Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 31

“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”

“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”

1-3. (a) Kodi tingaphunzire chiyani za chibadwa cha anthu mwa kuona zimene zimachitika pakati pa makolo ndi mwana wawo wakhanda? (b) Kodi mwachibadwa pamachitika zotani munthu wina akamatikonda, nanga ndi funso lofunika liti limene tingadzifunse?

MAKOLO amasangalala kuona mwana wawo wobadwa kumene akumwetulira. Kaŵirikaŵiri amayandikizitsa nkhope zawo ku nkhope ya khandalo, n’kumaseŵera nalo ndi kumalimwetulira kwambiri. Amafunitsitsa ataona nalonso likumwetulira. Ndipodi mosakhalitsa limayamba kumwetulira mosangalatsa. Kumwetulirako kumasonyeza chikondi mwa njira yakeyake, ndipo chimakhala chiyambi chakuti mwanayo azionetsa makolo ake kuti nayenso amawakonda monga mmene iwo amamukondera.

2 Kumwetulira kwa mwana kumatikumbutsa mfundo yofunika ya chibadwa cha anthu. Mwachibadwa wina akamatikonda nafenso timamukonda. Ndi mmene tinapangidwira. (Salmo 22:9) Pamene tikukula, timamka tidziŵa bwino mmene tingakondere omwe akutikonda. Mwina mungakumbukire mmene makolo anu, achibale anu, kapena anzanu anali kukukonderani pamene munali mwana. Inu munayamba kusangalatsidwa nawo mu mtima mwanu, ndipo malingalirowo anakula n’kuonekera mu zochita zanu. Nanunso munawasonyeza kuti mumawakonda. Kodi zoterezi zikuchitikanso pa ubwenzi wanu ndi Yehova Mulungu?

3 Baibulo limati: “Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Mwakumbutsidwa m’Chigawo Choyamba mpaka Chachitatu m’buku lino kuti Yehova Mulungu wasonyeza mphamvu zake, chilungamo chake, ndi nzeru zake mwachikondi kuti inu mupindule. Ndipo m’Chigawo Chachinayi mwaona kuti iye wasonyeza chikondi chake mwachindunji kwa anthu, ndiponso kwa inu monga munthu payekha, m’njira zochititsa chidwi kwambiri. Tsopano nali funso. Tinganene kuti limeneli ndi funso lofunika kwambiri limene mungadzifunse: ‘Kodi ndidzachitapo chiyani pa chikondi cha Yehova?’

 Zimene Kukonda Mulungu Kumatanthauza

4. Kodi anthu asokonezeka motani pa chimene kukonda Mulungu kumatanthauza?

4 Yehova, Woyambitsa chikondi, amadziŵa bwino kuti chikondi chili ndi mphamvu yaikulu yochititsa anthu ena kuonetsa makhalidwe awo abwino. Choncho ngakhale kuti anthu osakhulupirika akupitirizabe kukhala opanduka, iye wakhalabe n’chidaliro chakuti anthu ena adzalabadira chikondi chake. Ndipodi anthu mamiliyoni ochuluka atero. Komabe, n’zomvetsa chisoni kuti zipembedzo za dziko loipali zasokoneza anthu pankhani ya chimene kukonda Mulungu kumatanthauza. Anthu ochuluka amati amakonda Mulungu, koma amaoneka kuti amaganiza kuti kukonda Mulungu ndi maganizo chabe oti aziwalankhula. Inde, kukonda Mulungu kungayambe m’njira imeneyo, monganso mmene poyamba mwana wakhanda angasonyezere kuti amakonda makolo ake mwa kuwamwetulira. Komabe, kwa anthu akuluakulu chikondi chimaphatikizapo zambiri.

5. Kodi Baibulo limati kukonda Mulungu kumatanthauzanji, nanga n’chifukwa chiyani tanthauzo limenelo liyenera kutisangalatsa?

