1, 2. Kodi ndi “kalata” iti imene Yehova anatilembera, ndipo n’chifukwa chiyani?

KODI mukukumbukira nthaŵi yomalizira imene munalandira kalata yochokera kwa munthu amene mumam’konda yemwe amakhala kutali? Pali zinthu zochepa zimene zimatisangalatsa mofanana ndi momwe imatisangalatsira kalata yokhala ndi mawu akukhosi a munthu amene timam’konda. Timasangalala kumva za mmene akukhalira, zimene zikumuchitikira, ndiponso zimene akuganiza kuti achite. Kulankhulana koteroko kumachititsa anthu okondana kukhala oyandikana kwambiri, ngakhale kuti wina angakhale ali kutali.

2 Motero, n’chiyani chikanatisangalatsa kwambiri kuposa kulandira uthenga wolembedwa wochokera kwa Mulungu amene timam’konda? Tingatero kuti Yehova anatilembera “kalata,” yomwe ndi Mawu ake, Baibulo. M’mawu akewo amatiuza amene iye ali, zinthu zimene wachita, zimene akufuna kuchita, ndi zina zambiri. Yehova watipatsa Mawu ake chifukwa amafuna kuti tiyandikane naye. Mulungu wathu wanzeru zonse anasankha njira yabwino kwambiri yolankhulirana nafe. Mmene Baibulo linalembedwera ndiponso zimene zili m’Baibulomo, zimasonyeza nzeru zosayerekezeka.

N’chifukwa Chiyani Mawu Olembedwa Ali Abwino?

3. Kodi Yehova anapereka Chilamulo kwa Mose m’njira yotani?

3 Ena angalingalire kuti, ‘N’chifukwa chiyani Yehova sanagwiritse ntchito njira yochititsa chidwi kwambiri—mwachitsanzo, mawu omveka kuchokera kumwamba—polankhula ndi anthu?’ Inde, panthaŵi zina Yehova analankhula kuchokera kumwamba kudzera mwa angelo omuimira. Mwachitsanzo, anachita zimenezi pamene anali kupereka Chilamulo kwa mtundu Israyeli. (Agalatiya 3:19) Mawu amene anachoka kumwambawo anali ochititsa mantha kwambiri moti Aisrayeli oopsedwawo anapempha kuti Yehova asalankhule nawo m’njira imeneyi koma kudzera mwa Mose. (Eksodo 20:18-20) Motero, Mose anangouzidwa ndi pakamwa  mawu onse a m’Chilamulo chomwe chinali ndi malamulo pafupifupi 600.

4. Fotokozani chifukwa chake kuuza ena mawu a pakamwa sikukanakhala njira yodalirika yoperekera malamulo a Mulungu kwa anthu a mibadwo yonse.

4 Koma bwanji ngati Chilamulocho chikanati chisalembedwe? Kodi Mose akanatha kukumbukira mwatsatanetsatane mawu onse a m’Chilamulo chokhala ndi mfundo zambirimbiricho, n’kuwafotokoza mosaphonya ku mtundu wonsewo? Nanga bwanji mibadwo ya m’tsogolo? Kodi iwo akanangodalira zowauza? Imeneyo sikanakhala njira yodalirika yoperekera malamulo a Mulungu ku mibadwo yonse ya anthu mpaka lerolino. Talingalirani zimene zikanachitika ngati mukanati mufotokoze nkhani inayake kwa anthu amene ali pa mzere wautali mwa kuuza munthu woyambirira. Ndiye iyeyo afotokozere mnzake, nayenso afotokozere wina, n’kumangotero mpaka kukafika kwa munthu womalizira. Zimene munthu womalizirayo adzamva zidzasiyana kwambiri ndi mmene nkhaniyo inalili poyamba. Panalibe vuto limenelo pa mawu a Chilamulo cha Mulungu.

5, 6. Kodi Yehova analangiza Mose kuchitanji ndi mawu Ake, nanga n’chifukwa chiyani kukhala ndi Mawu a Yehova olembedwa kuli kotipindulitsa?

