Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 9

“Kristu Mphamvu ya Mulungu”

“Kristu Mphamvu ya Mulungu”

1-3. (a) Kodi n’chiyani chinaopsa ophunzira pa nyanja ya Galileya, ndipo Yesu anachitanji? (b) N’chifukwa chiyani Yesu moyenerera akutchedwa kuti “Kristu mphamvu ya Mulungu”?

OPHUNZIRA anachita mantha kwambiri. Anali kuwoloka nyanja ya Galileya pamene mwadzidzidzi panabwera namondwe. Mosakayikira iwo anali atakumanapo kale ndi anamondwe pa nyanja imeneyi popezatu ena a amunaŵa anali ozoloŵera kusodza. * (Mateyu 4:18, 19) Koma ameneyu anali “namondwe wamkulu wa mphepo,” ndipo sanachedwe kuchititsa nyanjayo kukalipa kwambiri. Amunawo anapalasa ngalawayo mwaphuma, koma namondweyo anali kuwaposa mphamvu. Mafunde anali ‘kugavira m’ngalawa’ ndipo inayamba kudzaza madzi. Ngakhale kuti panali chipwirikiti choterechi, Yesu anali m’tulo tofa nato kumbuyo kwa ngalawayo atatopa ndi kuphunzitsa khamu la anthu tsikulo. Poopa kufa, ophunzirawo anamudzutsa namuchonderera kuti: “Ambuye, tipulumutseni, tili kutayika.”—Marko 4:35-38; Mateyu 8:23-25.

2 Yesu sanachite mantha. N’chidaliro chonse anadzudzula mphepo ndi nyanja kuti: “Tonthola, khala bata.” Mosakhalitsa mphepo ndi nyanjayo zinamvera, namondweyo analeka ndipo mafunde anatha panyanjapo, ndipo “kunangwa bata lalikulu.” Tsopano ophunzirawo anachita mantha aakulu. Anali kunong’onezana kuti: “Uyu ndani nanga?” Zoonadi, ndi munthu wotani amene angadzudzule mphepo ndi nyanja ngati kuti akudzudzula mwana wosamvera?—Marko 4:39-41; Mateyu 8:26, 27.

3 Komatu Yesu sanali munthu wamba. Mphamvu ya Yehova inali kugwira ntchito pa iye ndiponso kuonekera mwa iye m’njira  zapadera. Mtumwi wouziridwa ndi Mulungu, Paulo, anamutchula moyenerera kuti “Kristu mphamvu ya Mulungu.” (1 Akorinto 1:24) Kodi mphamvu ya Mulungu imaonekera motani mwa Yesu? Nanga moyo wathu umakhudzidwa motani ndi mmene Yesu amagwiritsira ntchito mphamvu?

Mphamvu za Mwana Wobadwa Yekha wa Mulungu

4, 5. (a) Kodi ndi mphamvu ndi udindo wotani umene Yehova anapatsa Mwana wake wobadwa yekha? (b) Kodi Mwana ameneyu anali kugwiritsa ntchito chiyani pogwira ntchito ya Atate wake ya kulenga?

4 Talingalirani mphamvu zimene Yesu anali nazo asanakhale munthu. Yehova anasonyeza “mphamvu yake yosatha” pamene analenga Mwana wake wobadwa yekha, yemwe kenako anadzadziŵika kuti Yesu Kristu. (Aroma 1:20; Akolose 1:15) Zitatero, Yehova anapatsa Mwana ameneyu mphamvu zochuluka ndiponso udindo waukulu kwambiri. Anamuuza kuti agwire ntchito Yake ya kulenga. Baibulo limanena kuti za Mwanayu: “Zonse zinalengedwa ndi [“mwa,” NW] Iye; ndipo kopanda Iye sikunalengedwa kanthu kalikonse.”—Yohane 1:3.

5 Tingangozindikira pang’ono chabe kukula kwa ntchito imeneyo. Talingalirani mphamvu zimene zinafunika kuti pakhale angelo amphamvu miyandamiyanda, thambo limodzi ndi milalang’amba yake mabiliyoni ochuluka, ndiponso dziko lapansi lokhala ndi zamoyo zamitundumitundu. Kuti akwanitse kugwira ntchito zimenezo, Mwana wobadwa yekhayo anali kugwiritsa ntchito mphamvu yaikulu kwambiri m’chilengedwe chonse, mzimu woyera wa Mulungu. Mwana ameneyu anasangalala kwambiri kukhala Mmisiri yemwe Yehova anagwiritsa ntchito polenga zinthu zina zonse.—Miyambo 8:22-31.

