Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 5

Mphamvu za Kulenga—“Amene Analenga Zakumwamba ndi Dziko Lapansi”

Mphamvu za Kulenga—“Amene Analenga Zakumwamba ndi Dziko Lapansi”

1, 2. Kodi dzuŵa limasonyeza motani mphamvu za kulenga za Yehova?

KODI chimachitika n’chiyani pamene mukuwotha moto madzulo kukuzizira? Mumakhala potalikirana nawo bwino kuti muzimva kutenthera kwa motowo. Mukasendera kufupi kwambiri, mumamva kutentha kwambiri. Mukasendera kutali kwambiri, mphepo imakugwiraninso ndipo mumakongwa.

2 Pali “moto” wina umene timawotha masana. Kuchokera pano pamene ife tili, pali mtunda wa makilomita 150 miliyoni kukafika pamene pali “motowo”! * Dzuŵa liyeneratu kukhala lamphamvu kwambiri. Tangoganizani, mumamva kutentha kwake lili patali ngati pamenepo! Komatu, dziko lapansi limazungulira ng’anjo yaikulu yotentha kwambiri imeneyo litatalikana nayo bwino zedi. Ngati likanayandikira kwambiri, madzi onse padziko lapansi akanaphwera; likanatalikira kwambiri, madzi onse akanaundana. Kuyandikira kwambiri kapena kutalikira kwambiri kukanachititsa dziko lathuli kukhala lopanda chamoyo. Kuwala kwa dzuŵa n’kofunika kwambiri kuti padziko lapansi pakhale zamoyo, komanso ndi kwaudongo, kumatheketsa zinthu kuchitika, ndiponso n’kosangalatsa.—Mlaliki 11:7.

Yehova ‘anakonza kuunikandi dzuŵa’

3. Kodi dzuŵa limachitira umboni choonadi chofunikira chiti?

3 Komabe, anthu ambiri saliŵerengera kwenikweni dzuŵa ngakhale kuti miyoyo yawo imadalira pa ilo. Motero sazindikira zimene dzuŵa limatiphunzitsa. Baibulo limati za Yehova: “Munakonza kuunika ndi dzuŵa.” (Salmo 74:16) Inde, dzuŵa limalemekeza Yehova, “amene analenga zakumwamba ndi dziko lapansi.” (Salmo 19:1; 146:6) Lili chabe chimodzi cha zinthu zakuthambo zosaŵerengeka zomwe zimatiphunzitsa za mphamvu zazikulu za kulenga za Yehova. Tiyeni tiphunzire zina mwa izo mozamirapo, kenako tidzaphunzira za dziko lapansi ndi zamoyo zimene zili pa dzikoli.

 ‘Kwezani Maso Anu Kumwamba Muone’

4, 5. Kodi dzuŵa n’lamphamvu motani nanga n’lalikulu bwanji, komabe n’lotani poliyerekezera ndi nyenyezi zina?

4 Mwinamwake mukudziŵa kuti dzuŵa lathuli ndi nyenyezi. Limaoneka lalikulu kuposa nyenyezi zomwe timaona usiku chifukwa, poliyerekezera ndi nyenyezizo, ilo lili pafupi kwambiri. Kodi n’lamphamvu motani? Pakatikati pa dzuŵa m’potentha pafupifupi madigiri seshasi 15,000,000. Ngati mutatenga kachibenthu ka pakati pa dzuŵa kakakulu ngati njere ya therere lobala n’kukaika pa dziko lapansi pano, kuti musapse mungafunike kuima pa mtunda wa makilomita 140 kuchokera pamene mwakaikapo! Pa sekondi iliyonse, dzuŵa limatulutsa mphamvu zofanana ndi zimene zimatuluka pakaphulika mabomba a nyukiliya mamiliyoni mazana ochuluka.

