1, 2. Kodi anthu lerolino amatayikiridwa zinthu zotani, nanga zimenezi zimatikhudza motani?

MWANA wataya kapena wawononga chidole chake chimene amachikonda kwambiri ndipo akulira momvetsa chisoni. Akuchititsatu chifundo kwambiri! Komabe, kodi munayamba mwaonapo mmene nkhope ya mwana imawalira pamene kholo limupezeranso chimene anataya? Kwa khololo, siingakhale nkhani yovuta kupeza chidolecho ngakhale kuchikonzanso. Koma mwanayo chimwemwe chadzaza tsaya ndipo akungodabwa kuti zachitika bwanji. Chomwe chimaoneka kuti chatayika mpaka kalekale achibwezeretsa!

2 Yehova, Kholo labwino koposa, ali ndi mphamvu zobwezeretsa zinthu zimene ana ake a padziko lapansi angaone ngati zinatayikiratu. Sikuti zinthu zake tikunena zidole. Mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zino, timatayikiridwa zinthu zofunika kwambiri. (2 Timoteo 3:1-5) Zinthu zambiri zimene anthu amaikirapo mtima wawo zikuoneka kukhala zili pangozi nthaŵi zonse; zinthu monga nyumba, katundu, ntchito, ngakhalenso thanzi. Timachitanso mantha tikalingalira za kuwonongeka kwa chilengedwe ndi kuti chotsatirapo chake n’chakuti mitundu yambirimbiri ya zamoyo ikutheratu psiti. Koma palibe chimene chimatipweteka mofanana ndi imfa ya munthu yemwe timam’konda. Timathedwa nzeru podzimva kuti tataya munthu komanso tilibe ndi mphamvu zomwe.—2 Samueli 18:33.

3. Kodi n’chiyembekezo cholimbikitsa chotani chimene chili pa Machitidwe 3:21, ndipo kodi Yehova adzachikwaniritsa pogwiritsa ntchito chiyani?

3 Motero n’zolimbikitsatu kwambiri kuphunzira za mphamvu za Yehova zobwezeretsa zinthu! Monga momwe tionere, pali zinthu zambirimbiri zimene Mulungu angabwezeretse ndiponso zimene adzabwezeretsa kwa ana ake a padziko lapansi. Ndipo Baibulo limasonyeza kuti Yehova amafuna ‘kukonzanso zinthu zonse.’ (Machitidwe 3:21) Kuti akwaniritse zimenezi, Yehova adzagwiritsa ntchito Ufumu Waumesiya, womwe wolamulira wake ndi Mwana  wake, Yesu Kristu. Umboni umasonyeza kuti Ufumu umenewu unayamba kulamulira kumwamba mu 1914. * (Mateyu 24:3-14) Kodi adzabwezeretsa chiyani? Tiyeni tilingalire zina mwa ntchito zikuluzikulu za Yehova za kubwezeretsa. Imodzi mwa zimenezi tingaione ndi kuizindikira pakali pano. Zina zidzachitika pamlingo wokulirapo m’tsogolo muno.

Kubwezeretsa Kulambira Koyera

4, 5. N’chiyani chinachitikira anthu a Mulungu mu 607 B.C.E., ndipo kodi Yehova anawapatsa chiyembekezo chotani?

4 Chinthu china chimene Yehova wabwezeretsa kale ndi kulambira koyera. Kuti timvetse bwino zimenezi, tiyeni tiphunzire mwachidule mbiri ya ufumu wa Yuda. Pophunzira zimenezi tidzasangalala kudziŵa mmene Yehova wakhala akugwiritsira ntchito mphamvu zake zobwezeretsa.—Aroma 15:4.

5 Taganizirani mmene Ayuda okhulupirika anali kumvera mu 607 B.C.E. pamene Yerusalemu anawonongedwa. Mzinda umene anali kuukonda unaphwasulidwa; makoma ake anagwetsedwa. Choipa kwambiri chinali chakuti kachisi waulemerero amene Solomo anamanga, likulu la kulambira Yehova koyera pa dziko lonse, anamusiya ali bwinja. (Salmo 79:1) Amene anapulumuka anawatenga kukakhala akapolo ku Babulo, ndipo dziko lawo analisiya lili bwinja momwe munayamba kukhala nyama za m’tchire. (Yeremiya 9:11) Malinga n’kuona kwa anthu, panalibe chabwino chilichonse. (Salmo 137:1) Koma Yehova, yemwe anali atanena kale za chiwonongeko chimenechi, anapereka chiyembekezo chakuti nthaŵi yobwezeretsa zimenezi idzafika.

