Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 20

“Wa Mtima Wanzeru”—Komatu Wodzichepetsa

“Wa Mtima Wanzeru”—Komatu Wodzichepetsa

1-3. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndi wodzichepetsa?

ATATE akufuna kuphunzitsa mwana wawo wamng’ono zinthu zofunika kwambiri. Akufunitsitsa kuti zimufike pamtima mwanayo. Kodi ayenera kumuphunzitsa mwa njira yotani? Kodi ayenera kuimirira moopseza mwanayo ndi kumalankhula mwaukali? Kapena ayenera kunyonyomala kuti afanane ndi msinkhu wa mwanayo ndi kumalankhula modekha ndi mosangalatsa? Ndithudi, atate wanzeru ndi wodzichepetsa angamulankhule modekha.

2 Kodi Yehova ndi Atate wotani, wodzikuza kapena wodzichepetsa, waukali kapena wodekha? Yehova amadziŵa zonse, ndipo ali ndi nzeru zonse. Komabe, kodi munaona kuti kukhala wodziŵa zinthu ndiponso wanzeru sikuchititsa munthu kukhala wodzichepetsa? Monga mmene Baibulo limanenera, ‘chidziŵitso chimatukumula.’ (1 Akorinto 3:19; 8:1) Koma Yehova, amene ndi “wa mtima wanzeru,” alinso wodzichepetsa. (Yobu 9:4) Zimenezi sizikutanthauza kuti ndi wotsika kwa ena kapenanso kuti si wamkulu, koma kuti iye si wodzikuza. N’chifukwa chiyani zili choncho?

3 Yehova ndi woyera. Motero iye si wodzikuza chifukwa chakuti kudzikuza kumadetsa munthu. (Marko 7:20-22) Ndiponso, taonani zimene mneneri Yeremiya anauza Yehova, iye anati: “Mosalephera moyo wanu [Yehova mwiniyo] udzakumbukira nuŵeramira pa ine.” * (Maliro 3:20, NW) Tangolingalirani! Yehova, Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse, anali wofunitsitsa ‘kuŵerama,’ kapena kuti kukhala pamalo otsika omwe panali Yeremiya, n’cholinga chakuti amusamalire bwino munthu wopanda ungwiroyo. (Salmo  113:7) Inde, Yehova ndi wodzichepetsa. Koma kodi kudzichepetsa kwa Mulungu kumaphatikizapo chiyani? Kodi kukugwirizana motani ndi nzeru? Nanga n’chifukwa chiyani kuli kofunika kwa ife?

Mmene Yehova Amasonyezera Kuti Ndi Wodzichepetsa

4, 5. (a) Kodi kudzichepetsa n’chiyani, nanga kumaonekera motani? N’chifukwa chiyani sikuyenera kuonedwa monga kufooka kapena mantha? (b) Kodi Yehova anasonyeza kudzichepetsa motani pa zomwe anali kuchita ndi Davide, nanga kudzichepetsa kwa Yehova ndi kofunika motani kwa ife?

4 Kudzichepetsa ndiko kukhala wosadzitukumula, wosadzitamandira, komanso kusakhala wonyada. Kudzichepetsa ndi khalidwe la mu mtima wa munthu ndipo limaonekera pamene munthu ali wofatsa, woleza mtima, ndi wololera. (Agalatiya 5:22, 23) Komabe, munthu wa makhalidwe okondweretsa Mulungu ameneŵa sayenera kuonedwa ngati kuti ndi wofooka kapena wamantha. Yehova amakwiya mwachilungamo ndiponso amagwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga; akanakhala kuti ndi wofooka kapena wamantha  sibwenzi akuchita zimenezi. Koma, mwa kukhala wodzichepetsa ndi wofatsa, Yehova amaonetsa kuti ali ndi nyonga kwambiri, zomwe ndi mphamvu zimene amadzilamulira nazo bwino lomwe pa zimene amachita. (Yesaya 42:14) Kodi kudzichepetsa n’kogwirizana motani ndi nzeru? Buku lina lofotokoza za m’Baibulo limati: “Pomaliza, tingalongosole kudzichepetsa . . . mogwirizana ndi kusadziona kukhala wopambana ena, ndipo ndiwo maziko ofunika kwambiri a nzeru zonse.” Motero munthu sangakhale ndi nzeru zenizeni ngati si wodzichepetsa. Kodi timapindula motani ndi kudzichepetsa kwa Yehova?

