1-3. (a) Kodi Solomo anaonetsa motani nzeru zapadera pamene anathetsa mkangano wolimbirana mwana? (b) Kodi Yehova amalonjeza kutipatsa chiyani, nanga ndi mafunso otani amene akubuka?

UNALI mlandu wovuta kwambiri, akazi aŵiri anali kukanganirana mwana. Akaziwo anali kukhala m’nyumba imodzi, ndipo onse anabereka ana aamuna m’masiku oyandikana. Kenaka khanda limodzi linapezeka litafa. Ndiyeno akaziwo anali kulimbirana mwana wamoyoyo. * Panalibe anthu ena apadera ochitira umboni zimene zinachitika. Nkhaniyi mwina inakambidwapo m’khoti laling’ono n’kulephera kuithetsa. Pomaliza pake, mkanganowo anapita nawo kwa Solomo, mfumu ya Israyeli. Kodi iye anamudziŵa mayi wake weniweni wa mwanayo?

2 Atamvetsera kukangana kwa akaziwo kwa kanthaŵi, Solomo anaitanitsa chimpeni. Ndiyeno, momveka wotsimikizadi, analamula kuti mwanayo amudule pakati ndipo mkazi aliyense amupatse mbali imodzi. Nthaŵi yomweyo mayi wake weniweni anachonderera mfumuyo kuti ipatse khandalo, mwana wake wokondedwa, mkazi winayo. Koma mkazi winayo anali kuumirira kuti mwanayo amudule pakati basi. Tsopano Solomo anadziŵa zoona zake. Iye anali kudziŵa mmene mayi amachitira chifundo ndi mwana wake wobereka yekha, ndipo anagwiritsa ntchito zimenezi pothetsa mkanganowu. Talingalirani mmene mayi wake wa mwanayu anamvera bwino mu mtima mwake Solomo atamupatsa khandalo n’kunena kuti: “Uyo ndiye amake.”—1 Mafumu 3:16-27.

3 Pamenepa panagonatu nzeru zapadera, kodi si choncho? Anthu atamva mmene Solomo anaweruzira mlanduwo, anagwidwa  ndi mantha, “pokhala anaona kuti nzeru ya Mulungu inali mwa iye.” Inde, nzeru za Solomo zinali mphatso yochokera kwa Mulungu. Yehova anamupatsa “mtima wanzeru ndi wakuzindikira.” (1 Mafumu 3:12, 28) Koma bwanji ifeyo? Kodi ifenso tikhoza kulandira nzeru zochokera kwa Mulungu? Inde, chifukwa mouziridwa ndi Mulungu, Solomo analemba kuti: “Yehova apatsa nzeru.” (Miyambo 2:6) Yehova amalonjeza kupereka nzeru—luso logwiritsa ntchito bwino zimene ukudziŵa, kumvetsetsa kwako zinthu, ndi kuzindikira—kwa amene akuifunafuna moona mtima. Kodi nzeru yochokera kumwamba tingaipeze bwanji? Ndipo kodi tingatani kuti izigwira ntchito m’moyo wathu?

“Tatenga Nzeru”—Motani?

4-7. Tchulani zinthu zinayi zofunika kuti munthu atenge nzeru.

4 Kodi tiyenera kukhala ndi mitu yogwira zinthu msanga kapena kukhala ophunzira kwambiri kuti tilandire nzeru za Mulungu? Ayi. Yehova ndi wofunitsitsa kutigaŵira nzeru zake mosasamala kanthu kuti tili ndi moyo wotani kapena tinaphunzira motani. (1 Akorinto 1:26-29) Komano tifunika kuyamba ndife kuchitapo kanthu, chifukwa Baibulo limatilimbikitsa kuti ‘titenge nzeru.’ (Miyambo 4:7) Kodi zimenezi tingazichite bwanji?

