1, 2. Kodi ndi zinthu zodabwitsa zotani zimene Eliya anali ataona pamoyo wake, koma ndi zochitika zodabwitsa zedi zotani zimene anaona pamene anali pa phanga pa phiri la Horebu?

ELIYA anali ataonapo kale zinthu zodabwitsa. Anali ataona makungubwi akumubweretsera chakudya kaŵiri patsiku pamene iye ankakhala mobisala. Anali ataona mbiya ziŵiri zosatha ufa ndi mafuta kwa nthaŵi yaitali pamene kunali njala. Anaonanso moto ukugwa kuchokera kumwamba poyankha pemphero lake. (1 Mafumu, machaputala 17, 18) Komatu, Eliya anali asanaonepo chodabwitsa chilichonse chonga ichi.

2 Atadzipanikiza kukhoma pafupi ndi khomo la phanga pa phiri la Horebu, anaona zochitika zingapo zodabwitsa zedi. Poyamba panali mphepo. Iyenera kuti inawomba kwambiri ndi kuchita phokoso logonthetsa m’khutu, pakuti inali yamphamvu kwabasi moti inang’amba mapiri ndi kuphwanya matanthwe. Kenako panali chivomezi, chomwe chinatulutsa mphamvu zikuluzikulu za pansi pathaka. Ndiyeno kunabwera moto. Pamene unali kudutsa pamalowo, ndithudi Eliya anamva chifundizi cha kutentha kwake konyeketsa zinthuko.—1 Mafumu 19:8-12.

“Taonani Yehova anapitapo”

3. Kodi Eliya anaona umboni wa mbali iti ya umunthu wa Mulungu, nanga ife umboni wa mbali yomweyi ya umunthu wa Mulungu tingauone kuti?

3 Zochitika zonsezi zomwe Eliya anaona zinali ndi chinthu chimodzi chofanana, zonse zinali kusonyeza mphamvu zazikulu za Yehova Mulungu. Inde, sitifunika kuchita kuona chozizwitsa kuti tizindikire kuti Mulungu ndi wamphamvu. Mphamvu zake zimaoneka mosavuta. Baibulo limatiuza kuti chilengedwe chimapereka umboni wa ‘mphamvu yosatha ndi umulungu’ wa Yehova. (Aroma 1:20) Tangoganizirani za kuwala kopha maso kwa mphezi ndi kugunda kwa mvula, kugwa kosangalatsa kwa madzi pamathithi, kukula kochititsa mantha kwa thambo lodzala ndi nyenyezi! Kodi simuona mphamvu za Mulungu m’zinthu zimenezi? Komatu, ndi anthu ochepa chabe lerolino amene amazindikira mphamvu za Mulungu. Ndipo ochepanso mwa ameneŵa ndiwo  amaona mphamvuzo moyenera. Komabe kumvetsetsa mbali imeneyi ya umunthu wa Mulungu kumatipatsa zifukwa zochuluka zoti tiyandikire kwa Yehova. M’chigawo chino tiphunzira mwatsatanetsatane mphamvu zosayerekezeka za Yehova.

Mbali Yofunika Kwambiri ya Umunthu wa Yehova

4, 5. (a) Ndi kugwirizana kotani kumene kulipo pakati pa dzina la Yehova ndi mphamvu zake? (b) N’chifukwa chiyani kuli koyenera kuti Yehova anasankha ng’ombe kuimira mphamvu zake?

4 Yehova ali ndi mphamvu zapadera. Yeremiya 10:6 amati: “Palibe akunga Inu, Yehova; muli wamkulu, ndipo dzina lanu lili lalikulu ndi lamphamvu.” Onani kuti akugwirizanitsa mphamvu ndi dzina la Yehova. Kumbukirani kuti dzinali limatanthauza kuti “Iye Amachititsa Kukhala.” Kodi n’chiyani chimene chimachititsa kuti Yehova azitha kupanga chilichonse chimene akufuna ndiponso kukhala chilichonse chimene wasankha kukhala? Makamaka ndi mphamvu. Inde, Yehova ndi wokhoza kuchita chifuno chake n’kuchikwaniritsa mosaletseka ndi kalikonse. Mphamvu zoterozo ndi mbali imodzi yofunika kwambiri ya umunthu wake.

