1, 2. Kodi Aisrayeli anali m’mavuto otani pamene amaloŵa m’dera la Sinai m’chaka cha 1513 B.C.E., nanga ndi motani mmene Yehova anawakhazikira mtima pansi?

AISRAYELI anali m’mavuto pamene amaloŵa m’dera la Sinai kumayambiriro kwa chaka cha 1513 B.C.E. Anali kuyembekeza kuyenda ulendo wochititsa mantha wodutsa ‘m’chipululu chachikulu ndi choopsa momwe munali njoka zamoto ndi zinkhanira.’ (Deuteronomo 8:15) Panalinso mitundu yodana nawo imene inali kudzamenyana nawo. Yehova ndiye anachititsa anthu ake kukhala m’mavuto ameneŵa. Iye monga Mulungu wawo, kodi adzatha kuwateteza?

2 Mawu aŵa a Yehova anali okhazika mtima pansi kwambiri: “Inu munaona chimene ndinachitira Aigupto; ndi kuti ndanyamula inu monga pa mapiko a mphungu, ndi kubwera nanu kwa ine ndekha.” (Eksodo 19:4) Yehova anakumbutsa anthu ake kuti anawalanditsa kwa Aigupto; anawanyamula kukawasiya kumalo otetezeka pogwiritsa ntchito mphungu, mophiphiritsa tingatero. Koma palinso zifukwa zina zomwe “mapiko a mphungu” alili fanizo labwino la chitetezo cha Mulungu.

3. N’chifukwa chiyani “mapiko a mphungu” akufanizira bwino chitetezo cha Mulungu?

3 Mphungu imagwiritsa ntchito mapiko ake akuluakulu komanso amphamvuwo m’njira zambiri kuwonjezera pa kuuluka pamwamba kwambiri. Pamene kwatentha kwambiri, mphungu yaikazi imatambasula mapiko ake, omwe ikawafunyulula angakwane mamita aŵiri, kuti ipange mthunzi wotetezera ana ake kuti angapse ndi dzuŵa. Panthaŵi zina imafungatira ana ake m’mapiko powateteza ku mphepo yozizira. Monga momwe mphungu imatetezera ana ake, Yehovanso anatchingira ndi kuteteza mtundu watsopanowo wa Israyeli. Tsopano pamene anali m’chipululu, anthu ake akanapitiriza kuthaŵira mu mthunzi wa mapiko ake amphamvuwo malinga ngati  akanakhalabe okhulupirika. (Deuteronomo 32:9-11; Salmo 36:7) Koma kodi ifeyo lerolino moyenerera tingayembekeze Mulungu kutiteteza?

Lonjezo la Chitetezo cha Mulungu

4, 5. N’chifukwa chiyani tingakhale n’chidaliro chonse mu lonjezo la Mulungu loteteza anthu ake?

4 Ndithudi Yehova ndi wokhoza kuteteza atumiki ake. Iye ndi “Mulungu Wamphamvuyonse,” dzina laudindo losonyeza kuti ali ndi mphamvu zosaletseka. (Genesis 17:1) Mofanana ndi funde lomwe silingaimitsidwe, mphamvu imene Yehova amagwiritsa ntchito singaletsedwe. Popeza iye amatha kuchita chilichonse chogwirizana ndi chifuno chake, tingafunse kuti, ‘Kodi ndi chifuno cha Yehova kugwiritsa ntchito mphamvu zake kuteteza anthu ake?’

5 Mwa mawu amodzi okha, tingayankhe funsolo kuti inde! Yehova amatitsimikizira kuti adzateteza anthu ake. “Mulungu ndiye pothaŵirapo pathu ndi mphamvu yathu, thandizo lopezekeratu m’masautso,” limatero Salmo 46:1. Popeza kuti Mulungu ‘sanama,’ tingakhale n’chidaliro chonse mu lonjezo lake lakuti adzateteza anthu ake. (Tito 1:2) Tiyeni tione mafanizo ena omveka bwino amene Yehova amagwiritsa ntchito pofotokoza mmene amatetezera anthu ake.