5 Choyamba, tifunika kuopa Mulungu. “Chiyambi cha nzeru ndicho [“nzeru zimayamba mwa,” The New English Bible] kuopa Yehova,” imatero Miyambo 9:10. Kuopa Mulungu ndiko maziko a nzeru zenizeni. Chifukwa chiyani? Kumbukirani kuti nzeru zimaphatikizapo luso logwiritsa ntchito bwino zimene munthu akudziŵa. Kuopa Mulungu si kuunthama pamaso pake mwamantha, koma kumuŵeramira momupatsa ulemu, momulemekeza, ndi momudalira. Kuopa kotereku n’kwabwino ndipo n’kolimbikitsa kwambiri. Kumatilimbikitsa kugwirizanitsa moyo wathu ndi zimene tikudziŵa za chifuno cha Mulungu ndiponso njira zake. Ndi njira yokhayi yanzeru imene tingatsatire, palibenso ina, chifukwa nthaŵi zonse miyezo ya Yehova imabweretsa mapindu abwino kwambiri kwa amene amaitsatira.

6 Chachiŵiri, tiyenera kukhala odzichepetsa. Munthu sangakhale ndi nzeru za Mulungu ngati si wodzichepetsa. (Miyambo 11:2) N’chifukwa chiyani zili choncho? Tikakhala odzichepetsa,  timakhala ofunitsitsa kuvomera kuti sitidziŵa zinthu zonse, kuti zoganiza zathu si nthaŵi zonse pamene zimakhala zolondola, ndi kuti timafunika kudziŵa mmene Yehova amaonera nkhanizo. Yehova ‘amakaniza odzikuza,’ koma amasangalatsidwa kupatsa nzeru anthu a mtima wodzichepetsa.—Yakobo 4:6.

Kuti titenge nzeru za Mulungu, tiyenera kuchita khama kuzifunafuna

7 Chofunika chachitatu ndi kuphunzira Mawu olembedwa a Mulungu. Nzeru za Yehova zinaululidwa m’Mawu ake. Kuti titenge nzeru imeneyo, tiyenera kuchita khama kuifunafuna. (Miyambo 2:1-5) Chofunika chachinayi ndi pemphero. Ngati moona mtima tipempha nzeru kwa Mulungu, iye adzatipatsa mosaumira. (Yakobo 1:5) Iye adzatiyankha pamene tipempha thandizo la mzimu wake. Ndipo mzimu wake ungatithandize kupeza chuma chimene chili m’Mawu ake chomwe chingatithandize kuthetsa mavuto, kupeŵa ngozi, ndi kusankha zochita zanzeru.—Luka 11:13.

8. Ngati tatengadi nzeru za Mulungu, kodi zidzaoneka motani?

8 Monga tinaonera m’Mutu 17, nzeru za Yehova n’zothandiza. Motero ngati tatengadi nzeru za Mulungu zidzaonekera mu zimene timachita. Wophunzira Yakobo anafotokoza zipatso za nzeru za Mulungu pamene analemba kuti: “Nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere [“yololera,” NW], yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankhu, yosadzikometsera pamaso.” (Yakobo 3:17) Pamene tikukambirana mbali iliyonse ya mbali za nzeru za Mulungu zimenezi, tingadzifunse kuti, ‘Kodi nzeru yochokera kumwamba ikugwira ntchito m’moyo wanga?’

“Yoyera, Nikhalanso Yamtendere”

9. Kodi kukhala woyera kumatanthauzanji, ndipo n’chifukwa chiyani kuli koyenera kuti chiyero ndilo khalidwe loyamba kutchulidwa la nzeru?

9 “Iyamba kukhala yoyera.” Kukhala woyera kumatanthauza kukhala waudongo ndi wosaipitsidwa, osati kunja kokha komanso m’kati. Baibulo limati nzeru imaloŵa mu mtima, komatu nzeru yakumwamba singaloŵe mu mtima umene waipitsidwa ndi maganizo oipa, zikhumbo zoipa, ndi zolinga zoipa. (Miyambo 2:10; Mateyu 15:19, 20) Komabe, ngati mtima wathu uli woyera, ndiko kuti monga mmene kungakhalire kotheka kwa anthu  opanda ungwiro, ‘tidzasiyana nacho choipa n’kuchita chokoma.’ (Salmo 37:27; Miyambo 3:7) Kodi si koyenera kuti chiyero ndilo khalidwe loyamba kutchulidwa la nzeru? Indedi, ngati sitili oyera mwamakhalidwe ndi mwauzimu, kodi makhalidwe enawo a nzeru yochokera kumwamba tingawasonyeze motani?