5 Popeza sitingamvetsetse mmene mphamvu zake zonse zilili, Yehova amatithandiza kuti tizimvetsetse pogwiritsa ntchito mafanizo. Monga taonera, amagwiritsa ntchito ng’ombe kuimira mphamvu zake. (Ezekieli 1:4-10) Anasankha nyama yoyenera, chifukwa ngakhale ng’ombe zimene timaŵeta ndi nyama zikuluzikulu komanso zamphamvu. Anthu a ku Palestina wa m’nthaŵi za m’Baibulo sanali kukumana kaŵirikaŵiri ndi nyama yamphamvu kuposa ng’ombe, ngatinso anali kukumana nayo n’komwe. Koma iwo anali kudziŵa ng’ombe zinazake zoopsa kwambiri—njati za mtundu wotchedwa aurochs, zimene tsopano zinatha. (Yobu 39:9-12) Mfumu ya Roma Juliasi Kaisara panthaŵi ina anati ng’ombe zimenezi zinali pafupifupi zofanana msinkhu ndi njovu. Iye anati: “N’zamphamvu zedi, komanso n’zaliŵiro kwambiri.” Talingalirani mmene mungadzionere kukhala wochepa ndi wopanda mphamvu poimirira pafupi ndi nyama yoteroyo!

6. N’chifukwa chiyani Yehova yekha ndiye amatchedwa kuti “Wamphamvuyonse”?

6 Mofananamo, munthu ndi wofooka ndi wopanda mphamvu  pomuyerekezera ndi Mulungu wa mphamvu, Yehova. Kwa iye, ngakhale mitundu yamphamvu zedi n’njofanana ndi fumbi logwera pa sikelo. (Yesaya 40:15) Mosiyana ndi cholengedwa chilichonse, Yehova ali ndi mphamvu zopanda malire, pakuti iye yekha ndiye amatchedwa “Wamphamvuyonse.” * (Chivumbulutso 15:3) Yehova ndi “wolimba mphamvu” ndipo ali ndi ‘mphamvu zazikulu.’ (Yesaya 40:26) Iye ndi gwero la mphamvu nthaŵi zonse ndipo mphamvuzo sizichepa kapena kutha. Sadalira chinachake kuti chimupatse nyonga, chifukwa ‘mphamvu ndi yake ya Mulungu.’ (Salmo 62:11) Komabe, kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake m’njira zotani?

Mmene Yehova Amagwiritsira Ntchito Mphamvu Zake

7. Kodi mzimu woyera wa Yehova n’chiyani, nanga mawu a zinenero zoyambirira omwe agwiritsidwa ntchito m’Baibulo amapereka lingaliro lotani?

7 Mzimu woyera umayenda mosefukira kuchokera kwa Yehova. Mzimuwu ndi mphamvu ya Mulungu imene ikugwira ntchito. Ndipotu pa Genesis 1:2 (NW), Baibulo limaunena kuti ndi “mphamvu yogwira ntchito” ya Mulungu. Mawu achihebri ndi achigiriki oyambirira amene amatembenuzidwa kuti “mzimu” m’nkhani zina angatembenuzidwe kuti “mphepo,” “mpweya,” ndi “nthunzi.” Malinga n’kunena kwa olemba mabuku otanthauzira mawu, mawu a chinenero choyambiriracho ali ndi lingaliro la mphamvu yosaoneka ikugwira ntchito. Mofanana ndi mphepo, mzimu wa Mulungu sitingauone ndi maso, koma umachititsa zinthu zooneka ndipo zinthuzo tingazizindikire.

8. M’Baibulo, kodi mzimu wa Mulungu umatchedwa kuti chiyani mophiphiritsa, nanga n’chifukwa chiyani kuli koyenerera kuuyerekezera ndi zinthu zimenezi?

