Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 11

Njira Zake Zonse Ndi Chilungamo

Njira Zake Zonse Ndi Chilungamo

 

PANALIBE chilungamo m’pang’onong’ono pomwe. Mnyamata wokongolayo sanalakwe chilichonse, komatu anali m’ndende atamunamizira kuti anafuna kugwiririra mkazi. Koma aka sikoyamba kuti anthu amuchitire zinthu zopanda chilungamo. M’mbuyomo ali ndi zaka 17, mnyamatayu, Yosefe, abale ake enieni, omwe anatsala pang’ono kumupha, anamupereka kwa anthu ena. Panthaŵi imeneyo anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku dziko lina. Ku dzikolo, sanavomere kugona ndi mkazi wa bwana wake pamene mkaziyo anali kumunyengerera. Mkazi wokanidwa mochititsa manyaziyo anamusemera chinyawu, ndipo zimenezi ndizo zinamuloŵetsa m’ndende. Zomvetsa chisoni n’zakuti palibe aliyense amene anali kuoneka kuti angaloŵererepo kuti athandize Yosefe.

Yosefe anavutika mosalungama ‘m’dzenje’ la ndende

2 Komabe, Mulungu “wakukonda chilungamo ndi chiweruzo” anali kuona zonsezo. (Salmo 33:5) Yehova anachitapo kanthu kuti athetse kusalungamako. Anayendetsa zinthu m’njira yakuti Yosefe anamasulidwa. Kuposa pamenepo, Yosefe, munthu amene anaikidwa ‘m’dzenje’ la ndende, kenako anapatsidwa udindo waukulu kwambiri ndiponso waulemu wapadera. (Genesis 40:15; 41:41-43; Salmo 105:17, 18) Pamapeto pake Yosefe anaoneka kuti analibe mlandu, ndipo anagwiritsa ntchito udindo wake wapamwambawo pothandiza kuti cholinga cha Mulungu chichitike.—Genesis 45:5-8.

3. N’chifukwa chiyani n’zosadabwitsa kuti tonse timafuna kutichitira zinthu mwachilungamo?

3 Nkhani yotereyi imatikhudza mitima, kodi sichoncho? Kodi ndani wa ife amene sanaonepo zinthu zikuchitika mopanda chilungamo kapena kuvutikapo ndi zoterozo? Ndithudi, aliyense amafuna kumuchitira zoyenera ndi mosakondera. N’zosadabwitsa, chifukwa Yehova anatipatsa makhalidwe amene amasonyeza  umunthu wake, ndipo chilungamo ndi khalidwe limodzi mwa makhalidwe ake akuluakulu. (Genesis 1:27) Tifunika kumvetsetsa mmene Yehova amaonera chilungamo kuti tithe kumudziŵa bwino. Motero tingazindikire ndi kuyamikira kwambiri njira zake zodabwitsa ndi kuyandikana naye.

Kodi Chilungamo N’chiyani?

4. Malinga ndi mmene anthu amaonera zinthu, kodi nthaŵi zambiri amati chilungamo n’chiyani?

4 Malinga ndi mmene anthu amaonera zinthu, nthaŵi zambiri amati chilungamo ndicho kugwiritsa ntchito malamulo mosakondera. Buku lotchedwa kuti Right and Reason—Ethics in Theory and Practice limanena kuti “chilungamo n’chogwirizana ndi malamulo, udindo umene munthu ayenera kukwaniritsa, ufulu, ndi ntchito, ndipo chimapereka chigamulo chake mosakondera kapena mogwirizana ndi zifukwa zomveka bwino.” Komatu chilungamo cha Yehova chimaposa pa kungogwiritsa ntchito malamulo chifukwa chakuti akufunika kugwira ntchito pamenepo kapenanso chifukwa choti ali ndi udindo wogwiritsa ntchito malamulowo.

5, 6. (a) Kodi mawu a zinenero zoyambirira omwe atembenuzidwa kuti “chilungamo” ndi “chiweruzo” kapena kuti “chiweruziro” amatanthauzanji? (b) Kodi kunena kuti Mulungu ndi wolungama zimatanthauza chiyani?

