Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 CHIGAWO CHOYAMBA

“Wolimba Mphamvu”

“Wolimba Mphamvu”

M’chigawo chino, tikambirana nkhani za m’Baibulo zimene zimapereka umboni wa mphamvu za Yehova za kulenga, kuwononga, kuteteza, ndi kubwezeretsa zinthu. Kumvetsetsa mmene Yehova Mulungu, yemwe ndi “wolimba mphamvu,” amagwiritsira ntchito “mphamvu zake zazikulu” kudzachititsa mitima yathu kukhala ndi ulemu waukulu kwa iye.—Yesaya 40:26.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 4

“Yehova Ndiye . . . wa Mphamvu Yaikulu”

Kodi tiyenera kuopa Mulungu chifukwa choti ndi wamphamvu? Tingati inde komanso ayi.

MUTU 5

Mphamvu za Kulenga—“Amene Analenga Zakumwamba ndi Dziko Lapansi”

Tikaganizira zinthu zazikulu zimene Mulungu analenga monga dzuwa komanso zinthu zing’onozing’ono monga timbalame, tingaphunzire zambiri zokhudza iye.

MUTU 6

Mphamvu Zowononga—‘Yehova Ndi Munthu Wankhondo’

N’chifukwa chiyani “Mulungu wamtendere” nthawi zina amamenya nkhondo?

MUTU 7

Mphamvu Zoteteza—“Mulungu Ndiye Pothaŵirapo Pathu”

Mulungu amateteza atumiki ake mwa njira ziwiri, koma njira inayo ndiyofunika kwambiri.

MUTU 8

Mphamvu Zobwezeretsa—Yehova ‘Akupanga Zonse Kukhala Zatsopano’

Panopa Yehova wabwezeretsa kale kulambira koona. Kodi m’tsogolomu adzabwezeretsa chiyani?

MUTU 9

“Kristu Mphamvu ya Mulungu”

Kodi zozizwitsa komanso zinthu zimene Yesu ankaphunzitsa zimasonyeza chiyani zokhudza Mulungu?

MUTU 10

‘Khalani Otsanzira Mulungu’ Pamene Mukugwiritsa Ntchito Mphamvu

Mutakhala ndi mphamvu zambiri, kodi mungatati kuti muzizigwiritsa ntchito moyenera?