Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 10

‘Khalani Otsanzira Mulungu’ Pamene Mukugwiritsa Ntchito Mphamvu

‘Khalani Otsanzira Mulungu’ Pamene Mukugwiritsa Ntchito Mphamvu

1. Kodi anthu opanda ungwiro amakodwa mosavuta mu msampha wosaoneka uti?

“PALIBE munthu wokhala ndi mphamvu yemwe m’kupita kwanthaŵi sakodwa mu msampha wosaoneka.” Mawu amenewo omwe ananenedwa ndi wandakatulo wina wa m’zaka za m’ma 1800, amatchula za ngozi imene sioneka. Ngoziyi ndiyo kugwiritsa ntchito mphamvu molakwa. N’zachisoni kuti anthu opanda ungwiro amakodwa mosavuta mu msampha umenewu. Ndithudi, m’mbiri yonse ya anthu ‘wina wapweteka mnzake pomulamulira.’ (Mlaliki 8:9) Kusonyeza mphamvu mopanda chikondi kwavutitsa anthu ochuluka zedi.

2, 3. (a) Kodi chochititsa chidwi n’chiyani ndi mmene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu? (b) Kodi mphamvu zathu zingakhale chiyani, ndipo mphamvu zonse zoterozo tiyenera kuzigwiritsa ntchito motani?

2 Komabe, kodi si zochititsa chidwi kuti Yehova Mulungu, amene ali ndi mphamvu zopanda malire, sagwiritsa ntchito mphamvuzo molakwa? Monga taonera m’mitu yapitayi, iye nthaŵi zonse amagwiritsa ntchito mphamvu zake, kaya zikhale mphamvu za kulenga, kuwononga, kuteteza, kapena kubwezeretsa zinthu, mogwirizana ndi zolinga zake zachikondi. Tikamasinkhasinkha mmene amasonyezera mphamvu zake, timaona kuti n’kofunika kuti timuyandikire. Ndiyeno zimenezo zimatha kutichititsa ‘kukhala otsanzira Mulungu’ pamene tikugwiritsa ntchito mphamvu zathu. (Aefeso 5:1) Koma kodi anthu ofookafe tili ndi mphamvu zotani?

3 Kumbukirani kuti munthu analengedwa “m’chifanizo” ndi m’chikhalidwe cha Mulungu. (Genesis 1:26, 27) Motero ifenso tili ndi mphamvu, koma pang’ono chabe. Mphamvu zathu zingakhale monga izi: kukhala wodziŵa kuchita zinthu, kugwira ntchito; kukhala wolamulira ena; kutha kulimbikitsa ena kuchita zinazake, makamaka amene amatikonda; kukhala munthu wanyonga (wadzitho); kapena chuma chakuthupi. Ponena  za Yehova, wamasalmo anati: “Chitsime cha moyo chili ndi Inu.” (Salmo 36:9) Motero, kaya ndi mwachindunji kapena ayi, Mulungu ndiye gwero la mphamvu iliyonse imene tingakhale nayo. Motero tifunika kuigwiritsa ntchito m’njira zimene zimamusangalatsa. Kodi zimenezi tingazichite motani?

Chinsinsi Chake Chagona pa Chikondi

4, 5. (a) Kodi chinsinsi chogwiritsa ntchito bwino mphamvu n’chiyani, nanga chitsanzo cha Mulungu mwiniyo chimationetsa zimenezi motani? (b) Kodi chikondi chidzatithandiza motani kugwiritsa ntchito bwino mphamvu zathu?

4 Chinsinsi chogwiritsa ntchito mphamvu moyenera ndicho chikondi. Kodi zimenezi sitiziona m’chitsanzo cha Mulungu mwiniyo? Kumbukirani zomwe tinafotokoza m’Mutu Woyamba za mbali zinayi zikuluzikulu za umunthu wa Mulungu; zomwe ndi mphamvu, chilungamo, nzeru ndi chikondi. Mwa mbali zinayizi, ndi mbali iti imene imaposa zonse? Chikondi. “Mulungu ndiye chikondi,” amatero 1 Yohane 4:8. Inde, chikondi ndiwo umunthu weniweniwo wa Yehova; zonse zimene amachita zimachitika ndi chikondi. Motero zonse zimene amachita zosonyeza mphamvu zake zimachitika chifukwa cha chikondi ndipo pamapeto pake zimakhala zothandiza awo amene amamukonda.

