1, 2. (a) Kodi ndi mafunso otani amene mungakonde kufunsa Mulungu? (b) Kodi Mose anafunsa chiyani kwa Mulungu?

KODI mungayerekeze kukhala mukucheza ndi Mulungu? N’kochititsa mantha zedi kungolingalira chabe kuti Wolamulira Wamkulu wa chilengedwe chonse akulankhula nawe! Poyamba mukukayikakayika, koma kenako mukuyankha bwinobwino. Iye akumvetsera, akukuyankhani, ndipo akukuchititsani kukhala womasuka kufunsa funso lililonse limene mungafune. Ndiye, kodi inu mungafunse funso lotani?

2 Kalekalelo, panali munthu yemwe zofanana ndendende ndi zimenezi zinamuchitikirapo. Dzina lake ndi Mose. Komatu mukhoza kudabwa ndi funso limene anasankha kufunsa Mulungu. Sanafunse za iye mwini, za tsogolo lake, ngakhale za mavuto a anthu. Iye anafunsa za dzina la Mulungu. Funsoli lingakudabwitseni, chifukwa Mose anali kudziŵa kale dzina la Mulungu. Ndiye kuti funso lake linali kutanthauza zambiri. Inde, linali funso lofunika kwambiri limene Mose akanafunsa. Yankho lake limakhudza tonsefe. Lingakuthandizeni kuchita zinthu zofunika kwambiri kuti muyandikire kwa Mulungu. Motani? Tiyeni tione mmene iwo anachezera mochititsa chidwi.

3, 4. Kodi n’zochitika zotani zomwe zinachititsa Mose kulankhulana ndi Mulungu, nanga ndi iti yomwe inali mfundo yaikulu ya kucheza kwawo?

3 Mose anali wa zaka 80. Panali patatha zaka makumi anayi kuchokera pamene anathaŵa ku Igupto komwe anthu a mtundu wake, Aisrayeli, anali akapolo. Tsiku lina, pamene anali kudyetsa nkhosa za apongozi ake, anaona chinthu chachilendo. Chitsamba chinali kuyaka moto koma icho osanyeka. Chinali kungoyakabe, ngati kuunika kooneka m’phiri. Mose anayandikira kuti aone chimene chinali kuchitika. Iye ayenera kuti anadzidzimuka kwambiri pamene anamva mawu omulankhula kuchokera pa motowo! Kenako Mulungu ndi Mose analankhulana kwanthaŵi yaitali kupyolera mwa mngelo. Ndipo  monga mukudziŵira, panthaŵiyi Mulungu anatuma Mose wamanthayo, kusiya moyo wamtendere womwe anali nawo ndi kubwerera ku Igupto kukalanditsa Aisrayeli mu ukapolo.—Eksodo 3:1-12.

4 Pamenepa Mose akanafunsa Mulungu funso lina lililonse. Koma taonani funso limene anasankha kufunsa: “Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nawo, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? Ndikanena nawo chiyani?”—Eksodo 3:13.

5, 6. (a) Kodi ndi choonadi chosavuta kumva komanso chofunika kwambiri chiti chimene funso la Mose likutiphunzitsa? (b) Ndi chinthu cholakwika chotani chimene chachitidwa pa dzina la Mulungu? (c) N’chifukwa chiyani kuli kofunika kwambiri kuti Mulungu waulula dzina lake kwa anthu?

5 Funso limenelo choyamba limatiphunzitsa kuti Mulungu ali ndi dzina lake. Choonadi chosavuta kumva chimenechi sitiyenera kuchipeputsa. Komatu n’zimene amachita ambiri. M’mabaibulo ambiri dzina la Mulungu alichotsamo ndipo m’malo mwake aikamo mayina audindo monga “Ambuye” ndi “Mulungu.” Chimenechi ndi chinthu chimodzi mwa zinthu zomvetsa chisoni ndi zolakwika kwambiri zimene zachitika ndi zolinga za chipembedzo. Ndiiko komwe, kodi n’chiyani chimene mumayambirira kuchita pamene mwakumana ndi munthu wina? Kodi simuyamba mwam’funsa dzina lake? N’chimodzimodzinso podziŵa Mulungu. Si munthu wopanda dzina yemwe alibe chidwi ndi anthu ena; ndiponso si munthu woti sitingathe kumudziŵa kapena kumumvetsa. Ngakhale kuti saoneka, iye ndi munthu ndipo ali ndi dzina; dzina lake ndi Yehova.