5 Mwanzeru Yehova anasankha kuti mawu ake alembedwe. Analangiza Mose kuti: “Ulembere mawu aŵa; pakuti monga mwa mawu aŵa ndapangana ndi iwe ndi Israyeli.” (Eksodo 34:27) Ndimo mmene nyengo yolemba Baibulo inayambira, m’chaka cha 1513 B.C.E. Kwa zaka 1,610 zotsatira, Yehova ‘analankhula m’manenedwe ambiri ndi mosiyanasiyana’ kwa anthu pafupifupi 40 amene kenako analemba Baibulo. (Ahebri 1:1) M’kati mwa nthaŵi imeneyo, alembi odzipereka anali kukopera zolembedwazo mosamalitsa kwambiri pofuna kukhala ndi makope olondola bwino a Malemba, ndi kuti Malembawo asungike.—Ezara 7:6; Salmo 45:1.

6 Ndithudi Yehova watidalitsa polankhula nafe ndi mawu olembedwa. Kodi munalandirapo kalata yomwe inakusangalatsani kwambiri, mwinamwake chifukwa chakuti inakulimbikitsani kwambiri, kotero kuti munaisunga n’kumaiŵerenga mobwerezabwereza? “Kalata” imene Yehova anatilembera ilinso choncho. Chifukwa chakuti Yehova analemba mawu ake, timawaŵerenga nthaŵi  zonse ndi kumasinkhasinkha pa zimene mawuwo amanena. (Salmo 1:2) Tingalandire “chitonthozo cha malembo” nthaŵi iliyonse pamene tikuchifuna.—Aroma 15:4.

N’chifukwa Chiyani Anagwiritsa Ntchito Anthu Polemba?

7. Kodi nzeru za Yehova zikuonekera motani pa kugwiritsa ntchito kwake anthu kulemba Mawu ake?

7 Mwa nzeru zake, Yehova anagwiritsa ntchito anthu kuti alembe Mawu ake. Talingalirani izi: Ngati Yehova akanagwiritsa ntchito angelo kuti alembe Baibulo, kodi zolemba zawo zikanakhala zogwira mtima ngati mmene zilili panopo? Zoonadi, angelo akanalongosola Yehova mwapamwamba monga mmene iwo amamuonera, akananena za mmene iwo alili odzipereka kwa iye, ndipo akanasimba za atumiki aumunthu okhulupirika a Mulungu. Koma kodi tikanathadi kuzimvetsa zimenezi kuchokera pa kaonedwe ka zolengedwa zauzimu zangwiro, zomwe zimadziŵa zinthu zochuluka, zaona zinthu zambiri, ndipo zili ndi mphamvu kwambiri kuposa ife?—Ahebri 2:6, 7.

“Lemba lililonse adaliuzira Mulungu”

8. Kodi anthu olemba Baibulo anawalola m’njira yotani kugwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza? (Onaninso mawu a m’munsi.)

8 Mwa kugwiritsa ntchito anthu polemba Mawu ake, Yehova anatipatsadi zimene timafunika, buku ‘louziridwa ndi Mulungu’ koma lofotokozabe zinthu monga mmene anthu amafotokozera. (2 Timoteo 3:16) Kodi zimenezi anazichita bwanji? M’nkhani zambiri, n’zachionekere kuti analola anthu olembawo kugwiritsa ntchito luso lawo la kuganiza posankha “mawu okondweretsa, ndi zolemba zowongoka ngakhale mawu oona.” (Mlaliki 12:10, 11) Ndicho chifukwa chake nkhani za m’Baibulo zinalembedwa mosiyanasiyana; zimasonyeza moyo ndi umunthu wa wolemba aliyense. * Komatu, anthu ameneŵa “analankhula mawu ochokera kwa Mulungu atagwidwa ndi mzimu woyera.” (2 Petro 1:21, NW) Motero, pomalizira pake tinakhaladi ndi “mawu a Mulungu.”—1 Atesalonika 2:13.

9, 10. N’chifukwa chiyani kugwiritsa ntchito anthu kulemba Baibulo kunalipangitsa kukhala losangalatsa ndi lokopa?