10, 11. (a) Kodi n’chifukwa chiyani n’kofunika kuti tizikhala amtendere? (b) Ngati muona kuti mwakhumudwitsa wolambira mnzanu, kodi mungaonetse motani kuti ndinu wokhazikitsa mtendere? (Onaninso mawu a m’munsi.)

10 “Nikhalanso yamtendere.” Nzeru yakumwamba imatichititsa kukhala a mtendere, womwe ndi chipatso cha mzimu wa Mulungu. (Agalatiya 5:22) Timayesetsa kupeŵa kusokoneza ‘chomangira cha mtendere’ chimene chimagwirizanitsa anthu a Yehova. (Aefeso 4:3) Timachitanso khama kubwezeretsa mtendere pamene wasokonezeka. N’chifukwa chiyani zimenezi n’zofunika? Baibulo limati: “Khalani mumtendere; ndipo Mulungu wa chikondi ndi mtendere akhale pamodzi ndi inu.” (2 Akorinto 13:11) Motero malinga ngati tipitiriza kukhala mwamtendere, Mulungu wa mtendere adzakhala pamodzi nafe. Mmene timachitira zinthu ndi olambira anzathu zimakhudza mwachindunji ubwenzi wathu ndi Yehova. Kodi tingaonetse motani kuti timakhazikitsa mtendere? Lingalirani chitsanzo ichi.

11 Kodi muyenera kuchitanji ngati mwaona kuti mwakhumudwitsa wolambira mnzanu? Yesu anati: “Chifukwa chake ngati uli kupereka mtulo wako pa guwa la nsembe, ndipo pomwepo ukakumbukira kuti mbale wako ali ndi kanthu pa iwe, usiye pomwepo mtulo wako kuguwako, nuchoke, nuyambe kuyanjana [“kukhazikitsa mtendere wako,” NW] ndi mbale wako, ndipo pamenepo idza nupereke mtulo wako.” (Mateyu 5:23, 24) Mungagwiritse ntchito uphungu umenewu mwa kuyamba inuyo kupita kukaonana ndi mbale wanuyo. Ndi cholinga chotani? Kuti ‘mukakhazikitse mtendere wanu’ ndi iye. * Kuti zimenezi  zitheke mungafunike kuvomera, osati kukana, kuti nkhaniyo ikumupweteka mumtima. Ngati mulankhula naye ndi cholinga chobwezeretsa mtendere ndi kukhalabe ndi maganizo omwewo, ndithudi mukhoza kuthetsa kusamvana kulikonse komwe kungakhalepo, mukhoza kupepesana, ndi kukhululukirana. Pamene muyamba ndinuyo kuchitapo kanthu kuti mukhazikitse mtendere, mumasonyeza kuti nzeru za Mulungu zikukutsogolerani.

“Yololera, Yomvera Bwino”

12, 13. (a) Kodi mawu amene atembenuzidwa kuti “kulolera” pa Yakobo 3:17, NW, amatanthauza chiyani? (b) Kodi tingaonetse motani kuti ndife ololera?

12 “Yololera.” Kodi kukhala wololera kumatanthauzanji? Malinga n’kunena kwa akatswiri a Baibulo, mawu achigiriki oyambirira omwe anatembenuzidwa kuti “yaulere [“yololera,” NW]” pa Yakobo 3:17 ndi ovuta kutembenuza.  Otembenuza ena agwiritsa ntchito mawu monga “yodekha,” “yodziletsa,” ndi “yoganizira ena.” Mawu achigirikiwo kwenikweni amatanthauza kuti “kuvomereza.” Kodi tingaonetse motani kuti mbali imeneyi ya nzeru yochokera kumwamba ikugwira ntchito mwa ife?

