Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 19

“Nzeru ya Mulungu M’chinsinsi Chopatulika”

“Nzeru ya Mulungu M’chinsinsi Chopatulika”

1, 2. Kodi ndi “chinsinsi chopatulika” chiti chimene chiyenera kutichititsa chidwi, ndipo n’chifukwa chiyani?

ZINSINSI! Chifukwa chakuti nkhani zachinsinsi zimachititsa chidwi, zimatenga anthu mtima, ndiponso zimadabwitsa, nthaŵi zambiri anthu amavutika kusunga pakamwa. Komabe, Baibulo limati: “Kubisa kanthu ndi ulemerero wa Mulungu.” (Miyambo 25:2) Inde, pokhala Wolamulira Wamkulu ndiponso Mlengi, Yehova moyenerera saulula zinthu zina kwa anthu mpaka itakwana nthaŵi yake yoziululira.

2 Komabe, pali chinsinsi china chochititsa chidwi chimene Yehova waulula m’Mawu ake. Chimatchedwa kuti “chinsinsi [chopatulika, NW] cha chifuniro [cha Mulungu].” (Aefeso 1:9) Mungapindule kwambiri pochiphunzira kuposa kungokhutiritsa chilakolako chanu chofuna kudziŵa. Kudziŵa chinsinsi chimenechi kukhoza kukupulumutsani ndiponso mungathe kuonako nzeru zosayerekezeka za Yehova.

Chinaululika Pang’onopang’ono

3, 4. Kodi ulosi wolembedwa pa Genesis 3:15 unapereka chiyembekezo motani, ndipo unaphatikizapo “chinsinsi chopatulika” chiti?

3 Pamene Adamu ndi Hava anachimwa, zinaoneka ngati cholinga cha Yehova chokhala ndi paradaiso padziko lapansi wokhalamo anthu angwiro chalepheretsedwa. Koma mofulumira Mulungu anasamalira vuto limeneli. Ananena kuti: “Ndidzaika udani pakati pa iwe [njoka] ndi mkaziyo, ndi pakati pa mbewu yako ndi mbewu yake; ndipo idzalalira mutu wako, ndipo iwe udzalalira chitende chake.”—Genesis 3:15.

4 Ameneŵa anali mawu ovuta kuwamvetsa. Kodi mkaziyu anali ndani? Kodi njokayo inali ndani? Kodi ndi ndani anali “mbewu” imene inali kudzalalira mutu wa njokayo? Mayankho a Adamu ndi Hava anali ongoganizira chabe. Komabe, mawu a Mulungu anapatsa mwana wokhulupirika aliyense wa anthu aŵiri  osakhulupirikawo chiyembekezo chabwino. Chilungamo chidzapambana. Cholinga cha Yehova chidzakwaniritsidwa. Koma motani? Eya, pamenepa ndipo panagona chinsinsi! Baibulo limachitcha “nzeru ya Mulungu m’chinsinsi [chopatulika, NW], yobisikayo.”—1 Akorinto 2:7.

5. Perekani chitsanzo chosonyeza chifukwa chimene Yehova anaululira chinsinsi chake pang’onopang’ono.

5 Popeza kuti Yehova ndi “wakuvumbulutsa zinsinsi,” m’kupita kwanthaŵi anali kudzafotokoza mfundo zofunikira zokhudza mmene chinsinsi chimenechi chidzachitikira. (Danieli 2:28) Koma adzachita zimenezi pang’onopang’ono, mfundo iliyonse panthaŵi yake. Mwachitsanzo, tingaganizire momwe atate wachikondi amayankhira pamene mwana wamng’ono awafunsa kuti, “Kodi Ababa, ine ndinachokera kuti?” Atate wanzeru amamuuza zinthu zokha zimene mwana wamng’onoyo akhoza kuzimvetsa. Pamene mwanayo akukula, atatewo amamuuza zambiri. M’njira yofananayo, Yehova amadziŵa pamene anthu ake ali okonzeka kuwaululira chifuno chake ndi cholinga chake.—Miyambo 4:18; Danieli 12:4.