6, 7. (a) Kodi mbusa wa m’nthaŵi za m’Baibulo anali kupereka chitetezo chotani ku nkhosa zake? (b) Kodi Baibulo limapereka fanizo lotani losonyeza kuti Yehova amafunitsitsa kuteteza nkhosa zake ndi kuzisamalira?

6 Yehova ndi Mbusa, ndipo ife “ndife anthu ake ndi nkhosa za pabusa pake.” (Salmo 23:1; 100:3) Pali nyama zochepa zomwe zimafuna kuthandizidwa kwambiri mofanana ndi momwe nkhosa zoŵeta zilili. Mbusa wa m’nthaŵi za m’Baibulo anali kufunika kukhala wolimba mtima kuti ateteze nkhosa zake ku mikango, mimbulu, ndi zimbalangondo, komanso kwa akuba. (1 Samueli 17:34, 35; Yohane 10:12, 13) Koma panali nthaŵi zina pamene nkhosa zimafuna kutetezedwa ndi munthu wachifundo. Nkhosa ikaberekera kutali ndi khola, mbusa wosamalira  bwino anali kuyang’anira nkhosa yaberekayo panthaŵi imene ikufunika thandizo ndiyeno amanyamula kamwana kosatha kudzitetezako ndi kupita nako kukhola.

“Nadzawatengera pa chifuwa chake”

7 Mwa kudziyerekeza ndi mbusa, Yehova akutitsimikizira kuti amafunitsitsa kutiteteza. (Ezekieli 34:11-16) Kumbukirani mmene Yesaya 40:11 amafotokozera Yehova. Lembali, lomwe tinalifotokoza m’Mutu 2 wa buku lino, limati: “Iye adzadyetsa zoŵeta zake ngati mbusa, nadzasonkhanitsa ana a nkhosa pachapa pake, nadzawatengera pa chifuwa chake.” Kodi zimatani kuti kamwana kankhosa kakhale pa “chifuwa” cha mbusa, ndiko kuti pa chovala chake chakumtunda chomwe wachipinda? Kamwana kankhosako kangafike pamene pali mbusayo, mwinanso kangamakhudzekhudze mwendo wake. Komabe, mbusayo ndiye ayenera kuŵerama n’kunyamula kankhosako ndi kukaika mosamala bwino pa chifuwa chake pomwe kangakhale motetezeka. Ndi chithunzithunzi chabwinotu kwambiri cha chifundo kuonetsa kuti Mbusa wathu Wamkulu amafunitsitsa kutitchinjiriza ndi kutiteteza!

8. (a) Kodi ndani amene Mulungu amalonjeza kuwateteza, ndipo zimenezi zikuoneka motani pa Miyambo 18:10? (b) Kodi kuthaŵira m’dzina la Mulungu kumaloŵetsapo chiyani?

8 Sikuti popeza Mulungu analonjeza ndiye basi amateteza munthu aliyense. Iye amateteza okhawo amene amamuyandikira. Miyambo 18:10 imati: “Dzina la Yehova ndilo linga lolimba; wolungama athamangiramo napulumuka.” M’nthaŵi za m’Baibulo, nthaŵi zina anthu anali kumanga nsanja m’chipululu kuti azithaŵiramo. Koma munthu yemwe moyo wake unali pachisweyo ndiye amafunika kuthamangira mu nsanjayo kuti apulumuke. N’chimodzimodzi ndi kuthaŵira m’dzina la Mulungu. Zimenezi zimafuna zambiri osati kumangobwerezabwereza kutchula dzina la Mulungu; dzina lake si mawu amatsenga. M’malo mwake, timafunika kumudziŵa ndi kumukhulupirira Mwini wake wa dzina limenelo ndi kumakhala ndi moyo mogwirizana ndi miyezo yake yolungama. Yehova ndi wokoma mtimatu kwambiri potitsimikizira kuti ngati timukhulupirira, adzakhala linga lotiteteza!