5 Nafenso, chikondi chidzatithandiza kugwiritsa ntchito bwino mphamvu zathu. Ndiiko komwe, Baibulo limatiuza kuti chikondi chili “chokoma mtima” ndipo “sichitsata za mwini yekha.” (1 Akorinto 13:4, 5) Motero sitidzachita zinthu mwaukali kapena mwankhanza ndi anthu amene tikuwalamulira chifukwa timawakonda. Koma tidzalemekeza anthu ena ndi kuika zofuna zawo ndi malingaliro awo patsogolo pa zathu.—Afilipi 2:3, 4.

6, 7. (a) Kodi kuopa Mulungu n’kutani, ndipo n’chifukwa chiyani khalidwe limeneli lidzatithandiza kupeŵa kugwiritsa ntchito mphamvu molakwa? (b) Perekani fanizo losonyeza kugwirizana kwa kuopa kusakondweretsa Mulungu ndi kukonda Mulungu.

6 Chikondi n’chogwirizana ndi khalidwe linanso lomwe lingatithandize kupeŵa kugwiritsa ntchito mphamvu molakwa. Khalidweli ndilo kuopa Mulungu. Kodi kuopa Mulungu n’kofunika motani? Miyambo 16:6 imati: “Apatuka pa zoipa poopa Yehova.” Ndithudi, kugwiritsa ntchito mphamvu molakwa ndi imodzi mwa njira zimene tifunika kupatukamo. Sitidzazunza anthu  amene timawalamulira ngati timaopa Mulungu. Chifukwa chiyani? Chimodzi mwa zifukwazo n’chakuti timadziŵa kuti Mulungu adzatiimba mlandu wa momwe timachitira zinthu ndi anthu oterowo. (Nehemiya 5:1-7, 15) Koma kuopa Mulungu kumaphatikizapo zambiri. Mawu a chinenero choyambirira otanthauza “kuopa” nthaŵi zambiri amanena za kuchitira Mulungu ulemu waukulu. Motero Baibulo limati kuopa kumayendera limodzi ndi kukonda Mulungu. (Deuteronomo 10:12, 13) Mantha aulemu ameneŵa amaphatikizapo kukhala ndi malingaliro abwino oopa kusakondweretsa Mulungu, osati pachifukwa chokha choopa zotsatirapo zake, koma chifukwa chakuti timamukondadi.

7 Tifanizire motere: Ganizirani za mnyamata wamng’ono amene amagwirizana zedi ndi atate wake. Mnyamatayo amazindikira kuti atate wake amasangalatsidwa naye ndipo amamukonda. Koma iye amadziŵanso zimene atate wakewo amafuna kuti iye azichita, ndipo amadziŵa kuti ngati achita zamaseŵera atate wake adzamulanga. Mnyamatayu sanjenjemera akaona atate wakewo, koma amawakonda kwambiri. Mwanayu amasangalala pochita zimene zidzakondweretsa atate wakewo. Ndimo mmene kuopa Mulungu kulili. Chifukwa chakuti Yehova, Atate wathu wakumwamba, timamukonda, timaopa kuchita chilichonse chimene ‘chikamuvutitsa mu mtima mwake.’ (Genesis 6:6) M’malo mwake, timalakalaka kukondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11) N’chifukwa chake tikufuna kugwiritsa ntchito bwino mphamvu zathu. Tiyeni tione mmene tingachitire zimenezi.

M’banja

8. (a) Kodi amuna ali ndi udindo wotani m’banja, nanga ayenera kuusonyeza motani? (b) Kodi mwamuna angaonetse motani kuti amachitira ulemu mkazi wake?

