1-3. (a) Kodi Aigupto anaopsa Aisrayeli motani? (b) Kodi Yehova anamenyera nkhondo motani anthu ake?

AISRAYELI anali atapanikizika pakati pa mapiri ovuta kukwera ndi nyanja yoti sakanatha kuwoloka. Gulu lankhondo la Aigupto, gulu lankhanza lomwe linali kupha anthu mopanda chifundo, linali kuwathamangira litatsimikiza mtima kuwafafaniziratu. * Komabe Mose analimbikitsa anthu a Mulungu kuti asataye mtima. Anawatsimikizira kuti: “Yehova adzakugwirirani nkhondo.”—Eksodo 14:14.

2 Ngakhale zinali tero, zikuoneka kuti Mose anafuulira kwa Yehova, ndipo Mulungu anamuyankha kuti: “Ufuuliranji kwa ine? . . . Nyamula ndodo yako, nutambasulire dzanja lako kunyanja, nuigaŵe.” (Eksodo 14:15, 16) Tayerekezerani kuti mukuona zinthu zimene zikuyamba kuchitika. Mwamsangamsanga Yehova akulamula mngelo, ndipo mtambo ukuchoka kutsogolo kwa Aisrayeli nukaima kumbuyo kwawo, mwinamwake ukuyala monga khoma ndi kutsekereza Aigupto kuti asaukire. (Eksodo 14:19, 20; Salmo 105:39) Mose akutambasula dzanja lake. Nyanjayo ikugaŵika pakati ndi mphepo yamphamvu imene ikukankha madzi. Mwanjira inayake madziwo akuunjikana naima chilili ngati makoma. Akupanga njira yaikulu yokwana kudutsapo mtundu wonsewo!—Eksodo 14:21; 15:8.

3 Atasonyezedwa mphamvu zazikulu chonchi, Farao anayenera kulamula asilikali ake kuti abwerere kwawo. Koma m’malo mwake, Farao wonyadayo akulamula kuti amenye nkhondo. (Eksodo 14:23) Mosalingalira konse Aiguptowo akuloŵa m’nyanjamo pothamangira Aisrayeliwo, koma mosakhalitsa pa gulu  lawo pabuka chipwirikiti chifukwa choti mawiro a magaleta awo ayamba kuzuka. Pamene Aisrayeli afika tsidya linalo, Yehova akulamula Mose kuti: “Tambasulira dzanja lako kunyanja, kuti madziwo abwerere kudzamiza Aigupto, magaleta awo, ndi apakavalo awo.” Makoma a madziwo akugwa ndipo akukwirira Farao ndi ankhondo ake!—Eksodo 14:24-28; Salmo 136:15.

Pa Nyanja Yofiira, Yehova anakhala munthu “wankhondo”

4. (a) Kodi pa Nyanja Yofiira Yehova anakhala ndani? (b) Kodi anthu ena angamve bwanji pokhala ndi chithunzi choterechi cha Yehova m’maganizo mwawo?

4 Kulanditsidwa kwa mtundu wa Israyeli pa Nyanja Yofiira kunali chinthu chosaiwalika m’mbiri ya zochita za Mulungu ndi anthu. Pa nyanjayo Yehova anakhaladi munthu “wankhondo.” (Eksodo 15:3) Komabe, kodi inuyo mukumva bwanji pokhala ndi chithunzi choterechi cha Yehova? Kunena zoona, nkhondo zavutitsa anthu kwambiri ndi kuwasoŵetsa mtendere. Kodi mwinatu m’malo mokhala ndi mtima woyandikana ndi Mulungu mumalephera kumuyandikira chifukwa cha mmene iye amagwiritsira ntchito mphamvu zowononga?

Kusiyana kwa Nkhondo za Mulungu ndi Mikangano ya Anthu

5, 6. (a) N’chifukwa chiyani Mulungu amatchedwa moyenerera kuti “Yehova wa makamu”? (b) Kodi nkhondo za Mulungu zimasiyana motani ndi nkhondo za anthu?

5 M’zinenero zoyambirira za Baibulo, Mulungu amapatsidwa dzina laudindo lakuti “Yehova wa makamu” nthaŵi zotsala pang’ono kukwana 300 m’Malemba Achihebri ndipo nthaŵi ziŵiri m’Malemba Achigiriki Achikristu. (1 Samueli 1:11) Pokhala kuti ndi Wolamulira Wamkulu, Yehova amalamulira gulu lankhondo lalikulu la makamu a angelo. (Yoswa 5:13-15; 1 Mafumu 22:19) Gulu lankhondo limeneli lingathe kuwononga mochititsa mantha kwabasi. (Yesaya 37:36) Kuphedwa kwa anthu sikusangalatsa pokuganizira. Komabe, tikumbukire kuti nkhondo za Mulungu n’zosiyana ndi mikangano yopanda pake ya anthu. Atsogoleri ankhondo ndi andale nthaŵi zina amanena kuti anali ndi zolinga zabwino poputa anzawo. Koma pa  nkhondo za anthu nthaŵi zonse pamakhala dyera ndi kudzikonda.