 9 Baibulo ndi losangalatsa ndi lokopa kwambiri chifukwa choti linalembedwa ndi anthu. Olembawo anali anthu omva zinthu zomwe ife timamva. Pokhala opanda ungwiro, anakumana ndi ziyeso komanso mavuto ofanana ndi athu. Panthaŵi zina, mzimu wa Yehova unali kuwauzira kulemba mmene iwo anali kumvera mumtima mwawo ndiponso zimene analimbana nazo. (2 Akorinto 12:7-10) Motero polemba anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti nkhaniyo inali kuchitikira iwo, mawu amene mngelo sakanawalemba chomwecho.

10 Mwachitsanzo, talingalirani za Mfumu Davide ya Israyeli. Atachita machimo akuluakulu, Davide anapeka nyimbo mmene ananenamo mawu a kukhosi kwake, napempha kuti Mulungu amukhululukire. Iye analemba kuti: “Mundiyeretse kundichotsera choipa changa. Chifukwa ndazindikira machimo anga; ndipo choipa changa chili pamaso panga chikhalire. Onani, ndinabadwa m’mphulupulu: Ndipo mayi wanga anandilandira m’zoipa. Musanditaye kundichotsa pamaso panu; musandichotsere mzimu wanu woyera. Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa.” (Salmo 51:2, 3, 5, 11, 17) Kodi simukukhudzika mtima ndi mmene wolembayo anavutikira? Ndaninso wina, kupatulapo munthu wopanda ungwiro, yemwe akananena mawu otereŵa kuchokera pansi pamtima?

N’chifukwa Chiyani Lili Buku Lonena za Anthu?

11. Kodi ndi zitsanzo zotani za zochitika zenizeni m’moyo zimene zinalembedwa m’Baibulo kuti ‘zitilangize’?

11 Palinso chinthu china chimene chimapangitsa Baibulo kukhala lokopa. Nkhani zake zochuluka zimanena za anthu, anthu enieni, amene anatumikira Mulungu ndiponso amene sanam’tumikire. Timaŵerenga za zimene zinawachitikira, mavuto awo, ndi zimene zinawapatsa chimwemwe. Timaona zotsatira za zimene anasankha m’moyo wawo. Nkhani zimenezo zinalembedwa kuti ‘zitilangize.’ (Aroma 15:4) Mwa zitsanzo za zochitika zenizeni m’moyo zimenezi, Yehova amatiphunzitsa m’njira zogwira mtima. Taonani zitsanzo izi.

12. Kodi nkhani za m’Baibulo zosimba za anthu osakhulupirika zimatithandiza m’njira yotani?

 12 Baibulo limatiuza za anthu osakhulupirika, ngakhalenso oipa, ndi zomwe zinawachitikira. M’nkhani zoterezi timaona mmene munthu amasonyezera makhalidwe oipa, motero timamvetsa mosavuta. Mwachitsanzo, ndi lamulo lotani loletsa kusakhulupirika limene lingakhale lamphamvu kuposa chitsanzo cha zochitika zenizeni za Yudase yemwe anasonyeza kusakhulupirika pokonza chiwembu chopha Yesu? (Mateyu 26:14-16, 46-50; 27:3-10) Nkhani ngati zimenezi zimatikhudza mitima kwambiri, ndipo zimatithandiza kuzindikira makhalidwe onyansa n’kumawapewa.

13. Kodi Baibulo limatithandiza mwa njira yanji kumvetsetsa makhalidwe ofunikira?

13 Baibulo limasimbanso za atumiki a Mulungu ambiri okhulupirika. Timaŵerenga za kudzipereka kwawo ndi kukhulupirika kwawo. Timaona zitsanzo za anthu omwe anasonyeza makhalidwe amene tifunika kukhala nawo kuti tiyandikire kwa Mulungu. Mwachitsanzo, lingalirani za chikhulupiriro. Baibulo limatifotokozera kuti chikhulupiriro n’chiyani ndiponso limatiuza kuti n’chofunika kwambiri ngati tikufuna kukondweretsa Mulungu. (Ahebri 11:1, 6) Koma m’Baibulo mulinso zitsanzo zomveka bwino za anthu amene anasonyeza chikhulupiriro. Taganizirani chikhulupiriro chimene anasonyeza Abrahamu pamene anayesa kupereka Isake nsembe. (Genesis, chaputala 22; Ahebri 11:17-19) M’nkhani zoterezi, mawu akuti “chikhulupiriro” amakhala ndi tanthauzo lalikulu ndipo savuta kumva. N’chinthu chanzeru kwambiri kuti Yehova sangotilimbikitsa kukhala ndi makhalidwe ofunikira, koma kuti amatipatsanso zitsanzo za anthu amene anasonyeza makhalidwe amenewo!