13 “Kufatsa [“kulolera,” NW] kwanu kuzindikirike ndi anthu onse,” amatero Afilipi 4:5. Baibulo lina limati: “Khalani ndi mbiri yakuti ndinu wololera.” (The New Testament in Modern English, lotembenuzidwa ndi J. B. Phillips) Taonani kuti nkhani sili kwenikweni pa mmene ife timadzionera koma pa mmene ena amationera, kuti timadziŵika ndi mbiri yotani. Munthu wololera sangoumirira pa chimene lamulo likunena kapenanso kufuna kuti zinthu zichitike mmene iye akufunira basi. Koma amakhala wofunitsitsa kumva malingaliro a ena ndipo ngati kuli koyenera amavomereza zimene enawo akufuna. Pochita zinthu ndi anthu ena amakhala wodekha osati waukali kapena wankhanza. Ngakhale kuti zimenezi n’zofunika kwambiri kwa Akristu onse, zili zofunika mwapadera kwa akulu. Anthu amakopeka ndi munthu wodekha, ndipo akulu odekha savuta kulankhula nawo. (1 Atesalonika 2:7, 8) Ndi bwino kudzifunsa kuti, ‘Kodi ine anthu amandiona kuti ndine wolingalira ena, kuti ndimavomereza malingaliro a ena, kuti ndine wodekha?’

14. Kodi tingaonetse motani kuti ndife ‘omvera bwino’?

14 “Yomvera bwino.” Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “yomvera bwino” amapezeka malo okhawa m’Malemba Achigiriki Achikristu. Malinga n’kunena kwa katswiri wina, mawu ameneŵa “kaŵirikaŵiri amagwiritsidwa ntchito ndi anthu ankhondo.” Amapereka lingaliro la “kukopeka mosavuta” ndiponso “kugonjera.” Munthu amene nzeru yochokera kumwamba ikumutsogolera amagonjera mosavuta ku zimene Malemba akunena. Sadziŵika monga munthu womva zake zokha yemwe safuna kumva mfundo zotsutsana ndi zake. Koma amasintha mofulumira akapatsidwa umboni womveka bwino wa m’Malemba wakuti akuchita zinthu zolakwika kapena kuti wasankha zinthu zolakwika. Kodi ndimo mmene ena amakudziŵirani inuyo?

 “Yodzala Chifundo ndi Zipatso Zabwino”

15. Kodi chifundo n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani kuli koyenera kuti “chifundo” ndi “zipatso zabwino” zikutchulidwira pamodzi pa Yakobo 3:17?

15 “Yodzala chifundo ndi zipatso zabwino.” * Chifundo ndi mbali yofunika kwambiri ya nzeru yochokera kumwamba, chifukwa nzeru yoteroyo ikunenedwa kuti ndi “yodzala chifundo.” Taonani kuti “chifundo” ndi “zipatso zabwino” zatchulidwira pamodzi. Zimenezi n’zoyenera, chifukwa m’Baibulo mawu akuti chifundo kaŵirikaŵiri amanena za kuthandiza ena powadera nkhaŵa, kapena kuti kuwamvera chisoni kumene kumabweretsa zipatso zochuluka za zochita zokoma mtima. Buku lina limati chifundo ndi “kumvera chisoni munthu wina amene zinthu zoipa zamuchitikira ndi kuyesa kuchitapo kanthu pa vutolo.” Motero munthu amene ali ndi nzeru ya Mulungu sakhala wopanda nsangala, wosasamala za ena, kapenanso sangokhala wophunzira kwambiri chabe. Koma iye amakhala waubwenzi, amakhudzika mtima, ndipo amazindikira mofulumira zimene zikuchitikira ena. Kodi tingasonyeze motani kuti ndife odzala chifundo?

16, 17. (a) Kuwonjezera pa kukonda Mulungu, kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kugwira nawo ntchito yolalikira, ndipo n’chifukwa chiyani? (b) Kodi ndi m’njira zotani mmene tingasonyezere kuti ndife odzala chifundo?