8 Mzimu woyera wa Mulungu umasinthasintha mosalekeza. Yehova amaugwiritsa ntchito pochita chilichonse chomwe akulingalira. Motero, n’koyenerera kuti m’Baibulo mzimu wa Mulungu umatchedwa mophiphiritsa kuti “chala” chake, “dzanja [lake] lamphamvu,” kapenanso “mkono [wake] wotambasuka.” (Luka 11:20; Deuteronomo 5:15; Salmo 8:3) Monga mmene munthu angagwiritsire ntchito dzanja lake pogwira ntchito zosiyanasiyana zofuna nyonga kapena maluso osiyanasiyana, Mulungunso angagwiritse  ntchito mzimu wake kukwaniritsa cholinga chake chilichonse, monga ngati kulenga atomu yochepetsetsayo kapena kugaŵanitsa Nyanja Yofiira kaya kuchititsa Akristu a m’zaka za zana loyamba kulankhula zinenero zachilendo.

9. Kodi mphamvu zolamulira za Yehova ndi zochuluka motani?

9 Yehova amasonyezanso mphamvu mwa udindo wake monga Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse. Kodi mungalingalire kukhala muli ndi miyandamiyanda ya anthu anzeru ndi okhoza bwino kuchita zinthu omwe ali ofunitsitsa kuchita zimene inu mukuwalamula? Yehova ali ndi mphamvu zolamulira zoterozo. Ali ndi anthu omutumikira omwe kaŵirikaŵiri m’Malemba amawatchula kuti khamu. (Salmo 68:11; 110:3) Komabe munthu ndi cholengedwa chofooka pomuyerekezera ndi mngelo. Inde, pamene gulu la nkhondo la Asuri linaukira anthu a Mulungu, mngelo mmodzi yekha anapha asilikali a Asuri 185,000 mu usiku umodzi wokha! (2 Mafumu 19:35) Angelo a Mulungu ndi “a mphamvu zolimba.”—Salmo 103:19, 20.

10. (a) N’chifukwa chiyani Wamphamvuyonseyo amatchedwa kuti Yehova wa makamu? (b) Kodi ndani amene ali wamphamvu kwambiri pa zolengedwa zonse za Yehova?

10 Kodi angelo alipo angati? Mneneri Danieli anaona masomphenya a kumwamba mmene anaona zolengedwa zauzimu zoposa pa 100 miliyoni zikuimirira ku mpando wachifumu wa Yehova, koma palibe chilichonse chosonyeza kuti iye anaona angelo onse amene Yehova analenga. (Danieli 7:10) Ndiye kuti angelo angakhale alipo mamiliyoni mazanamazana. Choncho Mulungu amatchedwa kuti Yehova wa makamu. Dzina la udindo limeneli limafotokoza udindo wake wamphamvu kwambiri monga Mtsogoleri wa gulu lalikulu ndi lolinganizidwa bwino la angelo amphamvu. Waika wina kukhala wolamulira zolengedwa zauzimu zonsezi, ndiye Mwana wake wokondedwa, “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Pokhala mngelo wamkulu—mkulu wa angelo, aserafi, ndi akerubi onse—Yesu ndiye wamphamvu kwambiri pa zolengedwa zonse za Yehova.

11, 12. (a) Kodi mawu a Mulungu amasonyeza mphamvu mwa njira zotani? (b) Kodi Yesu anachitira umboni motani kuchuluka kwa mphamvu za Yehova?

11 Pali njira inanso imene Yehova amasonyezera mphamvu. Ahebri 4:12 amati: “Mawu a Mulungu ali amoyo, ndi ochitachita.” Kodi mwaiona mphamvu yapadera ya mawu a Mulungu, kapena  kuti uthenga wouziridwa ndi mzimu umene tsopano ukupezeka m’Baibulo? Ungatilimbikitse, ungakulitse chikhulupiriro chathu, ndipo ungatithandize kusintha kuti tikhale ndi moyo wabwino. Mtumwi Paulo anachenjeza okhulupirira anzake za anthu a makhalidwe oipa kwambiri. Ndiyeno anatinso: “Ena a inu munali otere.” (1 Akorinto 6:9-11) Inde, “mawu a Mulungu” anaonetsa mphamvu zake mwa anthuwo ndipo anawathandiza kusintha.

12 Mphamvu za Yehova n’zazikulu kwambiri ndiponso amazigwiritsa ntchito m’njira zabwino kwambiri moti palibe chilichonse chingamulepheretse kuzisonyeza. Yesu ananena kuti: “Zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.” (Mateyu 19:26) Kodi Yehova amasonyeza mphamvu zake pa cholinga chotani?