5 Yehova amafotokoza chimene kumukonda kumatanthauza. Mawu ake amati: “Ichi ndi chikondi cha Mulungu, kuti tisunge malamulo ake.” Motero kukonda Mulungu kuyenera kusonyezedwa ndi zochita. N’zoona kuti ambiri sasangalala kuti azimvera munthu wina. Komatu vesili limanenanso kuti: “Ndipo malamulo [a Mulungu] sali olemetsa.” (1 Yohane 5:3) Malamulo a Yehova ndiponso mfundo zake za makhalidwe abwino zinalinganizidwa kuti zitipindulitse, osati kutipondereza. (Yesaya 48:17, 18) Mawu a Mulungu ndi odzala ndi mfundo za makhalidwe abwino zimene zimatithandiza kumuyandikira kwambiri. Motani? Tiyeni tipende mbali zitatu za ubwenzi wathu ndi Mulungu. Mbalizi ndi kulankhulana naye, kumulambira, ndi kumutsanzira.

Kulankhulana ndi Yehova

6-8. (a) Kodi Yehova tingamumvetsere bwanji? (b) Kodi tingatani kuti Malemba azikhala amoyo pamene tikuwaŵerenga?

6 Mutu 1 unayamba ndi funso lakuti, “Kodi mungayerekeze kukhala mukucheza ndi Mulungu?” Tinaona kuti zimenezi sizinali zongoyerekezera. Mose anachezapo ndi Mulungu. Nanga bwanji  ifeyo? Ino si nthaŵi imene Yehova akutumiza angelo ake kuti alankhule ndi anthu. Koma Yehova ali ndi njira zabwino kwambiri zolankhulirana nafe lerolino. Kodi tingamumvetsere motani Yehova?

7 Popeza kuti “lemba lililonse adaliuzira Mulungu,” timamvetsera Yehova mwa kuŵerenga Mawu ake, Baibulo. (2 Timoteo 3:16) Choncho Mfumu Davide analangiza atumiki a Yehova kuti aziliŵerenga “usana ndi usiku.” (Salmo 1:1, 2) Timafunika kuchita khama ndithu kuti tichite zimenezi. Koma khama limenelo n’loyenera. Monga tinaonera m’Mutu 18, Baibulo lili ngati kalata yofunika kwambiri imene tinalandira kuchokera kwa Atate wathu wakumwamba. Motero kuliŵerenga sikuyenera kukhala ntchito yosautsa. Tikamaŵerenga Malemba tiyenera kuwachititsa kukhala amoyo. Kodi tingazichite motani zimenezi?

8 Onani nkhanizo m’maganizo anu pamene mukuziŵerenga m’Baibulo. Yesani kuona anthu otchulidwa m’Baibulo monga anthu enieni. Yesetsani kumvetsetsa moyo wawo, zimene zinali kuwachitikira, ndiponso zolinga zawo. Ndiyeno, ganizirani mwakuya zimene mukuŵerenga; dzifunseni mafunso onga akuti: ‘Kodi nkhani imeneyi ikundiphunzitsa chiyani za Yehova? Kodi ndi khalidwe lake liti limene ndikuona pamenepa? Kodi ndi mfundo iti ya makhalidwe abwino imene Yehova akufuna kuti ndiphunzire, nanga ndingaigwiritse ntchito motani pa moyo wanga?’ Ŵerengani, lingaliraponi, ndipo gwiritsani ntchito zimene mukuŵerengazo. Mawu a Mulungu adzakhala amoyo kwa inu mukamachita zimenezi.—Salmo 77:12; Yakobo 1:23-25.

9. Kodi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” ndani, nanga n’chifukwa chiyani n’kofunika kumumvetsera mwatcheru?

9 Yehova amatilankhulanso kudzera mwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Monga mmene ananeneratu Yesu, pali kagulu ka Akristu odzozedwa kamene kaikidwa kuti kazipereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake” m’masiku otsiriza ovuta ano. (Mateyu 24:45-47) Tikamaŵerenga mabuku okonzedwa kuti atithandize kudziŵa molondola zinthu za m’Baibulo, ndiponso tikamafika pa misonkhano yachikristu ya pampingo ndi ikuluikulu yomwe, kagulu ka kapolo kameneko kamakhala kakutidyetsa mwauzimu. Popeza kuti ndi kapolo wa Kristu, timaonetsa nzeru  pogwiritsa ntchito mawu a Yesu akuti: ‘Yang’anirani mamvedwe anu.’ (Luka 8:18) Timamvetsera mwatcheru chifukwa timazindikira kuti kagulu ka kapolo ndi imodzi mwa njira zimene Yehova amalankhulira nafe.

