Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 17

‘Ha! Kuya Kwake kwa Nzeru za Mulungu!’

‘Ha! Kuya Kwake kwa Nzeru za Mulungu!’

1, 2. Kodi cholinga cha Yehova cha tsiku lachisanu ndi chiŵiri chinali chotani, ndipo kodi nzeru zake zinayesedwa motani pamene tsikuli linkayamba?

ZAWONONGEKA! Anthu, omwe analengedwa m’tsiku lachisanu ndi chimodzi la kulenga, ndiwo zolengedwa zomwe zinalemekeza Mlengi mwapadera kwambiri. Koma mwadzidzidzi iwo anachoka pamalo apamwamba zedi n’kufika pamalo otsika kwambiri. Yehova anali atanena kuti “zonse zimene adazipanga,” kuphatikizapo anthu, “zinali zabwino.” (Genesis 1:31) Koma pamene tsiku lachisanu ndi chiŵiri linkayamba, Adamu ndi Hava anasankha kupanduka limodzi ndi Satana. Analoŵa mu uchimo, kupanda ungwiro, ndi imfa.

2 Zinaoneka ngati kuti iwo alepheretsa cholinga cha Yehova cha tsiku lachisanu ndi chiŵiri. Tsikuli, mofanana ndi masiku asanu ndi limodzi oyambirirawo, linali loti likhale lautali wokwana zaka masauzande ambirimbiri. Yehova analiyeretsa, ndipo m’tsikuli dziko lonse lapansi linali kudzasanduka paradaiso momwe mudzakhala anthu angwiro. (Genesis 1:28; 2:3) Koma popeza kuti anthu anapanduka, nadzetsa mavuto oopsa, kodi zimenezi zidzatheka bwanji? N’chiyani chimene Mulungu adzachita? Nzeru za Yehova zinayesedwa kwambiri ndi nkhaniyi, mwinanso tingati ameneŵa anali mayeso akulu kwambiri kuposa ena alionse.

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani zimene Yehova anachita ndi kupanduka kwa mu Edene zili chitsanzo chogometsa cha nzeru zake? (b) Kodi kudzichepetsa kuyenera kutichititsa kukumbukira choonadi chotani nthaŵi zonse pamene tikuphunzira nzeru za Yehova?

3 Yehova anachitapo kanthu nthaŵi yomweyo. Anapereka chilango kwa opandukawo mu Edene, ndipo nthaŵi yomweyo, anapereka chithunzithunzi cha cholinga chake chosangalatsa kwambiri chothetsa mavuto amene anthu opandukawo anali atangowayambitsa kumene. (Genesis 3:15) Cholinga chofika patali cha Yehova chinayambira mu Edene mpaka m’zaka masauzande onse a mbiri ya anthu, n’kupitirirabe m’tsogolo kwambiri. N’chosavuta kwambiri, komatu panagona nzeru zakuya moti woŵerenga Baibulo  angakhale ndi moyo wopindulitsadi pophunzira ndi kusinkhasinkha cholinga chimenechi. Ndiponso, n’zotsimikizika kwambiri kuti cholinga cha Yehova chidzachitika. Chidzathetsa kuipa konse, uchimo, ndiponso imfa. Chidzachititsa anthu okhulupirika kukhala angwiro. Zonsezi zidzachitika tsiku lachisanu ndi chiŵiri lisanathe, kotero kuti mosasamala kanthu za zochitika zina zilizonse, Yehova adzakhala atakwaniritsa cholinga chake cha dziko lapansi ndi anthu panthaŵi yake yeniyeniyo.

4 Timazizwa nazo nzeru zoterozo, kodi si choncho? Mtumwi Paulo anafika polemba kuti: ‘Ha! kuya kwake kwa nzeru za Mulungu!’ (Aroma 11:33) Pamene tikuphunzira mbali zosiyanasiyana za khalidwe la Mulungu limeneli, kukhala odzichepetsa nthaŵi zonse kudzatichititsa kukumbukira choonadi chofunika kwambiri ichi: tikhoza kungofukulako pamwamba chabe pa nzeru zochuluka za Yehova. (Yobu 26:14) Poyamba, tiyeni tione chimene khalidwe lomwe timazizwa naloli limatanthauza.

Kodi Nzeru Zaumulungu N’chiyani?

5, 6. Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kudziŵa zinthu ndi nzeru, nanga Yehova amadziŵa zinthu zochuluka motani?