6. Atafa padziko lapansi ndi kuukitsidwa, kodi ndi mphamvu ndi udindo wotani umene Yesu anapatsidwa?

6 Kodi Mwana wobadwa yekhayo akanalandiranso mphamvu zowonjezeka ndiponso udindo wina? Yesu atafa padziko lapansi ndi kuukitsidwa, iye anati: “Mphamvu zonse zapatsidwa kwa Ine Kumwamba ndi padziko lapansi.” (Mateyu 28:18) Inde, Yesu ndi wokhoza ndiponso wapatsidwa ufulu wosonyeza mphamvu m’chilengedwe chonse. Pokhala ‘Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye,’ wavomerezedwa ‘kuthetsa chiweruzo [“maboma,”  NW] chonse ndi ulamuliro wonse ndi mphamvu yomwe,’ zooneka ndi zosaoneka, zomwe zimatsutsana ndi Atate wake. (Chivumbulutso 19:16; 1 Akorinto 15:24-26) Mulungu “sanasiyapo kanthu kosamugonjera” Yesu, ndiko kuti kupatulapo Yehova mwiniyo.—Ahebri 2:8; 1 Akorinto 15:27.

7. N’chifukwa chiyani tingakhale otsimikiza kuti Yesu sadzagwiritsa ntchito molakwa mphamvu zimene Yehova wamupatsa?

7 Kodi tiyenera kuda nkhaŵa kuti Yesu akhoza kugwiritsa ntchito molakwa mphamvu zake? M’pang’onong’ono pomwe! Yesu amawakonda kwambiri Atate wake ndipo sangachite chinthu chosawasangalatsa. (Yohane 8:29; 14:31) Yesu amadziŵa bwino kuti Yehova sagwiritsa ntchito molakwika mphamvu zake zazikuluzo. Yesu wachita kuona yekha kuti Yehova amafunafuna mipata ‘yodzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.’ (2 Mbiri 16:9) Ndithudi, Yesu amakonda anthu mofanana ndi Atate wake, motero tingakhale n’chidaliro chakuti Yesu nthaŵi zonse adzagwiritsa ntchito mphamvu zake mopindulitsa. (Yohane 13:1) Pankhaniyi, Yesu wapanga mbiri yabwino zedi. Tiyeni tione mphamvu zimene anali nazo pamene anali pano padziko lapansi ndiponso zimene zinali kumuchititsa kuti azigwiritse ntchito.

“Wamphamvu . . . M’mawu”

8. Atadzozedwa, kodi Yesu anapatsidwa mphamvu zochita chiyani, ndipo anagwiritsa ntchito motani mphamvu zake?

8 Mwachionekere, Yesu sanachitepo zozizwitsa ali mnyamata pamene amakula ku Nazarete. Koma zinthu zinasintha atabatizidwa m’chaka cha 29 C.E., ali ndi zaka pafupifupi 30 zakubadwa. (Luka 3:21-23) Baibulo limatiuza kuti: “Mulungu anamudzoza iye ndi Mzimu Woyera ndi mphamvu; amene anapitapita nachita zabwino, nachiritsa onse osautsidwa ndi Mdyerekezi.” (Machitidwe 10:38) “Nachita zabwino,” kodi zimenezi sizikusonyeza kuti Yesu anagwiritsa ntchito moyenera mphamvu zake? Atadzozedwa, anakhala “mneneri wamphamvu m’ntchito, ndi m’mawu.”—Luka 24:19.

9-11. (a) Kodi Yesu nthaŵi zambiri anali kuphunzitsira kuti, ndipo maloŵa anapereka mavuto otani? (b) N’chifukwa chiyani makamu a anthu anazizwa ndi kaphunzitsidwe ka Yesu?