Atate wanzeru amachita zinthu ndi ana ake modzichepetsa ndi modekha

5 Mfumu Davide anaimbira Yehova kuti: “Mwandipatsa chikopa cha chipulumutso chanu: ndipo dzanja lamanja lanu landigwiriziza, ndipo chifatso chanu [“kudzichepetsa kwanu,” NW] chandikuza ine.” (Salmo 18:35) Tingati, Yehova anaŵerama kuti asamalire munthu wopanda ungwiro ameneyu, namuteteza ndi kumugwiriziza tsiku ndi tsiku. Davide anazindikira kuti akanapulumuka, ngakhalenso kufika pa kukhala mfumu yaikulu, pachifukwa chokha chakuti Yehova anali wofunitsitsa kudzichepetsa mwanjira imeneyi. Ndithudi, ndani wa ife amene akanayembekeza kupulumuka chikhala kuti Yehova si wodzichepetsa, si wofunitsitsa kuŵerama kuti atisamalire monga Atate wofatsa ndi wachikondi?

6, 7. (a) Kodi Yehova ndi wodzichepetsa m’lingaliro lotani? (b) Kodi pali kugwirizana kotani pakati pa kufatsa ndi nzeru, nanga ndani amene amapereka chitsanzo chachikulu pankhaniyi?

6 Kudzichepetsa ndi khalidwe labwino kwambiri lofunika kuti anthu okhulupirika azilikulitsa. Limayendera limodzi ndi nzeru. Mwachitsanzo, Miyambo 11:2 imanena kuti: “Nzeru ili ndi odzichepetsa.” Komabe, Baibulo silinena kuti Yehova ndi wodzichepetsa m’lingaliro lofanana ndi mmene anthu amakhalira odzichepetsa. Chifukwa chiyani? Sikuti iye ndi wosadzichepetsa. Koma kudzichepetsa, monga momwe kwagwiritsidwira ntchito m’Malemba ponena za anthu, kumapereka lingaliro lakuti moyenerera munthuyo amadziŵa malire a zimene angachite. Wamphamvuyonseyo alibe zofooka kapena malire alionse kusiyapo kokha malire odziikira yekha chifukwa cha miyezo yake yolungama. (Marko 10:27; Tito 1:2) Ndiponso, pokhala Wam’mwambamwamba, palibe wina woti angamulamulire. Motero Yehova sali wodzichepetsa m’lingaliro limenelo.

 7 Komabe, Yehova ndi wodzichepetsa m’lingaliro lakuti ndi wofunitsitsa kuchita zinthu ndi anthu wamba. Ndiponso Yehova ndi wofatsa. Amaphunzitsa atumiki ake kuti kukhala wofatsa n’kofunika kwambiri kuti munthu akhale ndi nzeru zenizeni. Motero Mawu Ake amanena za “nzeru yofatsa.” * (Yakobo 3:13) Yehova amapereka chitsanzo chabwino kwambiri pankhaniyi. Tiyeni tione mmene amachitira zimenezi.

Modzichepetsa Yehova Amagaŵira Ena Maudindo Ndiponso Amamvetsera

8-10. (a) N’chifukwa chiyani zili zochititsa chidwi kuti Yehova amasonyeza kufunitsitsa kugaŵira ena maudindo ndiponso kumvetsera? (b) Kodi Wamphamvuyonseyo wadzichepetsa motani pochita zinthu ndi angelo ake?

8 Yehova ndi wofunitsitsa kugaŵira ena maudindo ndi kuwamvetsera, ndipo zimenezi zimatipatsa umboni wochititsa chidwi wakuti iye ndi wodzichepetsa. N’zodabwitsa kwambiri kuti iye amachita zimenezi, chifukwatu Yehova safunika thandizo kaya uphungu. (Yesaya 40:13, 14; Aroma 11:34, 35) Komabe, mobwerezabwereza Baibulo limatisonyeza kuti Yehova amadzichepetsa motero.