6-8. (a) Kodi ndi nkhani iti imene imapezeka mobwerezabwereza mu zolemba za aneneri achihebri, nanga maulosi amenewo anakwaniritsidwa motani poyamba? (b) M’nthaŵi zamakono zino, kodi anthu a Mulungu aona motani kukwaniritsidwa kwa maulosi ambiri a kubwezeretsa?

6 Ndipotu kubwezeretsa zinthu inali nkhani imene aneneri achihebri  anali kuibwereza kaŵirikaŵiri mu zolemba zawo. * Yehova, mwa aneneriŵa, analonjeza kuti dzikolo lidzabwereranso mwakale; mudzakhalanso anthu, lidzakhala lachonde, ndi lotetezeka ku nyama zolusa ndiponso kwa adani. Iye analongosola dziko lawo lobwezeretsedwalo monga paradaiso weniweni! (Yesaya 65:25; Ezekieli 34:25; 36:35) Koposa zonse, anali kudzayambiranso kulambira koyera ndi kumanganso kachisi. (Mika 4:1-5) Maulosi ameneŵa anapatsa Ayuda amene anali mu ukapolowo chiyembekezo chabwino, ndipo anawathandiza kupirira ukapolo wawowo wa zaka 70 ku Babulo.

7 M’kupita kwa nthaŵi, nthaŵi yobwezeretsa inakwana. Ayuda atamasuka ku Babulo anabwerera ku Yerusalemu namanganso kachisi wa Yehova. (Ezara 1:1, 2) Yehova ankawadalitsa ndi kupatsa chonde dziko lawo ndiponso kulilemeretsa, malinga ngati kulambira kwawo kunali koyera. Anawateteza kwa adani awo ndi ku nyama zolusa zomwe zinkakhala m’dziko lawolo kwa zaka zambirimbiri. Ayeneratu kuti anasangalala kwambiri ndi mphamvu zobwezeretsa za Yehova! Komabe zochitika zimenezo zinali kukwaniritsidwa koyamba ndiponso kochepa chabe kwa maulosi a kubwezeretsa zinthu. Kukwaniritsidwa kwakukulu kunali kudzachitika mu “masiku otsiriza,” masiku athu ano, pamene Woloŵa Ufumu wa Mfumu Davide wolonjezedwa kalekalelo akakhala pa mpando wachifumu.—Yesaya 2:2-4; 9:6, 7.

8 Yesu atakhala pa mpando wachifumu mu Ufumu wakumwamba m’chaka cha 1914, mosakhalitsa anayamba kusamalira zofunika zauzimu za anthu a Mulungu okhulupirika padziko lapansi. Monga momwe Koresi, wogonjetsa wa ku Perisiya, anamasulira Ayuda otsala ku Babulo mu 537 B.C.E., Yesu anamasulanso otsalira a Ayuda auzimu, otsatira ake. Anawamasula ku zochita za Babulo wamakono, ufumu wadziko lonse wa zipembedzo zonyenga. (Aroma 2:29; Chivumbulutso 18:1-5) Kuchokera m’chaka cha 1919 kupita m’tsogolo, kulambira koyera kwabwezeretsedwa pa malo ake oyenera m’miyoyo ya Akristu enieni. (Malaki 3:1-5) Kuyambira nthaŵi imeneyo, anthu a Yehova akhala akumulambira mu kachisi wake wauzimu woyeretsedwa, yemwe ndi makonzedwe a Mulungu a kulambira koyera. N’chifukwa chiyani zimenezi zili zofunika kwa ife lerolino?

 Chifukwa Chake Kubwezeretsa Kwauzimu Kuli Kofunika

9. Atumwi onse atafa, kodi Matchalitchi Achikristu anachita zotani zokhudzana ndi kulambira Mulungu, koma kodi Yehova wachitanji m’masiku athu ano?