9 Kodi ndi motani mmene Yesu analili wamphamvu m’mawu?  Nthaŵi zambiri anali kuphunzitsira panja—m’magombe a nyanja ndi m’mphepete mwa mapiri ndiponso m’misewu ndi m’misika. (Marko 6:53-56; Luka 5:1-3; 13:26) Omvera ake akanatha kuchoka mosavuta ngati mawu ake sanali kuwasangalatsa. M’nyengo yomwe anthu anali asanayambe kusindikiza mabuku, omvera amene anasangalala ndi ziphunzitso za Yesu anali kusunga mawu ake m’maganizo ndi m’mitima yawo. Motero zimene Yesu anali kuphunzitsa zinafunika kukhala zokopa kwambiri, zomveka bwino, ndi zosavuta kukumbukira. Koma zimenezi sizinali vuto kwa Yesu. Mwachitsanzo, talingalirani ulaliki wake wa pa phiri.

10 Tsiku lina mmaŵa chakumayambiriro kwa chaka cha 31 C.E., khamu la anthu linasonkhana m’mphepete mwa phiri pafupi ndi nyanja ya Galileya. Ena anachokera ku Yudeya ndi ku Yerusalemu, mtunda wa makilomita 100 mpaka 110. Ena anachokera mbali ya kumpoto m’madera a ku nyanja a Turo ndi Sidoni. Anthu ambiri odwala anayandikira Yesu kuti amukhudze, ndipo anawachiritsa onse. Pamene panalibe munthu ndi m’modzi yemwe wodwala kwambiri pa khamulo, iye anayamba kuwaphunzitsa. (Luka 6:17-19) Atamaliza kulankhula patapita nthaŵi, iwo anadabwa ndi zimene anamva. Chifukwa chiyani?

11 Patatha zaka zingapo, munthu wina amene anamva ulaliki umenewo analemba kuti: “Makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake: pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu.” (Mateyu 7:28, 29) Zonena za Yesu zinali zogwira mtima. Anali kulankhula m’malo mwa Mulungu ndipo anagwiritsa ntchito Mawu a Mulunguyo popereka umboni wa zimene anali kuphunzitsa. (Yohane 7:16) Yesu anali kulankhula zomveka bwino, anali kulimbikitsa anthu motenga mtima, ndipo anali ndi mfundo zosatsutsika. Mawu ake anali kukhudza mfundo zofunika kwambiri za nkhani ndipo anali kufika omvetsera ake pamtima. Anawaphunzitsa mmene angakhalire achimwemwe, mmene angapempherere, mmene angafunire Ufumu wa Mulungu, ndi mmene angakonzere tsogolo losungika. (Mateyu 5:3–7:27) Mawu ake anagalamutsa mitima ya anthu amene anali ndi njala ya choonadi ndi chilungamo. Anthu oterowo anali ofunitsitsa ‘kudzikana’ ndi kusiya zawo zonse kuti amutsate iye. (Mateyu 16:24;  Luka 5:10, 11) Umenewu ndi umbonitu waukulu kwambiri wakuti mawu a Yesu analidi ndi mphamvu!

“Wamphamvu M’ntchito”

12, 13. Kodi Yesu anali “wamphamvu m’ntchito” mu lingaliro lotani, nanga zozizwitsa zake zinali zosiyanasiyana motani?

12 Yesu analinso “wamphamvu m’ntchito.” (Luka 24:19) Mauthenga Abwino amasimba za zozizwitsa zosiyanasiyana zoposa 30 zimene iye anachita—zonsezo mu “mphamvu ya Yehova.” * (Luka 5:17, NW) Zozizwitsa za Yesu zinakhudza miyoyo ya anthu ambiri. Zozizwitsa ziŵiri zokha, kudyetsa amuna 5,000 ndipo kenako amuna 4,000 osaŵerengera pamodzi ndi “akazi ndi ana,” mwinamwake zinaphatikizapo khamu la anthu lofika pa 20,000!—Mateyu 14:13-21; 15:32-38.