8 Choyamba, lingalirani za m’banja. Aefeso 5:23 amati: “Mwamuna ndiye mutu wa mkazi.” Kodi mwamuna ayenera kusonyeza motani udindo wopatsidwa ndi Mulungu umenewu? Baibulo limauza amuna kuti azikhala ndi akazi awo ‘monga mwa chidziŵitso, ndi kuwachitira ulemu monga chotengera chochepa mphamvu.’ (1 Petro 3:7) Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “ulemu” amatanthauza kuona chinthu kukhala “chapamwamba,  chonyaditsa, . . . kuchilemekeza.” Mawu ena ochokera ku mawu ameneŵa amatembenuzidwa kuti “mphatso” (NW) ndiponso kuti “mtengo wake.” (Machitidwe 28:10; 1 Petro 2:7) Mwamuna amene amachitira mkazi wake ulemu sam’panda; ndiponso sam’chititsa manyazi kapena kum’nyoza; sachititsa mkazi wakeyo kuona kuti ndi wosafunikira. Koma amazindikira kuti mkazi wakeyo ndi munthu womunyadira, motero amamulemekeza. Mwa mawu ake ndi zochita zake, kaya pamene ali okha kapena ali pa anthu, mwamunayo amasonyeza kuti mkazi wake ndi chinthu chapamwamba kwa iye. (Miyambo 31:28) Mkazi amamukonda ndi kumulemekeza mwamuna wotereyu; chofunikanso kwambiri n’chakuti Mulungu amakondwera naye.

Amuna ndi akazi amagwiritsa ntchito bwino mphamvu zawo mwa kusonyezana chikondi ndi kulemekezana

9. (a) Kodi akazi ali ndi mphamvu zotani m’banja? (b) Kodi n’chiyani chingathandize mkazi kugwiritsa ntchito maluso ake kuti athandize mwamuna wake, ndipo n’chiyani chingatsatirepo?

9 Akazi nawonso ali ndi mphamvu m’banja. Baibulo limatiuza za akazi oopa Mulungu amene, mosaswa umutu wabwino, analimbikitsa amuna awo kuchita zinthu zothandiza kapenanso anawathandiza kupeŵa kusankha kuchita zolakwika. (Genesis 21:9-12; 27:46–28:2) Mkazi akhoza kukhala wanzeru kwambiri kuposa mwamuna wake, kapena akhoza kukhala ndi maluso ena amene mwamuna wake alibe. Komatu, mkaziyo ayenera kukhala ndi “ulemu waukulu” kwa mwamuna wake ndi ‘kumugonjera monga kwa Ambuye.’ (Aefeso 5:22, 33, NW) Mkazi akakhala ndi cholinga chosangalatsa Mulungu m’maganizo mwake, amatha kugwiritsa ntchito maluso ake pa kuthandiza mwamuna wake m’malo momamupeputsa kapena kuyesa kumulamulira. ‘Mkazi wanzeru’ wotereyu amagwirizana kwambiri ndi mwamuna wake pomanga banja lawo. Mwakutero amakhalabe pamtendere ndi Mulungu.—Miyambo 14:1.

10. (a) Kodi Mulungu wapatsa makolo udindo wotani? (b) Kodi mawu akuti “chilango” amatanthauza chiyani, nanga chiyenera kuperekedwa motani? (Onaninso mawu a m’munsi.)

10 Makolo nawo ali ndi udindo umene Mulungu anawapatsa. Baibulo limalangiza kuti: “Atate inu, musakwiyitse ana anu, koma pitirizani kuwalera m’chilango ndi kuwongolera maganizo kwa Yehova.” (Aefeso 6:4, NW) M’Baibulo, mawu akuti “chilango” angatanthauze “kulera, kuphunzitsa, kulangiza.” Ana  amafunika kulangidwa; amasangalala ndi kuchita zinthu bwino pamene apatsidwa malangizo, ndi malire omveka bwino ochitira zinthu. Baibulo limati chilango, kapena malangizo oterowo amachitika limodzi ndi chikondi. (Miyambo 13:24) Motero ‘nthyole yolangira’ siyenera kukhala yozunzira, kaya mwamalingaliro kapena mwakuthupi. * (Miyambo 22:15; 29:15) Kupereka chilango chokhwima kapena chankhanza, chopanda n’chikondi chomwe, ndiko kugwiritsa ntchito molakwa udindo wamakolo ndipo chikhoza kuwononga mzimu wa mwana. (Akolose 3:21) Koma chilango chabwino, choperekedwa m’njira yoyenera, chimauza ana kuti makolo awo amawakonda ndi kuti makolowo amasangalala kudziŵa kuti anawo akukula kukhala anthu otani.