6. (a) Kodi ntchito ya pangano n’chiyani? (b) N’chifukwa chiyani chili chinthu chapadera kuti Yehova anakhazikitsa mapangano ndi anthu?

6 Kodi Yehova anaziulula motani zimenezi? Anaulula zinthu zambiri mwa kugwiritsa ntchito mapangano angapo. Mwinamwake panthaŵi ina inu munalemberanapo pangano ndi munthu wina, kaya linali logula nyumba kapena lobwereka ndi kubwereketsa ndalama. Pangano loterolo linakutsimikizirani mwalamulo kuti aliyense adzachita zimene mwagwirizanazo. Koma n’chifukwa chiyani Yehova afunika kupanga mapangano ndi anthu? Mawu ake ndi okwanira kutsimikizira zimene akulonjeza. Zimenezi n’zoonadi, komatu nthaŵi zambiri Mulungu mokoma mtima wachirikiza mawu akewo ndi mapangano alamulo. Mapangano osasweka ameneŵa, amatipatsa ife anthu opanda ungwiro chifukwa chomveka kwambiri chokhulupiririra malonjezo a Yehova.—Ahebri 6:16-18.

 Pangano ndi Abrahamu

7, 8. (a) Kodi Yehova anapanga pangano lotani ndi Abrahamu, ndipo zinaonetsanji za chinsinsi chopatulika? (b) Kodi Yehova mwapang’onopang’ono anachepetsa motani mzere wobadwiramo Mbewu yolonjezedwa?

7 Patadutsa zaka zoposa 2,000 kuchokera pamene anthu anathamangitsidwa mu Paradaiso, Yehova anauza mtumiki wake wokhulupirika Abrahamu kuti: “Kuchulukitsa ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba, . . . m’mbewu zako mitundu yonse ya dziko lapansi idzadalitsidwa: chifukwa wamvera mawu anga.” (Genesis 22:17, 18) Ili silinali lonjezo chabe; Yehova analikonza monga pangano lalamulo ndipo analichirikiza ndi lumbiro lake losasinthika. (Genesis 17:1, 2; Ahebri 6:13-15) N’chinthu chapaderatu kwambiri kuti Ambuye Mfumu anachitadi pangano kuti adalitse anthu!

“Ndidzachulukitsa mbewu zako monga nyenyezi za kumwamba”

8 Pangano la Abrahamu linaulula kuti Mbewu yolonjezedwayo idzakhala munthu, chifukwa chakuti anali kudzakhala mbadwa ya Abrahamu. Komano munthu wake ndani? M’kupita kwanthaŵi, Yehova anaulula kuti mwa ana a Abrahamu, Isake ndiye amene adzakhala kholo la Mbewuyo. Mwa ana aŵiri a Isake, Yakobo ndiye anasankhidwa. (Genesis 21:12; 28:13, 14) Kenako, Yakobo ananena mawu aŵa kwa mmodzi wa ana ake 12 amuna: “Ndodo yachifumu siidzachoka mwa Yuda, kapena wolamulira pakati pa mapazi ake, kufikira atadza Silo [“Iye Amene Chili Chake”]; ndipo anthu adzamvera iye.” (Genesis 49:10) Tsopano zinadziŵika kuti Mbewuyo idzakhala mfumu yochokera mwa Yuda!

Pangano ndi Mtundu wa Israyeli

9, 10. (a) Kodi Yehova anapanga pangano lotani ndi mtundu wa Israyeli, ndipo panganolo linapereka chitetezo chotani? (b) Kodi Chilamulo chinaonetsa motani kuti anthu afunika dipo?

9 M’chaka cha 1513 B.C.E., Yehova anapanga makonzedwe amene anakonza njira yoti mbali zinanso za chinsinsi chopatulikacho ziululike. Anapanga pangano ndi mbadwa za Abrahamu, mtundu wa Israyeli. Ngakhale kuti tsopano silikugwiranso ntchito, pangano la Chilamulo cha Mose limeneli linali lofunika kwambiri pa cholinga cha Yehova chobweretsa Mbewu yolonjezedwa. Motani?  Taonani njira zitatu izi. Yoyamba, Chilamulo chinali monga khoma lowateteza. (Aefeso 2:14) Malamulo ake olungamawo anali monga malire pakati pa Ayuda ndi anthu Akunja. Motero Chilamulo chinathandiza kuti mzere wobadwiramo Mbewu yolonjezedwa usafafanizike. Makamaka chinali chifukwa cha kutetezedwa kumeneko kuti mtunduwu unali udakalipo pamene nthaŵi yoikika ya Mulungu inakwana yoti Mesiya abadwe mu fuko la Yuda.