6 Mosiyana ndi anthu, Yehova sachita zinthu mongotengeka mtima. Deuteronomo 32:4 amati: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” Mawu a Mulungu amatsutsa kukhala ndi mkwiyo wosalamulirika, nkhanza, ndi chiwawa. (Genesis 49:7; Salmo 11:5) Motero Yehova sachita kanthu popanda chifukwa chomveka. Mphamvu zake zowononga amazigwiritsa ntchito mosamala kwambiri ndiponso pakakhala kuti palibe njira ina yothetsera vutolo. Zili monga ananenera mwa mneneri wake Ezekieli kuti: “Ngati ndikondwera nayo imfa ya woipa? ati Ambuye Yehova, si ndiko kuti abwerere kuleka njira yake, ndi kukhala ndi moyo?”—Ezekieli 18:23.

7, 8. (a) Kodi molakwa Yobu ananena chiyani za kuvutika kwake? (b) Kodi Elihu anawongolera motani kuganiza kwa Yobu pa nkhaniyi? (c) Kodi tingaphunzirepo chiyani pa zimene zinachitikira Yobu?

7 Nangano n’chifukwa chiyani Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zowononga? Tisanayankhe funsoli, tingakumbukire za Yobu yemwe anali munthu wolungama. Satana anakayikira ngati Yobu, komanso munthu wina aliyense, angakhalebe wokhulupirika poyesedwa. Yehova anayankha zokayikira za Satanazo mwa kumulola kuti ayese kukhulupirika kwa Yobu. Chotsatira chake chinali chakuti Yobu anavutika ndi matenda, kuwonongeka kwa chuma chake, ndi kufa kwa ana ake. (Yobu 1:1–2:8) Posadziŵa nkhani zomwe zinali kuloŵetsedwamo, molakwa Yobu anati anali kuvutika chifukwa Mulungu anali kumulanga popanda chifukwa. Anafunsa Mulungu chifukwa chimene anamuikira kukhala “chandamali” Chake, “mdani” Wake.—Yobu 7:20; 13:24.

8 Mnyamata wina wotchedwa Elihu anaonetsa poyera kuti Yobu anali kuganiza molakwika nanena kuti: “Mukuti, Chilungamo changa chiposa cha Mulungu.” (Yobu 35:2) Inde, n’kupanda nzeru kuganiza kuti tikudziŵa bwino kuposa Mulungu kapena kulingalira kuti iye wachita mosayenera. “N’kutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama,”  analengeza motero Elihu. Pambuyo pake anati: “Kunena za Wamphamvuyonse, sitingamusanthule; ndiye wa mphamvu yoposa; koma mwa chiweruzo ndi chilungamo chochuluka samasautsa.” (Yobu 34:10; 36:22, 23; 37:23) Tingakhale otsimikiza kuti pamene Mulungu amenya nkhondo, amakhala ndi zolinga zabwino. Tili ndi zimenezi m’malingaliro, tiyeni tifufuze zina mwa zifukwa zimene Mulungu wamtendereyo nthaŵi zina amakhalira munthu wankhondo.—1 Akorinto 14:33.

Chimene Chimakakamiza Mulungu wa Mtendere Kumenya Nkhondo

9. N’chifukwa chiyani Mulungu wa mtendere amamenya nkhondo?

9 Atatamanda Mulungu monga munthu “wankhondo,” Mose ananena kuti: “Afanana ndi inu ndani mwa milungu, Yehova? Afanana ndi inu ndani, wolemekezedwa, woyera?” (Eksodo 15:11) Mneneri Habakuku analemba mawu ofanana ndi ameneŵa kuti: “Inu wa maso osalakwa, osapenya choipa, osakhoza kupenyerera chovuta.” (Habakuku 1:13) Ngakhale kuti Yehova ndi Mulungu wa chikondi, alinso Mulungu wa chiyero, ndi chilungamo. Nthaŵi zina, makhalidwe ameneŵa amamukakamiza kugwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga. (Yesaya 59:15-19; Luka 18:7) Motero Mulungu saipitsa chiyero chake pamene amenya nkhondo. Koma m’malo mwake, amamenya nkhondo chifukwa chakuti ndi woyera.—Eksodo 39:30.