11. Kodi ana angagwiritse ntchito bwino motani mphamvu zawo?

11 Nanga bwanji ana? Kodi angagwiritse ntchito bwino motani mphamvu zawo? Miyambo 20:29 imanena kuti: “Ulemerero wa anyamata ndiwo mphamvu yawo.” Ndithudi njira yabwino kwambiri pazonse imene achinyamata angagwiritsire ntchito mphamvu ndi nyonga zawo ndiyo kutumikira “Mlengi” wathu. (Mlaliki 12:1) Achinyamata ayenera kukumbukira kuti zochita zawo zikhoza kukhudza maganizo a makolo awo. (Miyambo 23:24, 25) Pamene ana amvera makolo awo oopa Mulungu ndi kumamatira pa njira yoyenera, makolo awowo amakondwera kwabasi. (Aefeso 6:1) ‘Ambuye amakondwera nalo’ khalidwe lotero.—Akolose 3:20.

Mu Mpingo

12, 13. (a) Kodi akulu ayenera kukhala ndi malingaliro otani pa udindo wawo mu mpingo? (b) Perekani fanizo losonyeza chifukwa chimene akulu ayenera kusamalira nkhosa mokoma mtima.

12 Yehova wapereka oyang’anira kuti azitsogolera mu mpingo wachikristu. (Ahebri 13:17) Amuna okhoza kutsogolera ameneŵa amayenera kugwiritsa ntchito udindo womwe Mulungu  wawapatsa pothandiza gulu la nkhosa ndi kuchititsa nkhosazo kukhala ndi moyo wabwino. Kodi udindo wawowo umapatsa akulu ufulu wochita umbuye pa okhulupirira anzawo? M’pang’onong’ono pomwe! Akulu afunika kuona ntchito imene ali nayo mu mpingo mosamala bwino ndi modzichepetsa. (1 Petro 5:2, 3) Baibulo limauza oyang’anira kuti: “Muŵete Eklesia wa Mulungu, umene anaugula ndi mwazi wa iye [“Mwana wake,” NW] yekha.” (Machitidwe 20:28) Chimenechitu ndi chifukwa champhamvu kwabasi chochitira zinthu mokoma mtima ndi nkhosa iliyonse m’gululo.

13 Tingachitire fanizo motere. Bwenzi lanu lapamtima lakupemphani kuti mulisungire katundu wamtengo wapatali. Inu mukudziŵa kuti bwenzi lanu linalipira ndalama zambiri pogula katunduyo. Kodi simungamugwire mosamala kwambiri kuti asawonongeke? Mofananamo, Mulungu wapatsa akulu udindo wosamalira katundu wamtengo wapatali zedi: mpingo, womwe anthu ake amafanizidwa ndi nkhosa. (Yohane 21:16, 17) Yehova amazikonda nkhosa zake; amazikondatu kwambiri moti anazigula ndi magazi amtengo wapatali a Mwana wake wobadwa yekha, Yesu Kristu. Panalibenso mtengo wina wokwera kuposa pamenepa umene Yehova akanalipirira nkhosa zake. Akulu odzichepetsa amakumbukira zimenezi ndipo amasamalira nkhosa za Yehova moyenerera.

“Lilime Lili ndi Mphamvu”

14. Kodi lilime lili ndi mphamvu yotani?

14 “Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo,” limatero Baibulo. (Miyambo 18:21) Lilime likhozadi kuwononga kwambiri. Ndani wa ife amene mawu sanamupwetekepo omwe munthu wina analankhula mosaganizira bwino kapenanso ngakhale momupeputsa? Koma lilime lilinso ndi mphamvu yokonza zinthu. “Lilime la anzeru lilamitsa,” imatero Miyambo 12:18. Inde, mawu abwino olimbikitsa angakhale ngati mafuta otonthoza ndi ochiritsa mtima. Taonani zitsanzo izi.