14, 15. Kodi Baibulo limatiuza chiyani za mkazi wina amene anafika pa kachisi, ndipo nkhani imeneyi imatiphunzitsanji za Yehova?

14 Nkhani za zochitika zenizeni pa moyo wa anthu ena zomwe zili m’Baibulo kaŵirikaŵiri zimatiphunzitsa kanthu kena kokhudza umunthu wa Yehova. Talingalirani za mkazi yemwe timaŵerenga kuti Yesu anamuona pa kachisi. Yesu anakhala pansi pafupi ndi mosungiramo zopereka namapenya anthu akuponya zopereka zawo. Panafika anthu ambiri olemera ndipo anapereka “mwa zochuluka zawo.” Komano Yesu anayamba kupenyetsetsa mkazi wina wamasiye, waumphaŵi. Mkaziyu anapereka “tindalama tiŵiri tating’ono  tofa kakobiri kamodzi.” * Zinali ndalama zokhazi zimene anali nazo. Yesu, yemwe anasonyeza bwino kwambiri mmene Yehova amaonera zinthu, anati: “Mkazi wamasiye amene waumphaŵi anaponya zambiri koposa onse akuponya mosungiramo.” Malinga ndi mawu amenewo, mkaziyu anaponyamo zambiri kuposa kuphatikiza pamodzi za ena onse.—Marko 12:41-44; Luka 21:1-4; Yohane 8:28.

15 Kodi sizikusonyeza kenakake, kuti mwa anthu onse amene anabwera ku kachisi tsiku limenelo, mkazi wamasiye ameneyu ndiye anasankhidwa n’kutchulidwa m’Baibulo? Mwa chitsanzo chimenechi, Yehova amatiphunzitsa kuti iye ndi Mulungu amene amayamikira. Amasangalala kulandira zopereka zathu za moyo wonse, mosasamala kanthu kuti ndi zotani poziyerekeza ndi zimene ena angathe kupereka. Ndithudi Yehova anasankha njira yabwino zedi yotiphunzitsira choonadi chosangalatsa chimenechi!

Zimene M’Baibulo Mulibe

16, 17. Kodi nzeru za Yehova zimaonekanso motani mwa zimene anasankha kuti zisalembedwe m’Mawu ake?

16 Polemba kalata yopita kwa munthu amene mumam’konda, n’zosatheka kulembamo nkhani iliyonseyo imene mungakhale nayo. Motero mumasankha mwanzeru zoti mulembe. Mofananamo, Yehova anasankha kuti m’Mawu ake asimbemo za anthu ena ake ndi zochitika zina zake. Koma si nthaŵi zonse pamene Baibulo limalongosola chilichonse mwatsatanetsatane m’nkhani zimenezi. (Yohane 21:25) Mwachitsanzo, pamene Baibulo linena za chiweruzo cha Mulungu, zimene limafotokoza sizingayankhe funso lililonse limene tingakhale nalo. Nzeru za Yehova zimaonekanso mwa zimene anasankha kuti zisalembedwe m’Mawu ake. Motani?

17 Baibulo linalembedwa mwa njira imene imayesa zimene zili mu mtima mwathu. Ahebri 4:12 amati: “Mawu [kapena kuti, uthenga] a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita, ndi akuthwa koposa lupanga lakuthwa konsekonse, napyoza kufikira kugaŵira moyo  ndi mzimu . . . nazindikiritsa zolingirira ndi zitsimikizo za mtima.” Uthenga wa Baibulo umafika m’kati mwenimweni, umavumbula zimenedi timaganiza ndiponso zolinga zathu. Amene amaliŵerenga n’cholinga chofuna kulipeza zifukwa kaŵirikaŵiri amakhumudwa ndi nkhani zimene sizinena zambiri zowakhutiritsa. Anthu oterowo akhozanso kukayikira ngati Yehova alidi wachikondi, wanzeru, ndi wachilungamo.

