1-3. Kodi anthu akwawo kwa Yesu anachitanji ndi chiphunzitso chake, ndipo analephera kuzindikira chiyani chokhudza iye?

OMVETSERAWO anazizwa. Mwamuna wachinyamatayo Yesu anaimirira patsogolo pawo mu sunagoge ndi kumaphunzitsa. Sanali mlendo kwa iwo, chifukwa anakulira m’mudzi mwawo momwemo ndipo anali kugwirira ntchito limodzi kwa zaka zambiri pamene iye anali kalipentala. Mwina ena a iwo anali kukhala m’nyumba zimene Yesu anamanga nawo, kapena mwina polima minda yawo anali kugwiritsa ntchito mapulawo ndi magoli amene iye anapanga. * Koma kodi iwo analabadira motani ziphunzitso za munthu ameneyu yemwe kale anali kalipentala?

2 Ambiri amene anali kumvetsera anazizwa, nafunsa kuti: “Uyu adazitenga kuti nzeru zimenezi?” Koma ananenanso kuti: “Mmisiri wa mitengo uyu, mwana wa Mariya.” (Mateyu 13:54-58; Marko 6:1-3) Anthu akwawo kwa Yesu ameneŵa analingalira momvetsa chisoni kuti, ‘Kalipentala uyu ndi munthu wa kwathu konkuno.’ Ngakhale kuti mawu ake anali anzeru, iwo anamukana. Komatu iwo sanadziŵe kuti nzeru zimene anali kuwapatsa sizinali zake.

3 Kodi Yesu anazitenga kuti nzeru zimenezi? “Chiphunzitso changa sichili changa,” iye anatero, “koma cha Iye amene anandituma Ine.” (Yohane 7:16) Mtumwi Paulo anafotokoza kuti Yesu “anayesedwa kwa ife nzeru ya kwa Mulungu.” (1 Akorinto 1:30) Nzeru za Yehova mwiniyo zimaululika mwa Mwana wake, Yesu. Inde, izi zinalidi choncho moti Yesu anafika mpaka ponena kuti: “Ine ndi Atate ndife amodzi.” (Yohane 10:30) Tiyeni tiphunzire mbali zitatu zimene Yesu anaonetsera “nzeru ya kwa Mulungu.”

 Zimene Anaphunzitsa

4. (a) Kodi mfundo yaikulu ya uthenga wa Yesu inali yotani, ndipo n’chifukwa chiyani uthengawo unali wofunika kwambiri? (b) N’chifukwa chiyani nthaŵi zonse uphungu wa Yesu unali wothandiza ndi wopindulitsa kwambiri kwa omvetsera ake?

4 Choyamba, talingalirani zimene Yesu anaphunzitsa. Mfundo yaikulu ya uthenga wake inali yakuti “Uthenga Wabwino wa Ufumu.” (Luka 4:43) Unali uthenga wofunika kwambiri chifukwa cha mbali imene Ufumuwo udzachita potsimikizira kuti ulamuliro wa Yehova ndi wolungama ndi kubweretsa madalitso osatha kwa anthu. Pophunzitsa, Yesu analinso kupereka uphungu wanzeru pa moyo watsiku ndi tsiku. Anasonyeza kuti analidi ‘Wauphungu Wodabwitsa’ yemwe ananenedweratuyo. (Yesaya 9:6) Inde, kodi uphungu wake ukanalekeranji kukhala wodabwitsa? Anali kudziŵa kwambiri Mawu a Mulungu limodzi ndi chifuno Chake, anali kumvetsetsa bwino chibadwa cha anthu, ndipo anali kukonda kwambiri anthu. Motero nthaŵi zonse uphungu wake unali wothandiza ndi wopindulitsa kwambiri kwa omvetsera ake. Mawu a Yesu anali “mawu a moyo wosatha.” Inde, munthu angapeze moyo wosatha pamene atsatira uphungu wake.—Yohane 6:68.