10 Yachiŵiri, Chilamulo chinaonetsa poyera kuti anthu afunika dipo. Popeza chinali changwiro, Chilamulo chinaonetsa kuti anthu ochimwa sangathe kuchitsatira bwino lomwe. Motero chinalipo “chifukwa cha zolakwa, kufikira ikadza mbewu imene adailonjezera.” (Agalatiya 3:19) Mwa nsembe za nyama, Chilamulo chinali kutetezera kwa kanthaŵi machimo a anthu. Koma popeza kuti, monga analembera Paulo, “sikutheka kuti mwazi wa ng’ombe zamphongo, ndi mbuzi ukachotsera machimo,” nsembe zimenezi zinali kungochitira chithunzi nsembe ya dipo ya Kristu. (Ahebri 10:1-4) Motero kwa Ayuda okhulupirika, pangano limenelo linali ‘namkungwi wakuwafikitsa kwa Kristu.’—Agalatiya 3:24.

11. Kodi ndi chiyembekezo chabwino chiti chimene pangano la Chilamulo linapatsa mtundu wa Israyeli, koma n’chifukwa chiyani mtunduwo unalephera kuchilandira?

11 Yachitatu, pangano limenelo linapatsa mtundu wa Israyeli chiyembekezo chabwino kwambiri. Yehova anawauza kuti ngati adzakhala okhulupirika pa panganolo, adzakhala ‘ufumu wa ansembe ndi mtundu wopatulika.’ (Eksodo 19:5, 6) M’kupita kwanthaŵi, anthu oyambirira a ufumu wakumwamba wa ansembe anachokeradi mu mtundu wa Israyeli wakuthupi ameneyo. Komabe, monga mtundu, Aisrayeli anapandukira pangano la Chilamulo, anakana Mbewu yaumesiya, ndipo analephera kulandira zimene anali kuyembekezazo. Nangano ndani ena amene anali kudzaloŵa ufumu wa ansembewo kuti ukhale ndi anthu okwanira bwino lomwe? Ndipo kodi mtundu wodalitsika umenewo ukanagwirizana motani ndi Mbewu yolonjezedwayo? Mbali zimenezi za chinsinsi chopatulika zinali kudzaululika m’nthaŵi yoikika ya Mulungu.

 Pangano la Ufumu wa Davide

12. Kodi Yehova anapanga pangano lotani ndi Davide, nanga linasonyeza chiyani chokhudza chinsinsi chopatulika cha Mulungu?

12 M’kati mwa zaka zoyambira 1100 kufika 1000 B.C.E., Yehova anasonyeza mbali zina za chinsinsi chopatulika pamene anachita pangano linanso. Analonjeza mfumu yokhulupirika Davide kuti: “Ine ndidzaukitsa mbewu yako pambuyo pako, . . . ndipo ndidzakhazikitsa ufumu wake. . . . Ndidzakhazikitsa chimpando cha ufumu wake ku nthaŵi zonse.” (2 Samueli 7:12, 13; Salmo 89:3) Tsopano mzere wobadwiramo Mbewu yolonjezedwa unachepetsedwa kufika pa banja la Davide. Koma kodi munthu wamba akanatha kulamulira “ku nthaŵi yonse”? (Salmo 89:20, 29, 34-36) Ndipo kodi mfumu yaumunthu imeneyo ikanatha kulanditsa anthu ku uchimo ndi imfa?

13, 14. (a) Malinga n’kunena kwa Salmo 110, kodi Yehova akulonjeza chiyani kwa Mfumu yake yodzozedwa? (b) Kodi ndi mbali zina ziti zokhudza Mbewu imene inali kubwera zomwe zinaululidwa ndi aneneri a Yehova?