5 Tingazindikire bwino kukula ndi kuya kwa chilungamo cha Yehova mwa kulingalira mawu a zinenero zoyambirira omwe anawagwiritsira ntchito m’Baibulo. M’Malemba Achihebri, anagwiritsa ntchito mawu atatu ofunika zedi. Mawu amene kaŵirikaŵiri amatembenuzidwa kuti “chiweruzo” kapena “chiweruziro” angatembenuzidwenso kuti “zoyenera.” (Genesis 18:25) Mawu ena aŵiriwo nthaŵi zambiri amatembenuzidwa kuti “chilungamo.” M’Malemba Achigiriki Achikristu, mawu amene amatembenuzidwa kuti “chilungamo” amatanthauziridwa kuti “kukhala choyenera.” Motero palibe kusiyana kwenikweni pakati pa mawu akuti chilungamo ndi akuti chiweruzo.—Amosi 5:24.

6 Choncho pamene Baibulo limati Mulungu ndi wolungama, limatiuza kuti iye amachita zinthu zoyenera ndi zosakondera,  ndi kuti nthaŵi zonse amachita zimenezi mopanda tsankhu. (Aroma 2:11) Ndithudi sitingayembekeze kuti angachite zosiyana ndi zimenezi. Munthu wokhulupirika Elihu anati: “N’kutali ndi Mulungu kuchita choipa, ndi Wamphamvuyonse kuchita chosalungama.” (Yobu 34:10) N’zosathekadi kuti Yehova ‘achite chosalungama.’ Chifukwa chiyani? Pa zifukwa zikuluzikulu ziŵiri.

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani Yehova sangathe kuchita chosalungama? (b) Kodi n’chiyani chimene chimachititsa Yehova kukhala wolungama pochita zinthu ndi ena?

7 Choyamba, iye ndi woyera. Monga tinaonera m’Mutu 3, Yehova ndi waudongo kwambiri ndiponso wolungama. Motero sangachite zinthu mosalungama. Lingalirani zomwe zimenezi zikutanthauza. Chiyero cha Atate wathu wakumwamba chimatipatsa chifukwa chomveka chokhulupirira kuti iye sangazunze ana ake. Yesu anali ndi chidaliro choterechi. Usiku wa tsiku lomaliza kukhala ndi moyo pa dziko lapansi, anapemphera kuti: “Atate Woyera, sungani aŵa [ophunzira] m’dzina lanu.” (Yohane 17:11) M’Malemba, ndi Yehova yekha amene amanenedwa kuti “Atate Woyera.” Izi n’zoyenera, chifukwa palibe atate waumunthu aliyense amene angafanane Naye pa kukhala woyera. Yesu anali ndi chikhulupiriro chonse kuti Atate, yemwe ndi waudongo pakalikonse ndipo ndi wosakhudzidwa m’pang’onong’ono pomwe ndi uchimo, adzawasunga bwino ophunzira ake.—Mateyu 23:9.

8 Chachiŵiri, chikondi chopanda dyera ndicho umunthu weniweni wa Mulungu. Chikondi choterechi chimamuchititsa kukhala wolungama pochita zinthu ndi ena. Koma kupanda chilungamo kwa mtundu uliwonse—kuphatikizapo kusankhana mitundu, tsankhu, ndi kukondera—kaŵirikaŵiri kumayamba chifukwa cha dyera ndi umbombo, zimene zili zochita zotsutsana ndi chikondi. Ponena za Mulungu wa chikondi, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Yehova ndiye wolungama; akonda zolungama.” (Salmo 11:7) Yehova iye mwini anati: “Ine Yehova ndikonda chiweruziro.” (Yesaya 61:8) Kodi si zokhazika mtima  pansi kudziŵa kuti Mulungu wathu amasangalala kuchita zimene zili zoyenera kapena kuti zolungama?—Yeremiya 9:24.

Chifundo Limodzi ndi Chilungamo Chenicheni cha Yehova

9-11. (a) Kodi chilungamo cha Yehova ndi chogwirizana motani ndi chifundo chake? (b) Kodi chilungamo cha Yehova limodzi ndi chifundo chake zaoneka motani ndi mmene amachitira zinthu ndi anthu ochimwa?