9 Mwachitsanzo, talingalirani chochitika chosaiwalika pa moyo wa Abrahamu. Abrahamu analandira alendo atatu, mmodzi wa iwo anamutchula kuti “Mbuyanga [“Yehova,” NW].” Alendowo anali angelo, koma mmodzi wa iwo anabwera m’dzina la Yehova ndipo anali kuchita zinthu m’dzina Lake. Pamene mngeloyo anali kulankhula ndi kuchita zinthu, anali kwenikweni Yehova amene anali kunena ndi kuchita zimenezo. M’njira imeneyi, Yehova anauza Abrahamu kuti Iye anamva ‘kulira kwakukulu kwa Sodomu ndi Gomora.’ Yehova anati: “Ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziŵa.” (Genesis 18:3, 20, 21) Inde, uthenga wa Yehova sunatanthauze kuti Wamphamvuyonseyo ‘adzatsika’ iyemwini. M’malo mwake, iye anatumanso angelo kuti akamuimire. (Genesis 19:1) Chifukwa chiyani? Kodi payekha Yehova, yemwe amaona zonse, sakanatha ‘kudziŵa’ zenizenidi zimene zinali kuchitika m’dera limenelo? Akanatha kutero. Komano modzichepetsa, Yehova  anapatsa angelo amenewo ntchito yokafufuza zimene zinali kuchitika ndiponso kukachezera Loti ndi banja lake ku Sodomu.

10 Ndiponso, Yehova amamvetsera. Panthaŵi ina anafunsa angelo ake kuti apereke malingaliro awo a mmene angawonongere mfumu yoipa Ahabu. Yehova sanafunike thandizo loterolo pankhaniyi. Komatu, anavomereza malingaliro a mngelo wina n’kumutuma kuti aonetsetse kuti zimene ananenazo zachitika. (1 Mafumu 22:19-22) Kodi kumeneku sikunali kudzichepetsa?

11, 12. Kodi Abrahamu anaona motani kuti Yehova ndi wodzichepetsa?

11 Yehova ndi wofunitsitsanso kumvetsera anthu opanda ungwiro omwe akufuna kunena malingaliro awo. Mwachitsanzo, nthaŵi yoyamba imene Yehova anauza Abrahamu kuti anali kufuna kuwononga Sodomu ndi Gomora, munthu wokhulupirikayo anadabwa zedi. “Musamatero ayi,” anatero Abrahamu, natinso: “Kodi sadzachita zoyenera Woweruza wa dziko lonse lapansi?” Anafunsa ngati Yehova sakanawononga mizindayo ngati munali anthu olungama 50. Yehova anamutsimikizira kuti sadzawononga. Koma Abrahamu anafunsanso; anachepetsa nambala ya anthu olungamawo kufika pa 45, kenako pa 40, n’kumangoichepetsabe. Ngakhale kuti Yehova anali kumutsimikizira kuti sangawononge, Abrahamu anafunsabe mpaka nambalayo inafika pa anthu teni. Mwina panthaŵiyi Abrahamu anali asanamvetsetse kuti Yehova ndi wachifundo kwambiri. Mulimonse mmene zinalili, moleza mtima ndiponso modzichepetsa, Yehova analola bwenzi lake ndi mtumiki wake Abrahamu kunena zakukhosi kwake mwa njira imeneyi.—Genesis 18:23-33.

12 Kodi ndi anthu angati anzeru ndi ophunzira kwambiri amene angamvetsere moleza mtima moteromo kwa munthu yemwe ndi mbuli? * Ndimo mmenetu Mulungu wathu alili wodzichepetsa. Pa kukambirana komweku, Abrahamu anaonanso kuti Yehova sakwiya msanga. (Eksodo 34:6) Mwina chifukwa chozindikira kuti sanayenere kufunsa zimene Wam’mwambamwambayo anali kuchita, Abrahamu anapempha kaŵiri konse kuti: “Asakwiyetu Ambuye.” (Genesis 18:30, 32) Inde Yehova sanamukwiyiredi. Ndithudi iye ali ndi “nzeru yofatsa.”

 Yehova Ndi Wololera

13. Kodi liwu lakuti “kulolera” limatanthauzanji malinga ndi mmene lagwiritsidwira ntchito m’Baibulo, nanga n’chifukwa chiyani liwu limeneli likulongosola bwino Yehova?