13 Mouziridwa, Davide analemba kuti: “Yehova ananena kwa Ambuye wanga, Khalani pa dzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani anu chopondapo mapazi anu. Yehova walamulira, ndipo sadzasintha, Inu ndinu wansembe kosatha monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke.” (Salmo 110:1, 4) Mawu a Davide anagwira ntchito mwachindunji pa Mbewu yolonjezedwa, kapena kuti Mesiya. (Machitidwe 2:35, 36) Mfumu imeneyi idzalamulira, osati ili mu Yerusalemu, koma ili kumwamba ku “dzanja lamanja” la Yehova. Zimenezi zikachititsa Mfumuyi kukhala ndi mphamvu osati pa dziko la Israyeli lokha, koma pa dziko lonse lapansi. (Salmo 2:6-8) Apa panaululika zinanso. Onani kuti Yehova analumbira kuti Mesiya adzakhala “wansembe . . . monga mwa chilongosoko cha Melikizedeke.” Mofanana ndi Melikizedeke, yemwe anali mfumu ndiponso wansembe m’masiku a Abrahamu, Mbewu imene inali kubwerayo idzaikidwa mwachindunji ndi Mulungu kukhala Mfumu ndiponso Wansembe!—Genesis 14:17-20.

14 M’zaka zotsatira, Yehova anagwiritsa ntchito aneneri ake kuulula mbali zina za chinsinsi chake chopatulika. Mwachitsanzo, Yesaya anaulula kuti Mbewuyo idzafa imfa yansembe. (Yesaya 53:3-12) Mika ananena za malo amene Mesiya adzabadwirako.  (Mika 5:2) Danieli analosera za nthaŵi yeniyeni imene Mbewuyo idzaoneka ndiponso kufa.—Danieli 9:24-27.

Chinsinsi Chopatulika Chiululika!

15, 16. (a) Kodi zinachitika motani kuti Mwana wa Yehova ‘abadwe ndi mkazi’? (b) Kodi ndi choloŵa chanji chimene Yesu analandira kuchokera kwa makolo ake aumunthu, ndipo ndi liti pamene anafika monga Mbewu yolonjezedwa?

15 Sizinali kudziŵika kuti maulosi ameneŵa adzachitika motani mpaka pamene Mbewuyo inaonekera. Agalatiya 4:4 amati: “Pokwaniridwa nthaŵi, Mulungu anatuma Mwana wake, wobadwa ndi mkazi.” M’chaka cha 2 B.C.E., mngelo anauza namwali wachiyuda wotchedwa Mariya, kuti: “Taona, udzakhala ndi pakati, nudzabala mwana wamwamuna, nudzamutcha dzina lake Yesu. Iye adzakhala wamkulu, nadzatchedwa Mwana wa Wamkulukulu: ndipo Ambuye Mulungu adzamupatsa Iye mpando wachifumu wa Davide atate wake . . . Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe: chifukwa chakenso Choyeracho chikadzabadwa, chidzatchedwa Mwana wa Mulungu.”—Luka 1:31, 32, 35.

16 Kenako, Yehova anasamutsa moyo wa Mwana wake kuchoka kumwamba n’kuuika m’mimba mwa Mariya kotero kuti anabadwa mwa mkazi. Mariya anali mkazi wopanda ungwiro. Komatu Yesu sanatengere kupanda ungwiro kwa Mariyayo, chifukwa Iye anali “Mwana wa Mulungu.” Komabe, kukhala ndi makolo aumunthu omwe anali mbadwa za Davide, kunachititsa Yesu kukhala woyenera mwachibadwa ndiponso mwalamulo kuloŵa ufumu wa Davide. (Machitidwe 13:22, 23) Pamene Yesu anali kubatizidwa m’chaka cha 29 C.E., Yehova anamudzoza ndi mzimu woyera, n’kunena kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa.” (Mateyu 3:16, 17) Eya, Mbewu ija inafika tsopano! (Agalatiya 3:16) Tsopano inali nthaŵi youlula zina zambiri zokhudza chinsinsi chopatulika.—2 Timoteo 1:10.