18, 19. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kusokonezeka maganizo ngati nkhani inayake ya m’Baibulo ikudzutsa mafunso amene sitingapeze mayankho ake mwamsanga? (b) Kodi chimafunika n’chiyani kuti timvetsetse Mawu a Mulungu, nanga ndi motani mmene umenewu ulili umboni wa nzeru zosaneneka za Yehova?

18 Koma mosiyana ndi zimenezo, pamene tiphunzira Baibulo mosamala bwino ndiponso tili ndi mtima wofunadi kudziŵa, timafika poona Yehova monga mmene Baibulo lathunthu limamusonyezera. Motero, sitivutika maganizo ngati nkhani ina imadzutsa mafunso amene sitingapeze mayankho ake mwamsanga. Tipereke chitsanzo: Posonkhanitsa pamodzi zidutswa zomwazikana za chithunzi chachikulu kuti tipangenso chithunzicho, mwinamwake poyamba sitingapeze kachidutswa kenakake kamene kakufunika kapenanso mwina sitingaone kuti kachidutswa kena kafunika kukaika pati. Komatu, tikhoza kukhala titasonkhanitsa zidutswa zokwanira kutithandiza kuzindikira kuti chithunzi chonse chiyenera kuoneka motani. Mofananamo, pamene tikuphunzira Baibulo, mwapang’onopang’ono timaphunzira kuti Yehova ndi Mulungu wotani, ndipo timaona chithunzi chake chooneka bwino. Ngakhale kuti pa nthaŵi yoyamba sitingamvetsetse nkhani inayake kapenanso kuzindikira mmene ikugwirizanirana ndi umunthu wa Mulungu, tinaphunzira kale zambiri za Yehova pa kuphunzira kwathu Baibulo zomwe zingatithandize kuona kuti iye mosakayika konse ndi Mulungu wachikondi ndi wachilungamo.

19 Motero kuti timvetsetse Mawu a Mulungu tifunika kuwaŵerenga ndi kuwaphunzira tili ndi mtima wofunadi kudziŵa, komanso tikhale ndi maganizo abwino. Kodi umenewu si umboni wa nzeru zosaneneka za Yehova? Anthu anzeru kwambiri akhoza kulemba mabuku amene anthu okha omwe ali “anzeru ndi akudziŵitsa” zinthu ndiwo angawamvetse. Koma kulemba buku limene angalimvetse ndi anthu okha amene ali ndi zolinga zabwino mumtima mwawo, kumafunatu nzeru za Mulungu!—Mateyu 11:25.

 Buku Lokhala ndi ‘Nzeru Zenizeni’

20. Kodi n’chifukwa chiyani ndi Yehova yekha amene angatiuze njira yabwino kwambiri yokhalira ndi moyo, ndipo kodi m’Baibulo muli chiyani chimene chingatithandize?

20 M’Mawu ake, Yehova amatiuza njira yabwino kwambiri yokhalira ndi moyo. Monga Mlengi wathu, iye amadziŵa bwino zimene timafunika kuposa mmene ife timadziŵira. Ndipo zinthu zofunika kwambiri pa moyo wa munthu—kuphatikizapo chikhumbo cha kukondedwa, kukhala wachimwemwe, ndi kumagwirizana ndi ena popanda zovuta—sizinasinthe. Baibulo lili ndi ‘nzeru zenizeni’ zochuluka zimene zingatithandize kukhala ndi miyoyo yabwino. (Miyambo 2:7) Chigawo chilichonse cha buku lino lothandiza pophunzira chili ndi mutu wina umene ukusonyeza mmene tingagwiritsire ntchito uphungu wanzeru wa m’Baibulo. Tiyeni tionepo chitsanzo chimodzi chokha.

21-23. Kodi ndi uphungu wanzeru wotani umene ungatithandize kupewa kusunga mkwiyo ndi kuipidwa?

21 Kodi munaonapo kuti anthu amene amasungira anzawo zinthu kukhosi ndiponso amene amasunga mkwiyo nthaŵi zambiri amadzivulaza okha pamapeto pake? Mkwiyo ndi katundu wolemetsa kunyamula pa moyo wamunthu. Tikakhala ndi mkwiyo, maganizo athu onse amakhala pa zimenezo ndipo umatilanda mtendere ndiponso chimwemwe. Zofufuza za asayansi zimasonyeza kuti munthu amene amasunga mkwiyo angadwale mosavuta matenda a mtima ndi matenda ena okhalitsa ochuluka. Kalekale kwambiri kafukufuku wa asayansi ameneyu asanachitike, Baibulo linanena mwanzeru kuti: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo.” (Salmo 37:8) Koma kodi tingazichite motani zimenezi?