5 Kukhala wanzeru n’kosiyana ndi kudziŵa zinthu. Makompyuta amadziŵa zinthu zambiri, komatu munthu sanganene makina amenewo kuti ndi anzeru. Ngakhale ndi choncho, kudziŵa zinthu kumagwirizana ndi kukhala ndi nzeru. (Miyambo 10:14) Mwachitsanzo, ngati mukufuna malangizo anzeru pochiza matenda aakulu, kodi mukhoza kuonana ndi munthu amene zachipatala amazidziŵa pang’ono kapenanso amene sazidziŵa n’komwe? Ayi, simungatero. Motero kudziŵa zinthu molondola n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi nzeru zenizeni.

6 Yehova amadziŵa zinthu zambiri kwabasi. Pokhala ‘Mfumu ya nthaŵi zosatha,’ ndiye yekha amene wakhalako kunthaŵi zonse. (Chivumbulutso 15:3) Ndipo kwa zaka zosadziŵika zonsezo, wakhala akudziŵa chilichonse. Baibulo limanena kuti: “Palibe cholengedwa chosaonekera pamaso pake, koma zonse zikhala za pambalambanda ndi zovundukuka pamaso pake pa Iye amene tichita naye.” (Ahebri 4:13; Miyambo 15:3) Pokhala Mlengi, Yehova amazindikira bwino zimene anapanga, ndipo waona zochita zonse za anthu kuchokera pachiyambi pake. Amaona za mumtima wa  munthu aliyense, osaphonyapo kalikonse. (1 Mbiri 28:9) Popeza kuti Yehova anatilenga monga anthu okhala ndi ufulu wosankha, iye amasangalala pamene aona kuti tikusankha kuchita zinthu zanzeru pamoyo wathu. Pokhala “Wakumva pemphero,” amamva mapemphero osaŵerengeka panthaŵi ina iliyonse! (Salmo 65:2) Ndipo n’zosachita kunena kuti Yehova amakumbukira zinthu; osaiwala ngakhale pang’ono.

7, 8. Kodi Yehova amasonyeza motani kuti amamvetsetsa zinthu, kuti ndi wozindikira, komanso kuti ndi wanzeru?

7 Yehova sangodziŵa chabe zinthu zochuluka. Amaonanso kugwirizana kwa mfundo zosiyanasiyana, ndipo amazindikira chithunzithunzi chonse chimene mfundo zochuluka kwambiri zikupereka. Amapenda mfundo zonse n’kugamulapo; nasiyanitsa chabwino ndi choipa, chofunika ndi chosafunika. Ndiponso, iye sangoona zapamwamba zokha, amaonanso za mumtima mwenimwenimo. (1 Samueli 16:7) Motero Yehova amamvetsetsa ndiponso amazindikira mmene zinthu zilili. Zimenezi ndi zoposa kungodziŵa zinthuzo. Koma kukhala ndi nzeru kumapambana zonsezo.

8 Munthu wanzeru ndi amene poyamba kugwira ntchito amakhala atasonkhanitsa pamodzi zimene akudziŵa, kuzindikira kwake zinthu, ndi kuzimvetsetsa kwake. Ndipotu, mawu ena a chinenero choyambirira cha m’Baibulo amene atembenuzidwa kuti “nzeru” kwenikweni amatanthauza “kugwira ntchito kothandiza” kapena “nzeru zothandiza.” Motero nzeru za Yehova si mawu chabe ongolankhula. Ndi zothandiza ndipo zimachitikadi. Chifukwa chodziŵa zinthu zambirimbiri ndiponso chifukwa chozimvetsa bwino, Yehova nthaŵi zonse amapanga zosankha zabwino kwambiri ndipo amazichita m’njira yabwino koposa. Imeneyo ndiyotu nzeru yeniyeni! Yehova amasonyeza kuti mawu amene ananena Yesu ndi oona. Yesu anati: “Nzeru iyesedwa yolungama ndi ntchito zake.” (Mateyu 11:19) Ntchito za Yehova m’chilengedwe chonse zimapereka umboni wamphamvu wa nzeru zake.

Umboni wa Nzeru za Mulungu

9, 10. (a) Ndi nzeru zamtundu wanji zimene Yehova amaonetsa, nanga kodi wazisonyeza motani? (b) Kodi ndi motani mmene selo limaperekera umboni wa nzeru za Yehova?