9 Chilungamo cha Yehova ndi chenicheni ndipo sichipereŵera kalikonse, mofanana ndi mbali ina iliyonse ya umunthu wake wosayerekezeka. Potamanda Yehova, Mose analemba kuti: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; Iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:3, 4) Nthaŵi zonse pamene Yehova wasonyeza chilungamo, chimakhala chosalakwika—samvera chisoni kwambiri komanso sachita nkhanza kwambiri.

10 Chilungamo cha Yehova ndi chogwirizana kwambiri ndi chifundo chake. Salmo 116:5 limati: “Yehova ngwa chifundo ndi wolungama; ndi Mulungu wathu ngwa nsoni.” Inde, Yehova ndi wolungama ndiponso wachifundo. Makhalidwe aŵiriŵa si osemphana. Sasukulutsa chilungamo chake pamene akusonyeza chifundo, ngati kuti akanapanda kutero akanapereka chiweruzo chokhwima kwambiri. Koma m’malo mwake, iye amaonetsa makhalidwe aŵiriŵa panthaŵi imodzimodzi, ngakhalenso pa chochitika chimodzimodzi chomwecho. Taonani chitsanzo ichi.

11 Anthu onse analandira choloŵa cha uchimo, choncho amayenera kulandiranso chilango cha uchimowo chomwe ndi imfa. (Aroma 5:12) Koma Yehova sasangalala ndi imfa ya ochimwa. Iye ndi “Mulungu wokhululukira, wachisomo, ndi wansoni.” (Nehemiya 9:17) Komabe pokhala woyera, sangalole zinthu zosalungama. Ndiyeno, kodi iye angawasonyeze chifundo motani anthu omwe analandira uchimo? Yankho lake timalipeza mu choonadi china chofunika kwambiri cha Mawu a Mulungu: makonzedwe a dipo amene Yehova anapanga kuti apulumutse anthu. Tidzaphunzira zambiri za makonzedwe  achikondi ameneŵa mu Chaputala 14. Makonzedweŵa amasonyeza chilungamo kwambiri ndipo panthaŵi imodzimodziyo amasonyeza chifundo kwabasi. Mwa makonzedwe ameneŵa, Yehova angachitire chifundo ochimwa olapa uku akutsatirabe mfundo zake za chilungamo chenicheni.—Aroma 3:21-26.

Chilungamo cha Yehova Ndi Chokondweretsa

12, 13. (a) N’chifukwa chiyani chilungamo cha Yehova chimatiyandikizitsa kwa iye? (b) Kodi Davide ananenanji za chilungamo cha Yehova, nanga zimenezi zingatilimbikitse motani?

12 Chilungamo cha Yehova si khalidwe losasangalatsa limene limatilepheretsa kumuyandikira, koma ndi khalidwe labwino limene limatipangitsa kumuyandikira. Baibulo limalongosola momveka bwino kuti chilungamo cha Yehova n’chachifundo. Tiyeni tione njira zina zosangalatsa zimene Yehova amasonyezera chilungamo chake.

13 Chilungamo changwiro cha Yehova chimamuchititsa kukhala wokhulupirika ndi wodalirika kwa atumiki ake. Wamasalmo Davide anachita kudzionera yekha mbali imeneyi ya chilungamo cha Yehova. Kuchokera pa zimene zinamuchitikira ndiponso pa kuphunzira kwake njira za Mulungu, kodi Davide anati chiyani? Analengeza kuti: “Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake: Asungika kosatha.” (Salmo 37:28) Ndi mawu olimbikitsa bwanji! Nthaŵi zonse Mulungu wathu sadzataya amene ali okhulupirika kwa iye. Motero tingadalire kuti ali woyandikana nafe ndi kuti amatisamalira mwachikondi. Chilungamo chake chimatitsimikizira zimenezi!—Miyambo 2:7, 8.