5 Dzuŵa n’lalikulu kwambiri moti mukhoza kuloŵa mapulaneti aakulu ngati dziko lathu lapansili okwanira 1,300,000. Kodi ndiye kuti dzuŵa ndilo nyenyezi yaikulu kwambiri? Ayi, akatswiri a sayansi ya zakuthambo amalitcha kuti nyenyezi yaing’ono yachikasu. Mtumwi Paulo analemba kuti “nyenyezi isiyana ndi nyenyezi m’ulemerero.” (1 Akorinto 15:41) Iye sanadziŵe bwino mmene mawu ouziridwa amenewo alili oona. Pali nyenyezi ina yaikulu zedi moti  ngati ataiika pamalo pamene pali dzuŵa, dziko lathu lapansili likhoza kukhala m’kati mwa nyenyezi imeneyo. Nyenyezi inanso yaikulu kwambiri itati iikidwe pamalo omwewo ikhoza kudutsa dziko lapansi n’kukafika ku pulaneti yotchedwa Setani. Pulaneti limenelo lilitu kutali kwambiri ndi dziko lapansi lino. Chombo cha mumlengalenga chinatenga zaka zinayi kuti chikafike pa pulaneti imeneyo, komatu chinali kuthamanga pa liŵiro loposa kuŵirikiza nthaŵi 40 pa liŵiro la chipolopolo chophulitsidwa ndi mfuti yamphamvu kwambiri!

6. Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti nyenyezi n’zochuluka kwambiri malinga ndi kuona kwa anthu?

6 Chochititsa kakasi kwambiri kuposa kukula kwa nyenyezi ndicho kuchuluka kwa nyenyezizo. Baibulo limasonyeza kuti nyenyezi zilipo zosaŵerengeka, n’zovuta kuziŵerenga monga “mchenga wa kunyanja.” (Yeremiya 33:22) Mawu ameneŵa akutanthauza kuti pali nyenyezi zochuluka zedi kuposa zimene maso athuŵa angaone popanda kugwiritsa ntchito chida chilichonse. Ndiiko  komwe, ngati wolemba Baibulo, monga ngati Yeremiya, anayang’ana kumwamba usiku nayesa kuŵerenga nyenyezi zimene anali kuziona, akanangoŵerenga 3,000 zokha kapena kupitirirapo pang’ono, chifukwa ndizo nyenyezi zimene diso la munthu palokha likhoza kuziona pa usiku wowala bwino. Tingayerekeze nambala imeneyi ndi mchenga wongodzala kumanja. Komabe, zenizeni n’zakuti nyenyezi n’zochuluka kwabasi, monga mchenga wa kunyanja. * Ndani angathe kuziŵerenga zonsezo?

“Azitcha zonse mayina awo”

7. (a) Kodi mlalang’amba wathu wa Milky Way uli ndi nyenyezi pafupifupi zingati, ndipo nambala imeneyo ndi yaikulu motani? (b) N’chifukwa chiyani n’zochititsa chidwi kuti akatswiri a sayansi ya zakuthambo amalephera kuŵerenga milalang’amba yonse, nanga zimenezi zimatiphunzitsanji za mphamvu za kulenga za Yehova?

7 Yesaya 40:26 amayankha kuti: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse mayina awo.” Salmo 147:4 limati: “Aŵerenga nyenyezi momwe zili.” Kodi “nyenyezi momwe zili” ndi zingati? Limenelo ndi funso lovuta. Akatswiri a sayansi ya zakuthambo amati mu mlalang’amba wathu wokhawu, womwe amautcha kuti Milky Way, muli nyenyezi zoposa 100 biliyoni. * Koma mlalang’amba wathuwu ndi umodzi chabe mwa milalang’amba yambirimbiri, ndipo yambiri mwa iyo ili ndi nyenyezi zoposa wathuwu. Kodi milalang’amba ilipo ingati? Akatswiri ena a zakuthambo amati ilipo 50 biliyoni. Ena aŵerengera kuti ingakhalepo yochuluka kufika pa 125 biliyoni. Choncho munthu akulephera kudziŵa kuti milalang’amba yonse ndi ingati, nanjinanji nambala ya mabiliyoni a nyenyezi zonse pamodzi zomwe zili m’milalang’ambayo sangaidziŵe n’komwe. Komatu, Yehova amadziŵa nambala yake. Ndiponso, iyetu amapatsa nyenyezi iliyonse dzina lakelake!