9 Kodi munachitapo kaso ndi luso la mmisiri wina amene amapanga zinthu zokongola zimene zimagwira ntchito bwino? Mmisiri  woteroyo alitu ndi nzeru zochititsa chidwi. (Eksodo 31:1-3) Yehova ndiye amapereka nzeru zoterozo ndiponso ndiye mwini wake weniweni. Mfumu Davide ananena za Yehova kuti: ‘Ndikuyamikani chifukwa chakuti chipangidwe changa n’choopsa ndi chodabwitsa; ntchito zanu n’zodabwitsa; moyo wanga uchidziŵa ichi bwino ndithu.’ (Salmo 139:14) Inde, pamene tiphunzira kwambiri za thupi lamunthu, m’pamenenso timazizwa kwambiri ndi nzeru za Yehova.

10 Mwachitsanzo: Moyo wanu unayamba ndi selo limodzi—selo la dzira la amayi anu lomwe linakhwima litaphatikana ndi umuna wa abambo anu. Posakhalitsa, selo limenelo linayamba kugaŵikana. Inuyo, amene munakhalapo chifukwa cha kugaŵikana kumeneko, munapangidwa ndi maselo pafupifupi mabiliyoni 100,000. Maselowo ndi ang’onoang’ono zedi. Maselo pafupifupi 10,000 akhoza kukwanira pa njere ya therere lobala. Komatu, lililonse linalengedwa mocholowana kwambiri. Selo lili ndi tinthu tambirimbiri m’kati mwake kuposa makina kapena fakitale ina iliyonse imene anthu apanga. Akatswiri a sayansi amati selo lili ngati mzinda wa malinga—wokhala ndi zipata zoloŵera ndi zotulukira zoyang’aniridwa bwino, dongosolo la zamaulendo, njira zolankhulirana, malo opanga mphamvu, mafakitale, zipangizo zotayira zonyansa ndi kukonzanso zinthu zogwiritsidwa kale ntchito, dongosolo la chitetezo, ndipo ngakhalenso likulu la mzinda wonse pa phata la selolo. Ndiponso, m’maola ochepa chabe, selo likhoza kudzigaŵa pakati n’kukhala maselo aŵiri ofanana ndendende ndi loyamba lija!

11, 12. (a) Kodi n’chiyani chimachititsa kugaŵikana kwa maselo a mwana yemwe akukula m’mimba mwa amayi ake, ndipo kodi zimenezi zikugwirizana motani ndi Salmo 139:16? (b) Kodi ubongo wa munthu umasonyeza motani kuti ‘tinapangidwa modabwitsa’?

11 N’zoona kuti si maselo onse omwe ali ofanana. Pamene maselo a mwana yemwe ali m’mimba mwa amayi ake akupitiriza kugaŵikana, iwo amayamba kugwira ntchito zosiyanasiyana. Ena amakhala a minyewa imene imatumiza ndi kulandira mauthenga ku ubongo; ena amakhala maselo a mafupa, minofu, magazi, kapena maso. Ndondomeko ya kugaŵikana konseko imakonzedwa mu “laibulale” ya selolo ya mabuku a malangizo a mwana woti abadwe, yotchedwa DNA. N’zopatsa chidwi kuona kuti Davide anauziridwa kunena mawu aŵa kwa Yehova: “Ndisanaumbidwe ine maso anu anandipenya, ziwalo zanga zonse zinalembedwa m’buku mwanu.”—Salmo 139:16.

 12 Ziwalo zina zathupi ndi zovuta kwambiri kuzimvetsetsa. Mwachitsanzo, talingalirani za ubongo wa munthu. Anthu ena anena kuti ubongo ndi wovuta kwambiri kuumvetsa mwa zinthu zonse zimene zapezeka m’chilengedwe. Uli ndi maselo a minyewa yotumiza ndi kulandira mauthenga okwana ngati 100 biliyoni—ochuluka pafupifupi ngati nyenyezi zimene zili mu mlalang’amba wathu. Lililonse la maselo amenewo limapanga mphanda masauzande ambirimbiri polumikizana ndi maselo ena. Akatswiri a sayansi amati mu ubongo wa munthu mukhoza kuloŵa chidziŵitso chonse chimene chili mu malaibulale onse a dziko lapansi, komabe amatinso n’kosatheka kudziŵa kuti ungasunge chidziŵitso chochuluka motani. Ngakhale kuti akatswiri a sayansi aphunzira chiwalo ‘chopangidwa modabwitsa’ chimenechi kwa zaka zambirimbiri, amavomera kuti sadzafika pomvetsetsa bwino mmene chimagwirira ntchito.

