yesu ndi Mlandu

N’chifukwa chiyani Pilato anatumiza Yesu kuti akaweruzidwe ndi Herode? Kodi Analibe Mphamvu Zoperekera Chilango kwa Yesu?

MUTU 129

Pilato Ananena Kuti: “Taonani! Mwamuna Uja Ndi Uyu!”

Pilato anadziwa kuti Yesu anali ndi makhalidwe abwino.

MUTU 130

Pilato Anapereka Yesu Ndipo Anthu Anamutenga Kuti Akamuphe

N’chifukwa chiyani Yesu anauza amayi omwe anali ndi chisoni kuti adzilirire okha ndi ana awo osati kulirira iyeyo?

MUTU 131

Mfumu Yosalakwa Inavutika Itapachikidwa Pamtengo

Yesu analonjeza chigawenga china kuti chidzakhala naye m’Paradaiso.

MUTU 132

“Ndithudi Munthu Uyu Analidi Mwana wa Mulungu”

Mdima wodabwitsa womwe unagwa masana, chivomerezi champhamvu komanso kung’ambika kwa nsalu, zinasonyeza kuti Yesu anali Mwana wa Mulungu.

MUTU 133

Anakonza Thupi la Yesu ndi Kukaliika M’manda

N’chifukwa chiyani ankafunika kuika thupi la Yesu m’manda dzuwa lisanalowe?

MUTU 134

M’manda a Yesu Munalibe Kanthu Chifukwa Anali Ataukitsidwa

Yesu ataukitsidwa, anaonekera choyamba kwa wophunzira wake wamkazi osati kwa atumwi ake.

MUTU 135

Yesu Ataukitsidwa Anaonekera kwa Anthu Ambiri

Kodi Yesu akanawatsimikizira bwanji ophunzira ake kuti anali ataukitsidwa?

MUTU 136

Anaonekera M’mbali Mwanyanja ya Galileya

Yesu anafunsa Petulo katatu kuti anene ngati amakondadi Yesuyo.

MUTU 137

Anaonekera kwa Anthu Ambiri Mwambo wa Pentekosite Usanachitike

Yesu ataukitsidwa koma asanapite kumwamba, anauza ophunzira ake mobwerezabwereza kuti adzalandira mzimu woyera. Anawauzanso mmene mzimuwo udzawathandizire.

MUTU 138

Khristu Anakhala Kudzanja Lamanja la Mulungu

Kodi Yesu akutani pamene akudikira kugonjetsa adani ake?

MUTU 139

Yesu Adzabweretsa Paradaiso Kenako Adzamaliza Kugwira Ntchito Imene Anapatsidwa

Padakali zambiri zoti Yesu achite asanapereke Ufumu kwa Atate ndi Mulungu wake.

Kuti Mutsanzire Yesu Muyenera . . .

Nthawi zonse Yesu ankasonyeza makhalidwe 8.

Kalozera wa Malemba

Gwiritsani ntchito kalozera ameneyu kuti mupeze pamene vesi lililonse la m’Mauthenga Abwino lafotokozedwa m’bukuli

Kalozera wa Mafanizo

Pezani mutu m’bukuli umene ukunena za fanizo lomwe mukufuna.

Maulosi Ena Onena za Mesiya

Onani zimene zinachitika pa moyo wa Yesu komanso ulosi umene unaneneratu za zimene zinachitikazo. Kenako onani lemba lomwe likunena mmene zimenezo zinakwaniritsidwira komanso mutu wa m’bukuli womwe uli ndi nkhani imeneyo.

Malo Amene Yesu Anakhalako Komanso Kuphunzitsa

Malo amene Yesu anachitiko utumiki wake.