Mphamvu Zokhala ndi Cholinga

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova si gwero la mphamvu lopanda umunthu? (b) Kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake m’njira zotani?

13 Mzimu wa Yehova uli ndi mphamvu kuposa mphamvu ina iliyonse yopangidwa ndi zinthu zooneka; ndipo Yehova si mphamvu yopanda umunthu, kaya malo ochokerapo mphamvu chabe. Iye ndi Mulungu yemwe ali ndi umunthu ndipo amalamulira mphamvu zake zonse. Komano, n’chiyani chimamuchititsa kugwiritsa ntchito mphamvu zakezo?

14 Monga mmene tionere, Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zake polenga, powononga, poteteza, pokonzanso zinthu—mwachidule tingoti pochita chilichonse chimene chikuyenerera zolinga zake zangwiro. (Yesaya 46:10) M’zochitika zina, Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake poulula mbali zofunikira za umunthu wake ndi miyezo yake. Chofunika kwambiri, amagwiritsa ntchito mphamvu zake pokwaniritsa chifuno chake, chomwe ndi kutsimikizira kuti iye ndiye wolamulira ndi kuyeretsa dzina lake loyera mwa Ufumu Waumesiya. Palibe chimene chingalepheretse cholinga chimenechi.

15. Kodi Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake ndi cholinga chotani chokhudza atumiki ake, nanga zimenezi anazisonyeza motani kwa Eliya?

15 Yehova amagwiritsanso ntchito mphamvu zake potithandiza aliyense payekha. Taonani zimene 2 Mbiri 16:9 amanena: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera  wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.” Chitsanzo chake ndi zimene zinachitikira Eliya, zomwe zatchulidwa koyambirira kwa mutu uno. N’chifukwa chiyani Yehova anamuonetsa mphamvu zaumulungu mochititsa mantha moteromo? Mfumukazi Yezebeli woipayo anali atalumbira kuti apha Eliya. Mneneriyu anali kuthaŵa pofuna kupulumutsa moyo wake. Anaona kuti analipo yekhayekha, anali wamantha, ndipo anagwa ulesi, ngati kuti ntchito yaikulu yonse imene anagwira inangopita pachabe. Kuti alimbikitse munthu wovutika maganizo ameneyu, Yehova anakumbutsa Eliya momveka bwino za mphamvu za Mulungu. Mphepo, chivomezi, ndi moto zinasonyeza kuti Munthu wamphamvu kwambiri m’chilengedwe chonse anali limodzi ndi Eliya. Kodi akanaopanji kwa Yezebeli, pokhala kuti iye anali limodzi ndi Mulungu wamphamvuyonse?—1 Mafumu 19:1-12. *

16. N’chifukwa chiyani kusinkhasinkha za mphamvu zazikulu za Yehova kungatilimbikitse?

16 Ngakhale kuti ino si nthaŵi yake yochita zozizwitsa, Yehova sanasinthe; adakali mmene analili m’masiku a Eliya. (1 Akorinto 13:8) Lerolino ndi wofunitsitsabe kugwiritsa ntchito mphamvu zake kuthandiza amene amamukonda. N’zoona kuti iye amakhala m’malo okwezeka a mizimu, koma sikuti ali kutali nafe. Mphamvu zake n’zopanda malire, motero kutalikirana si vuto. M’malo mwake, “Yehova ali pafupi ndi onse akuitanira kwa Iye.” (Salmo 145:18) Panthaŵi ina pamene mneneri Danieli anapempha Yehova kuti amuthandize, mngelo anamufikira iye asanathe n’komwe kupempherako! (Danieli 9:20-23) Palibe chomwe chingalepheretse Yehova kuthandiza ndi kulimbikitsa anthu amene amawakonda.—Salmo 118:6.

Kodi Mphamvu za Mulungu Zimamupangitsa Kukhala Wovuta Kumufikira?