17. Kodi tanthauzo la Genesis 3:15 linamveketsedwa bwanji?

17 Panthaŵi ya utumiki wake, Yesu anadziŵikitsa njoka yonenedwa pa Genesis 3:15 kukhala Satana ndipo mbewu ya njokayo kukhala otsatira a Satana. (Mateyu 23:33; Yohane 8:44) Pambuyo pake, zinaululika mmene onseŵa adzawonongedwere kosatha.  (Chivumbulutso 20:1-3, 10, 15) Ndipo mkazi anadziŵikitsidwa kukhala “Yerusalemu Wokwezeka,” gulu la Yehova lakumwamba longa mkazi la zolengedwa zauzimu. *Agalatiya 4:26, NW; Chivumbulutso 12:1-6.

Pangano Latsopano

18. Kodi “pangano latsopano” cholinga chake n’chiyani?

18 Mwinamwake zomwe zinaululika usiku woti Yesu aphedwa maŵa lake ndizo zapadera kwambiri pa zonse. Usiku umenewo Yesu ananena za “pangano latsopano” kwa ophunzira ake okhulupirika. (Luka 22:20) Mofanana ndi pangano la Chilamulo cha Mose lomwe linali kuloŵedwa m’malo, pangano latsopanoli linali kudzatulutsa ‘ufumu wa ansembe.’ (Eksodo 19:6; 1 Petro 2:9) Komabe, pangano ili linali kudzakhazikitsa, osati mtundu wakuthupi, koma mtundu wauzimu, “Israyeli wa Mulungu,” womwe anthu ake onse adzakhala otsatira odzozedwa, okhulupirika a Kristu. (Agalatiya 6:16) Anthu a m’pangano latsopano ameneŵa mogwirizana ndi Yesu adzadalitsa anthu onse!

19. (a) N’chifukwa chiyani pangano latsopano likutulutsa bwinobwino ‘ufumu wa ansembe’? (b) N’chifukwa chiyani Akristu odzozedwa akutchedwa kuti “chilengedwe chatsopano,” ndipo ndi angati amene adzatumikira limodzi ndi Kristu kumwamba?

19 Koma, kodi n’chifukwa chiyani pangano latsopano likutulutsa bwinobwino ‘ufumu wa ansembe’ woti udalitse anthu? N’chifukwa chakuti m’malo motsutsa ophunzira a Kristu kuti ndi ochimwa, panganoli limawathandiza kukhululukidwa machimo awo mwa nsembe ya Kristuyo. (Yeremiya 31:31-34) Iwo akakhala ndi mbiri yoyera kwa Yehova, iye amawatenga kuti akhale a m’banja lake lakumwamba ndipo amawadzoza ndi mzimu woyera. (Aroma 8:15-17; 2 Akorinto 1:21) Motero iwo ‘amabadwanso ku chiyembekezo cha moyo . . . chosungika m’Mwamba.’ (1 Petro 1:3, 4) Popeza kuti malo okwezeka amenewo ndi atsopano kotheratu kwa anthu, Akristu odzozedwa, obadwa ndi mzimu amatchedwa  kuti “wolengedwa watsopano [“chilengedwe chatsopano,” NW].” (2 Akorinto 5:17) Baibulo limanena kuti m’kupita kwanthaŵi anthu okwanira 144,000 ali kumwamba, adzalamulira nawo anthu owomboledwa.—Chivumbulutso 5:9, 10; 14:1-4.

20. (a) Kodi ndi mbali iti ya chinsinsi chopatulika imene inaululika m’chaka cha 36 C.E.? (b) Kodi ndani adzasangalala ndi madalitso amene Abrahamu analonjezedwa?