6 Ndiponso, Mulungu akaulula dzina lake ndiye kuti chinthu china chachikulu ndi chosangalatsa chili pafupi kuchitika. Akutiuza kuti timudziŵe. Akufuna kuti tisankhe chochita chabwino kwambiri pamoyo wathu, ndicho kumuyandikira. Komatu Yehova sanangotiuza chabe dzina lake. Watiphunzitsanso kuti iyeyo ndi wotani.

Tanthauzo la Dzina la Mulungu

7. (a) Kodi zikuoneka kuti dzina la Mulungu limatanthauza chiyani? (b) Kodi Mose makamaka anafuna kudziŵa chiyani pofunsa Mulungu dzina Lake?

7 Yehova anadzisankhira yekha dzina lake, dzina la tanthauzo  kwabasi. Zikuoneka kuti dzina lakuti “Yehova” limatanthauza kuti “Iye Amachititsa Kukhala.” M’chilengedwe chonse, palibe aliyense amene amafanana naye chifukwa chakuti iye ndiye anachititsa zinthu zonse kuti zikhaleko, ndipo amakwaniritsa zolinga zake zonse. Mfundo yokhayi ndi yodzetsa nthumanzi. Koma kodi tanthauzo la dzina la Mulunguli limangosonyeza kuti iye ndi mlengi basi? Ndithudi Mose anafuna kudziŵa zambiri. Iye ankadziwa kuti Yehova ndiye mlengi ndipo dzina la Mulungu ankalidziwa. Dzina la Mulungu silinali lachilendo. Anthu anakhala akuligwiritsa ntchito kwa zaka mazana ambiri. Mosakayikira, Mose pofunsa dzina la Mulungu anali kufunsa za munthu amene dzinalo limaimira. Kwenikweni anali kunena kuti: ‘Kodi anthu anu Aisrayeli ndingawauze zotani za inu zimene zidzawachititsa kukukhulupirirani, zomwe zidzawapatsa chidaliro chakuti inu mudzawalanditsadi?’

8, 9. (a) Kodi Yehova anayankha motani funso la Mose, nanga cholakwika n’chiyani ndi mmene mabaibulo ambiri amatembenuzira yankho Lake? (b) Kodi mawu akuti “ndidzakhala chimene ndidzakhala” amatanthauzanji?

8 Poyankha, Yehova anatchula mfundo yochititsa chidwi kwambiri yokhudza makhalidwe ake. Mfundo imeneyi ikukhudzana ndi tanthauzo la dzina lake. Anauza Mose kuti: “Ndidzakhala chimene ndidzakhala.” (Eksodo 3:14, NW) Baibulo lathu la Chicheŵa ndi mabaibulo ena ambiri amatembenuza vesili kuti: “Ine ndine yemwe ndili Ine.” Koma mabaibulo omasuliridwa mosamala amasonyeza kuti Mulungu sanali kungotsimikizira za kukhalapo kwake. M’malo mwake, anali kuphunzitsa Mose, ndiponso ifeyo, kuti Iye ‘adzakhala,’ kapena kuti adzasankha kukhala chilichonse chimene chikufunika kuti akwaniritse malonjezo Ake. Baibulo lotembenuzidwa ndi J. B. Rotherham limatembenuza vesili kuti: “Ndidzakhala chilichonse chimene ndifuna.” Katswiri wina wa chilankhulo cha Chihebri cha m’Baibulo analongosola vesili motere: “Zochitika zilizonse kapena zofunika zilizonse zomwe zingakhalepo . . . , Mulungu ‘adzakhala’ chimene chikufunikacho.”