5. Kodi ndi ziti zina mwa nkhani zimene Yesu anatchula mu Ulaliki wa pa Phiri?

5 Ulaliki wa pa Phiri ndi chitsanzo chachikulu cha nzeru zosayerekezeka zomwe Yesu anali kuphunzitsa. Ulaliki umenewu, monga walembedwera pa Mateyu 5:3-7:27, ungaperekedwe mwina m’mphindi 20 zokha. Komabe, uphungu womwe uli mmenemu ndi wothandiza nthaŵi ina iliyonse, ndipo ndi wogwira bwino ntchito lerolino monga momwe unalili utangoperekedwa. Yesu anakhudza nkhani zambiri, kuphatikizapo mmene munthu angakhalire bwino ndi ena (5:23-26, 38-42; 7:1-5, 12), mmene angakhalire ndi khalidwe loyera (5:27-32), ndi mmene angakhalire ndi moyo watanthauzo (6:19-24; 7:24-27). Komatu Yesu sanangouza omvetsera ake chimene chinali chanzeru kuchita; anawasonyeza mwa kufotokoza momveka bwino mmene angachitire, kulingalira nawo, ndiponso kupereka umboni wake.

6-8. (a) Kodi Yesu akupereka zifukwa zotani zokhutiritsa maganizo a munthu kuti apeŵe kuda nkhaŵa? (b) Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti uphungu wa Yesu ukuonetsa nzeru yochokera kumwamba?

 6 Mwachitsanzo, taonani uphungu wanzeru wa Yesu polimbana ndi nkhaŵa za zinthu zakuthupi, monga unalembedwera mu Mateyu chaputala 6. Iye anatilangiza kuti: “Musadere nkhaŵa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala.” (Vesi 25) Chakudya ndi zovala ndi zinthu zofunika kwambiri pamoyo, ndipo n’kwachibadwa kudera nkhaŵa mmene munthu angapezere zimenezi. Koma Yesu anatiuza kuti “musadere nkhaŵa” zinthu zimenezo. * Chifukwa chiyani?

7 Tamvetserani mmene Yesu akulongosolera mokhutiritsa. Popeza Yehova anatipatsa moyo ndi thupi, kodi sangatipatse chakudya chochirikiza moyowo ndi zovala zoveka thupilo? (Vesi 25) Ngati Mulungu amapatsa mbalame chakudya ndipo amaveka maluŵa mokongola, nanga anthu amene amamulambira ndiye adzawasamalira kwambiri motani? (Mavesi 26, 28-30) Ndithudi, n’zopanda tanthauzo kukhala ndi nkhaŵa yonkitsa. Singawonjezere moyo wathu ngakhale pang’ono. * (Vesi 27) Kodi tingapeŵe motani kukhala ndi nkhaŵa? Yesu akutipatsa uphungu wakuti: Pitirizani kuika kulambira Mulungu pa malo oyamba m’moyo wanu. Amene amachita zimenezi angakhale ndi chidaliro chakuti Atate wawo wakumwamba ‘adzawawonjezera’ zofuna zawo zonse za tsiku ndi tsiku. (Vesi 33) Pomaliza, Yesu akupereka malingaliro othandiza kwambiri akuti, thanani kaye ndi zochitika za tsiku limodzi. N’chifukwa chiyani kuwonjezera nkhaŵa za maŵa pa nkhaŵa za lero? (Vesi 34) Ndiponso, pali chifukwa chanji chodandaulira kwambiri ndi zinthu zimene mwina sizingachitike n’komwe? Tingapeŵe kwambiri kudwala mtima m’dziko losautsali mwa kugwiritsa ntchito uphungu wanzeru woterewu.

 8 N’zachionekere kuti uphungu umene Yesu anapereka ndi wothandiza lerolino mofanana ndi mmene unalili wothandiza pamene unaperekedwa pafupifupi zaka 2,000 zapitazo. Kodi umenewu si umboni wa nzeru yochokera kumwamba? Ngakhale uphungu wabwino kwambiri womwe alangizi aumunthu amapereka m’kupita kwanthaŵi sukhalanso wothandiza ndipo mosakhalitsa amaukonzanso kapena kuusintha. Komabe zimene anaphunzitsa Yesu zakhala nthaŵi yaitali ndipo zidakali zopindulitsa. Koma zimenezi siziyenera kutidabwitsa, chifukwa Phungu Wodabwitsa ameneyu anali kulankhula “mawu a Mulungu.”—Yohane 3:34.