10-12. (a) N’chifukwa chiyani pemphero lili mphatso yapamwamba kwambiri imene Yehova wapereka? (b) Kodi tingapemphere m’njira yotani yokondweretsa Yehova, nanga n’chifukwa chiyani tingakhale n’chidaliro chakuti iye amaona mapemphero athu kukhala ofunika kwambiri?

10 Koma bwanji za kulankhulana ndi Mulungu? Kodi Yehova tikhoza kulankhula naye? Ameneŵa ndi malingaliro ochititsa mantha. Ngati mutati muyese kukaonana ndi wolamulira wamphamvu kwambiri m’dziko lanu kuti mukakambirane naye mavuto anu, kodi mungaonane naye mosavuta? M’madera ena, kungoyesa kokha kuchita zimenezo kungakhale kuika moyo pachiswe. M’masiku a Estere ndi Moredekai, munthu akanatha kuphedwa chifukwa chopita kwa mfumu ya Perisiya popanda kuitanidwa ndi mfumuyo. (Estere 4:10, 11) Ndiyeno yerekezani kuti mukufika pamaso pa Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse, yemwe kwa iye anthu ngakhale amphamvu kwambiri “akunga ziwala.” (Yesaya 40:22) Kodi tiyenera kuchita mantha kwambiri kuti tilankhule naye? Ayi!

11 Yehova wapereka njira yotseguka kwa onse, komanso yapafupi, yolankhulirana naye, ndiyo pemphero. Ngakhale mwana wamng’ono kwambiri akhoza kupemphera ndi chikhulupiriro kwa Yehova m’dzina la Yesu. (Yohane 14:6; Ahebri 11:6) Komatu, pemphero limatithandizanso kumuuza zakukhosi kwathu ndiponso maganizo athu osautsa kwambiri—ngakhale maganizo opweteka amene amativuta kulongosola. (Aroma 8:26) N’zopanda phindu kuyesa kuchititsa chidwi Yehova ndi mapemphero onenedwa bwino ndi mawu okometseredwa, kapena mapemphero ataliatali omangobwerezabwereza mawu. (Mateyu 6:7, 8) Komabe, Yehova saika malire akuti tilankhule naye kwautali wotani kapena mwa kaŵirikaŵiri motani. Mawu ake amatiuza kuti ‘tizipemphera kosaleka.’—1 Atesalonika 5:17.

12 Kumbukirani kuti Yehova ndiye yekha amene amatchedwa kuti “Wakumva pemphero,” ndipo pamene akumvetsera amam’mveradi chisoni munthu. (Salmo 65:2) Kodi amangopirira  nawo mapemphero a atumiki ake okhulupirika? Ayi, koma amam’sangalatsa. Mawu ake amati mapemphero oterowo ali ngati chofukiza, chomwe akachitentha chimatulutsa utsi wa fungo lokoma ndi lonunkhira bwino. (Salmo 141:2; Chivumbulutso 5:8; 8:4) N’zolimbikitsatu kwambiri kuganizira kuti mapemphero athu ochokera pansi pamtima amakwera kumwamba mofananamo ndipo amakondweretsa Ambuye Mfumu! Motero ngati mukufuna kuyandikana ndi Yehova, pempherani kwa iye modzichepetsa nthaŵi ndi nthaŵi, tsiku lililonse. Muuzeni zakukhosi kwanu ndipo fotokozani zonse mosabisa. (Salmo 62:8) Atate wanu wakumwamba auzeni za nkhaŵa zanu, chisangalalo chimene muli nacho, zimene mukuyamikira, ndiponso zomwe mukutamanda. Chotsatira chake chidzakhala chakuti ubwenzi wanu ndi iye udzalimba kwambiri nthaŵi zonse.