8. (a) Kodi mungafotokoze motani kukula kwa mlalang’amba wa Milky Way? (b) N’chiyani chomwe Yehova amagwiritsa ntchito polamula kayendedwe ka zinthu zakuthambo?

8 Tingathe kukhala oopa Mulungu kwambiri pamene tisinkhasinkha  za kukula kwa milalang’amba. Anthu amati m’mimba mwa mlalang’amba wa Milky Way ndi motalika kufanana ndi mtunda umene kuwala kumayenda pa zaka 100,000. Kuwala kumayenda mothamanga kwambiri pa liŵiro la makilomita 300,000 pa sekondi imodzi. Ndiyeno taganizirani, pa liŵiro limenelo kuwala kungatenge zaka 100,000 kuti kudutse m’mimba mwa mlalang’amba wathuwu! Ndipo milalang’amba ina ndi ikuluikulu kuŵirikiza nthaŵi zambiri kukula kwa mlalang’amba wathu. Baibulo limati Yehova ‘akuyala’ thambo lalikulu limeneli ngati kuti akuyala nsalu. (Salmo 104:2) Iye amalinganizanso kayendedwe ka zolengedwa zimenezi. Kuyambira pa kafumbi kochepetsetsa kopezeka pakati pa nyenyezi ina ndi inzake kufika pa mlalang’amba waukulu kwambiri, chilichonse chimayenda mogwirizana ndi malamulo amene Mulungu anakonza ndi kuwayambitsa kugwira ntchito. (Yobu 38:31-33) Motero akatswiri a sayansi anena kuti kuyenda kotsatirika bwino kwa zinthu zakuthambo n’kofanana ndi kukonza masitepe a gule wovuta kuvina! Ndiyeno taganizani za Amene analenga zinthu zimenezi. Kodi simukupereka ulemu kwa Mulungu wokhala ndi mphamvu za kulenga zochuluka choncho?

“Analenga Dziko Lapansi ndi Mphamvu Yake”

9, 10. Kodi malo amene pali dzuŵa lathuli limodzi ndi zinthu zonse zimene zimayenda molizungulira, pamene pali pulaneti la Jupita, dziko lapansi, ndi mwezi amaonetsa motani mphamvu za Yehova?

9 Mphamvu za kulenga za Yehova zimaoneka bwino pamudzi wathuwu, dziko lapansi. Anaika dziko lapansi pamalo osamalika bwino zedi m’chilengedwe chachikuluchi. Asayansi ena amakhulupirira kuti m’milalang’amba yambiri simungakhale pulaneti lokhala ndi zamoyo monga pulaneti lathu lino. Mwachionekere, gawo lalikulu la mlalang’amba wathu wa Milky Way silinalinganizidwe kuti lizichirikiza moyo. Pakatikati pa mlalang’ambawu m’podzaza nyenyezi. Pamatuluka mpweya wapoizoni wochuluka, ndipo kaŵirikaŵiri nyenyezi zimatsala pang’ono kuwombana. M’mphepete mwa mlalang’ambawu mulibe zinthu zambiri zofunika kwambiri pamoyo. Dzuŵa lathuli limodzi ndi zinthu zonse zimene zimayenda molizungulira zinaikidwa pamalo abwino a pakati pa mbali ziŵirizo.