13 Timaonanso kudzichepetsa kwa Yehova m’khalidwe lina labwino kwambiri, kulolera. N’zomvetsa chisoni kuti khalidwe limeneli limasoŵa pakati pa anthu opanda ungwiro. Kuwonjezera pa kukhala wofunitsitsa kumvetsera zolengedwa zake zanzeru, Yehova alinso wofunitsitsa kuvomereza kuti pachitike zinthu zina pamene mfundo zolungama za makhalidwe abwino sizikuwombana ndi zochitikazo. Monga momwe lagwiritsidwira ntchito m’Baibulo, liwu lakuti “kulolera” kwenikweni limatanthauza “kuvomereza.” Khalidwe limenelinso limadziŵikitsa nzeru za Mulungu. Yakobo 3:17 amati: ‘Nzeru yochokera kumwamba imakhala . . . yaulere [“yololera,” NW].’ Kodi Yehova wanzeru zonseyo ndi wololera mu lingaliro lotani? Njira imodzi ndi yakuti iye amasintha mogwirizana ndi zochitika. Kumbukirani kuti dzina lake lenilenilo limatiphunzitsa kuti Yehova amadzichititsa kukhala chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse zolinga zake. (Eksodo 3:14) Kodi zimenezi sizikusonyeza mzimu wosintha malingana ndi zochitikazo ndiponso wololera?

14, 15. Kodi masomphenya a Ezekieli a galeta lakumwamba la Yehova amatiphunzitsanji za gulu lakumwamba la Yehova, ndipo limasiyana motani ndi mabungwe adziko lapansi?

14 M’Baibulo muli ndime ina yochititsa chidwi imene imatithandiza kumvetsetsako pang’ono mmene Yehova amasinthira mogwirizana ndi zochitika. Mneneri Ezekieli anaona masomphenya a gulu lakumwamba la Yehova la zolengedwa zauzimu. Anaona galeta lalikulu mochititsa mantha, “galimoto” la Yehova lomwe Iye amaliyendetsa nthaŵi zonse. Kuyenda kwake ndiko kunali kochititsa chidwi kwambiri. Mawiro ake akuluakuluwo anali ndi mbali zinayi ndiponso anali ndi maso paliponse moti anali kuona kulikonse komanso mwadzidzidzi anali kusintha mbali yoloŵera, popanda kuima ngakhale kutembenuka. Ndipotu galeta lalikulu limeneli silinali kuyenda moguguzika monga chigalimoto chachikulu cha anthu chokanika kuyenda. Linali kuyenda pa liŵiro ngati la mphezi ndi kumakhotera kumbali ina lili pa liŵiro lomwelo! (Ezekieli 1:1, 14-28) Inde, gulu la Yehova, mofanana ndi Wolamulira Wamkulu wamphamvuyonse amene amaliyendetsa, limasintha  kwambiri mogwirizana ndi zimene zikuchitika. Limachitapo kanthu pa zochitika zimene zimasinthasintha ndiponso pa zofunika zazikulu zofunika kusamalira zimene nazonso zimasinthasintha.

15 Anthu angangoyeserako chabe kutsanzira kusinthasintha koteroko. Komabe, kaŵirikaŵiri anthu limodzi ndi mabungwe awo amaumirira chinthu chimodzimodzi m’malo mosintha malinga n’zimene zikuchitika, amauma mtima m’malo movomereza zinazake kuti zichitike. Mwachitsanzo: Sitima yonyamula mafuta kapena yonyamula katundu ingakhale yochititsa chidwi chifukwa cha kukula kwake ndi mphamvu zake. Koma kodi sitima yoteroyo ingachitenji patagwa zamwadzidzidzi? Ngati panjanji patagwera chinthu sitima ya katundu ikubwera, sizingatheke kuti sitimayo ikhotere kumbali. Imavutikanso kuti iime mwadzidzidzi. Sitima yonyamula katundu wambiri zedi ingayendebe itamanga mabuleki kwa mtunda woposa kilomita imodzi isanaime! N’chimodzimodzi ndi sitima ya mafuta. Ikhoza kuyendabe mtunda wa makilomita eyiti koma atazimitsa injini zake. Ngakhale injini zake ataziika mu giya yobwerera m’mbuyo, sitima ya mafuta ingapitebe kutsogolo kwa makilomita atatu, isanayambe kubwerera m’mbuyo! N’zofanana ndi mabungwe a anthu omwe amaumirira chinthu chimodzimodzi ndiponso si ololera. Kaŵirikaŵiri anthu chifukwa cha kunyada amakana kusintha kuti agwirizane ndi zimene zikufunika komanso zimene zikuchitika. Kuumirira pa chinthu chimodzi kotereku kwawonongetsa ndalama za mabungwe ena ndipo kwagwetsa ngakhale maboma amene. (Miyambo 16:18) Ndifetu osangalala kwambiri kuti Yehova ndiponso gulu lake ndi osiyana kwambiri ndi mabungwe ngati amenewo!