10. (a) Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene kwanthaŵi yoyamba kunakhala kofunika kuti Mulungu amenye nkhondo? (b) Kodi njira yokha yothetsera chidani chonenedweratu pa Genesis 3:15 ndi yotani, nanga zimenezo zidzabweretsa madalitso otani kwa anthu olungama?

10 Talingalirani za zimene zinachitika pambuyo poti anthu aŵiri oyambirirawo, Adamu ndi Hava, apandukira Mulungu. (Genesis 3:1-6) Ngati Yehova akananyalanyaza kusalungama kwawo, udindo wake monga Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse ukanaoneka wotsika. Pokhala Mulungu wachilungamo, sakanachitira mwina koma kuwapatsa chilango cha imfa. (Aroma 6:23) Mu ulosi woyambirira wa m’Baibulo, iye ananeneratu kuti padzakhala udani pakati pa atumiki ake  ndi otsatira “njoka,” Satana. (Chivumbulutso 12:9; Genesis 3:15) M’kupita kwa nthaŵi, chidani chimenechi chidzatha kokha mwa kuphwanya Satana. (Aroma 16:20) Komatu chiweruzo chimenecho chidzabweretsa madalitso ochuluka kwa anthu olungama, chidzachotsa zochita za Satana ndi kutsegula njira yoti padziko lonse pakhale paradaiso. (Mateyu 19:28) Mpaka panthaŵiyo, awo amene akhalira Satana kumbuyo aziopsezabe anthu a Mulungu mwakuthupi ndi mwauzimu. Nthaŵi zina Yehova afunika kuloŵererapo.

Mulungu Amachitapo Kanthu Kuti Achotse Kuipa

11. N’chifukwa chiyani Mulungu anakakamizika kubweretsa chigumula padziko lonse?

11 Chigumula cha m’masiku a Nowa ndi chitsanzo cha kuloŵererapo kwa Mulungu kumeneko. Genesis 6:11, 12 amati: “Dziko lapansi linavunda pamaso pa Mulungu, dziko lapansi ndipo linadzala ndi chiwawa. Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yawo pa dziko lapansi.” Kodi Mulungu akanalola anthu oipa kuthetseratu makhalidwe abwino onse padziko lapansi? Ayi. Yehova anakakamizika kubweretsa chigumula padziko lonse kuti achotsepo anthu amene anali kuumirira za chiwawa ndiponso makhalidwe oipa.

12. (a) Kodi Yehova ananena chiyani za “mbewu” ya Abrahamu? (b) N’chifukwa chiyani Aamori anali kudzafafanizidwa?

12 Zinalinso choncho ndi chiweruzo cha Mulungu pa Akanani. Yehova anati mwa Abrahamu mudzatuluka “mbewu” imene ikadalitsa mabanja onse a dziko lapansi. Mogwirizana ndi cholinga chimenecho, Mulungu analamula kuti ana a Abrahamu adzapatsidwa dziko la Kanani, dziko limene munali kukhala anthu otchedwa Aamori. Kodi Mulungu angakhale n’chifukwa chomveka chotani kuti akakamize anthuŵa kuchoka m’dziko lawo? Yehova ananena kuti anthuwo akawathamangitsa m’dziko lawolo patapita zaka ngati 400, kufikira ‘mphulupulu za Aamori zitakwanira.’ * (Genesis 12:1-3; 13:14, 15; 15:13, 16; 22:18)  Pa nyengo imeneyo, makhalidwe a Aamori anaipa kwambiri. Dziko la Kanani linadzala ndi kulambira mafano, kuphana, ndi chiwerewere. (Eksodo 23:24; 34:12, 13; Numeri 33:52) Anthu a m’dzikolo anali kuphanso ana powapereka nsembe pamoto. Kodi Mulungu woyera angalole anthu ake kukhala pakati pa zoipa zoterozo? Ayi! Iye anati: “Dziko lomwe lidetsedwa; chifukwa chake ndililanga, ndi dzikoli lisanza okhala m’mwemo.” (Levitiko 18:21-25) Komabe Yehova sanaphe anthuwo mwachisawawa. Akanani onse ofuna moyo, monga ngati Rahabi ndi Agibeoni, anawapulumutsa.—Yoswa 6:25; 9:3-27.

Kumenya Nkhondo Chifukwa cha Dzina Lake

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani Yehova anakakamizika kuyeretsa dzina lake? (b) Kodi Yehova anachotsa motani chitonzo pa dzina lake?