9 Kodi zimenezi zinatanthauzanji kwa Aisrayeli? Ngakhale kuti patsogolo pawo panali zopinga ndi mavuto aakulu, Yehova anali kudzakhala chilichonse chimene chikafunika kuti awalanditse  ku ukapolo ndi kuwabweretsa m’Dziko Lolonjezedwa. Ndithudi dzinalo linawapatsa chidaliro mwa Mulungu. Ifenso lerolino lingatipatse chidaliro chofananacho. (Salmo 9:10) Chifukwa chiyani?

10, 11. Kodi dzina la Yehova limatiuza motani kuti tizimuganizira monga Atate wosinthasintha kwabasi ndiponso wabwino zedi pa onse? Perekani chitsanzo.

10 Tiyeni tifanizire motere. Makolo amadziŵa mmene ayenera kukhalira osinthasintha posamalira ana awo. Patsiku limodzi lokha, kholo lingafunike kukhala nesi, wophika, mphunzitsi, wopereka chilango, woweruza, ndi zina zambiri. Ambiri amathyoka m’nkhongono ndi kuchuluka kwa ntchito zimene amayembekezeredwa kugwira. Amaona kuti ana awo amakhala ndi chikhulupiriro chonse mwa iwo; anawo sakayika konse kuti Ababa kapena Amama apoletsa bala, athetsa mikangano yonse, akonza chidole chilichonse chimene chawonongeka, ndipo ayankha funso lililonse limene lingabwere m’malingaliro awo ofuna kudziŵa zinthu nthaŵi zonse. Makolo ena amadziona kuti n’ngosayenera kuwakhulupirira chonchi, ndipo nthaŵi zina amakhumudwa kumene chifukwa cholephera kuchita zinthu zina. Amamva kuti sangayesere m’pang’ono pomwe kuchita ntchito zochuluka mwa zimenezi.

11 Yehova nayenso ndi kholo lachikondi. Komatu, mosapatuka pa miyezo yake yangwiro, angathe kukhala chilichonse kuti asamalire ana ake a padziko lapansi m’njira yabwino kwambiri. Motero dzina lake lakuti Yehova, limatiuza kuti tizimuganizira monga Atate wabwino kwambiri pa onse. (Yakobo 1:17) Sipanatenge nthaŵi kuti Mose ndi Aisrayeli onse okhulupirika aone kuti Yehova alidi wogwirizana ndi dzina lake. Iwo akunthunthumira, anamuona akukhala Mkulu wa Nkhondo wosagonjetseka, Wolamulira zinthu zonse zachilengedwe, Wopereka Malamulo, Woweruza, Wolemba Mapulani, Wopereka chakudya ndi madzi, Wosunga zovala ndi nsapato, ndi zina zambiri mosafanana ndi wina aliyense.

12. Kodi maganizo a Farao pa Yehova anali osiyana motani ndi a Mose?

12 Choncho Mulungu watidziŵitsa dzina lake, watiphunzitsa zinthu zochititsa chidwi kwambiri zokhudza iyeyo, mwini wake wa dzinalo, ndiponso watisonyeza kuti zimene amanena  zokhudza iye ndi zoona. Mosakayikira Mulungu amafuna kuti timudziŵe. Kodi tikuchitapo chiyani? Mose anafuna kudziŵa Mulungu. Kufunitsitsa kumeneku kunasintha moyo wake ndi kumuchititsa kuyandikira kwambiri kwa Atate wake wakumwamba. (Numeri 12:6-8; Ahebri 11:27) N’zachisoni kuti anthu ochepa chabe m’nthaŵi ya Mose ndiwo anali n’chikhumbo chofananacho. Mose atatchula dzina la Yehova kwa Farao, wolamulira wa Igupto wodzitukumulayo anakalipa kuti: “Yehova ndani?” (Eksodo 5:2) Farao sanafune kuphunzira zochuluka za Yehova. M’malo mwake, monyodola anati Mulungu wa Israyeli ndi wosafunika kapena ndi wosayenera. Malingaliro amenewo ndi ofala kwambiri lerolino. Amatseka anthu m’maso kuti asadziŵe choonadi chofunika kwambiri chakuti Yehova ndiye Ambuye Mfumu.