10 Dziko lapansi limatetezedwa ndi pulaneti lina lomwe lili kutali  komanso n’lalikulu kwambiri lotchedwa Jupita. Chifukwa chakuti n’lalikulu kuŵirikiza nthaŵi zoposa 1,000 kuposa Dziko Lapansi, pulaneti la Jupita limakoka zinthu mwamphamvu zedi. Kodi chimatsatira n’chiyani? Limakoka zinthu zimene zikuzungulira mumlengalenga kuti ziziloŵera kumene ilo lilili. Akatswiri a sayansi amaŵerengera kuti kukanakhala kuti panalibe pulanetili, zinthu zochokera mumlengalenga zomwe zimagwa pa dziko lapansi pano, bwenzi zikugwa mwamphamvu kwambiri kuŵirikiza nthaŵi 10,000 pa mmene zimagwera pakali pano. Chinanso chomwe tikuchidziŵa bwino n’chakuti dziko lathuli lili ndi setilaiti yapadera, mwezi. Kuwonjezera pa kukhala chokongoletsera ndi “chounikira usiku,” mwezi umachititsa dziko kuima mopendekeka pamodzimodzi nthaŵi zonse. Kupendekeka kumeneku n’kumene kumachititsa kuti padziko lapansi pazikhala nyengo zosasinthasintha ndi zodziŵika bwino, chinthu china chofunika kwambiri kuti padzikoli pakhale zamoyo.

11. Kodi mumlengalenga mwa dziko lapansi munalinganizidwa motani kuti mukhale ngati chotchinga choteteza?

11 Mphamvu za kulenga za Yehova zimaonekera m’mbali iliyonse ya mmene dziko lapansi linapangidwira. Talingalirani za mumlengalenga, mmene mumakhala ngati chotchinga choteteza. Dzuŵa limatulutsa cheza chabwino ndi china chakupha. Pamene cheza chakupha chifika pamwamba pa mlengalenga wa dziko lapansi, chimasintha mpweya wa okosijeni kuti ukhale mpweya wotchedwa ozoni. Ndiyeno ozoni amene amayala pamwambayo amayamwa gawo lalikulu la cheza chimenecho. Tinganene kuti, pulaneti lathuli linalinganizidwa kukhala ndi chophimba choteteza chakechake.

12. Kodi kusintha kwa madzi mumlengalenga kumasonyeza motani mphamvu za Yehova za kulenga?

12 Imeneyo ndi mbali imodzi chabe ya mumlengalenga mmene timaonamu, momwe muli mpweya wamitundumitundu wosakanikirana bwino moyenera kuchirikiza zolengedwa zokhala padzikoli kapena pafupi ndi dzikoli. Kusintha kwa madzi ndi chimodzi cha zinthu zodabwitsa zimene zimachitika mumlengalenga. Chaka chilichonse dzuŵa limachititsa madzi ochuluka zedi, oposa pa makyubiki kilomita 400,000 ochokera m’nyanja zamchere, kukhala thunzi yomwe imaulukira m’mlengalenga. Madziwo amapanga mitambo yomwe imauluzidwira kwina ndi kwina ndi mphepo  yamumlengalenga. Madzi ameneŵa, amene tsopano amakhala opanda tizitsotso ndi oyera bwino, amagwa pansi monga mvula, chipale chofeŵa, ndi madzi oundana nadzazanso mitsinje ndi nyanja. Zimachitika monga amanenera Mlaliki 1:7 kuti: “Mitsinje yonse ithira m’nyanja, koma nyanja yosadzala; komwe imukira mitsinjeyo, komweko ibweranso.” Ndi Yehova yekha amene akanayambitsa kuti madzi azizungulira chonchi.

13. Kodi mu zomera ndi m’nthaka ya dziko lapansi timaonamo umboni wotani wa mphamvu za Mlengi?

13 Paliponse pamene timaona chamoyo, timaona umboni wa mphamvu za Mlengi. Kungoyambira mitengo italiitali kwambiri yomwe imatalika kuposa nyumba za nsanjika 30 kufika pa zomera zing’onozing’ono kwabasi zooneka ndi maikulosikopu zomwe zimadzala m’nyanja zamchere n’kumapereka mpweya wochuluka womwe timapuma, timaona mphamvu za Yehova za kulenga. Dothi lenilenili n’lodzala ndi zinthu zamoyo—nyongolotsi, tomera ting’onoting’ono topanda masamba tooneka tankhungunkhungu, ndi tizilombo ting’onoting’ono, zonse zikugwirira pamodzi ntchito zosiyanasiyana zothandiza zomera kuti zikule. Mpake kuti Baibulo limati nthaka ili ndi mphamvu.—Genesis 4:12.