Mmene Anali Kuphunzitsira

9. Kodi asilikali ena ananenanji za kaphunzitsidwe ka Yesu, nanga n’chifukwa chiyani iwo sanali kungokokomeza?

9 Mbali yachiŵiri imene Yesu anaonetsera nzeru za Mulungu inali kaphunzitsidwe kake. Panthaŵi ina, asilikali omwe anatumidwa kukamugwira anabwerako chimanjamanja, nati: “Nthaŵi yonse palibe munthu analankhula chotero.” (Yohane 7:45, 46) Iwoŵatu sanali kungokokomeza. Pa anthu onse amene akhalako ndi moyo, Yesu, yemwe anali “wochokera Kumwamba,” ndiye anali wodziŵa zinthu zambiri ndiponso ndiye anaona zochitika zambiri kuposa wina aliyense moti ankalankhula kuchokera pa zimenezo. (Yohane 8:23) Analidi kuphunzitsa mosafanana ndi munthu aliyense. Taonani njira ziŵiri chabe zimene Mphunzitsi wanzeruyu anagwiritsa ntchito.

“Makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake”

10, 11. (a) N’chifukwa chiyani timachita chidwi kwambiri ndi mmene Yesu anagwiritsira ntchito mafanizo? (b) Kodi nthano n’chiyani, nanga n’chitsanzo chiti chimene chikusonyeza chifukwa chake nthano za Yesu zinali zogwira mtima kwambiri pophunzitsa?

10 Kugwiritsa ntchito mafanizo mogwira mtima. ‘Yesu anaphiphiritsira m’mafanizo kwa makamu a anthu,’ tikuuzidwa choncho. “Ndipo kopanda fanizo sanalankhula kanthu kwa iwo.” (Mateyu 13:34) Timachitadi chidwi kwambiri ndi luso lake losayerekezeka lophunzitsa choonadi chofunika kwambiri pogwiritsa ntchito zinthu zochitika tsiku ndi tsiku. Alimi akudzala mbewu, akazi akukonzekera kuphika mkate, ana akuseŵera pamsika, asodzi akuponya makoka, abusa akufunafuna nkhosa zosokera—zimenezi zinali zinthu zomwe omvetsera ake anali  ataziona nthaŵi zambiri. Pamene choonadi chofunika kwambiri chafanizidwa ndi zinthu zomwe anthu anazizoloŵera, choonadicho chimakhomerezeka mofulumira ndiponso chimazika mizu m’maganizo ndi mu mtima mwa munthu.—Mateyu 11:16-19; 13:3-8, 33, 47-50; 18:12-14.

11 Kaŵirikaŵiri Yesu anali kusimba nthano, ndiko kuti tinkhani tophunzitsa chikhalidwe kapena choonadi pa nkhani zauzimu. Popeza kuti nkhani sizivuta kuzimvetsa ndi kuzikumbukira kusiyana ndi kungopereka malingaliro, nthano zimenezo zinathandiza anthu kusunga ziphunzitso za Yesu. M’nthano zambiri, Yesu anali kupereka chithunzi chomveka bwino cha Atate wake chomwe chinali chovuta kuchiiwala. Mwachitsanzo, ndani yemwe sangamve mfundo imene ili mu nthano ya mwana woloŵerera, yakuti pamene munthu amene analoŵerera walapa moona mtima, Yehova adzamumvera chifundo ndipo adzamulandiranso mwachikondi?—Luka 15:11-32.

12. (a) Kodi Yesu anagwiritsa ntchito mafunso m’njira yotani pophunzitsa? (b) Kodi Yesu anawathetsa mawu motani anthu amene ankakayikira ulamuliro wake?

12 Kugwiritsa ntchito mafunso mwaluso. Yesu anali kugwiritsa ntchito mafunso kuti omvetsera ake agamulepo okha pankhaniyo, kuti apende zolinga zawo, kapenanso kuti adzisankhire chochita. (Mateyu 12:24-30; 17:24-27; 22:41-46) Pamene atsogoleri achipembedzo anakayikira ngati Yesu anali ndi ulamuliro wopatsidwa ndi Mulungu, iye anayankha kuti: “Ubatizo wa Yohane uchokera Kumwamba kodi, kapena kwa anthu?” Atazizwa nalo funsolo, anakambirana okhaokha kuti: “Tikati, Kumwamba, Iye adzati kwa ife, Munalekeranji kumvera iye? Koma tikati, Kwa anthu, tiopa khamulo la anthu; pakuti onse amuyesa Yohane mneneri.” Kenako anayankha kuti: “Sitidziŵa ife.” (Marko 11:27-33; Mateyu 21:23-27) Mwa kufunsa funso losavuta kuyankha, Yesu anawathetsa mawu ndipo anavumbula chinyengo chimene chinali m’mitima yawo.