14. Kodi Chilamulo chimene Yehova anapatsa Israyeli chimaonetsa motani kuti iye amadera nkhaŵa anthu ovutika?

14 Chifukwa chakuti ndi wachilungamo, Mulungu amazindikira bwino kwambiri zimene anthu ovutika akufunika. Yehova amadera nkhaŵa anthu ovutika, ndipo zimenezi zimaoneka mosavuta m’Chilamulo chimene anapatsa Aisrayeli. Mwachitsanzo, m’Chilamulocho munali makonzedwe apadera otsimikizira kuti ana amasiye ndi akazi amasiye anali kusamalidwa. (Deuteronomo 24:17-21) Pozindikira kuti moyo  udzakhala wovuta kwa mabanja oterowo, Yehova mwiniyo anali Woweruza wawo ndi Mtetezi wawo monga ngati tate, yemwe ‘anaweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye.’ (Deuteronomo 10:18; Salmo 68:5) Yehova anachenjeza Aisrayeli kuti ngati angazunze akazi ndi ana osoŵa chitetezo, iye ndithudi adzamva kulira kwawo. Iye anati: ‘Mkwiyo wanga udzayaka.’ (Eksodo 22:22-24) Ngakhale kuti mkwiyo si khalidwe lina lalikulu la Yehova, molungama iye amakwiya ngati mwadala anthu sakuchita zachilungamo, makamaka pamene ovutikawo ndi anthu odzichepetsa ndi osoŵa thandizo.—Salmo 103:6.

15, 16. Kodi ndi umboni wochititsa chidwi kwambiri wotani umene umasonyeza kuti Yehova alibe tsankhu?

15 Yehova akutitsimikiziranso kuti ‘sasamalira nkhope za anthu kapena kulandira chokometsera mlandu.’ (Deuteronomo 10:17) Mosiyana ndi anthu ambiri amene ali ndi udindo kaya mphamvu, Yehova satengeka ndi chuma chakuthupi kapena kaonekedwe ka munthu. Iye sakondera kaya kuchita tsankhu m’pang’onong’ono pomwe. Taonani umboni wochititsa chidwi uwu wakuti Yehova alibe tsankhu. Mwayi wokhala olambira ake oona, omwe akuyembekeza moyo kosatha, sunaperekedwe kwa anthu osankhika ochepa okha. Koma “m’mitundu yonse, wakumuopa iye ndi wakuchita chilungamo alandiridwa naye.” (Machitidwe 10:34, 35) Aliyense angakhale ndi chiyembekezo chabwino kwambiri chimenechi mosasamala kanthu kuti ndi munthu wotani m’dera lakwawo, kaya kuti ali ndi khungu lamtundu wanji, kapenanso kuti akukhala m’dziko liti. Kodi chimenechi sindicho chilungamo chenicheni?

16 Palinso mbali ina ya chilungamo changwiro cha Yehova imene tifunika kuilingalira ndi kuizindikira. Iyi ikukhudza mmene Yehova amachitira ndi anthu olakwira miyezo yake yolungama.

Samasula Wopalamula

17. Fotokozani chifukwa chake zochitika zosayenerera za m’dzikoli sizitsutsa chilungamo cha Yehova m’pang’ono pomwe.

17 Ena angalingalire kuti: ‘Popeza kuti Yehova salekerera makhalidwe  osalungama, nanga n’chifukwa chiyani lerolino anthu akuvutika popanda chifukwa ndipo makhalidwe oipa nawonso ali ponseponse m’dzikoli?’ Zochitika zosayenerera zimenezo sizitsutsa chilungamo cha Yehova m’pang’ono pomwe. Zochitika zambirimbiri zopanda chilungamo m’dziko loipali zili zotsatirapo za uchimo umene anthu analandira kuchokera kwa Adamu. M’dziko limene anthu opanda ungwiro asankha kuyenda m’njira zawo zauchimo, zochitika zopanda chilungamo n’zambirimbiri, koma sikuti zikhala mpaka kalekale.—Deuteronomo 32:5.

18, 19. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti Yehova sadzalola anthu amene amaswa mwadala malamulo ake olungama kukhalapo mpaka kalekale?