Ambuye Mfumu Yehova

13, 14. (a) N’chifukwa chiyani Yehova amapatsidwa mayina audindo ambirimbiri m’Baibulo, nanga ena a mayinawo ndi ati? (Onani bokosi pa tsamba 14.) (b) N’chifukwa chiyani Yehova ali woyenera mwapadera kutchedwa kuti “Ambuye Mfumu”?

13 Yehova moyenerera ali ndi mayina audindo ambirimbiri m’Malemba. Mayina ameneŵa saposa dzina lake lenileni, koma amatiphunzitsa zina zomwe dzina lakelo limaimira. Mwachitsanzo, amatchedwa kuti “Ambuye Mfumu Yehova.” (2 Samueli 7:22, NW) Dzina lapamwamba limeneli, lomwe limapezeka nthaŵi mazana angapo m’malemba oyambirira a Baibulo, limatiuza udindo wa Yehova. Iye yekha ndiye ali ndi ufulu wokhala Wolamulira wa chilengedwe chonse. Taonani chifukwa chake.

14 Yehova ndi wapadera pokhala Mlengi. Pa Chivumbulutso 4:11 pamati: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.” Mawu amtengo wake ameneŵa sanganenedwe kwa wina aliyense. Kalikonse m’chilengedwe chonsechi kalipo chifukwa cha Yehova! Popanda kukayikira kulikonse, Yehova ndi woyenera ulemu, mphamvu, ndi ulemerero zomwe Ambuye Mfumu ndi Mlengi wa zinthu zonse amayenera kulandira.

15. N’chifukwa chiyani Yehova akutchedwa “Mfumu yosatha”?

 15 Dzina lina la udindo limene Yehova yekha ndiye amatchulidwa nalo ndi “Mfumu yosatha.” (1 Timoteo 1:17; Chivumbulutso 15:3) Kodi limatanthauzanji? N’kovuta kuti timvetsetse popeza ndife anthu a maganizo opereŵera, koma Yehova ndi wosatha kaya tibwerere m’mbuyo ku nthaŵi zakale ngakhalenso pamene tipita m’tsogolo. Salmo 90:2 limati: “Inde, kuyambira nthaŵi yosayamba kufikira nthaŵi yosatha, Inu ndinu Mulungu.” Motero Yehova alibe chiyambi; iye wakhalako nthaŵi zonse. Amatchedwa molondola kuti “Nkhalamba ya kale lomwe;” iye analipo kwa nthaŵi yosadziŵika munthu wina aliyense kapena chinthu china chilichonse m’chilengedwe chonse chisanakhalepo! (Danieli 7:9, 13, 22) Kodi ndani angakayikire kuti Iye ali ndi ufulu wokhala Ambuye Mfumu?

16, 17. (a) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova sitingamuone, nanga n’chifukwa chiyani zimenezi siziyenera kutidabwitsa? (b) Kodi ndi m’lingaliro lotani mmene Yehova ali weniweni kwambiri kuposa chilichonse chimene tingachione kapena kuchigwira?

16 Komatu anthu ena amakayikira ufulu wake umenewo, monga anachitira Farao. Nthaŵi zina vutoli limakhalapo chifukwa anthu opanda ungwiro amakonda kudalira zinthu zimene amaziona ndi maso. Ambuye Mfumu sitingamuone. Iye ndi munthu wauzimu, sangaoneke ndi maso aumunthu. (Yohane 4:24) Komanso, ngati munthu wathupi ndi mwazi atati aime pamene pali Yehova Mulungu, akhoza kufa. Yehova anauza Mose kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona ine ndi kukhala ndi moyo.”—Eksodo 33:20; Yohane 1:18.