13 Chifukwa choti Yehova ndi woyera, dzina lakenso ndi loyera. (Levitiko 22:32) Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kupemphera kuti: “Dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:9) Kupanduka kwa mu Edene kunanyoza dzina la Mulungu, ndipo kunayambitsa kukayikira makhalidwe a Mulungu ndi mmene amalamulirira. Yehova sakanalekerera miseche ndi kupanduka koteroko. Iye anakakamizika kuti achotse chitonzo chonse pa dzina lake.—Yesaya 48:11.

14 Talingaliraninso za Aisrayeli. Kwanthaŵi yonse yomwe anali akapolo ku Igupto, lonjezo la Mulungu kwa Abrahamu lakuti mwa Mbewu yake mabanja onse a dziko lapansi adzadalitsidwa linaoneka kukhala losatheka. Koma mwa kuwalanditsa ndi kuwakhazikitsa kukhala mtundu, Yehova anachotsa chitonzo chonse pa dzina lake. Motero mneneri Danieli popemphera anakumbukira kuti: “Ambuye Mulungu wathu, . . . munatulutsa anthu anu m’dziko la Aigupto ndi dzanja lamphamvu, ndi kudzitengera mbiri [“dzina,” NW].”—Danieli 9:15.

15. N’chifukwa chiyani Yehova analanditsa Ayuda ku ukapolo ku Babulo?

15 Chochititsa chidwi n’chakuti, Danieli anapemphera chomwechi panthaŵi imene Ayuda anali kufuna kuti Yehova achitenso zinthu chifukwa cha dzina Lake. Ayuda osamverawo  anali mu ukapolo, koma tsopano ku Babulo. Likulu la dziko lawo, Yerusalemu, linali bwinja lokhalokha. Danieli anadziŵa kuti ngati Ayuda atabwereranso kwawo ndiye kuti dzina la Yehova lidzakwezedwa. Choncho Danieli anapemphera kuti: ‘Ambuye, khululukirani; Ambuye, mverani nimuchite; musachedwa, chifukwa cha inu nokha, Mulungu wanga; pakuti mudzi wanu ndi anthu anu anatchedwa dzina lanu.’Danieli 9:18, 19.

Kumenyera Nkhondo Anthu Ake

16. Fotokozani chifukwa chake kufunitsitsa kwa Yehova kuteteza dzina lake sikutanthauza kuti salingalira ena kayanso kuti ndi wodzikonda.

16 Kodi pokhala wofunitsitsa kuteteza dzina lake ndiye kuti Yehova salingalira ena kapena kuti ndi wodzikonda? Ayi, chifukwa pamene achita zinthu mogwirizana ndi chiyero chake ndi kukonda chilungamo kwake, iye amateteza anthu ake. Talingalirani nkhani ya mu Genesis chaputala 14. M’chaputalachi timaŵerengamo za mafumu anayi amene pankhondo anagwira Loti, mphwake wa Abrahamu pamodzi ndi banja lake lomwe. Mothandizidwa ndi Mulungu, Abrahamu mosayembekezeka anagonjetsa chigulu cha asilikali amphamvu! Nkhani ya kupambana kumeneku ndithudi inali yoyamba kulembedwa “m’buku la Nkhondo za Yehova,” buku limene mwachionekere munalembedwanso nkhondo zina zomwe sizinatchulidwe m’Baibulo. (Numeri 21:14) Kupambana nkhondo zina zambiri kunali kudzatsatirapo.

17. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova anamenyera nkhondo Aisrayeli ataloŵa m’dziko la Kanani? Perekani zitsanzo.

17 Aisrayeli atatsala pang’ono kuloŵa m’dziko la Kanani, Mose anawatsimikizira kuti: “Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, Iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakuchitirani m’Aigupto.” (Deuteronomo 1:30; 20:1) Kuyambira pa Yoswa, yemwe analoŵa m’malo mwa Mose, n’kupitirira m’nthaŵi ya Oweruza ndi ya mafumu okhulupirika a Yuda, Yehova anamenyeradi nkhondo anthu ake. Anawathandiza kugonjetsa modabwitsa adani awo pa nkhondo zambiri.—Yoswa 10:1-14; Oweruza 4:12-17; 2 Samueli 5:17-21.

18. (a) Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kuyamikira kuti Yehova sanasinthe? (b) Kodi chidzachitike n’chiyani pamene udani wofotokozedwa pa Genesis 3:15 ufika pachimake?