Mmene Yehova Alili Wololera

16. Kodi Yehova anasonyeza motani kulolera pa zomwe anali kuchita ndi Loti asanawononge Sodomu ndi Gomora?

16 Talingaliraninso za kuwonongeka kwa Sodomu ndi Gomora. Mngelo wa Yehova anapatsa Loti ndi banja lake malangizo omveka bwino akuti: “Thaŵira kuphiri.” Komabe izi sizinamusangalatse Loti moti anakana nati: “Iyayitu, mfumu.” Loti anali wotsimikiza kuti ngati atathaŵira kumapiriko akafa, choncho anachonderera kuti amulole iye ndi banja lake kuthaŵira ku mudzi wina wapafupi wotchedwa Zoari. Koma pajatu Yehova anafuna  kuwononganso mudzi umenewo. Ndiponso, panalibe zifukwa zenizeni zoti Loti achitire mantha. Yehova akanathadi kupulumutsa Loti kumapiriko! Komabe, Yehova anavomereza zimene Loti anachonderera ndipo sanawononge Zoari. “Taona, ndikuvomereza iwe pamenepanso,” mngeloyo anamuuza motero Loti. (Genesis 19:17-22) Kodi Yehova sanalolere pamenepa?

17, 18. Pa zimene anachita ndi anthu a ku Nineve, kodi Yehova anasonyeza motani kuti ndi wololera?

17 Yehova amachitaponso kanthu munthu akalapa moona mtima. Amachita zinthu zachifundo ndi zoyenera nthaŵi zonse. Taonani zimene zinachitika mneneri Yona atatumidwa ku mzinda woipa ndi wachiwawa wa Nineve. Pamene Yona anali kuyenda m’misewu ya Nineve, anali kulengeza uthenga wouziridwa wosavuta, wakuti: Mzinda wamphamvuwo uwonongedwa pakatha masiku 40. Komabe, zinthu zinasintha kwabasi. Anthu a ku Nineve analapa.—Yona, chaputala 3.

18 Tingaphunzire zambiri poyerekeza mmene Yehova anachitira ndi mmene anachitira Yona zinthu zitasintha chomwechi. Pachochitikachi, Yehova anasintha mogwirizana ndi zochitikazo; anadzichititsa kukhala Wokhululukira machimo m’malo mokhala munthu “wankhondo.” * (Eksodo 15:3) Koma Yona sanathe kusintha ndipo analibe chifundo. M’malo mokhala wololera monga Yehova, iye anachita mofanana ndi sitima yonyamula katundu ija kapena yonyamula mafuta imene tinatchula ijanso. Anali atalengeza chiwonongeko, choncho iwo anayenera kuwonongeka basi! Komabe, moleza mtima Yehova anaphunzitsa mneneri wake wosaleza mtimayu phunziro losaiwalika la kukhala wololera ndi wachifundo.—Yona, chaputala 4.

Yehova ndi wololera ndipo amamvetsetsa zimene sitingathe kuchita

19. (a) N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yehova ndi wololera pa zimene amatiyembekeza kuchita? (b) Kodi Miyambo 19:17 ikusonyeza motani kuti Yehova ndi Mbuye ‘wabwino ndi wololera’ ndiponso wodzichepetsa kwambiri?

19 Pomaliza, Yehova ndi wololera m’zimene amatiyembekezera kuchita. Mfumu Davide anati: “Adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.” (Salmo 103:14) Yehova amamvetsa  bwino zimene sitingathe kuchita ndiponso kupanda ungwiro kwathu kuposa mmene eni akefe timachitira. Satiyembekeza kuchita zimene sitingathe kuchita. Baibulo limasiyanitsa anthu amene ali ambuye “abwino ndi aulere [“ololera,” NW]” ndi aja amene ali “aukali.” (1 Petro 2:18) Kodi Yehova ndi Mbuye wotani? Taonani zimene Miyambo 19:17 imanena: “Wochitira waumphawi chifundo abwereka Yehova.” Ndithudi, ndi mbuye wabwino ndi wololera yekha amene angamazindikire kalikonse kamene mwachifundo ena akuchitira aumphaŵi. Kuposa pamenepo, lembali likupereka malingaliro akuti Mlengi wa chilengedwe chonse amadziona kuti afunika kuchitira zabwino anthu wamba amene amachita zachifundo zimenezo! Kumeneku ndi kudzichepetsa kwabasi.