“Anaona Yesu ali kuyenda panyanja”

13 Zozizwitsa za Yesu zinali kusiyanasiyana kwambiri. Anali ndi mphamvu pa ziŵanda moti sanali kuvutika pozitulutsa. (Luka 9:37-43) Anali ndi mphamvu pa zinthu zooneka, anasandutsa madzi kukhala vinyo. (Yohane 2:1-11) Modabwitsa kwambiri ophunzira ake, iye anayenda pa nyanja ya Galileya pomwe panali kuwomba mphepo yaikulu. (Yohane 6:18, 19) Anali kugonjetsa matenda, anachiritsa anthu olemala, odwala kwanthaŵi yaitali, ndiponso amene anali pafupi kufa. (Marko 3:1-5; Yohane 4:46-54) Anthuŵa anawachiritsa mwa njira zosiyanasiyana. Anthu ena anawachiritsa ali kutali, pamene ena, Yesu mwiniyo anachita kuwagwira. (Mateyu 8:2, 3, 5-13) Ena ankachira nthaŵi yomweyo pamene ena ankachira pang’onopang’ono.—Marko 8:22-25; Luka 8:43, 44.

14. Kodi Yesu anasonyeza kuti anali ndi mphamvu yosintha imfa pa zochitika zotani?

14 Mwapamwamba kwambiri, Yesu anali ndi mphamvu yosintha imfa. Pa zochitika zitatu zimene zinalembedwa, anaukitsa anthu akufa; anabwezera mwana wamkazi wazaka 12 kwa makolo ake, mwana m’modzi yekhayo kwa mayi ake amasiye, ndi mchimwene wokondedwa kwa alongo ake. (Luka 7:11-15; 8:49-56; Yohane  11:38-44) Panalibe chochitika chimene chinali chosatheka kwa Yesu. Mtsikana wazaka 12 ameneyo anamuukitsira pamalo omwe anamugoneka atangomwalira kumene. Mwana wa mkazi wamasiyeyo anamuukitsira pa chithatha chimene anamunyamulirapo, mosakayikira linali tsiku lomwe anafalo. Ndipo anaukitsa Lazaro kuchokera m’manda atakhala wakufa kwa masiku anayi.

Kugwiritsa Ntchito Mphamvu Mopanda Dyera, Mozindikira, ndi Molingalira Ena

15, 16. Kodi pali umboni wotani wakuti Yesu sanali kugwiritsa ntchito mphamvu zake mwadyera?

15 Kodi mungaganizire mmene mphamvu za Yesu zikanagwiritsidwira ntchito molakwa ngati zikanapatsidwa kwa wolamulira wopanda ungwiro? Koma Yesu analibe uchimo. (1 Petro 2:22) Iye sanalole kuti aipitsidwe ndi kudzikonda, kufunitsitsa udindo, ndi umbombo zimene zimachititsa anthu opanda ungwiro kuzunza anzawo pogwiritsa ntchito mphamvu zawo.

16 Yesu sanachite dyera pogwiritsa ntchito mphamvu zake; sanazigwiritsepo ntchito mwa njira yakuti iye apeze phindu. Pamene anali ndi njala, anakana kusandutsa miyala kukhala mkate woti iyeyo adye. (Mateyu 4:1-4) Umboni woti sanapindule mwakuthupi pamene anali kugwiritsa ntchito mphamvu zake ndi wakuti iye anali ndi zinthu zochepa zedi. (Mateyu 8:20) Pali umboni winanso wosonyeza kuti analibe zolinga zadyera pochita ntchito zake zamphamvu. Pochita zozizwitsa, anali kutero modzipereka ndithu. Akachiritsa odwala, mphamvu inali kutuluka m’thupi lake. Anali kudziŵa kuti mphamvu yachoka moteremu ngakhale atachiritsa munthu m’modzi yekha. (Marko 5:25-34) Komatu, iye analola makamu a anthu kumukhudza ndipo anali kuchiritsidwa. (Luka 6:19) Anali ndi mzimu wodzipereka bwanji!

17. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti anali kugwiritsa ntchito mphamvu zake mozindikira?

17 Yesu anali kugwiritsa ntchito mphamvu zake mozindikira. Sanachitepo ntchito zamphamvu kungoti adzitamandire kayanso kuchita zionetsero zopanda cholinga. (Mateyu 4:5-7) Iye sanafune kusonyeza zizindikiro n’cholinga chosangalatsa Herode yemwe anachita naye chidwi molakwika. (Luka 23:8, 9) M’malo molengeza mphamvu zake, kaŵirikaŵiri Yesu anali kulangiza  anthu amene anawachiritsa kuti asauze wina aliyense. (Marko 5:43; 7:36) Sanafune kuti anthu adziŵe kuti anali yani chifukwa cha kumva malipoti osangalatsa.—Mateyu 12:15-19.