14. Kodi ndi mphamvu zobisika zotani zimene zilinso mu atomu yomwe ndi yochepa kwambiri?

14 Mosakayikira, Yehova “analenga dziko lapansi ndi mphamvu yake.” (Yeremiya 10:12) Mphamvu za Mulungu zimaoneka ngakhale mu zinthu zing’onozing’ono kwambiri zimene analenga. Mwachitsanzo, maatomu wani miliyoni mutawagundikiza pamodzi sangakhale ochindikala ngati tsitsi lamunthu. Ndipo ngakhale atomu atati aitalikitse kuti ifanane ndi nyumba ya nsanjika 14, thima lake lingafanane ndi m’bulu wa mchere wokhala pansanjika ya nambala seveni. Komatu, pathima lochepetsetsa pamenepo ndi pamene pamachokera mphamvu zosaneneka zimene zimatuluka bomba la nyukiliya likaphulika!

“Zonse Zakupuma”

15. Mwa kulongosola nyama zosiyanasiyana zakutchire, kodi Yehova anali kuphunzitsa Yobu chiyani?

15 Umboni wina wabwino wa mphamvu za kulenga za Yehova umaoneka mu nyama zambirimbiri zomwe zili pa dziko lapansi. Mu Salmo 148 munalembedwa zinthu zambiri zomwe zimalemekeza Yehova, ndipo vesi ya 10 imaphatikizapo “nyama za  kuthengo ndi zoŵeta zonse.” Pofuna kusonyeza chifukwa chake munthu ayenera kuopa Mlengi, panthaŵi ina Yehova analankhula ndi Yobu za nyama monga mkango, mbidzi, njati, mvuu, ndi ng’ona. Kodi mfundo yake inali yotani? Ngati munthu amachita mantha ndi zolengedwa zamphamvu, zoopsa, ndi zosazoloŵerana ndi anthu zimenezi, kodi ayenera kumva bwanji ndi Mlengi wa nyama zimenezi?—Yobu, machaputala 38-41.

16. Kodi n’chiyani chikukuchititsani chidwi ndi mbalame zina zimene Yehova analenga?

16 Salmo 148:10 likutchulanso “mbalame zakuuluka.” Koma ndiye n’zamitundumitundu bwanji! Yehova anauza Yobu za nthiŵatiŵa, imene ‘imaseka kavalo ndi wa pamsana pake.’ Inde, mbalameyi ndi yaitali mamita aŵiri ndi theka ndipo siuluka, koma imathamanga makilomita 65 pa ola limodzi ikumaponda mamita anayi ndi theka kuchokera pa phazi lina. (Yobu 39:13, 18) Komanso, mbalame ina yotchedwa alibatirosi nthaŵi yochuluka ya moyo wake imakhala ikuuluka pamwamba pa nyanja. Mbalameyi imatha kuuluka popanda kukupiza mapiko ake omwe ikawatambasula ndi atali mamita atatu. Imatha kuuluka kwa maola ambirimbiri itangoimitsa mapiko ake osawakupiza. Ndiyeno, tasiyanitsani ndi mbalame inanso yooneka ngati kachoso (kasongwe) yotchedwa bee hummingbird. Iyo ndi yaitali masentimita asanu okha basi ndipo ndiyo mbalame yochepa zedi pa mbalame zonse padziko lapansi. Imatha kukupiza mapiko ake nthaŵi 80 pa sekondi imodzi! Zikunyezimira ngati miyala ing’onoing’ono ya mtengo wapatali, mbalame za mtunduwu zimatha kuima m’malere monga ndege za helikoputala ndiponso zimatha kuuluka chafutambuyo.