22 Mawu a Mulungu amapereka uphungu wanzeru uwu: “Kulingalira [“luntha,” NW] kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.” (Miyambo 19:11) Luntha ndilo luso lotha kuona osati zapamwamba zokha ayi koma zam’kati mwenimwenimo, kuona mopitirira pa zinthu zachidziŵikire. Luntha limachititsa munthu kukhala womvetsetsa zinthu, chifukwa lingatithandize kuzindikira chifukwa chake munthu wina analankhula kapena anachita zinthu m’njira yoteroyo. Kuyesetsa kumvetsa zolinga zake zenizeni, mmene anali kumvera mwiniyo, ndi zimene zikumuchitikira kungatithandize kusiya kumuganizira zoipa kapenanso kuipidwa naye.

 23 Baibulo lilinso ndi malangizo ena aŵa: “[Pitirizani, NW] kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha.” (Akolose 3:13) Mawu akuti “pitirizani kulolerana wina ndi mnzake” akusonyeza kuti tifunika kukhala woleza mtima ndi ena, kumalolera makhalidwe awo amene tingaone kuti akutivutitsa. Kupirira koteroko kungatithandize kupewa kusungira ena kukhosi zinthu zosafunika n’komwe. Mawu akuti “kukhululukirana” ali ndi lingaliro loleka kukwiya. Mulungu wathu wanzeru amadziŵa kuti timafunika kukhululukira ena pakakhala chifukwa chomveka chowakhululukira. Zimenezi sikuti zimangopindulitsa enawo koma zimatithandizanso ifeyo kukhala ndi mtendere wa m’maganizo ndi mumtima. (Luka 17:3, 4) Komatu m’Mawu a Mulungu muli nzeru zapamwamba bwanji!

24. Kodi chimatsatira n’chiyani pamene tiyamba kukhala ndi moyo mogwirizana ndi nzeru zaumulungu?

24 Polimbikitsidwa ndi chikondi chake chopanda malire, Yehova anafuna kulankhula nafe. Anasankha njira yabwino koposa yochitira zimenezi, kutilembera “kalata” pogwiritsa ntchito anthu kuti alembe motsogozedwa ndi mzimu woyera. Chotsatira chake n’chakuti, m’kalata imeneyi muli nzeru za Yehova mwiniyo. Nzeru zimenezi ndi “zodalirika kwambiri.” (Salmo 93:5, NW) Pamene tiyamba kukhala ndi moyo mogwirizana ndi nzeru zimenezi n’kumazigaŵirako ena, mosachita kufunsa timayandikana ndi Mulungu wathu wanzeru zonse. M’mutu wotsatirawu, tikambirana chitsanzo china chachikulu cha nzeru zoona patali za Yehova; ndicho, luso lake loneneratu za m’tsogolo ndi kukwaniritsa cholinga chake.

^ ndime 8 Mwachitsanzo, Davide, yemwe anali mbusa, anagwiritsa ntchito zitsanzo za zochitika pamoyo woŵeta ziŵeto. (Salmo 23) Mateyu, yemwe anali wamsonkho, nthaŵi zambiri anali kutchula manambala ndi kuchuluka kwa ndalama. (Mateyu 17:27; 26:15; 27:3) Luka, yemwe anali dokotala, anagwiritsa ntchito mawu osonyeza kuti anali kudziŵa zachipatala.—Luka 4:38; 14:2; 16:20.

^ ndime 14 Kalikonse ka tindalama timeneti kanali ka lepitoni, ndalama yachiyuda yaing’ono kwambiri imene anali kuigwiritsa ntchito nthaŵi imeneyo. Malepitoni aŵiri anali ofanana ndi gawo limodzi mwa magawo 64 a malipiro a tsiku limodzi. Tindalama tiŵiri timeneti sitinali tokwanira kugula mpheta imodzi yomwe inali mbalame yotsika mtengo kwambiri imene anali kudya anthu osauka.