20. Kodi n’chiyani chikutsimikizira kuti Yehova amamva ndi kuyankha mapemphero athu?

20 Lerolinonso Yehova amachita ndi atumiki ake mofatsa ndi mololera chomwecho. Pamene tikupemphera ndi chikhulupiriro, iye amatimvera. Ndipo ngakhale kuti satumiza angelo opereka mauthenga kukalankhula nafe, tisalingalire kuti iye sayankha mapemphero athu. Kumbukirani kuti pamene mtumwi Paulo anapempha okhulupirira anzake kuti ‘amupempherere’ kuti amasulidwe m’ndende, ananenanso kuti: “Kuti kubwera kwanga kwa inu kufulumidwe.” (Ahebri 13:18, 19) Motero mapemphero athu akhoza kuchititsa Yehova kuchita zinthu zimene mwina sakanazichita motero!—Yakobo 5:16.

21. Kodi sitiyenera kulingalira chiyani pa kudzichepetsa kwa Yehova, koma m’malo mwake, tiyenera kuzindikira chiyani?

 21 Eya, Yehova posonyeza kudzichepetsa mwa kukhala wofatsa, wofunitsitsa kumvetsera, woleza mtima, ndi wololera sindiye kuti amanyalanyaza mfundo zake zachikhalidwe zolungama. Atsogoleri a Matchalitchi Achikristu angaganize kuti ndi wololera pokanda m’makutu mwa nkhosa zawo mwa kusukulutsa miyezo ya makhalidwe ya Yehova. (2 Timoteo 4:3) Koma chizoloŵezi cha anthu chovomereza zinthu n’cholinga chofuna kuyanjana ndi ena, sindiko kulolera kumene Mulungu amachita. Yehova ndi woyera; miyezo yake yolungama sadzaiipitsa konse. (Levitiko 11:44) Motero tiyeni tizikonda kulolera kwa Yehova chifukwa cha zimene kumatanthauza, umboni wakuti ndi wodzichepetsa. Kodi simukusangalala kwambiri poganiza kuti Yehova Mulungu, Munthu wanzeru kwambiri m’chilengedwe chonse, alinso wodzichepetsa kwambiri? Ndi chinthutu chokondweretsa kwambiri kuyandikana ndi Mulungu wochititsa mantha koma yemwe ali wofatsa, woleza mtima, ndi wololera ameneyu!

^ ndime 3 Alembi akale, kapena kuti Asoferimu, anasintha vesili kuti lizimveka kuti Yeremiya, osati, Yehova, ndiye amene anali kuŵerama. Mwachionekere iwo ankaganiza kuti n’kosayenera kunena kuti Mulungu angachite chinthu chodzichepetsa chimenecho. Chotsatira chake n’chakuti mabaibulo ambiri amaphonya mfundo imene ili mu vesi losangalatsa limeneli. Komabe, Baibulo la The New English Bible limanena molondola kuti Yeremiya anali kuuza Mulungu kuti: “Kumbukirani, O kumbukirani, ndi kundiŵeramira ine.”

^ ndime 7 Mabaibulo ena amati “kudzichepetsa kumene kumabwera ndi nzeru” ndiponso “kudekha kumene kumadziŵikitsa nzeru.”

^ ndime 12 N’zochititsa chidwi kuona kuti Baibulo limasiyanitsa kuleza mtima ndi kudzikuza. (Mlaliki 7:8) Kuleza mtima kwa Yehova kumatipatsa umboni winanso wakuti ndi wodzichepetsa.—2 Petro 3:9.

^ ndime 18 Pa Salmo 86:5, Yehova akunenedwa kuti ndi “wabwino, ndi wokhululukira.” Pamene Salmo limeneli linatembenuzidwira mu Chigiriki, mawu akuti “wokhululukira” anawatembenuza kuti e·pi·ei·kes′, kapena kuti “wololera.”