15, 16. Kodi tingagwiritse ntchito lilime m’njira zotani kuti tilimbikitse ena?

15 “Limbikitsani amantha mtima,” amatero 1 Atesalonika 5:14. Inde, ngakhale atumiki okhulupirika a Yehova nthaŵi zina amavutika maganizo. Kodi oterowo tingawathandize  motani? Ayamikireni mosapita m’mbali komanso moonadi kuti akhoze kuona kuti ali amtengo wapatali m’maso mwa Yehova. Auzeni mawu okhala ndi mphamvu a m’Baibulo osonyeza kuti Yehova amasamalira ndi kukonda anthu a “mtima wosweka” ndi a “mzimu wolapadi.” (Salmo 34:18) Pamene tigwiritsa ntchito mphamvu ya lilime kuti tilimbikitse ena, timasonyeza kuti tikutsanzira Mulungu wathu wachifundo, “amene amalimbitsa otaya mtima.”—2 Akorinto 7:6, Chipangano Chatsopano Cholembedwa m’Chicheŵa Chamakono.

16 Tingagwiritsenso ntchito mphamvu ya lilime lathu popereka chilimbikitso chomwe ena akuchifuna kwambiri. Kodi wokhulupirira mnzathu wafedwa wokondeka wake? Mawu achifundo osonyeza kuti zikutikhudza angalimbikitse munthu wachisoni. Kodi pali mbale kapena mlongo wokalamba amene akuona kuti ena samufuna? Tingatsimikizire okalamba kuti ndi ofunika kwambiri ndiponso kuti timawayamikira mwa kulankhula mawu abwino okhazika mtima pansi. Kodi wina akudwala matenda okhalitsa? Munthu wodwala angasangalale kwambiri ngati timuuza mawu okoma pa telefoni kapena pamene takamuona. Mlengi wathu amasangalalatu kwambiri pamene tigwiritsa ntchito mphamvu ya kulankhula kuti tinene mawu amene ali ‘abwino pomangirira’!—Aefeso 4:29.

Kuuza ena uthenga wabwino ndiyo njira yabwino kwambiri yogwiritsa ntchito mphamvu zathu

17. Kodi ndi m’njira yofunika iti imene tingagwiritse ntchito lilime kuti tipindulitse ena, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kuchita zimenezi?

 17 Palibe njira ina yofunika kwambiri yogwiritsa ntchito mphamvu ya lilime kuposa kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. “Oyenera kulandira zabwino usawamane; pokhoza dzanja lako kuwachitira zabwino,” imatero Miyambo 3:27. Ndi udindo wathu kuuza ena uthenga wabwino wopulumutsa moyo. Sikoyenera kungosunga patokha uthenga wofulumira umene Yehova watipatsa mowoloŵa manja kwambiri. (1 Akorinto 9:16, 22) Koma kodi Yehova amatiyembekeza kugwira ntchito imeneyi mpaka pati?

Kutumikira Yehova ndi ‘Mphamvu Zathu Zonse’

18. Kodi Yehova amatiyembekezera kuchitanji?

18 Chifukwa chakuti timakonda Yehova, timachita nawo utumiki  wachikristu ndi mtima wonse. Kodi Yehova amatiyembekezera kuchitanji pankhaniyi? Amatiyembekezera kuchita chimene aliyense wa ife, mosasamala kanthu za mmene moyo wathu ulili, angathe kuchita: “Chilichonse mukachichita, gwirani ntchito mochokera mumtima [“mwa moyo wonse,” NW], monga kwa Ambuye, osati kwa anthu ayi.” (Akolose 3:23) Yesu, pofotokoza lamulo lalikulu kwambiri pa onse anati: “Uzikonda Ambuye Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse, ndi mphamvu yako yonse.” (Marko 12:30) Inde, Yehova amayembekezera aliyense wa ife kuti tizimukonda ndi kumutumikira ndi moyo wathu wonse.

19, 20. (a) Popeza kuti moyo umaphatikizapo mtima, nzeru, ndi mphamvu, n’chifukwa chiyani zimenezinso zinatchulidwa pa Marko 12:30? (b) Kodi kutumikira Yehova ndi moyo wonse kumatanthauza chiyani?