 18 Yehova sanasinthe; cholinga chakenso choti dzikoli likhale paradaiso wamtendere sichinasinthe. (Genesis 1:27, 28) Mpaka pano Mulungu amadana ndi kuipa. Panthaŵi imodzimodziyo, anthu ake amawakonda kwambiri ndipo posachedwapa adzachitapo kanthu kuti awathandize. (Salmo 11:7) Inde, udani wofotokozedwa pa Genesis 3:15 ukuyembekezeka kutheratu posachedwa pompa, ndipotu mwachiwawa tsono. Kuti ayeretse dzina lake ndi kuteteza anthu ake, Yehova adzakhalanso munthu “wankhondo”!—Zekariya 14:3; Chivumbulutso 16:14, 16.

19. (a) Perekani fanizo losonyeza kuti tingamuyandikire Mulungu chifukwa chakuti amagwiritsa ntchito mphamvu zowononga. (b) Kodi kufunitsitsa kwa Mulungu kumenya nkhondo kuyenera kutikhudza motani?

19 Talingalirani fanizo ili: Tiyerekeze kuti chilombo choopsa chikufuna kugwira banja la munthu winawake ndiyeno mwamunayo akuyamba kuthandiza banja lakelo mpaka kupha chilombocho. Kodi mungayembekeze mkazi wake ndi ana ake kumachita naye mantha chifukwa cha zimenezi? Ayi, koma m’malo mwake mungayembekeze kuti iwo alimbikitsidwe ndi  chikondi chake chodzimana pa iwo. Mofananamo, sitiyenera kuopsedwa chifukwa chakuti Mulungu amagwiritsa ntchito mphamvu zowononga. Tiyenera kumukonda kwambiri poona kuti amafunitsitsa kumenya nkhondo potiteteza. Tiyeneranso kulemekeza kwambiri mphamvu zake zopanda malire. Motero, ‘tingatumikire Mulungu mwa kumuchitira ulemu ndi mantha.’—Ahebri 12:28.

Yandikirani kwa Munthu “Wankhondo”

20. Pamene tiŵerenga nkhani za m’Baibulo za nkhondo za Mulungu zomwe sitikuzimvetsetsa, kodi tiyenera kuchitanji, ndipo n’chifukwa chiyani?

20 Sikuti Baibulo limalongosola zifukwa zake Yehova anasankha kumenya nkhondo iliyonse mwa njira imene anaimenyerayo. Koma nthaŵi zonse tingakhale otsimikiza za mfundo iyi: Yehova sagwiritsa ntchito mphamvu zowononga mopanda chilungamo, mwanjiru, kayanso mwankhanza. Nthaŵi zambiri, kulingalira nkhani yake yonse m’Baibulo kapena pamene nkhaniyo inayambira kungatithandize kuona zinthu moyenera. (Miyambo 18:13) Ngakhale pamene sitikudziŵa mfundo zake zonse, kuphunzira kwambiri za Yehova ndi kusinkhasinkha pa makhalidwe ake ochititsa kaso kungatithandize kuchotsa malingaliro okayikira alionse amene tingakhale nawo. Pamene tichita zimenezi, timaona kuti tili ndi zifukwa zokwanira zodalirira Mulungu wathu, Yehova.—Yobu 34:12.

21. Ngakhale kuti nthaŵi zina Yehova amakhala munthu “wankhondo,” kodi iye amakondanji?

21 Ngakhale kuti Yehova amakhala munthu “wankhondo” pamene kuli kofunika kutero, zimenezi sizikutanthauza kuti iye ndi wokonda nkhondo. M’masomphenya a Ezekieli a galeta lakumwamba, Yehova akuoneka kukhala wokonzeka kumenyana ndi adani ake. Komatu Ezekieli anaona Mulungu atazunguliridwa ndi utawaleza womwe ndi chizindikiro cha mtendere. (Genesis 9:13; Ezekieli 1:28; Chivumbulutso 4:3) Ndithudi, Yehova ndi wofatsa ndi wokonda mtendere. “Mulungu ndiye chikondi,” analemba motero mtumwi Yohane. (1 Yohane 4:8) Yehova amaonetsa makhalidwe ake onse mosamala bwino. Koma ndiyetu tili ndi mwayi waukulu zedi kuti tikhoza kuyandikana ndi Mulungu wamphamvu komanso wachikondi wotereyu!

^ ndime 1 Malinga n’kunena kwa wolemba mbiri wachiyuda Josephus, Ahebri anali “kuwalondola ndi magaleta 600 limodzi ndi amuna 50,000 okwera pa akavalo komanso namtindi wa asilikali oyenda pansi okwana 200,000.”—Jewish Antiquities, II, 324 [xv, 3].

^ ndime 12 Mawu akuti “Aamori” panopo ayenera kuti akuphatikizapo anthu onse a m’Kanani.—Deuteronomo 1:6-8, 19-21, 27; Yoswa 24:15, 18.