13-15. Kodi nthano ya Msamariya yemwe anakhala mnansi ikuonetsa motani nzeru za Yesu?

13 Nthaŵi zina Yesu pophunzitsa ndi mafanizo anali kufunsamonso mafunso ochititsa munthu kuganiza. Pamene Myuda wina wachilamulo anafunsa Yesu chimene chinali chofunika  kuchita kuti apeze moyo wosatha, Yesu anamuuza za Chilamulo cha Mose, chomwe chimalamula kuti anthu azikonda Mulungu ndi anansi awo. Pofuna kudzisonyeza wolungama, munthuyo anafunsa kuti: “Ndipo mnansi wanga ndani?” Yesu anayankha mwa kumusimbira nkhani. Munthu wina Myuda anali yekhayekha paulendo ndipo panjira anakumana ndi achifwamba omwe anamusiya atatsala pang’ono kufa. Pamalopo panafika Ayuda aŵiri, woyamba kufika anali wansembe kenako Mlevi. Onse aŵiri sanamuthandize. Koma kenako Msamariya wina anafikanso pamalowo. Pogwidwa chifundo, iye anamanga mabala a wovulalayo ndipo mwachikondi anapita naye kumalo abwino, ku nyumba ya alendo kumene akanatha kuchira. Pomaliza nkhaniyo, Yesu anafunsa munthuyo kuti: “Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi wa iye uja adagwa m’manja a achifwamba?” Munthuyo anakakamizika kuyankha kuti: “Iye wakumuchitira chifundo.”—Luka 10:25-37.

14 Kodi nkhani imeneyi ikuonetsa motani nzeru za Yesu? M’masiku a Yesu, Ayuda anali kunena kuti “mnansi” wawo ndi munthu yekhayo amene anali kusunga miyambo yawo—Asamariya sanali kuwaphatikizapo. (Yohane 4:9) Chikhala kuti Yesu anasimba nkhaniyo monena kuti Msamariya ndiye anavulala ndipo Myuda ndiye anamuthandiza, kodi akanachotsa tsankhulo? Mwanzeru Yesu anakonza nkhaniyi kotero kuti Msamariya ndiye anasamalira Myuda mwachikondi. Ndiponso taonani funso limene Yesu anafunsa pamapeto pa nkhaniyo. Anasintha pamene panasumika mawu akuti “mnansi.” Tingati wachilamuloyo anafunsa kuti: ‘Kodi ndani amene ndiyenera kumusonyeza chikondi monga mnansi wanga?’ Koma Yesu anamufunsa kuti: “Uti wa awa atatu, uyesa iwe, anakhala mnansi?” Yesu anaika maganizo osati pa amene anachitiridwa chifundo, wovulalayo, koma pa amene anasonyeza chifundo, Msamariya. Mnansi weniweni amayamba ndiye kusonyeza chikondi kwa ena ngakhale kuti ndi a mitundu ina. Ndithudi Yesu sakanamveketsa mogwira mtima mfundo yake kuposa pamenepa.

15 Kodi n’zodabwitsa kuti anthu anazizwa ndi “chiphunzitso” cha Yesu ndi kukopeka naye? (Mateyu 7:28, 29) Panthaŵi ina “khamu lalikulu la anthu” linakhala limodzi naye kwa masiku atatu; mwinanso amangokhala osadya!—Marko 8:1, 2.

 Mmene Anali Kukhalira pa Moyo Wake

16. Kodi Yesu anapereka motani “umboni weniweni” wakuti nzeru ya Mulungu inali kumutsogolera?

16 Mbali yachitatu imene Yesu anaonetsera nzeru za Yehova inali mmene anali kukhalira pa moyo wake. Nzeru imakhala yothandiza; imachita zinthu zopindulitsa. “Ndani ali wanzeru pakati panu?” anafunsa motero wophunzira Yakobo. Ndiyeno anadziyankha kuti: “Khalidwe lake lolungama lipereketu umboni weniweni wakuti ali wanzeru.” (Yakobo 3:13, The New English Bible) Mmene Yesu anali kukhalira zinali kupereka “umboni weniweni” wakuti nzeru ya Mulungu inali kumutsogolera. Tiyeni tione mmene anasonyezera kuti anali munthu wolingalira bwino, ponse paŵiri, mmene anali kukhalira pa moyo wake ndiponso mmene anali kuchitira zinthu ndi ena.