9 Talingalirani zimene zakhala zikuchitika. Akristu kalelo m’zaka 100 zoyambirira za nyengo yathu ino anasangalala ndi madalitso auzimu ambiri. Koma Yesu ndi atumwi ananeneratu kuti kulambira koona kudzaipitsidwa mpaka kuzimiririka. (Mateyu 13:24-30; Machitidwe 20:29, 30) Atumwi onse atafa, panabadwa Matchalitchi Achikristu. Atsogoleri a matchalitchiŵa anatengera ziphunzitso ndi zochitika zachikunja. Anachititsanso kuti kufikira Mulungu kukhale kovuta kwambiri. Anati Mulungu ndi Utatu womwe munthu sangaumvetsetse ndipo anthu anali kuwaphunzitsa kuti machimo awo aziulula kwa ansembe komanso azipemphera kwa Mariya ndi kwa “oyera mtima” osiyanasiyana m’malo mopemphera kwa Yehova. Tsopano poti patha zaka mazana ochuluka pali mpatuko woterewu, kodi Yehova wachitanji? Mmene dziko lilili lerolinomu, dziko lodzala mabodza achipembedzo ndi makhalidwe osaopa Mulungu, iye waloŵererapo, nabwezeretsa kulambira koyera. Mosakokomeza, tinganene kuti kubwezeretsa kumeneku ndi chimodzi mwa zochitika zofunika kwambiri m’nthaŵi zathu zino.

10, 11. (a) Kodi ndi mbali ziŵiri ziti zimene paradaiso wauzimu akuphatikizapo, nanga inuyo zikukukhudzani motani? (b) Kodi Yehova wasonkhanitsa anthu otani mu paradaiso wauzimu, nanga adzakhala ndi mwayi woona chiyani?

10 Motero Akristu oona lerolino ali m’paradaiso wauzimu. Kodi paradaiso ameneyu akuphatikizapo chiyani? Pali mbali zikuluzikulu ziŵiri. Yoyamba ndiyo kulambira koyera kwa Mulungu woona, Yehova. Watipatsa kalambiridwe kopanda mabodza ndi kosapotoza ziphunzitso. Watipatsa chakudya chauzimu. Zimenezi zimatithandiza kuphunzira za Atate wathu wakumwamba, kumukondweretsa, ndi kuyandikana naye. (Yohane 4:24) Mbali yachiŵiri ya paradaiso wauzimu ikukhudza anthu. Monga ananenera Yesaya, mu “masiku otsiriza,” Yehova wawaphunzitsa njira za mtendere anthu omulambira. Wathetsa nkhondo pakati pathu. Ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, amatithandiza kuvala ‘umunthu watsopano.’ Amavomereza zochita zathu mwa kutipatsa mzimu woyera, umene umatichititsa kukhala ndi zipatso zabwino  kwambiri. (Aefeso 4:22-24; Agalatiya 5:22, 23) Mukamachita zinthu mogwirizana ndi mzimu wa Mulungu, mumakhaladi mu paradaiso wauzimu.

11 Yehova wasonkhanitsa mu paradaiso wauzimu ameneyu anthu amene amawakonda; anthu omwe amamukonda iye, amene amakonda mtendere, ndiponso amene ‘amazindikira zosoŵa zawo zauzimu.’ (Mateyu 5:3, NW) Amenewo ndiwo anthu omwe adzakhale ndi mwayi woona kubwezeretsa kwina kochititsa chidwi kwambiri—kubwezeretsa anthu ndiponso dziko lonse lapansi.

‘Taonani, Ndipanga Zonse Zikhale Zatsopano’

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani maulosi a kubwezeretsa ayenera kukwaniritsidwa m’njira inanso? (b) Kodi cholinga cha Yehova cha dziko lapansi n’chotani monga ananenera mu Edene, ndipo n’chifukwa chiyani zimenezi zimatipatsa chiyembekezo cha m’tsogolo?

12 Maulosi ochuluka a kubwezeretsa zinthu amanena zambiri kuposa kubwezeretsa kwauzimu kokha. Mwachitsanzo, Yesaya analemba kuti panthaŵi ina odwala, olemala, akhungu, ndi ogontha adzachiritsidwa ndipo ngakhale imfa yeniyeniyo idzamezedwa ku nthaŵi zonse. (Yesaya 25:8; 35:1-7) Malonjezo amenewo sanakwaniritsidwe mwakuthupi mu Israyeli wakale. Ndipo ngakhale kuti m’masiku athu ano taona maulosi ameneŵa akukwaniritsidwa mwauzimu, tili ndi zifukwa zokwanira zokhulupirira kuti m’tsogolomu adzakwaniritsidwa mwakuthupi ndiponso pamlingo waukulu. Kodi zimenezi tikuzidziŵa bwanji?