18-20. (a) Kodi n’chiyani chinali kuchititsa Yesu kugwiritsa ntchito mphamvu zake mothandiza? (b) Kodi mukumva bwanji ndi mmene Yesu anachiritsira munthu wina wogontha?

18 Munthu wamphamvu ameneyu, Yesu, anali wosiyana kwambiri ndi olamulira amene agwiritsa ntchito mphamvu mosalingalira m’pang’onong’ono pomwe za zinthu zimene ena akufunikira ndiponso za kuvutika kwawo. Yesu anali kuganizira anthu. Zinali kumukhudza kwambiri akaona anthu ovutika moti anali kuchitapo kanthu kuti awathandize mavuto awowo. (Mateyu 14:14) Ankalingalira mmene iwo anali kumverera ndi zimene ankafuna. Mtima wachifundo umenewu unali kumuchititsa kugwiritsa ntchito mphamvu zake mothandiza. Chitsanzo chochititsa kaso cha zimenezi chili pa Marko 7:31-37.

19 Pa chochitika chimenechi, makamu a anthu atapeza Yesu anamubweretsera odwala ambiri, ndipo iye anawachiritsa onse. (Mateyu 15:29, 30) Komano Yesu anasankhapo mwamuna wina m’modzi kuti amusamalire mwapadera. Munthuyu anali wogontha ndipo amavutika zedi polankhula. Mwina Yesu anazindikira kuti munthuyu anali kuchita mantha kapena manyazi. Pomuganizira, Yesu anamuchotsa pa gululo, nam’tengera pambali pa yekha. Kenako Yesu anagwiritsa ntchito zizindikiro pouza munthuyo zimene ankafuna kuchita. ‘Analonga zala zake m’makutu mwake, nalavula malovu, nakhudza lilime lake.’ * (Marko 7:33) Kenako, Yesu anagadamira kumwamba nausa moyo mopemphera. Zimenezi zinamuuza munthuyo kuti, ‘Zimene ndikufuna kukuchitira zichitika ndi mphamvu yochokera kwa Mulungu.’ Pamapeto pake Yesu anati: “Tatseguka.” (Marko 7:34) Ndiyeno munthuyo anayambanso kumva, ndipo anali kulankhula bwinobwino.

 20 Ndi zolimbikitsatu kwambiri kuganizira kuti ngakhale pamene anali kugwiritsa ntchito mphamvu zake zopatsidwa ndi Mulungu pochiritsa anthu ovutika, Yesu mwachifundo analingalira za mmene anthuwo anali kumvera! Kodi si zokhazika mtima pansi kudziŵa kuti Yehova wapereka Ufumu Waumesiya kwa Wolamulira wachifundo ndi wolingalira ena ameneyu?

Chionetsero cha Zinthu za M’tsogolo

21, 22. (a) Kodi zozizwitsa za Yesu zinapereka chithunzithunzi cha chiyani? (b) Popeza kuti Yesu amalamulira mphamvu zachilengedwe, kodi tingayembekeze chiyani mu ulamuliro wake wa Ufumu?

21 Ntchito zamphamvu zimene Yesu anachita padziko lapansi zinali chabe chithunzithunzi cha madalitso ochuluka amene adzabwera mu ulamuliro wake waufumu. M’dziko latsopano la Mulungu, Yesu adzachitanso zozizwitsa, koma tsopano adzazichita padziko lonse! Talingalirani zinthu zina zosangalatsa zimene tikuyembekeza m’tsogolomu.

22 Yesu adzabwezeretsa kugwirizana kwa zinthu zamoyo m’malo mmene zimakhala padziko lapansi. Kumbukirani kuti anaonetsa kuti akhoza kulamulira mphamvu zachilengedwe mwa kuletsa namondwe. Ndithudi, mu ulamuliro wa Ufumu wa Kristu, anthu sadzaopa kuvulazidwa ndi mphepo zamkuntho, zivomezi, mavokano, kapenanso masoka ena achilengedwe. Popeza kuti Yesu ndi Mmisiri, yemwe Yehova anagwiritsa ntchito polenga dziko lapansi ndi zamoyo zonse zimene zilimo, amadziŵa bwino kwambiri mmene dziko lapansi linapangidwira. Amadziŵa mmene angagwiritsire ntchito bwino zinthu za m’dzikoli. Mu ulamuliro wake, dziko lapansi lonseli lidzasanduka Paradaiso.—Luka 23:43.