17. Kodi ndi zochitika zotani zimene zikuonetsa kuti Yesu sanali kupitirira muyeso pochita zinthu pa moyo wake?

17 Kodi munaona kuti anthu amene salingalira bwino kaŵirikaŵiri amachita zinthu mopitirira muyezo? Pamafunika nzeru kuti munthu asachite zinthu mopyola m’lingo woyenera. Poonetsa nzeru za Mulungu, Yesu anali kuchita zinthu mosamala kwambiri. Koposa zonse, anali kuika zinthu zauzimu pa malo oyamba m’moyo wake. Anali wotanganidwa kwambiri ndi ntchito yolengeza uthenga wabwino. ‘Ndadzera ntchito imeneyi,’ iye anatero. (Marko 1:38) Nthaŵi zambiri zinthu zakuthupi sizinali zofunika kwambiri kwa iye; zikuonekatu kuti anali ndi katundu wochepa kwambiri. (Mateyu 8:20) Komabe, sikuti iye anali munthu wosasangalala kaya wodzimana monkitsa. Mofanana ndi Atate wake, “Mulungu wachimwemwe,” Yesu anali munthu wosangalala, kapena kuti “wachimwemwe,” ndipo anali kusangalatsanso anthu ena. (1 Timoteo 1:11, NW; 6:15, NW) Pamene anapezeka pa phwando laukwati, chochitika chimene nthaŵi zambiri panali nyimbo, kuimba, ndi kusangalala, iye sanapezekepo kuti asokoneze mwambowo. Vinyo atatha iye anasandutsa madzi kukhala vinyo wokoma, chakumwa chimene ‘chimakondweretsa mtima wa munthu.’ (Salmo 104:15; Yohane 2:1-11) Yesu anapita kunyumba za anthu ambiri amene anamuitanira chakudya, ndipo kaŵirikaŵiri anagwiritsa ntchito mipata yoteroyo kuphunzitsa anthu.—Luka 10:38-42; 14:1-6.

18. Kodi Yesu anasonyeza motani kulingalira mosaphonya pochita zinthu ndi ophunzira ake?

 18 Yesu anali kulingalira mosaphonya pochita zinthu ndi ena. Mmene anali kumvetsetsera chibadwa cha anthu kunamuthandiza kuona bwino lomwe zomwe ophunzira ake angachite. Anali kudziŵa bwino kuti ophunzira akewo ndi opanda ungwiro. Komatu, iye anazindikira makhalidwe abwino amene iwo anali nawo. Anaona kuti amuna ameneŵa omwe Yehova anali atawakoka akanatha kuchita zambiri. (Yohane 6:44) Ngakhale kuti iwo anali kuphonya pa zina, Yesu anali wofunitsitsa kuwakhulupirira. Poonetsa kuwadalira kumeneko, anapatsa ophunzira ake udindo waukulu kwambiri. Anawauza kuti achite ntchito yolalikira uthenga wabwino, ndipo anali n’chidaliro chakuti adzakwanitsa kugwira ntchito imeneyo. (Mateyu 28:19, 20) Buku la Machitidwe limatsimikizira kuti iwo mokhulupirika anaonetsetsa kuti akugwiradi ntchito imene anawalamula kugwirayo. (Machitidwe 2:41, 42; 4:33; 5:27-32) Motero n’zachionekere kuti Yesu sanalakwitse powadalira.