13 Kalelo mu Edene, Yehova sanabise cholinga chake cha dziko lapansi: Linali loti mukhale anthu achimwemwe, athanzi labwino, ndi ogwirizana. Amuna ndi akazi anafunika kusamalira dziko lapansili ndi zolengedwa zake zonse, nasandutsa dziko lonseli kukhala paradaiso. (Genesis 1:28) Zimenezo n’zosiyana kwambiri ndi mmene zinthu zilili panopa. Komabe, tingakhale n’chidaliro kuti zolinga za Yehova sizilephereka. (Yesaya 55:10, 11) Yesu, monga Mfumu Yaumesiya yoikidwa ndi Yehova, ndiye amene adzabweretse Paradaiso wa padziko lonse ameneyu.—Luka 23:43.

14, 15. (a) Kodi Yehova adzapanga zinthu ‘zonse kukhala zatsopano’ motani? (b) Kodi moyo udzakhala wotani m’Paradaiso, nanga inuyo n’chiyani chomwe chikukusangalatsani kwambiri?

14 Taganizirani kuti mwaona dziko lonse likusanduka Paradaiso!  Yehova akunena za nthaŵi imeneyo kuti: ‘Taonani, ndipanga zonse zikhale zatsopano.’ (Chivumbulutso 21:5) Talingalirani zomwe zimenezi zidzatanthauza. Pamene Yehova adzamaliza kugwiritsa ntchito pa dziko lakale lino mphamvu zake zowononga, padzatsala ‘miyamba yatsopano ndi dziko lapansi latsopano.’ Izi zikutanthauza kuti kuchokera kumwamba boma latsopano lidzalamulira anthu atsopano padziko lapansi omwe ndi anthu amene amakonda Yehova ndipo amachita chifuno chake. (2 Petro 3:13) Satana, limodzi ndi ziwanda zake, adzamuletsa kuchita kalikonse. (Chivumbulutso 20:3) Ndiyeno kwa nthaŵi yoyamba patapita zaka masauzande ambiri, anthu adzamasuka ku zoipitsa, zodanitsa, ndi zowononga zimenezo. Ndithudi anthu adzamva kukhala omasuka kwambiri.

15 Panthaŵiyo, tidzatha kusamalira dziko lokongolali monga momwe tinafunikira kuchitira poyambirirapo. Dziko lapansi lili ndi mphamvu zobwezeretsa zinthu lokha. Nyanja ndi mitsinje zoipitsidwa zikhoza kudziyeretsa ngati gwero la kuipitsako litachotsedwa; ndipo malo owonongeka chifukwa cha nkhondo akhoza kukhalanso bwinobwino ngati nkhondo zitatha. Zidzakhaladi zosangalatsa kwambiri kumachita zinthu mogwirizana ndi malamulo achilengedwe a dziko lapansi. Tidzathandiza dzikoli kukhala munda wonga paki, Edene wapadziko lonse wokhala ndi zomera ndi nyama zamitundumitundu! M’malo momawononga mwadala nyama ndi zomera, anthu adzakhala pamtendere ndi zolengedwa zonse za pa dziko lapansili. Ngakhalenso ana palibe chimene adzaopa pa nyama zakutchire.—Yesaya 9:6, 7; 11:1-9.

16. Mu Paradaiso, kodi ndi kubwezeretsa kotani kumene kudzakhudza munthu aliyense wokhulupirika?

16 Munthunso aliyense payekha adzabwezeretsedwa. Armagedo itatha, omwe adzapulumuke adzachiritsidwa mozizwitsa padziko lonse. Yesu adzagwiritsa ntchito mphamvu zake zopatsidwa ndi Mulungu kuti abwezeretse kuona kwa akhungu, kumva kwa ogontha, ndi matupi abwino kwa olemala ndi odwala, monga anachitira pamene anali padziko lapansi. (Mateyu 15:30) Okalamba adzasangalala kukhalanso ndi mphamvu ndi thanzi monga anyamata. (Yobu 33:25) Makwinya adzatha, manja ndi miyendo zidzawongoka, ndipo minofu idzakungana ndi mphamvu zatsopano. Anthu onse okhulupirika adzazindikira kuti zotsatirapo za uchimo ndi  kupanda ungwiro zikumka zichepa, kuti zikutha. Tidzamuyamikatu kwambiri Yehova Mulungu chifukwa cha mphamvu zake zazikulu zobwezeretsa zinthu! Tsopano tiyeni tikambirane mbali imodzi yokondweretsa kwambiri ya nthaŵi yosangalatsa imeneyi ya kubwezeretsa.