16 Njira yofunika kwambiri ndiyo kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. Kodi n’chiyani chimatilimbikitsa kugwira ntchito imeneyi? Makamaka n’chifukwa chakuti timakonda Mulungu. Komanso timagwira ntchitoyi chifukwa timachitira anthu ena chifundo, kapena kuti chisoni. (Mateyu 22:37-39) Lerolino anthu ambiri ndi “okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.” (Mateyu 9:36) Abusa achipembedzo onyenga awanyalanyaza anthuŵa ndipo awachititsa khungu mwauzimu. Chotsatira chake n’chakuti sadziŵa kuti Mawu a Mulungu akhoza kuwatsogolera mwanzeru. Sakudziŵanso zinthu zabwino zimene Ufumu udzabweretsa padzikoli posachedwapa. Motero pamene tilingalira zosoŵa zauzimu za anthu amene tikukhala nawo, timawamvera chisoni mu mtima  mwathu, zomwe zimatilimbikitsa kuchita chilichonse chimene tingathe kuti tiwauze cholinga chachikondi cha Yehova.

Pamene tichitira ena chifundo, kapena kuti chisoni, timaonetsa “nzeru yochokera kumwamba”

17 Kodi ndi m’njira zina ziti mmene tingasonyezere kuti ndife odzala chifundo? Kumbukirani fanizo la Yesu la Msamariya amene anapeza munthu wapaulendo atagona m’mbali mwa msewu, atamubera ndi kumumenya. Pomva chisoni, Msamariyayo ‘anamuchitira chifundo’ namumanga mabala ndi kumusamalira. (Luka 10:29-37) Kodi zimenezi sizikusonyeza kuti chifundo chimaphatikizapo kuthandiza anthu amene akuvutika? Baibulo limatiuza kuti ‘tizichitira onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Taonani zina zimene tingachite. Wokhulupirira mnzathu wokalamba angafunike kumuthandiza kuti apite ku misonkhano yachikristu ndi kubwerako. Mkazi wamasiye mu mpingo angafunike kumuthandiza kukonza nyumba yake. (Yakobo 1:27) Munthu amene walefuka angafune “mawu abwino” oti amulimbikitse. (Miyambo 12:25) Pamene tisonyeza chifundo m’njira zoterozo, timapereka umboni wakuti nzeru yochokera kumwamba ikugwira ntchito mwa ife.

“Yopanda Tsankhu, Yosadzikometsera Pamaso”

18. Ngati nzeru yochokera kumwamba ikutitsogolera, kodi tiyenera kuyesetsa kuchotsa chiyani m’mitima yathu, ndipo n’chifukwa chiyani?

18 “Yopanda tsankhu.” Nzeru za Mulungu zimapatsa mphamvu yopeŵa kusankhana mitundu ndi kunyadira mtundu wako. Ngati nzeru zoterozo zikutitsogolera, timayesetsa kuthetsa m’mitima mwathu chizoloŵezi chilichonse chokondera anthu ena. (Yakobo 2:9) Sitichitira anthu ena zabwino chifukwa cha kuphunzira kwawo, kupeza bwino kwawo, kapena maudindo awo mumpingo. Ndiponso sitinyoza wolambira mnzathu aliyense, kaya aoneke kuti ndi wosauka motani. Ngati anthu amenewo Yehova wawapatsa chikondi chake, ndithudi iwo amayenera chikondi chathu.

19, 20. (a) Kodi mawu achigiriki omwe anenedwa kuti “kudzionetsera pamaso” anayambira pati? (b) Kodi timasonyeza motani kuti ‘timakonda abale ndi chikondi chosanyenga,’ nanga n’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika?

19 “Yosadzikometsera pamaso.” Mawu achigiriki omwe anenedwa kuti “kudzikometsera pamaso” anganene za “munthu amene  anachita nawo seŵero.” M’nthaŵi zakale, Agiriki ndi Aroma pochita maseŵero anali kuvala zinyawu. Motero mawu achigiriki a “kudzikometsera pamaso,” kapena kuti chinyengo, anayamba kugwiritsidwa ntchito kwa munthu amene ankachita zinthu monyengezera, kapena amene anali kumata ena phula m’maso. Mbali imeneyi ya nzeru za Mulungu iyenera kukhudza osati kokha mmene timachitira zinthu ndi olambira anzathu, koma zimenenso timawaganizira.