20 Odzozedwa ameneŵa limodzi ndi Yesu amakhala “mbewu ya Abrahamu.” * (Agalatiya 3:29) Oyamba amene anasankhidwa anali Ayuda akuthupi. Koma m’chaka cha 36 C.E., mbali inanso ya chinsinsi chopatulika inaululika, ndiyo yakuti: Akunja, kapena kuti anthu amene si Ayuda, nawonso adzakhala ndi chiyembekezo chopita kumwamba. (Aroma 9:6-8; 11:25, 26; Aefeso 3:5, 6) Kodi Akristu odzozedwa ndiwo okha omwe adzasangalale ndi madalitso amene Abrahamu analonjezedwa? Ayi, chifukwa dziko lonse likupindula ndi nsembe ya Yesu. (1 Yohane 2:2) M’kupita kwanthaŵi, Yehova anaulula kuti “khamu lalikulu” la anthu omwe chiŵerengero chawo sichinatchulidwe adzapulumuka pamene dongosolo la zinthu la Satana likutha. (Chivumbulutso 7:9, 14) Enanso miyandamiyanda adzaukitsidwa ali ndi chiyembekezo chokhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso!—Luka 23:43; Yohane 5:28, 29; Chivumbulutso 20:11-15; 21:3, 4.

Nzeru za Mulungu ndi Chinsinsi Chopatulika

21, 22. Kodi chinsinsi chopatulika cha Yehova chimasonyeza nzeru zake m’njira zotani?

21 Chinsinsi chopatulika chinaonetsa “nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu” m’njira yodabwitsa kwambiri. (Aefeso 3:8-10) Yehova anasonyeza nzeru zozamadi pokonza chinsinsi chimenechi, komanso pochiulula pang’onopang’ono! Analingalirapo mwanzeru kuti anthu sangakwanitse kudziŵa zonse, ndipo anawalola kuonetsa zimenedi zinali mu mtima mwawo.—Salmo 103:14.

22 Yehova anasonyezanso nzeru zosayerekezeka posankha Yesu  kukhala Mfumu. Mwana wa Yehova ndi wodalirika kwambiri kuposa cholengedwa china chilichonse m’chilengedwe chonse. Pamene anali munthu wokhala ndi magazi ndi thupi, Yesu anakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Iye amawamvetsa kwambiri mavuto a anthu. (Ahebri 5:7-9) Nanga bwanji olamulira anzake a Yesu? M’zaka mazanamazana apitaŵa, amuna ndiponso akazi osankhidwa m’mafuko onse, zinenero zonse, ndiponso a mbiri zosiyanasiyana, akhala akudzozedwa. Palibe vuto limene wina wa iwo sanakumanepo nalo n’kuligonjetsa. (Aefeso 4:22-24) Zidzakhala zosangalatsatu kwambiri kulamulidwa ndi mafumu ndi ansembe achifundo ameneŵa!

23. Kodi Akristu ali ndi mwayi wotani wokhudzana ndi chinsinsi chopatulika cha Yehova?

23 Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chinsinsicho chinabisika kuyambira pa nthaŵizo, ndi kuyambira pa mibadwoyo . . . anachionetsa tsopano kwa oyera mtima ake.” (Akolose 1:26) Inde, oyera odzozedwa a Yehova amvetsetsa zinthu zambiri zokhudzana ndi chinsinsi chopatulika, ndipo auzanso anthu mamiliyoni ambiri. Tonsefe tilitu ndi mwayi waukulu bwanji! Yehova “anatizindikiritsa ife chinsinsi [chopatulika, NW] cha chifuniro chake.” (Aefeso 1:9) Tiyeni tiuze ena chinsinsi chosangalatsa chimenechi, mwakutero tiwathandize kuona nzeru zosaneneka za Yehova Mulungu!

^ ndime 17 “Chinsinsi chopatulika cha kudzipereka kwaumulungu,” nachonso chinaululika mwa Yesu. (1 Timoteo 3:16, NW) Kwanthaŵi yaitali sizinali kudziŵika ngati munthu wina aliyense akhoza kukhalabe wokhulupirika bwino lomwe kwa Yehova. Yesu anaulula yankho lake. Anali wokhulupirika pa chiyeso chilichonse chimene Satana anamuikira.—Mateyu 4:1-11; 27:26-50.

^ ndime 20 Yesu anapanganso pangano la “ufumu” ndi gulu lomweli. (Luka 22:29, 30) Tinganene kuti, Yesu kwenikweni anapangana ndi “kagulu ka nkhosa” kameneka kuti adzalamulire limodzi naye kumwamba monga mbali yachiŵiri ya mbewu ya Abrahamu.—Luka 12:32.