Kulambira Yehova

13, 14. Kodi kulambira Yehova kumatanthauzanji, nanga n’chifukwa chiyani n’koyenera kuti tizichita zimenezo?

13 Pamene tikulankhulana ndi Yehova Mulungu, sikuti timangomumvetsera ndi kumulankhula monga mmene timachitira ndi mnzathu kapena wachibale wathu. Timakhala tikulambira Yehova; timamupatsa ulemu woyenera umene amafunika kulandira. Kulambira koona kumakhudza moyo wathu wonse. Kulambira kwathu kumasonyeza Yehova kuti timamukonda ndipo ndife odzipereka ndi moyo wonse kwa iye. Ndiponso, kumagwirizanitsa zolengedwa zokhulupirika zonse za Yehova, kaya zakumwamba kapena zapadziko lapansi. Mtumwi Yohane anamva m’masomphenya mngelo akulengeza lamulo lakuti: “M’lambireni Iye amene analenga m’mwamba ndi mtunda ndi nyanja ndi akasupe amadzi.”—Chivumbulutso 14:7.

14 Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kulambira Yehova? Talingalirani makhalidwe amene takambirana m’buku lino; makhalidwe monga chiyero, mphamvu, kudziletsa, chilungamo, kulimba mtima, chifundo, nzeru, kudzichepetsa, chikondi, kumvera ena chisoni, kukhulupirika, ndi ubwino. Taona kuti Yehova ndiye amaimira muyezo wapamwamba kwambiri wa khalidwe lililonse labwino. Pamene tiyesa kumvetsetsa makhalidwe ake onse pamodzi, timazindikira kuti sali chabe Amene ali wamkulu woti  tingachite naye kaso, koma ndi woposa pamenepo. Iye ndi waulemerero zedi ndipo ali patali kwambiri kuposa ifeyo. (Yesaya 55:9) Mosakayikira, Yehova ndiyedi Wolamulira wathu Wamkulu, ndipo akuyeneradi kuti tizimulambira. Komano, kodi Yehova tiyenera kumulambira motani?

15. Kodi Yehova tingamulambire motani “mumzimu ndi m’choonadi,” nanga misonkhano yachikristu imatipatsa mwayi wotani?

15 Yesu anati: “Mulungu ndiye mzimu; ndipo omulambira Iye ayenera kumulambira mumzimu ndi m’choonadi.” (Yohane 4:24) Zimenezi zikutanthauza kulambira Yehova ndi mtima wodzala chikhulupiriro ndi chikondi, motsogozedwa ndi mzimu wake. Zikutanthauzanso kulambira mogwirizana ndi choonadi; kudziŵa molondola zomwe zili m’Mawu a Mulungu. Timakhala ndi mwayi wosaneneka wolambira Yehova “mumzimu ndi m’choonadi” nthaŵi zonse pamene tisonkhana ndi olambira anzathu. (Ahebri 10:24, 25) Pamene tikuimba nyimbo zotamanda Yehova, pamene tipempherera pamodzi kwa iye, ndiponso  pamene timvetsera ndi kutenga nawo mbali pokambirana Mawu ake, timamusonyeza chikondi chathu mwa kulambira koyera.

Misonkhano yachikhristu ndi nthawi yabwino yolambira Yehova

16. Kodi lamulo limodzi mwa malamulo akuluakulu kwambiri amene Akristu oona apatsidwa ndi liti, nanga n’chifukwa chiyani timaona kuti tiyenera kulimvera?

16 Timalambiranso Yehova pamene tilankhula za iye kwa ena, kumuyamika pamaso pa anthu. (Ahebri 13:15) Inde, kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Yehova ndi lamulo limodzi mwa malamulo akuluakulu kwambiri amene Akristu oona apatsidwa. (Mateyu 24:14) Timamvera lamuloli mofunitsitsa chifukwa chokonda Yehova. Tikamaganiza za mmene “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano,” Satana Mdyerekezi, ‘wachititsira khungu maganizo awo a osakhulupirira,’ kulimbikitsa mabodza a njiru okhudza Yehova, kodi sitilakalaka kukhala Mboni za Mulungu wathu ndi kumafotokoza zoona zake pa mabodza amenewo? (2 Akorinto 4:4; Yesaya 43:10-12) Ndipo tikamasinkhasinkha za makhalidwe apamwamba a Yehova, kodi mumtima mwathu simudzala chikhumbo chofuna kuuza ena za iye? Ndithudi, sitingakhale ndi mwayi wina waukulu kuposa wothandiza anthu ena kudziŵa Atate wathu wakumwamba ndi kumamukonda monga mmene ife timachitira.