20 Mtumwi Petro ananena kuti chifukwa cha ‘kumvera kwathu choonadi,’ tiyenera ‘kukonda abale ndi chikondi chosanyenga.’ (1 Petro 1:22) Inde, sitiyenera kukonda abale athu kungoti tidzionetsere. Sitivala chinyawu kapena kuchita zinthu n’cholinga chonamiza ena. Tiyenera kuwakondadi zenizeni, kuchokera pansi pamtima. Ngati titero ndiye kuti okhulupirira anzathu adzatidalira, chifukwa adzadziŵa kuti tilidi mmene timaonekera. Kukhala woona mtima koteroko kumachititsa Akristu kukhala omasukirana ndi kumauzana zoona, ndiponso kumathandiza kuti anthu mumpingo azidalirana.

 “Sunga Nzeru Yeniyeni”

21, 22. (a) Kodi Solomo analephera motani kusunga nzeru? (b) Kodi nzeru tingazisunge bwanji, ndipo kodi tidzapindula motani pochita zimenezo?

21 Kukhala ndi nzeru zaumulungu ndi mphatso yochokera kwa Yehova, mphatso imene tiyenera kuiteteza. Solomo anati: “Mwananga, . . . sunga nzeru yeniyeni ndi kulingalira.” (Miyambo 3:21) N’zomvetsa chisoni kuti iye Solomo analephera kuchita zimenezo. Anali wanzeru kwa nthaŵi yonse imene anali ndi mtima womvera. Koma pamapeto pake akazi ake ambirimbiri achilendo anapatutsa mtima wake pa kulambira koyera kwa Yehova. (1 Mafumu 11:1-8) Zimene zinachitikira Solomo zikutipatsa chitsanzo chakuti zinthu zimene timadziŵa zimakhala zosapindulitsa ngati sitizigwiritsa ntchito bwino.

22 Kodi nzeru yeniyeni tingaisunge bwanji? Tiyenera kuŵerenga Baibulo nthaŵi zonse limodzi ndi mabuku ofotokoza za m’Baibulo okonzedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Komabe sitiyenera kungoŵerenga chabe mabukuŵa, tiyenera kuyesetsa kugwiritsa ntchito zimene tikuphunzirazo. Tili ndi zifukwa zokwana zogwiritsira ntchito nzeru za Mulungu. Tidzakhala ndi moyo wabwino tsopano lino. Zidzatithandiza ‘kugwira moyo weniweniwo,’ moyo m’dziko latsopano la Mulungu. (1 Timoteo 6:19) Ndipo chofunika kwambiri n’chakuti, kukulitsa kukhala ndi nzeru zochokera kumwamba kumatiyandikizitsa ku gwero la nzeru zonse, Yehova Mulungu.

^ ndime 1 Malinga n’kunena kwa 1 Mafumu 3:16, akazi aŵiriwo anali adama, kapena kuti mahule. Buku lotchedwa Insight on the Scriptures limati: “Akazi ameneŵa, kaya anali akazi achiyuda kapena anali akazi achilendo, zomwe zingakhale zotheka kwambiri, mwina anali mahule m’lingaliro lakuti anachita dama, osati kuti ankagulitsa matupi awo.”—Lofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.

^ ndime 11 Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “kuyanjana,” kapena kuti “kukhazikitsa mtendere wanu” mu Baibulo la New World Translation, akuchokera ku verebu lotanthauza kuti “‘kuchititsa kusintha, kusinthana,’ ndipo mwa kutero ‘kuyanjanitsa.’” Choncho cholinga chanu n’chakuti zinthu zisinthe, kuti muchotse malingaliro onyansidwa nanu omwe ali mu mtima mwa wolakwiridwayo, ngati zingatheke kutero.—Aroma 12:18.

^ ndime 15 Baibulo lina limatembenuza mawu ameneŵa kuti “yodzala chisoni ndi ntchito zabwino.”—A Translation in the Language of the People, lotembenuzidwa ndi Charles B. Williams.