 “Mulungu Wathu . . . Akhoza Kutilanditsa”

9. Kodi Yehova wachita zinthu zina motani kuwonjezera pa kulonjeza chitetezo?

9 Yehova wachitanso zina kuwonjezera pa kulonjeza chitetezo. M’nthaŵi za m’Baibulo, anaonetsa mozizwitsa kuti ndi wokhoza kuteteza anthu ake. Mu mbiri ya Israyeli, nthaŵi zambiri “dzanja” lamphamvu la Yehova linali kulepheretsa adani amphamvu kuchita chilichonse. (Eksodo 7:4) Komabe, Yehova anagwiritsanso ntchito mphamvu zake zoteteza pothandiza anthu paokha.

10, 11. Kodi ndi zitsanzo za m’Baibulo ziti zimene zimasonyeza mmene Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu zake zoteteza pothandiza anthu ena?

10 Anyamata atatu achihebri—Sadrake, Mesake, ndi Abedinego—atakana kugwadira fano lagolidi la Mfumu Nebukadinezara, mfumu yokalipayo inawaopseza kuti iwaponya m’ng’anjo yotentha kwambiri. “Mulungu amene adzakulanditsani m’manja mwanga ndani?” ananyoza motero Nebukadinezara, yemwe anali mfumu yamphamvu kwambiri padziko lapansi. (Danieli 3:15) Anyamata atatuwo anali n’chidaliro chonse kuti Mulungu wawo ali ndi mphamvu zowateteza, koma sanaganize kuti iye atero. Motero anayankha kuti: “Taonani, Mulungu wathu amene tim’tumikira akhoza kutilanditsa.” (Danieli 3:17) Indedi, ng’anjo yotenthayo, ngakhale pambuyo poti aisonkhezera maulendo asanu ndi aŵiri kuposa masiku onse, sinali chopinga kwa Mulungu wawo wamphamvu zonse. Iye anawateteza, ndipo mfumuyo inakakamizika kuvomereza kuti: “Palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.”—Danieli 3:29.

11 Yehova anasonyezanso mochititsa chidwi mphamvu zake zoteteza pamene anasamutsa moyo wa Mwana wake wobadwa yekha nauika m’mimba ya namwali wachiyuda Mariya. Mngelo anauza Mariya kuti ‘adzakhala ndi pakati nadzabala mwana wamwamuna.’ Mngeloyo anafotokoza kuti: “Mzimu Woyera adzafika pa iwe, ndi mphamvu ya Wamkulukulu idzakuphimba iwe.” (Luka 1:31, 35) Zikuoneka kuti Mwana wa Mulungu anali asanakhalepo wopanda chitetezo chokwanira ngati panthaŵiyi. Kodi uchimo ndi kupanda ungwiro kwa mayi wake waumunthuyo kukaipitsa mwana wosabadwayo? Kodi Satana  adzavulaza kapena kupha Mwanayo asanabadwe? Zosatheka konse! Yehova anapangatu khoma lotchinga Mariya kotero kuti panalibe chilichonse—kaya kupanda ungwiro, kaya mphamvu ina iliyonse yovulaza, kaya munthu wambanda, kapenanso chiwanda china chilichonse—chimene chikanawononga mwana yemwe anali kukula m’mimbayo, kuchokera pamene amake anaima mpaka kukula kwake konse. Yehova anapitiriza kuteteza Yesu pamene anali mnyamata. (Mateyu 2:1-15) Mpaka pa nthaŵi yoikika ya Mulungu, kunali kosatheka kuvulaza Mwana wake wokondedwa.