13, 14. (a) Kodi nyerere ndi zolengedwa zina zimasonyeza motani kuti ndi “zanzeru mwachibadwa,” ndipo kodi zimenezi zimatiphunzitsa chiyani za Mlengi wawo? (b) Kodi n’chifukwa chiyani tinganene kuti zinthu zolengedwa monga ngati utatavu zinapangidwa “mwanzeru”?

13 Komabe, anthu ndi chitsanzo chimodzi chokha cha nzeru za kulenga za Yehova. Salmo 104:24 limati: “Ntchito zanu zichulukadi, Yehova! Munazichita zonse mwanzeru; dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.” Nzeru za Yehova zimaoneka bwino m’cholengedwa chilichonse chimene timaona. Mwachitsanzo, nyerere ndi “zanzeru mwachibadwa.” (Miyambo 30:24, NW) Indedi, nyerere zimalinganiza bwino kwambiri mafunkha awo. M’mafunkha ena, nyerere zimasungamo nsabwe za zomera, n’kumaziyang’anira ndi kumapeza chakudya chake kuchokera ku tizilombo timeneti ngati kuti tizilomboti ndi ziŵeto. Nyerere zina zimakhala ngati alimi; zimakhala ngati “zalima” tomera tinatake tomwe sitichita maluŵa, sitikhala ndi masamba, ndiponso sitikhala tobiriŵira. Zolengedwa zina zambiri zinalinganizidwa kuti mwachibadwa zizichita zinthu zochititsa chidwi kwambiri. Ntchetche ikamauluka imagadabuzikagadabuzika m’njira yoti ngakhale ndege yotsogola kwambiri imene anthu apanga singathe. Mbalame zimasamukira malo ena pogwiritsa ntchito nyenyezi, malo amene kuli mphamvu yokoka yadziko, kapenanso mapu amene zili nawo m’mutu. Akatswiri a sayansi ya zamoyo amatha zaka zambirimbiri akuphunzira  makhalidwe ovuta kumvetsetsa amene analinganizidwa m’zolengedwa zimenezi. Koma ndiyetu Wolinganiza waumulunguyo ayenera kukhala wanzerutu kwambiri!

14 A sayansi aphunzira zambiri ku nzeru za kulenga za Yehova. Pali ngakhale gawo lina la uinjiniya limene limafufuza mmene zinthu zachilengedwe zinalinganizidwira ndi kumayesa kupanga zinthu mofananitsa ndi zimene apeza m’chilengedwecho. Mwachitsanzo, inu mungachite chidwi ndi kukongola kwa utatavu wa kangaude. Koma munthu yemwe ndi injiniya amaona utatavuwo monga chinthu cholinganizidwa mwaluso zedi. Mautatavu ena amene amaoneka ngati osalimba n’ngolimba kwambiri kuposa chitsulo kapenanso ulusi wa zovala zimene zipolopolo za mfuti zimalephera kuboola, ngati muyerekeza zofanana kukula kwake. Kodi ndi wolimba motani kwenikweni? Talingalirani kuti mwakulitsa utatavuwo mpaka kukhala waukulu ngati ukonde umene anthu amagwiritsa ntchito posodza ndi bwato. Utatavu woterowo ukhoza kuimitsa ndege imene ikuuluka! Inde, Yehova anazipanga “mwanzeru” zinthu zonsezi.

Kodi ndani analinganiza zolengedwa za padziko lapansi kuti zikhale “zanzeru mwachibadwa”?

Nzeru Zimaonekanso M’zinthu Zakuthambo

15, 16. (a) Kodi nyenyezi zakuthambo zimapereka umboni wotani wa nzeru za Yehova? (b) Kodi udindo wa Yehova monga Mtsogoleri Wamkulu wa gulu lalikulu lolinganizidwa bwino la angelo umapereka umboni wotani wa nzeru za Woyang’anira ameneyu?

15 Nzeru za Yehova zimaoneka m’ntchito yake m’chilengedwe chonse. Nyenyezi za kuthambo, zimene tinakambirana kwambiri ndithu m’Mutu 5, sizongomwazikanamwazikana mu mlengalenga monse. Chifukwa cha nzeru za “malamulo a thambo” a Yehova, nyenyezi kumwamba zinaikidwa bwino m’magulumagulu otchedwa milalang’amba yomwe nayonso ili m’magulumagulu, ndipo magulu a milalang’amba amenewo nawonso ali m’magulu akuluakulu kwambiri. (Yobu 38:33, Malembo Oyera) N’zosadabwitsa kuti Yehova amati zinthu zakuthambo zili “khamu”! (Yesaya 40:26) Komabe, pali khamu lina limene limaonetsa bwino kwambiri nzeru za Yehova.