17. Kodi nangumi wotchedwa blue whale ndi wamkulu motani, nanga patokha tiyenera kunenanji pambuyo polingalira nyama zimene Yehova analenga?

17 Salmo 148:7 limanena kuti ngakhale “zinsomba” zimalemekeza Yehova. Talingalirani za nyama imene ambiri amati ndiyo yaikulu kwambiri pa nyama zonse zomwe zinakhalako padziko lapansi lino, nangumi wotchedwa blue whale. “Chinsomba” cha m’nyanja zamchere chimenechi chimatha kukula kufika mamita 30 kapena kuposapo mlitali mwake. Kulemera kwake kungafanane ndi kulemera kwa njovu zikuluzikulu 30. Lilime lake lokha limalemera mofanana ndi njovu imodzi. Mtima wake ndi waukulu ngati galimoto yaing’ono. Chiwalo chachikulu chimenechi chimagunda  maulendo 9 okha pa mphindi imodzi, mosiyana kwambiri ndi mtima wa mbalame ija yotchedwa hummingbird womwe umagunda pafupifupi maulendo 1,200 pa mphindi imodzi. Nangumiyu ali ndi mtsempha wina waukulu zedi moti mwana akhoza kukwawamo bwinobwino. Ndithudi mitima yathu imatichititsa kubwereza mawu achilimbikitso amene amamaliza buku la Masalmo akuti: “Zonse zakupuma zilemekeze Yehova.”—Salmo 150:6.

Tiphunzirepo pa Mphamvu za Kulenga za Yehova

18, 19. Kodi zinthu zamoyo zimene Yehova analenga pa dziko lapansili n’zosiyanasiyana motani, nanga kodi chilengedwe chimatiphunzitsanji za ulamuliro wake?

18 Kodi tikuphunziranji pa mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake za kulenga? Timachita kakasi chifukwa cha kusiyanasiyana kwa chilengedwe. Wamasalmo wina anafuula kuti: “Nchito zanu zichulukadi, Yehova! . . . Dziko lapansi lidzala nacho chuma chanu.” (Salmo 104:24) N’zoonadi zimenezo! Akatswiri a sayansi ya zinthu zamoyo apeza mitundu ya zamoyo yopitirira wani miliyoni pa dziko lapansi; komatu zonena zawo zimasiyanasiyana kuti kaya pali mitundu yokwana 10 miliyoni, kaya 30 miliyoni, kapena yoposa pamenepo. Munthu waluso lojambula zithunzi ndi manja nthaŵi zina angaone kuti akusoŵa chojambula. Mosiyana ndi munthu waluso loterolo, luso lopanga zinthu la Yehova, ndiko kuti mphamvu yake yolingalira za zinthu zosiyanasiyana zatsopano ndi kuzilenga, mwachionekere silitha.

19 Mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu zake za kulenga zimatiphunzitsa za ulamuliro wake. Mawu enieniwo akuti  “Mlengi” amasiyanitsa Yehova ndi kanthu kalikonse m’chilengedwe chonse, zomwe zonse ndi “zolengedwa.” Ngakhale Mwana wobadwa yekha wa Yehova, amene anali “mmisiri” panthaŵi yolenga zinthu, m’Baibulo samutchula kuti Mlengi kapena Mlengi mnzake. (Miyambo 8:30; Mateyu 19:4) M’malo mwake, iye ndi ‘wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.’ (Akolose 1:15) Udindo wa Yehova monga Mlengi mwachibadwa umamupatsa ufulu wosonyeza mphamvu zonse zolamulira pa chilengedwe chonse.—Aroma 1:20; Chivumbulutso 4:11.