12. N’chifukwa chiyani Yehova anateteza anthu ena mozizwitsa m’nthaŵi za m’Baibulo?

12 N’chifukwa chiyani Yehova anateteza anthu ena mozizwitsa chotero? M’zochitika zambiri Yehova anateteza anthu ena n’cholinga choti ateteze chinthu chofunika kwambiri: kukwaniritsidwa kwa cholinga chake. Mwachitsanzo, kunali kofunika kwambiri kuti Yesu ali khanda apulumuke kuti cholinga cha Mulungu chikhoze kukwaniritsidwa, chomwe pamapeto pake chidzapindulitsa anthu onse. Nkhani zambiri zosonyeza mphamvu zoteteza zili mbali ya Malemba ouziridwa amene ‘analembedwa kutilangiza, kuti mwa chipiriro ndi chitonthozo cha malembo, tikhale ndi chiyembekezo.’ (Aroma 15:4) Inde, zitsanzo zimenezi zimalimbitsa chikhulupiriro chathu mwa Mulungu wathu wamphamvu zonse. Koma kodi ndi chitetezo chotani chimene tingayembekeze kwa Mulungu lerolino?

Zimene Chitetezo cha Mulungu Sichitanthauza

13. Kodi Yehova amafunika kutichitira zozizwitsa zivute zitani? Longosolani.

13 Lonjezo la Mulungu loteteza anthu ake silitanthauza kuti zivute zitani Yehova amafunika kutichitira zozizwitsa. Ayi, Mulungu wathu satilonjeza kuti tidzakhala opanda mavuto m’moyo wakale uno. Atumiki okhulupirika ochuluka a Yehova amakumana ndi mavuto aakulu, kuphatikizapo umphaŵi, nkhondo, matenda, ndi imfa. Yesu anauza ophunzira ake mosabisa mawu kuti ena a iwo adzaphedwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. N’chifukwa chake Yesu ananenetsa kuti m’pofunika kupirira mpaka pa mapeto. (Mateyu 24:9, 13) Yehova akanati azigwiritsa  ntchito mphamvu zake kulanditsa aliyense mozizwitsa m’zochitika zonse, chimenecho chikanakhala chifukwa chakuti Satana azinyoza Yehova ndiponso kuti azikayikira ngati kudzipereka kwathu kwa Mulungu wathu kulidi koona.—Yobu 1:9, 10.

14. Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti Yehova sateteza atumiki ake onse m’njira zofanana nthaŵi zonse?

14 Ngakhale m’nthaŵi za m’Baibulo, Yehova sanagwiritse ntchito mphamvu zake zoteteza kutchinjiriza mtumiki wake aliyense ku imfa yamwadzidzidzi. Mwachitsanzo, Herode anapha mtumwi Yakobo cha m’chaka cha 44 C.E.; komatu pasanapite nthaŵi yaitali, Petro analanditsidwa “m’dzanja la Herode” yemweyo. (Machitidwe 12:1-11) Ndipo Yohane, mbale wake wa Yakobo, anakhala ndi moyo kuposa onse aŵiri Petro ndi Yakobo. Ndithudi, sitingayembekeze Mulungu wathu kuteteza atumiki ake onse m’njira zofanana. Ndiponso, nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika zimatigwera tonsefe. (Mlaliki 9:11) Ndiyeno, ndi motani mmene Yehova amatitetezera lerolino?

Yehova Amatiteteza Mwakuthupi

15, 16. (a) Kodi pali umboni wotani wakuti Yehova wateteza mwakuthupi olambira ake monga gulu? (b) N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chidaliro kuti Yehova adzateteza atumiki ake tsopano lino ndiponso pa “chisautso chachikulu”?