17. Kodi mphamvu za Yehova zimatipatsa mantha m’lingaliro lotani, koma kodi sizitipatsa mantha a mtundu wanji?

17 Kodi tiyenera kumuopa Mulungu chifukwa cha mphamvu  zake? Tiyankhe ponse paŵiri kuti inde komanso ayi. Tikuti inde chifukwa khalidwe lake limeneli limatipatsa zifukwa zokwanira zokhalira ndi mantha aumulungu, kuopa kwaulemu ndi kolemekeza kumene takambirana mwachidule m’mutu wapitawo. Baibulo limatiuza kuti kuopa kotereku ndiko “chiyambi cha nzeru.” (Salmo 111:10) Komabe tikunenanso kuti ayi chifukwa mphamvu za Mulungu sizitipatsa chifukwa chilichonse choti tinjenjemere ndi mantha ngati kuti taona chinthu choopsa kapenanso kuti tizilephera kumufikira.

18. (a) N’chifukwa chiyani ambiri sakhulupirira anthu okhala ndi mphamvu? (b) Kodi tikudziŵa bwanji kuti mphamvu za Yehova sizingamuchititse kukhala ndi khalidwe loipa?

18 “Mphamvu zimapangitsa munthu kukhala ndi khalidwe loipa ndipo mphamvu zambiri zimapangitsa munthu kukhala ndi khalidwe loipa kwambiri.” Anatero wolemba mbiri wachingelezi Bwana Acton mu 1887. Anthu amabwereza kaŵirikaŵiri mawu ameneŵa, mwina chifukwa chakuti ambiri amaona kuti palibe yemwe angatsutse kuti ndi oona. Kaŵirikaŵiri anthu opanda ungwiro amagwiritsa ntchito molakwa mphamvu zawo, monga taonera nthaŵi ndi nthaŵi m’mbiri ya anthu. (Mlaliki 4:1; 8:9) Chifukwa cha zimenezi, ambiri sakhulupirira anthu omwe ali ndi mphamvu pa zinthu ndipo amafuna kutalikirana nawo. Eya, Yehova ali ndi mphamvu zonse. Kodi zamuchititsa kukhala ndi khalidwe loipa lililonse? Ndithudi ayi! Monga taonera, iye ndi woyera, ndi wosaipitsidwa m’pang’ono pomwe. Yehova ndi wosiyana ndi amuna ndi akazi opanda ungwiro omwe ali ndi mphamvu pa zinthu za m’dziko la khalidwe loipali. Iye sanagwiritsepo ntchito molakwa mphamvu zake, ndiponso sadzatero.

19, 20. (a) Kodi nthaŵi zonse Yehova amasonyeza mphamvu zake mogwirizana ndi makhalidwe ena ati, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zili zokhazika mtima pansi? (b) Kodi kudziletsa kwa Yehova mungakufanizire motani, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi n’zokondweretsa kwa inu?

19 Kumbukirani kuti mphamvu ndi mbali imodzi chabe ya umunthu wa Yehova. M’tsogolomu tiphunziranso za chilungamo chake, nzeru zake, ndi chikondi chake. Koma tisalingalire kuti Yehova amaonetsa makhalidwe ake mongoti khalidwelo lionekere basi zivute zitani, ngati kuti anangosonyeza khalidwe limodzi lokhalo panthaŵiyo. M’malo mwake, tiona m’mitu yotsatirayi kuti nthaŵi  zonse Yehova amasonyeza mphamvu zake mogwirizana ndi chilungamo chake, nzeru zake, ndi chikondi chake. Talingalirani khalidwe lina limene Mulungu ali nalo, khalidwe limene limaoneka kamodzikamodzi mwa atsogoleri a dzikoli—kudziletsa.

20 Tayerekezani kuti mwakumana ndi munthu wamkulu kwambiri ndi wamphamvu moti akukuchititsani mantha. Komano m’kupita kwa nthaŵi, mukuona kuti akuoneka kukhala wodekha. Nthaŵi zonse, iye ndi wokonzeka ndi wofunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zake pothandiza ndi kuteteza anthu, makamaka osoŵa chitetezo ndi ofooka. Sagwiritsa ntchito mphamvu zake molakwa. Mukuona anthu akumuneneza popanda zifukwa zomveka konse, koma khalidwe lake silikusintha; ndi wa phee, waulemu wake, komanso wokoma mtima. Mungayambe kudabwa ngati inunso mukanatha kukhala wodekha ndi wodziletsa chomwecho, makamaka ngati munali wamphamvu mofanana ndi iyeyo! Pamene mukumudziŵa bwino munthuyu, kodi simungayambe kumva kuti mukuyandikana naye? Tili ndi zifukwa zomveka kwambiri zoyandikirira kwa Yehova wamphamvuyonse. Talingalirani chiganizo chonse pamene pachokera mutu wa nkhani ino: ‘Yehova ndiye wolekerera mkwiyo, koma wa mphamvu yaikulu.’ (Nahumu 1:3) Yehova safulumira kugwiritsa ntchito mphamvu zake pokhaulitsa anthu, ngakhale anthu oipa. Iye sakwiya msanga ndipo ndi wokoma mtima. Ngakhale kuti nthaŵi zambiri  anthu amamuputa, waonetsadi kuti ndi “wolekerera mkwiyo.”—Salmo 78:37-41.