17. Kodi kulambira kwathu Yehova kumaphatikizapo chiyani, ndipo n’chifukwa chiyani tiyenera kumulambira mokhulupirika?

17 Kulambira kwathu Yehova kumaphatikizapo zambiri. Kumakhudza mbali iliyonse ya moyo wathu. (Akolose 3:23) Ngati timavomerezadi kuti Yehova ndiye Wolamulira wathu Wamkulu, tidzayesetsa kuchita zimene iye amafuna pa kalikonse—pa moyo wathu wabanja, ku ntchito kwathu, mu zochita zathu ndi ena, ngakhalenso pamene tikupuma. Tidzayesetsa kutumikira Yehova “ndi mtima wangwiro,” kumutumikira mokhulupirika. (1 Mbiri 28:9) Kulambira kotero sikulola munthu kukhala wa mitima iŵiri kapena kukhala wa chiphamaso—kukhala ndi moyo wachinyengo wooneka kuti amatumikira Yehova pamene kumbali amachita machimo akuluakulu. Kukhala wokhulupirika kumachititsa munthu kusakhala wachinyengo moteromo; ndipo kukhala wachikondi kumachititsa kuona chinyengocho kukhala chonyansa. Kuopa Mulungu kudzatithandizanso. Baibulo limati kuopa Mulungu kumatichititsa kupitiriza kukhalabe pa “ubwenzi” ndi Yehova.—Salmo 25:14, NW.

 Kutsanzira Yehova

18, 19. N’chifukwa chiyani n’zomveka kuganiza kuti anthu opanda ungwiro akhoza kutsanzira Yehova Mulungu?

18 Tamaliza chigawo chilichonse cha buku lino ndi mutu wonena za mmene ‘tingakhalire akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.’ (Aefeso 5:1) N’kofunika kukumbukira kuti ngakhale kuti ndife opanda ungwiro, tikhoza kutsanziradi njira yabwino zedi imene Yehova amagwiritsira ntchito mphamvu, amasonyezera chilungamo, amachitira zinthu mwanzeru, ndiponso mmene amaonetsera chikondi. Kodi timadziŵa bwanji kuti n’zothekadi kutengera Wamphamvuyonseyo? Kumbukirani kuti tanthauzo la dzina la Yehova limatiphunzitsa kuti iye amadzichititsa kukhala chilichonse chimene wasankha kuti akwaniritse zolinga zake. Moyenerera timachita mantha ndi nzeru zoterezi, koma kodi sitingathe kumutsanzira? N’zotheka.

19 Tinapangidwa m’chifanizo cha Mulungu. (Genesis 1:26) Motero anthu ndi osiyana ndi zolengedwa zina zonse padziko lapansi. Sitichita zinthu chifukwa chakuti tinabadwa ndi nzeru zochitira zinthuzo, kapena chifukwa cha zochitika zina m’malo amene tikukhala. Yehova anatipatsa mphatso ya mtengo wapatali, mphatso ya ufulu wodzisankhira zochita. Ngakhale kuti pali zina zimene sitingakwanitse kuchita ndiponso ndife opanda ungwiro, tili ndi ufulu wosankha kuti tikhala ndani. Kodi mukufuna kukhala munthu wachikondi, wanzeru, wachilungamo amene amagwiritsa ntchito bwino mphamvu? Mothandizidwa ndi mzimu wa Yehova, mukhoza kukhaladi munthu woteroyo! Taganizirani zabwino zimene mudzachita mutakhala munthu wotero.