15 Choyamba, talingalirani chitetezo chakuthupi. Pokhala olambira Yehova, tingayembekeze kutitetezera motero monga gulu. Apo ayi, Satana akanatilikwira mosavuta. Taganizirani izi: Satana, “mkulu wa dziko ili lapansi,” palibe china chimene amafuna koma kuthetsa kulambira koona. (Yohane 12:31; Chivumbulutso 12:17) Maboma ena amphamvu kwambiri padziko lapansi aletsa ntchito yathu yolalikira ndipo ayesetsa kuti angotifafaniziratu. Komatu, anthu a Yehova akhalabe olimba ndipo apitiriza kulalikira mosaleka! N’chifukwa chiyani mayiko amphamvu alephera kuletsa ntchito ya gulu la Akristu ochepaŵa ndi ooneka ngati opanda chitetezo? N’chifukwa chakuti Yehova watitchingira ndi mapiko ake amphamvu!—Salmo 17:7, 8.

16 Nanga bwanji za kutetezedwa mwakuthupi pa “chisautso chachikulu” chimene chikubweracho? Sitifunika kuopa pamene Mulungu apereka chiweruzo. Chifukwatu “Ambuye adziŵa  kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe.” (Chivumbulutso 7:14; 2 Petro 2:9) Pakali pano, tingakhale otsimikiza za zinthu ziŵiri nthaŵi zonse. Choyamba, Yehova sadzalola atumiki ake okhulupirika kuti afafanizidwe padziko lapansi. Chachiŵiri, adzafupa anthu okhulupirika powapatsa moyo wosatha m’dziko lake latsopano lolungama, ngati kungafunike, mwa kuwaukitsa. Kwa amene akumwalira, malo okha osungika amene iwo angakhalemo ndi m’chikumbukiro cha Mulungu.—Yohane 5:28, 29.

17. Kodi Yehova amatiteteza motani ndi Mawu ake?

17 Ngakhale tsopano lino, Yehova amatiteteza ndi “mawu” ake amoyo, amene ali ndi mphamvu yochiritsa mitima ya anthu ndi kuwalimbikitsa kusintha miyoyo yawo. (Ahebri 4:12) Mwa kugwiritsa ntchito mfundo zake zachikhalidwe, timatetezeka ku zinthu zina zowononga mwakuthupi. “Ine ndine Yehova, . . . amene ndikuphunzitsa kupindula,” amatero Yesaya 48:17. Mosakayikira, tingakhale ndi thanzi labwino komanso moyo wautali chifukwa chokhala ndi moyo womvera Mawu a Mulungu. Mwachitsanzo, chifukwa chogwiritsa ntchito uphungu wa Baibulo wakuti sitifunika kukhala achiwerewere koma tiyenera kudziyeretsa ku chodetsa chilichonse, timapeŵa makhalidwe onyansa ndi zizoloŵezi zovulaza zimene zimabweretsa mavuto aakulu m’miyoyo ya anthu ambiri osaopa Mulungu. (Machitidwe 15:29; 2 Akorinto 7:1) Tikuthokozatu kwabasi kuti Mawu a Mulungu amatiteteza!

Yehova Amatiteteza Mwauzimu

18. Kodi Yehova amatipatsa chitetezo chauzimu chotani?

18 Chofunika kwambiri n’chakuti Yehova amatiteteza mwauzimu. Mulungu wathu wachikondi amatiteteza kuti tisavulale mwauzimu potipatsa zomwe timafunikira kuti tithe kupirira ziyeso ndi kukhalabe naye paubwenzi. Motero Yehova amachita zinthu kuti apulumutse moyo wathu, osati kwa zaka zoŵerengeka chabe koma kosatha. Talingalirani zina zimene Mulungu amatipatsa kuti zititeteze mwauzimu.

19. Kodi mzimu wa Yehova ungatithandize motani kupirira chiyeso chilichonse chimene tingakumane nacho?

 19 Yehova ndi “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Pamene mavuto a moyo atithetsa nzeru, tingapepukidwe ngati timuuza za mumtima mwathu. (Afilipi 4:6, 7) Iye sangatichotsere ziyeso zathu mozizwitsa, koma poyankha mapemphero athu ochokera pansi pamtima, angatipatse nzeru za mmene tichitire ndi ziyesozo. (Yakobo 1:5, 6) Chachikulu kwambiri kuposa chimenechi n’chakuti Yehova amapereka mzimu woyera kwa amene amamupempha. (Luka 11:13) Mzimu wamphamvu zedi umenewo ungatithandize kupirira chiyeso kapena vuto lililonse limene tingakumane nalo. Ungatipatse mphamvu yoposa yachibadwa kuti tipirire mpaka Yehova atachotsa mavuto onse opweteka m’dziko latsopano limene layandikira kwambiri.—2 Akorinto 4:7.