 16 Monga tinaonera m’Mutu 4, Mulungu ali ndi dzina la udindo lakuti “Yehova wa makamu” chifukwa cha udindo wake monga Mtsogoleri Wamkulu wa gulu lalikulu lolinganizidwa bwino la zolengedwa zauzimu miyandamiyanda. Umenewu ndi umboni wa mphamvu za Yehova. Nangano nzeru zake zikukhudzidwa bwanji? Lingalirani izi: Yehova limodzi ndi Yesu saleka kugwira ntchito. (Yohane 5:17) Motero tingayembekezere kuti atumiki aungelo a Wam’mwambamwambayo nawonso akhala otangwanidwa nthaŵi zonse. Ndipo kumbukirani kuti iwo ndi oposa anthu popeza kuti ndi anzeru kwambiri ndiponso ndi amphamvu zedi. (Ahebri 1:7; 2:7) Komatu, nthaŵi zonse Yehova wakhala akupatsa angelo onsewo ntchito yokhutiritsa yomwe akhala akugwira mosangalala kwa zaka mabiliyoni ambirimbiri—akhala ‘akuchita mawu ake’ ndi ‘kuchita chomukondweretsa iye.’ (Salmo 103:20, 21) Woyang’anira ameneyu ayeneratu kukhala ndi nzeru zochuluka kwabasi!

Yehova Ndiye “Wanzeru Yekha”

17, 18. N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti Yehova ndiye “wanzeru Yekha,” nanga n’chifukwa chiyani nzeru zake ziyenera kutipatsa mantha aulemu?

17 Polingalira umboni woterewu, kodi n’zodabwitsa kuti Baibulo limalemekeza kwambiri nzeru za Yehova? Mwachitsanzo, limati Yehova ndiye “wanzeru Yekha.” (Aroma 16:27) Ndi Yehova yekha amene ali ndi nzeru pa chilichonse. Ndiye gwero la nzeru zenizeni zonse. (Miyambo 2:6) Ndicho chifukwa chake Yesu, ngakhale kuti ndiye wanzeru zedi pa zolengedwa zonse za Yehova, sanadalire nzeru zake koma analankhula monga mmene Atate wake anamuuzira.—Yohane 12:48-50.

18 Taonani mmene mtumwi Paulo analongosolera nzeru za Yehova kuti n’zapadera kwambiri. Iye anati: “Ha! kuya kwake kwa kulemera ndi kwa nzeru ndi kwa kudziŵa kwake kwa Mulungu! Osasanthulikadi maweruzo ake, ndi njira zake n’zosalondoleka!” (Aroma 11:33) Mwa kuyamba vesili ndi mawu ofuula akuti “Ha!” Paulo anasonyeza malingaliro amphamvu amene anali nawo mumtima mwake, mantha limodzi ndi ulemu waukulu. Mawu achigiriki akuti “kuya” amene iye anagwiritsa ntchito ndi ofanana kwambiri ndi mawu otanthauza “phompho.” Motero mawu ake amatipatsa chithunzithunzi cha m’maganizo chooneka bwino. Pamene tisinkhasinkha nzeru za Yehova, zimakhala ngati tikuyang’ana m’chidzenje chozama zedi, chimene pansi pake sipaoneka; chakuya  komanso chachikulu kwambiri moti sitingathe kudziŵa bwino kukula kwake, ndiponso ndi chokanika kuchifotokoza kaya kuchijambula mwatsatanetsatane. (Salmo 92:5) Kodi mfundo imeneyi siyenera kutichititsa kukhala odzichepetsa?

19, 20. (a) N’chifukwa chiyani chiwombankhanga chili chizindikiro choyenera cha nzeru za Mulungu? (b) Kodi Yehova wasonyeza motani kuti amatha kuona zochitika za m’tsogolo?