20. Kodi timapindula chiyani pamene titsanzira Yehova?

20 Mudzakondweretsa mtima wa Atate wanu wakumwamba. (Miyambo 27:11) Mungakhalenso ‘okondweretsa monsemo’ kwa Yehova chifukwa amamvetsetsa kuti pali zina zimene simungakwanitse kuchita. (Akolose 1:9, 10) Ndipo pamene mukupitiriza kukhala ndi makhalidwe abwino potsanzira Atate wanu wokondedwa, mudzapatsidwa mwayi wapadera. M’dziko lamdima lopatuka kwa Mulunguli, inu mudzanyamula kuunika. (Mateyu 5:1, 2, 14) Mudzathandiza kufalitsa padziko lonse mbali zina za  umunthu wopambana wa Yehova. Umenewu ndi ulemutu waukulu kwambiri!

“Yandikirani kwa Mulungu, Ndipo Adzayandikira kwa Inu”

Nthaŵi zonse yandikiranibe kwa Yehova

21, 22. Kodi ndi ulendo wosatha uti umene onse okonda Yehova ayenera kuyenda?

21 Malangizo osavuta amene ali pa Yakobo 4:8 sali chabe mawu onena za chimene tiyenera kukwaniritsa. Ndi mawu onena za ulendo umene tiyenera kuyenda. Malinga ngati tikhala okhulupirika, ulendo umenewo sudzatha. Tidzayandikirayandikirabe kwambiri kwa Yehova. Nthaŵi zonse padzakhala zina zokhudza iye zofunika kuziphunzira. Tisalingalire kuti buku lino latiphunzitsa zonse zokhudza Yehova. Inde, tangoyambako chabe kukambirana zonse zimene Baibulo limanena za Mulungu wathu! Ndipo ngakhale Baibulolo silitiuza zinthu zonse zokhudza Yehova. Mtumwi Yohane ananena kuti ngati zonse zimene Yesu anachita mu utumiki wake wapadziko lapansi zikanalembedwa, ‘dziko lapansi silikadakhala nawo malo a mabuku amene akadalembedwawo.’ (Yohane 21:25) Ngati tinganene zimenezi ponena za Mwana, nanga kuli bwanji za Atate?

22 Sitidzamaliza kuphunzira za Yehova ngakhale pamene tili ndi moyo wamuyaya. (Mlaliki 3:11) Ndiyeno taganizirani zimene zikutidikira m’tsogolomu. Pambuyo pokhala ndi moyo kwa zaka  mahandiredi ambirimbiri, masauzande, mamiliyoni, ngakhale mabiliyoni ambirimbiri, tidzadziŵa zinthu zochuluka zokhudza Yehova Mulungu kuposa mmene tikudziŵira panopa. Koma tidzaonabe kuti pali zinthu zodabwitsa zosaŵerengeka zoti tiziphunzire. Tidzakhala ofunitsitsa kuphunzira zambiri pakuti nthaŵi zonse tidzakhala ndi zifukwa za kumva monga anamvera wamasalmo yemwe anaimba kuti: “Kundikomera kuyandikiza kwa Mulungu.” (Salmo 73:28) Moyo wamuyaya udzakhala watanthauzo kwambiri ndi wa zochita zosiyanasiyana, ndipo nthaŵi zonse kuyandikana ndi Yehova kudzakhala mbali yopindulitsa kwambiri ya moyo umenewo.

23. Kodi mukulimbikitsidwa kuchitanji?

23 Chitanipo kanthu pa chikondi cha Yehova tsopano lino mwa kumukonda ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse, nzeru zanu zonse, ndi mphamvu zanu zonse. (Marko 12:29, 30) Chikondi chanu chikhaletu chokhulupirika ndi chosagwedera. Zimene mukusankha kuchita tsiku lililonse, kuyambira zing’onozing’ono mpaka zikuluzikulu, zonse zionetsetu mfundo imodzimodziyo imene muziitsatira—yakuti nthaŵi zonse mudzasankha njira imene idzakuthandizani kukhala ndi ubwenzi wolimba zedi ndi Atate wanu wakumwamba. Koposa zonse, nthaŵi zonse yandikiranibe kwa Yehova, ndipo iyenso akuyandikirenibe nthaŵi zonse—mpaka muyaya!