Kubwezera Moyo kwa Akufa

17, 18. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anadzudzula Asaduki? (b) N’zochitika zotani zimene zinachititsa Eliya kupempha Yehova kuti aukitse munthu?

17 M’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu ino, atsogoleri achipembedzo ena otchedwa Asaduki, sanakhulupirire za chiukiriro. Yesu anawadzudzula ndi mawu akuti: “Mungolakwa osadziŵa malembo, kapena mphamvu za Mulungu.” (Mateyu 22:29) Inde, Malemba amanena kuti Yehova ali ndi mphamvu zobwezeretsa zoterozo. Motani?

18 Talingalirani zimene zinachitika m’masiku a Eliya. Mkazi wamasiye ananyamula thupi lolobodoka la mwana wake mmodzi yekhayo. Mnyamatayo anali wakufa. Mneneri Eliya, yemwe anali mlendo wa mkazi wamasiyeyu kwa nthaŵi ndithu, ayenera kuti sanamvetse chomwe chimachitika. Poyambirira, iye anathandiza kupulumutsa mwana ameneyu kuti asafe ndi njala. Mwinamwake Eliya anafika pokondana naye kwambiri mwanayu. Mtima wa amake sunali m’malo m’pang’ono pomwe. Mnyamatayu ndiye yekha anali kumukumbutsa za mwamuna wake amene anamwalira kale. Ayenera kuti ankayembekezera mwana wakeyu kuti ndiye akamusamalira pamene wakalamba. Povutika maganizo, mkaziyu analingalira kuti akum’langa chifukwa cha zimene analakwa m’mbuyomo. Eliya sanapirire poona vutoli likukula chomwechi. Mosamala bwino ananyamula mtembowo pa chifuwa cha amake napita nawo m’chipinda chake, n’kupempha Yehova Mulungu kuti abwezeretse moyo wa mwanayo.—1 Mafumu 17:8-21.

19, 20. (a) Kodi Abrahamu anasonyeza motani kuti anali kukhulupirira mphamvu za Yehova zobwezeretsa zinthu, ndipo chikhulupiriro choterocho chinayambira pati? (b) Kodi Yehova anafupa motani chikhulupiriro cha Eliya?

19 Eliya sanali munthu woyamba kukhulupirira chiukiriro. Zaka mazana ambiri poyambirira pake, Abrahamu ankakhulupirira kuti Yehova anali ndi mphamvu zoterozo, ndipo anali ndi zifukwa zomveka. Pamene Abrahamu anali ndi zaka 100 ndipo Sara  anali ndi zaka 90, Yehova anabwezeretsa mphamvu zawo za kubala zomwe zinali zakufa, nachititsa Sara kubala mwana wamwamuna mozizwitsa. (Genesis 17:17; 21:2, 3) Pambuyo pake, pamene mnyamatayo anali wamkulu, Yehova anauza Abrahamu kupereka nsembe mwana wakeyo. Abrahamu anakhulupirira pozindikira kuti Yehova angachititse mwana wake wokondedwa Isake kukhalanso ndi moyo. (Ahebri 11:17-19) Chikhulupiriro chachikulu chimenecho chingapereke chifukwa chake Abrahamu, asanakwere m’phiri kukapereka nsembe mwana wake, anatsimikizira antchito ake kuti iye ndi Isake akabwerera limodzi.—Genesis 22:5.

“Taona, mwana wako ali moyo”

20 Yehova anapulumutsa Isake, motero sipanafunike chiukiriro panthaŵiyo. Komano m’nkhani ya Eliya, mwana wa mkazi wamasiyeyo anali atafa kale, koma panali pasanathe nthaŵi yaitali. Yehova anafupa chikhulupiriro cha mneneriyo mwa kuukitsa mwanayo! Kenako Eliya anapereka mwanayo kwa amake ndi mawu osaiwalika aŵa: “Taona, mwana wako ali moyo”!—1 Mafumu 17:22-24.

21, 22. (a) Kodi cholinga cha ziukiriro zolembedwa m’Malemba n’chiyani? (b) Mu Paradaiso, kodi ndi anthu ochuluka motani amene adzaukitsidwa, nanga ndani adzawaukitsa?