19 Yehova ndiye “wanzeru Yekha” mu lingaliro linanso: Ndiye yekha amene akhoza kuona za m’tsogolo. Kumbukirani kuti chiwombankhanga, chomwe chimaona patali, ndicho chimaimira nzeru za Yehova. Chiwombankhanga cha mtundu wofiirira kumutu ndi m’khosi chikhoza kulemera makilogalamu asanu okha basi, komatu maso ake amakhala akuluakulu kuposa a munthu wamkulu. Maso a chiwombankhanga ndi akuthwa kwambiri. Mbalameyi imatha kuona kanthu kakang’ono zedi kamene kali pansi, iyo ili m’mwamba pamtunda wa mamita mahandiredi ochuluka, mwina ngakhalenso makilomita angapo! Nthaŵi ina Yehova mwiniyo anati chiwombankhanga, “maso ake apenya kutali.” (Yobu 39:29, Malembo Oyera) M’lingaliro lofananalo, Yehova akhoza ‘kupenyetsetsa ali kutali’ ndi nthaŵi yochitikira zinthu za m’tsogolo.

20 M’Baibulo muli umboni wochuluka wosonyeza kuti zimenezi n’zoona. Muli maulosi ochuluka kwambiri, kapena kuti mbiri yomwe inalembedwa zochitikazo zisanachitike. Baibulo linaneneratu za zotsatirapo za nkhondo, kuyamba ndi kutha kwa maulamuliro  apadziko lonse, ndipo ngakhale maluso amene akazembe ankhondo adzagwiritsa ntchito—m’zochitika zina, zimenezi zinanenedwa kudakali zaka mahandiredi angapo.—Yesaya 44:25–45:4; Danieli 8:2-8, 20-22.

21, 22. (a) N’chifukwa chiyani palibe zifukwa zomveka zonenera kuti Yehova anaoneratu zonse zimene mudzasankha kuchita pamoyo wanu? Perekani fanizo. (b) Kodi timadziŵa bwanji kuti Yehova ndi waubwenzi kapenanso kuti si wouma mtima chifukwa cha nzeru zake?

21 Koma kodi zimenezi zikutanthauza kuti Mulungu anaoneratu kale zimene mudzasankha kuchita m’moyo wanu? Ena amene amaphunzitsa kuti Mulungu amaikiratu zam’tsogolo amayankha kuti inde. Komano, malingaliro amenewo amapeputsa nzeru za Yehova, chifukwa amasonyeza kuti sangalamulire luso lake loona za m’tsogolo. Tiyeni tifanizire motere: Ngati inu mukanakhala ndi mawu anthetemya poimba, kodi bwenzi mukungoimba nthaŵi zonse osalekeza? Ameneŵa akumveka kukhala malingaliro opanda pake, kodi si choncho? Mofananamo, Yehova ali ndi luso lodziŵiratu za m’tsogolo, koma saligwiritsa ntchito nthaŵi zonse. Kuchita zimenezi kungapondereze ufulu wathu wodzisankhira zinthu, ndipo imeneyi ndi mphatso yamtengo wapatali imene Yehova sadzatilanda.—Deuteronomo 30:19, 20.

22 Choipa kwambiri n’chakuti, malingaliro a kuikiratu zam’tsogolo amasonyeza kuti Yehova si waubwenzi, koma kuti ndi wouma mtima, salingalira ena, ndiponso alibe chifundo chifukwa cha nzeru zakezo. Komatu limeneli ndi bodza lamkunkhuniza! Baibulo limaphunzitsa kuti Yehova ndiye “wa mtima wanzeru.” (Yobu 9:4) Sindiye kuti ali ndi mtima weniweni. Koma Baibulo kaŵirikaŵiri limagwiritsa ntchito mawu ameneŵa ponena za makhalidwe enieni a munthu, kuphatikizapo zimene zimamuchititsa kuchita zinthu zina ndiponso mmene amamvera mumtima mwake, monga ngati kukhala ndi chikondi. Motero nzeru za Yehova, mofanana ndi makhalidwe ake ena, zimalamulidwa ndi chikondi.—1 Yohane 4:8.

23. Kodi tiyenera kuchitanji pokhala kuti nzeru za Yehova n’zoposa zathu?

23 Inde, nzeru za Yehova n’zodalirika kotheratu. Zimaposa kwambiri nzeru zathu moti Mawu a Mulungu amatilimbikitsa mwachikondi kuti: “Khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse, osachirikizika pa luntha lako; umulemekeze m’njira zako zonse, ndipo Iye adzawongola mayendedwe ako.” (Miyambo 3:5, 6) Tsopano tiyeni tifufuze nzeru za Yehova kuti tithe kuyandikira kwambiri kwa Mulungu wathu wanzeru zonse ameneyu.