17 Zimenezo sitiyenera kudabwa nazo. Mose anangoona mbali chabe ya ulemerero wa Yehova, mwachionekere anauona kupyolera mwa mngelo woimira Yehovayo. Kodi chinatsatirapo n’chiyani? Nkhope ya Mose ‘inanyezimira’ kwa kanthaŵi pambuyo pake. Aisrayeli anachita mantha ngakhale kuyang’ana nkhope ya Mose. (Eksodo 33:21-23; 34:5-7, 29, 30) Ndithudi palibe munthu aliyense amene angaone Ambuye Mfumu mu ulemerero wake wonse! Kodi izi zikutanthauza kuti iye sali weniweni monga zinthu zimene tingazione ndi kuzigwira? Ayi.  Timavomereza mosavuta kuti pali zinthu zambiri zomwe sitiziona, mwachitsanzo, timavomereza kuti pali mphepo, mphepo youlutsirapo mawu a wailesi, ndi maganizo. Ndiponso, Yehova ndi wachikhalire, sasintha chifukwa cha kupita kwa nthaŵi, ngakhale patapita zaka mabiliyoni osaŵerengeka. M’lingaliro limeneli, iye ali weniweni kwambiri kuposa chilichonse chimene tingachigwire kapena kuchiona, chifukwa za padzikoli zimakalamba ndi kuwola. (Mateyu 6:19) Komano, kodi tiyenera kumuganizira kuti ndi mphamvu chabe yosadziŵika bwino kapena Woyambitsa Zinthu wosamvetsetseka konse? Tiyeni tione.

Mulungu Ali ndi Umunthu

18. Kodi Ezekieli anaona masomphenya otani, nanga nkhope zinayi za “zamoyo” zomwe zinali pafupi ndi Yehova zikuimira chiyani?

18 Ngakhale kuti Mulungu sitingamuone, m’Baibulo muli ndime zosangalatsa zimene zimatithandiza kuzindikira za kumwamba. Imodzi mwa ndimezi ndi chaputala choyamba cha buku la Ezekieli. M’masomphenya, Ezekieli anaona gulu lakumwamba la Yehova, lomwe linali ngati galeta lalikulu zedi. Chochititsa chidwi kwambiri ndi mmene analongosolera zolengedwa zauzimu zamphamvu zomwe zinazungulira Yehova. (Ezekieli 1:4-10) “Zamoyo” zimenezi n’zogwirizanitsidwa zedi ndi Yehova, ndipo maonekedwe ake amatiuza kanthu kena kofunika kokhudza Mulungu amene zimatumikira. Chamoyo chilichonse chili ndi nkhope zinayi—nkhope ya ng’ombe, ya mkango, ya chiwombankhanga, ndi ya munthu. Ndithudi nkhope zimenezi zimaimira mbali zinayi zikuluzikulu za umunthu wa Yehova.—Chivumbulutso 4:6-8, 10.

19. Kodi ndi khalidwe liti lomwe (a) nkhope ya ng’ombe ikuimira? (b) nkhope ya mkango ikuimira? (c) nkhope ya chiwombankhanga ikuimira? (d) nkhope ya munthu ikuimira?

19 M’Baibulo, ng’ombe kaŵirikaŵiri imaimira mphamvu, ndipo m’poyenera chifukwa ng’ombe ndi nyama ya nyonga kwabasi. Pamene mkango kaŵirikaŵiri umaimira chilungamo, chifukwa kupereka chilungamo chenicheni kumafuna munthu wolimba mtima, khalidwe limene mikango imadziŵika nalo. Ziwombankhanga zimadziŵika bwino kuti zimaona zedi; zimatha kuona tinthu ting’onoting’ono tomwe tili kutali kwambiri.  Motero nkhope ya chiwombankhanga ikuimira bwino nzeru ya Mulungu yotha kuona patali. Nanga nkhope ya munthu? Eya, munthu, yemwe anapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, amasonyeza mwapadera khalidwe lalikulu la Mulungu, chikondi. (Genesis 1:26) Mbali zimenezi za umunthu wa Yehova—mphamvu, chilungamo, nzeru, ndi chikondi—zimatchulidwa kaŵirikaŵiri m’Malemba moti tikhoza kunena kuti ndiwo makhalidwe ofunika kwambiri a Mulungu.