21 Choncho kwa nthaŵi yoyamba m’Baibulo, tikuona Yehova akugwiritsa ntchito mphamvu zake pobwezeretsa moyo wa munthu. Pambuyo pake, Yehova anapatsanso mphamvu Elisa, Yesu, Paulo, ndi Petro kuti abwezeretse moyo kwa akufa. N’zoona kuti anthu amene anaukitsidwawo m’kupita kwa nthaŵi anafanso. Komabe nkhani za m’Baibulo zimenezi zimatipatsa chithunzithunzi chabwino cha zimene zidzachitika m’tsogolo.

22 M’Paradaiso, Yesu adzakwaniritsa udindo wake monga “kuuka ndi moyo.” (Yohane 11:25) Adzaukitsa anthu mamiliyoni osaŵerengeka, n’kuwapatsa mwayi wokhala ndi moyo kosatha m’Paradaiso padziko lapansi. (Yohane 5:28, 29) Talingalirani mmene zidzakhalire zosangalatsa anthu akugwirizananso kachiŵiri pamene mabwenzi ndi achibale okondedwa, omwe anasiyana kalekale chifukwa cha imfa, akukumbatirana mwa chimwemwe chosaneneka! Anthu onse adzatamanda Yehova chifukwa cha mphamvu zake zobwezeretsa.

23. Kodi ndi chochitika chiti chimene chinali chachikulu kwambiri pa zochitika zonse zosonyeza mphamvu za Yehova, ndipo zimenezi zimatsimikizira motani chiyembekezo chathu cha m’tsogolo?

 23 Yehova watitsimikizira kotheratu kuti ziyembekezo zimenezi zidzachitikadi. Pa chochitika chachikulu kwambiri pa zonse chosonyeza mphamvu zake, iye anaukitsa Mwana wake, Yesu, monga cholengedwa chauzimu champhamvu, namuika kukhala wachiŵiri kwa Yehova mwiniyo basi. Ataukitsidwa, Yesu anaonekera kwa anthu mazanamazana. (1 Akorinto 15:5, 6) Umboni umenewo uyenera kukhala wokwanira ngakhale kwa anthu okayikira. Yehova ali ndi mphamvu zobwezeretsa moyo.

24. N’chifukwa chiyani tingakhale n’chidaliro chakuti Yehova adzaukitsa akufa, nanga kodi n’chiyembekezo chotani chomwe aliyense wa ife anganyadire?

24 Sikuti Yehova ali ndi mphamvu zobwezeretsa moyo zokha kwa akufa, komanso iye ndi wofunitsitsa kuwapatsa moyowo. Munthu wokhulupirikayo Yobu anauziridwa kunena kuti Yehova kwenikweni amakhumba akufa atakhalanso ndi moyo. (Yobu 14:15) Kodi simukuchita chidwi ndi Mulungu wathu, yemwe ali wofunitsitsa kugwiritsa ntchito mphamvu zake zobwezeretsa m’njira yachikondi yoteroyo? Komabe, kumbukirani kuti chiukiriro ndi mbali imodzi chabe ya ntchito yaikulu yobwezeretsa ya Yehova imene adzagwira m’tsogolomu. Pamene mukupitiriza kuyandikana naye, nthaŵi zonse nyadirani chiyembekezo chabwino chimenecho chakuti mungathe kudzakhalapo ndi kuona Yehova ‘akupanga zonse kukhala zatsopano.’—Chivumbulutso 21:5.

^ ndime 3 “Nthaŵi za kukonzanso zinthu zonse” zinayamba pamene Ufumu Waumesiya unakhazikitsidwa, pa mpando wake wachifumu pali woloŵa ufumu wa mfumu yokhulupirika Davide. Yehova analonjeza Davide kuti wina amene adzaloŵe m’malo mwake adzalamulira kosatha. (Salmo 89:35-37) Koma Babulo atawononga Yerusalemu mu 607 B.C.E., palibe mbadwa yaumunthu iliyonse ya Davide imene inakhala pa mpando wachifumu wa Mulungu. Yesu, amene anabadwa padziko lapansi monga woloŵa m’malo mwa Davide, anakhala Mfumu yomwe inalonjezedwa kalekalelo, pamene anakhala pa mpando wachifumu kumwamba.

^ ndime 6 Mwachitsanzo, Mose, Yesaya, Yeremiya, Ezekieli, Hoseya, Yoweli, Amosi, Obadiya, Mika, ndi Zefaniya onse ananena za nkhani imeneyi.