19. Kodi Yesu anaonetsa motani kuti anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima”?

19 Monga taonera m’Mutu 20, Baibulo limagwirizanitsa kudzichepetsa komanso kufatsa ndi nzeru. N’zoona kuti Yehova ndiye amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhaniyi. Koma bwanji za Yesu? N’zosangalatsa kuona mmene Yesu analili wodzichepetsa pochita zinthu ndi ophunzira ake. Monga munthu wangwiro, iye anali wowaposa. Komatu iye sananyoze ophunzira  ake. Sanalakalake kuwachititsa kumva kukhala otsika kapena kuti sangathe kuchita zinthu. M’malo mwake, ankalingalira zinthu zomwe sangathe kuchita, ndipo anali woleza mtima akamaphonyetsa zina. (Marko 14:34-38; Yohane 16:12) Kodi si zochititsa chidwi kuti ngakhale ana anali omasuka naye Yesu? Ndithudi iwo ankasangalala kukhala naye pafupi chifukwa anaona kuti anali “wofatsa ndi wodzichepetsa mtima.”—Mateyu 11:29; Marko 10:13-16.

20. Kodi Yesu anaonetsa motani kuti anali wololera pamene anali kulankhula ndi mkazi wina wosakhala Myuda yemwe mwana wake anagwidwa ndi chiŵanda?

20 Yesu anasonyeza kudzichepetsa kwaumulungu m’njira inanso yofunika kwambiri. Anali wololera, kapena kuti ankavomereza zimene ena ankafuna, pamene kunali koyenera kuwachitira chifundo. Mwachitsanzo, takumbukirani nthaŵi imene mkazi wina yemwe sanali Myuda anamupempha kuchiritsa mwana wake wamkazi yemwe anagwidwa koopsa ndi chiŵanda. Mwa njira zitatu, Yesu poyambirira anasonyeza kuti sanafune kumuthandiza. Poyamba sanamuyankhe mkaziyo, kachiŵiri, ananena mwachindunji kuti sanatumidwe kwa anthu amene sanali Ayuda koma kwa Ayuda, ndipo kachitatu, anapereka fanizo limene mokoma mtima linafotokoza mfundo imodzimodziyo. Komabe, mkaziyo anaumirira, kusonyeza umboni wakuti anali ndi chikhulupiriro chapadera. Polingalira chochitika chapadera chimenechi, kodi Yesu anachitanji? Anachita zomwezo zimene anati sangachite. Anachiritsa mwana wake wa mkaziyo. (Mateyu 15:21-28) Kunalitu kudzichepetsa kwenikweni kumeneku, kodi si choncho? Ndipo kumbukirani kuti kudzichepetsa ndiko maziko a nzeru yeniyeni.

21. N’chifukwa chiyani tifunika kuyesetsa kutsanzira umunthu wa Yesu, kalankhulidwe kake, ndiponso mmene anali kuchitira zinthu?

21 Ndifetu othokoza kwambiri kuti Mauthenga Abwino amatiululira zolankhula ndiponso zochita za munthu wanzeru kwambiri amene anakhalako ndi moyo! Tikumbukire kuti Yesu anali chithunzithunzi chenicheni cha Atate wake. Mwa kutsanzira umunthu wa Yesu, kalankhulidwe kake, ndiponso mmene anali kuchitira zinthu, tidzakhala tikukulitsa nzeru yochokera kumwamba. M’mutu wotsatira, tiona mmene tingagwiritsire ntchito nzeru za Mulungu m’moyo wathu.

^ ndime 1 M’nthaŵi za m’Baibulo, akalipentala anali kupatsidwa ntchito yomanga nyumba, yokonza zinthu zamatabwa monga mipando ndi matebulo, ndiponso kupanga zipangizo zaulimi. Justin Martyr, yemwe anakhalapo ndi moyo m’zaka za m’ma 100 C.E., analemba za Yesu kuti: “Akakhala limodzi ndi amuna anali n’chizoloŵezi chogwira ntchito ya ukalipentala, n’kumapanga mapulawo ndi magoli.”

^ ndime 6 Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “kuda nkhaŵa” amatanthauza “kudodometsedwa maganizo.” Monga momwe agwiritsidwira ntchito pa Mateyu 6:25, amanena za kuopa chinachake komwe kumadodometsa kapena kupangitsa maganizo kusakhala pa chinthu chimodzi, ndi kukhala wopanda chimwemwe m’moyo.

^ ndime 7 Ndipotu, kufufuza kwa asayansi kwasonyeza kuti chifukwa chodandaula ndi kuganiza kwambiri tingakhale pangozi yodwala matenda a mtima ndi matenda enanso ambiri amene angafupikitse moyo wathu.