23. Monga Mfumu, kodi Yesu adzakwaniritsa motani zofunika zazikulu za anthu?

23 Nanga bwanji za zofunika zazikulu za anthu? Yesu anali wokhoza kudyetsa mokwanira bwino anthu masauzande ambiri pogwiritsa ntchito zakudya zochepa kwambiri zimene zinalipo. Zimenezi zikutitsimikizira kuti ulamuliro wake udzathetsa njala. Ndithudi, chakudya chochuluka chomwe chidzagaŵidwa mosakondera, chidzathetsa njala ku nthaŵi zonse. (Salmo 72:16) Kugonjetsa kwake matenda kumatiuza kuti anthu  odwala, akhungu, ogontha, ovulazidwa, ndi olemala adzachiritsidwa kotheratu ndipo sadzadwalanso. (Yesaya 33:24; 35:5, 6) Iye anali wokhoza kuukitsa akufa; zomwe zikutsimikizira kuti monga Mfumu yamphamvu yakumwamba, iye adzakhala ndi mphamvu zoukitsa anthu mamiliyoni osaŵerengeka amene Atate wake akuwakumbukira mosangalala.—Yohane 5:28, 29.

24. Pamene tikulingalira za mphamvu za Yesu, kodi tiyenera kukumbukira chiyani, ndipo n’chifukwa ninji?

24 Pamene tikulingalira za mphamvu za Yesu, tiyeni tikumbukire kuti Mwana ameneyu amatsanzira bwino kwambiri Atate wake. (Yohane 14:9) Motero, mmene Yesu amagwiritsira ntchito mphamvu zimatipatsa chithunzi chooneka bwino cha mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu. Mwachitsanzo, taganizirani mmene Yesu anachiritsira wakhate wina mokoma mtima. Atagwidwa ndi chifundo, Yesu anakhudza munthuyo ndi kunena kuti: “Ndifuna.” (Marko 1:40-42) M’nkhani zangati imeneyi, Yehova kwenikweni akunena kuti, ‘Ndimo mmene ndimagwiritsira ntchito mphamvu zanga!’ Kodi sizikukuchititsani kufuna kutamanda Mulungu wathu wamphamvuyonse ndi kumuthokoza chifukwa chakuti amagwiritsa ntchito mphamvu zake m’njira yachikondi yoteroyo?

^ ndime 1 Anamondwe a mwadzidzidzi amachitika kaŵirikaŵiri pa Nyanja ya Galileya. Chifukwa chakuti ili pamalo otsika kwambiri (otsika mamita ngati 200 pansi pa nyanja), mpweya ndi wotentha kwambiri panyanjapo kusiyana ndi m’madera oizungulira, ndipo izi zimasokoneza mpweya wa mumlengalenga. M’chigwa cha Yordano mumawomba mphepo zamphamvu zochokera ku phiri la Hermoni lomwe lili kumpoto kwa nyanjayi. Nyengo yabata ingasinthe mofulumira kukhala mkuntho wadzaoneni.

^ ndime 12 Kuwonjezera pamenepa, nthaŵi zina Mauthenga Abwino amaphatikiza zozizwitsa zambiri n’kuzifotokozera pamodzi. Mwachitsanzo, panthaŵi ina “mudzi wonse” unabwera kudzamuona, ndipo anachiritsa odwala “ambiri.”—Marko 1:32-34.

^ ndime 19 Kulavula malovu inali njira kapena chizindikiro cha kuchiritsa yomwe Ayuda limodzi ndi Akunja omwe anali kuivomereza, ndipo mabuku achirabi amafotokoza za kugwiritsa ntchito malovu pochiritsa. Yesu angakhale kuti analavula malovu pa kungofuna kuuza munthuyu kuti anali pafupi kuchiritsidwa. Mulimonse mmene zinalili, Yesu sanagwiritse ntchito malovu ake ngati mankhwala achilengedwe ochiritsira.