20. Kodi mphamvu zoteteza za Yehova zingasonyezedwe motani kupyolera mwa olambira anzathu?

20 Nthaŵi zina, mphamvu zoteteza za Yehova zingasonyezedwe kupyolera mwa olambira anzathu. Yehova wakokosa anthu ake kuti akhale gulu la abale la padziko lonse. (Yohane 6:44; 1 Petro 2:17) Mwa chikondi cha ubale umenewo, timaona umboni wooneka wa mphamvu ya mzimu woyera wa Mulungu yolimbikitsa anthu kusintha. Mzimu umenewo umabala  zipatso mwa ife, zomwe ndi makhalidwe osangalatsa amtengo wapatali omwe amaphatikizapo chikondi, chifundo, ndi kukoma mtima. (Agalatiya 5:22, 23) Motero, pamene tikuvutika ndiyeno wokhulupirira mnzathu n’kufuna kuti atipatse uphungu wothandiza kapena kutiuza mawu olimbikitsa omwe tikufunika, tingathokoze Yehova potisamalira bwino chotero.

21. (a) Kodi ndi chakudya cha panthaŵi yake chotani chomwe Yehova amatipatsa kupyolera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru”? (b) Kodi inuyo panokha mwapindula motani ndi zinthu zimene Yehova amatipatsa kuti zititeteze mwauzimu?

21 Palinso chinthu china chimene Yehova amatipatsa kuti chititeteze: chakudya chauzimu cha panthaŵi yake. Kuti atithandize kupeza mphamvu kuchokera m’Mawu ake, Yehova wauza “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azigaŵira chakudya chauzimu. Kapolo wokhulupirika amagwiritsa ntchito mabuku, kuphatikizapo magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani!, ndiponso misonkhano yampingo, yadera, ndi yachigawo kuti atipatse “zakudya panthaŵi yake”—zimene timafuna, panthaŵi yomwe tikuzifuna. (Mateyu 24:45) Kodi munayamba mwamvapo mfundo inayake pa msonkhano wachikristu—m’ndemanga, m’nkhani, ngakhalenso m’pemphero—imene inakupatsani mphamvu zimene munali kufuna ndi kukulimbikitsani? Kodi moyo wanu unayamba wakhudzidwapo ndi nkhani inayake yofalitsidwa mu imodzi ya magazini athu? Kumbukirani kuti Yehova amatipatsa zinthu zonsezi kuti atiteteze mwauzimu.

22. Kodi nthaŵi zonse Yehova amagwiritsa ntchito mphamvu zake motani, nanga n’chifukwa chiyani akamachita zimenezi amakhala akutithandiza?

22 Ndithudi Yehova ndiye chotchinjiriza “onse okhulupirira iye.” (Salmo 18:30) Timazindikira kuti tsopano lino iye sagwiritsa ntchito mphamvu zake potiteteza ku masoka onse. Komabe, nthaŵi zonse amagwiritsa ntchito mphamvu zake zoteteza poonetsetsa kuti cholinga chake chikuchitika. Akamachita zimenezi pamapeto pake zimakhala zothandizanso anthu ake. Ngati tiyandikana naye ndi kukhalabe okondedwa ake, Yehova adzatipatsa moyo wangwiro wosatha. Pokhala ndi chiyembekezo chimenecho, ndithudi tingaone kuvutika kulikonse m’dziko lino kukhala ‘kopepuka ndi kwa kanthaŵi.’—2 Akorinto 4:17.