20. Kodi tifunika kuda nkhaŵa kuti umunthu wa Yehova ungakhale utasintha, ndipo n’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?

20 Kodi tiyenera kuda nkhaŵa kuti Mulungu angakhale atasintha pa zaka masauzande angapo omwe adutsa kuchokera pamene analongosoledwa m’Baibulo? Ayi, chifukwa umunthu wa Mulungu susintha. Amatiuza kuti: “Ine Yehova sindisinthika.” (Malaki 3:6) M’malo mosintha mosalingalira bwino, Yehova amasonyeza kuti ndiye Atate wabwino mwa kachitidwe kake ka zinthu pa kalikonse kamene kakuchitika. Amaonetsa mbali za umunthu wake zimene zikufunikira kwambiri. Mwa mbali zinayizo, chikondi ndicho chimaposa zonse. Chimaonekera m’chilichonse chimene Mulungu amachita. Amasonyeza mphamvu zake, chilungamo chake, ndi nzeru zake mwachikondi. Ndipo Baibulo limanena chinachake chapadera chokhudza Mulungu  ndi khalidwe limeneli. Limati: “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:8) Taonani kuti silikunena kuti Mulungu ali ndi chikondi kapena kuti Mulungu ndi wachikondi. Koma likunena kuti Mulungu ndiye chikondi. Chikondi, umunthu wake weniweniwo, ndicho chimamusonkhezera pa zonse zimene amachita.

“Taonani, Uyu Ndiye Mulungu Wathu”

21. Kodi tidzamva bwanji pamene tikudziŵa bwino mbali za umunthu wa Yehova?

21 Kodi munamuonapo mwana wamng’ono akulozera anzake bambo ake ndiyeno mwachimwemwe ndi monyadira bwino n’kunena kuti, “Mwawaona ababa anga”? Amene amalambira Mulungu ali ndi zifukwa zomveka kuti azimva mofananamo ndi Yehova. Baibulo limaneneratu za nthaŵi imene anthu okhulupirika adzafuula kuti: “Taonani, uyu ndiye Mulungu wathu.” (Yesaya 25:8, 9) Pamene muzindikira kwambiri mbali za umunthu wa Yehova, m’pamenenso mudzamva kwambiri kuti muli ndi Atate wabwino zedi.

22, 23. Kodi Baibulo limasonyeza kuti Atate wathu wakumwamba ndi wotani, nanga timadziŵa motani kuti amafuna kuti tiyandikane naye?

22 Atate ameneyu sikuti ndi wopanda nsangala, kapena wopanda chidwi ndi anthu—ngakhale kuti n’zimene anthu ena achipembedzo ndi afilosofi onkitsa aphunzitsa. Sitikanakopeka ndi Mulungu wopanda nsangala, ndipo Baibulo silisonyeza Atate wathu wakumwamba kuti ndi wotero. M’malo mwake limati iye ndi “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Amanyansidwa kapenanso amamvera ena chisoni ndi zimene zikuchitika. ‘Amavutika mu mtima mwake’ pamene zolengedwa zake zanzeru ziphwanya malangizo amene amazipatsa kuti zizikhala ndi moyo wabwino. (Genesis 6:6; Salmo 78:41) Koma pamene tichita zinthu mwanzeru mogwirizana ndi Mawu ake, ‘timakondweretsa mtima’ wake.—Miyambo 27:11.

23 Atate wathu amafuna kuti tiyandikane naye. Mawu Ake amatilimbikitsa ‘kumufufuza ndi kumupeza, ngakhale sakhala patali ndi yense wa ife.’ (Machitidwe 17:27) Komano, kodi zingatheke bwanji kuti anthu ayandikire kwa Ambuye Mfumu ya chilengedwe chonse?