20. Kodi Yehova wapuma m’lingaliro lotani kuchokera pamene anamaliza kulenga zinthu za m’dziko lapansi?

20 Kodi Yehova anasiya kugwiritsa ntchito mphamvu zake za kulenga? Baibulo limanena kuti Yehova atamaliza ntchito yake yolenga pa tsiku lachisanu ndi chimodzi la kulenga, “anapuma tsiku lachisanu ndi chiŵiri ku ntchito yake yonse.” (Genesis 2:2) Mtumwi Paulo anasonyeza kuti “tsiku” lachisanu ndi chiŵiri limeneli ndi lalitali zaka masauzande ambiri, pakuti linali lidakalipo m’masiku ake. (Ahebri 4:3-6) Koma kodi ‘kupuma’ kukutanthauza kuti Yehova anasiyiratu kugwira ntchito iliyonse? Ayi, Yehova sasiya kugwira ntchito. (Salmo 92:4; Yohane 5:17) Ndiye kuti kupuma kwake kuyenera kungotanthauza kuti analeka kugwira ntchito yolenga zinthu zimene zili m’dziko lapansi. Komabe, ntchito yake yokwaniritsa zolinga zake yapitirizabe mosadodometsedwa. Ntchito imeneyi yaphatikizapo kuuzira Malemba Opatulika, ndiponso kutulutsa “chilengedwe chatsopano,” chomwe chidzafotokozedwa m’Mutu 19.—2 Akorinto 5:17, NW.

21. Kodi mphamvu za kulenga za Yehova zidzawakhudza motani kwa umuyaya wonse anthu okhulupirika?

21 Pamene tsiku lopuma la Yehova lidzatha, iye adzafotokoza ntchito zake zonse padziko lapansi kuti ndi “zabwino ndithu,” mofanana ndi mmene ananenera pamene limatha tsiku lachisanu ndi chimodzi la kulenga. (Genesis 1:31) Tidzaonabe panthaŵiyo kuti iye kenako adzasankha kugwiritsa ntchito motani mphamvu zake zopanda malirezo za kulenga. Mulimonse mmene zidzakhalire, tingakhale otsimikiza kuti tidzachitabe chidwi ndi mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu za kulenga. Kwa umuyaya wonse, tidzaphunzira zambiri za Yehova kupyolera m’chilengedwe chake. (Mlaliki 3:11) Pamene tipitiriza kuphunzira za iye, tidzakhala oopa Mulungu kwambiri, ndipo Mlengi wathu Wamkulu tidzayandikana naye kwambiri.

^ ndime 2 Kuti mumvetsetse nambala yaikulu kwambiri imeneyo, ganizirani izi: Kuti muyende mtunda wonsewo pa galimoto, ngakhale mutamayendetsa galimotoyo pa liŵiro la makilomita 160 pa ola limodzi kwa maola 24 patsiku, kungakutengereni zaka zoposa 100 mukanayenda!

^ ndime 6 Ena amaganiza kuti anthu akale m’nthaŵi za m’Baibulo anali kugwiritsa ntchito makina achikalekale oonera zinthu zakutali. Iwo amati, kodi anthu a m’nthaŵi imeneyo paokha akanadziŵa bwanji kuti nyenyezi n’zochuluka kwambiri, kuti n’zosaŵerengeka? Kulingalira kopanda maziko kotereku kumanyozetsa Yehova, Mlembi wa Baibulo.—2 Timoteo 3:16.

^ ndime 7 Talingalirani utali umene mukanatenga kuti muŵerenge nyenyezi 100 biliyoni zokha. Ngati munali okhoza kuŵerenga nyenyezi yatsopano pa sekondi iliyonse, n’kumangoŵerengabe kwa maola 24 patsiku, mungatenge zaka 3,171 kuti mumalize zonsezo!

Onaninso

NSANJA YA OLONDA (YOPHUNZIRA)

Chilengedwe Chimatithandiza Kukhulupirira Kwambiri Mulungu

Nkhaniyi itithandiza kuti tizikhulupirira kwambiri Mlengi komanso kuti tithandize ena kumudziwa bwino.