21. N’chifukwa chiyani Yehova sakakamiza anthu kuti azichita chifuno chake, ndipo kodi zimenezi zikutiphunzitsanji ponena za iye?

21 Talingalirani kudziletsa kwa Yehova mwa njira ina. Ngati inu munali ndi mphamvu pa kalikonse, kodi muganiza kuti bwenzi panthaŵi ina mukulakalaka kuchititsa anthu kuchita zinthu m’njira imene inuyo mukufuna? Yehova, ngakhale kuti ali ndi mphamvu zonse, sakakamiza anthu kuti amutumikire. Ngakhale kuti kutumikira Mulungu ndiyo njira yokha yopezera moyo wosatha, Yehova satikakamiza kumutumikira. M’malo mwake, iye amalemekeza munthu aliyense pomupatsa ufulu wosankha. Amachenjeza zimene zimatsatirapo ngati munthu wasankha mopusa ndipo amalongosola mapindu a kusankha mwanzeru. Komano iye amatisiya kuti tisankhe tokha chochita. (Deuteronomo 30:19, 20) Yehova sasangalatsidwa kuti munthu azimutumikira chifukwa chokakamizidwa kapena chifukwa choopsedwa ndi mphamvu zake zazikulu. Amafunafuna omwe angamutumikire modzifunira chifukwa chomukonda.—2 Akorinto 9:7.

22, 23. (a) N’chiyani chikusonyeza kuti Yehova amasangalala kupatsa ena mphamvu? (b) Tiphunzira chiyani m’mutu wotsatira?

22 Tiyeni tione chifukwa chomalizira chimene sitifunikira kuopsedwa ndi Mulungu Wamphamvuyonse. Anthu amphamvu amaopa kupatsako ena mphamvu zawo. Komatu Yehova amasangalala kupatsa mphamvu omulambira okhulupirika. Amapatsa ena, mwachitsanzo Mwana wake, mphamvu zochuluka ndithu. (Mateyu 28:18) Yehova amapatsanso mphamvu atumiki ake m’njira inanso. Baibulo limati: “Ukulu, ndi mphamvu, ndi ulemerero, ndi kulakika, ndi chifumu ndi zanu, Yehova; pakuti zonse zam’mwamba ndi za pa dziko lapansi ndi zanu. . . . M’dzanja mwanu muli mphamvu yaikulu; kukuza ndi kupatsa onse mphamvu kuli m’dzanja lanu.”—1 Mbiri 29:11, 12.

23 Inde, Yehova adzakhala wokondwa kukupatsani nyonga. Iye amaperekanso “ukulu woposa wamphamvu” kwa amene akufuna kumutumikira. (2 Akorinto 4:7) Kodi simukumva kukhala woyandikana ndi Mulungu wamphamvu wotereyu, amene amagwiritsa ntchito mphamvu zake mokoma mtima ndi mwa miyezo yapamwamba yotereyi? M’mutu wotsatira, tiona mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake polenga.

^ ndime 6 Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “Wamphamvuyonse” amatanthauza kuti “Wolamulira pa Zonse; Amene Ali ndi Mphamvu Zonse.”

^ ndime 15 Baibulo limati ‘Yehova sanakhala mu mphepomo . . . , m’chivomezicho . . . , m’motomo.’ Mosiyana ndi anthu amene amalambira milungu yongopeka ya zolengedwa, atumiki a Yehova samufunafuna mu mphamvu za chilengedwe. Iye ndi wamkulu kwambiri, sangakwanire kukhala m’chilichonse chimene analenga.—1 Mafumu 8:27.