19 Kodi kutumikira Mulungu ndi moyo wonse kumatanthauza chiyani? Moyo ukutanthauza munthu wathunthu, limodzi ndi zonse zimene thupi lake ndi maganizo ake zingathe kuchita. Ndiye popeza moyo ukuphatikizapo mtima, nzeru, ndi mphamvu, n’chifukwa chiyani zimenezinso zikutchulidwa pazokha pa Marko 12:30? Lingalirani fanizo ili. M’nthaŵi za m’Baibulo, munthu ankatha kudzigulitsa (kugulitsa moyo wake) kuti akhale kapolo. Komatu n’kutheka kuti kapoloyo sangatumikire ambuye wake ndi mtima wonse; sangagwiritse ntchito mphamvu zake zonse kaya nzeru zake zonse kuti zinthu za ambuye wake ziyende bwino. (Akolose 3:22) Choncho tingaone kuti Yesu anatchula mbali zina zimenezi pofuna kutsindika kuti sitiyenera kusiyapo kalikonse pamene tikutumikira Mulungu. Kutumikira Mulungu ndi moyo wonse kumatanthauza kudzipereka enife, kugwiritsa ntchito mphamvu zathu ndi nyonga zathu kumlingo wonse umene tingathe pomutumikira.

20 Kodi kutumikira ndi moyo wonse kukutanthauza kuti tonse tiyenera kuthera nthaŵi yofanana ndi nyonga zofanana mu utumiki? Zimenezi sizingatheke, chifukwa munthu aliyense zimamuchitikira zinthu zosiyana ndi anthu ena ndiponso amakhala ndi maluso osiyana ndi anthu ena. Mwachitsanzo, wachinyamata amene sadwaladwala komanso ndi wanyonga akhoza kutenga nthaŵi yochuluka akulalikira kusiyana ndi munthu amene  mphamvu zake zikutha chifukwa cha ukalamba. Munthu wosakwatira kapena kukwatiwa yemwe alibe udindo wosamalira banja angathe kuchita zambiri kusiyana ndi munthu amene akusamalira banja. Tiyenera kuthokoza kwambiri ngati tili ndi mphamvu ndiponso ngati zochitika zimatilola kuchita zochuluka mu utumiki. Ndithudi, sitidzafuna kukhala ndi mzimu wosuliza ena, kuyerekeza mmene ife tikuchitira mu utumiki ndi mmene amachitira ena. (Aroma 14:10-12) Koma tigwiritse ntchito mphamvu zathu polimbikitsa ena.

21. Kodi njira yabwino kwambiri ndi yofunika koposa yogwiritsa ntchito mphamvu zathu ndi iti?

21 Yehova watipatsa chitsanzo chabwino kwambiri pa kugwiritsa ntchito bwino mphamvu zake. Tikufuna kumutsanzira kumlingo umene tingathe monga anthu opanda ungwiro. Mphamvu zathu tingazigwiritse ntchito bwino ngati tilemekeza anthu amene timawalamulira. Ndiponso, tifunika kugwira ndi moyo wonse ntchito yolalikira yopulumutsa moyo imene Yehova watipatsa kuti tichite. (Aroma 10:13, 14) Kumbukirani kuti Yehova amasangalala pamene mupereka zabwino kwambiri zimene inuyo—moyo wanu—mungathe kupereka. Kodi mu mtima mwanu simukulakalaka mutachita zonse zimene mungathe potumikira Mulungu womvetsetsa ndi wachikondi wotereyu? Njira yabwino kwambiri ndiponso yofunika koposa yogwiritsira ntchito mphamvu zanu ndi yokhayi basi.

^ ndime 10 M’nthaŵi za m’Baibulo, mawu achihebri a “nthyole” anali kutanthauza kamtengo kapena kandodo, monga ngati kamene anali kugwiritsa ntchito mbusa poŵeta nkhosa. (Salmo 23:4) Mofananamo, “nthyole” ya udindo wamakolo imapereka malingaliro a kulangiza mwachikondi, osati kukhaulitsa mopanda chifundo kapena mwankhanza.