18 Ngakhale kuti Yehova amachitira chifundo kwambiri anthu amene amayandikana naye moona mtima, iye sadzalolera mpaka kalekale zochitika zimene zimabweretsa chitonzo pa dzina lake loyera. (Salmo 74:10, 22, 23) Mulungu wa chilungamo sanyozeka; sadzakhalira kumbuyo ochimwa mwadala kuti asalandire chiweruzo choŵaŵa choyenerana ndi zochita zawo. Yehova ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; . . . koma wosamasula wopalamula.” (Eksodo 34:6, 7) Mogwirizana ndi mawu ameneŵa, panthaŵi zina Yehova waona kukhala kofunika kulanga amene amaswa mwadala malamulo ake olungama.

19 Mwachitsanzo, lingalirani mmene Mulungu anali kuchitira zinthu ndi Israyeli wakale. Ngakhale pamene anakhazikika mu Dziko Lolonjezedwa, nthaŵi ndi nthaŵi Aisrayeli anali kukhala osakhulupirika. Ngakhale kuti njira zawo zoipa ‘zinamumvetsa chisoni’ Yehova, iye sanawataye mofulumira. (Salmo 78:38-41) M’malo mwake, mwachifundo anali kuwapatsa mwayi woti asinthe njira zawo. Anawachonderera kuti: “Sindikondwera nayo imfa ya woipa, koma kuti woipa aleke njira yake, nakhale ndi moyo; bwererani, bwererani, kuleka njira zanu zoipa, muferenji inu nyumba ya Israyeli?” (Ezekieli 33:11) Poona kuti moyo ndi wamtengo wapatali, Yehova anatuma aneneri ake mobwerezabwereza kuti mwina Aisrayeli asiye njira zawo zoipa. Koma mochulukira anthu ouma mitimawo anakana kumvera ndi kulapa.  Pomalizira pake, Yehova anawapereka m’manja mwa adani awo pofuna kuteteza dzina lake loyera ndi zonse zimene dzinalo limaimira.—Nehemiya 9:26-30.

20. (a) Kodi timaphunziranji za Yehova pa zimene iye anachita ndi Israyeli? (b) N’chifukwa chiyani mkango uli chizindikiro choyenerera cha chilungamo cha Yehova?

20 Zimene Yehova anali kuchita ndi Israyeli zimatiphunzitsa zambiri zokhudza iye. Timaphunzira kuti maso ake omwe amaona kalikonse, amaonanso zinthu zosalungama ndipo zimene amaona zimamukhudza mtima kwambiri. (Miyambo 15:3) Mitima yathu imakhalanso pansi podziŵa kuti amafuna kuchitira anthu chifundo ngati pali chifukwa chowachitira chifundocho. Ndiponso, timaphunzira kuti sadya mfulumira ndi chilungamo chake. Chifukwa chakuti Yehova ndi woleza mtima ndiponso amapirira kwambiri, anthu ambiri amanena molakwa kuti iye sadzaweruza anthu oipa. Koma zimenezi sizoona, chifukwa zimene Mulungu anali kuchita ndi Israyeli zimatiphunzitsanso kuti kuleza mtima kwake kuli ndi malire. Yehova sapatuka pa chilungamo. Mosiyana ndi anthu, omwe kaŵirikaŵiri safuna kuweruza ena, iye nthaŵi zonse amakhala wolimba mtima pa chimene chili cholungama. Moyenerera, mkango, womwe ndi chizindikiro cha kusonyeza chilungamo molimba mtima, umagwirizanitsidwa ndi kukhalapo kwa Mulungu ndi mpando  Wake wachifumu. * (Ezekieli 1:10; Chivumbulutso 4:7) Motero tingakhale otsimikiza kuti adzakwaniritsa lonjezo lake lochotsa khalidwe lopanda chilungamo pa dziko lapansili. Inde, tinganene mwachidule kuti iye amaweruza motere: kulimba mtima pamene kukufunika, kuchita chifundo nthaŵi iliyonse pamene kuli kotheka.—2 Petro 3:9.

Kuyandikana ndi Mulungu wa Chilungamo

21. Pamene tisinkhasinkha mmene Yehova amasonyezera chilungamo, kodi tiyenera kumuganizira mwa njira yotani, nanga n’chifukwa chiyani?

21 Pamene tisinkhasinkha mmene Yehova amasonyezera chilungamo, tisamulingalire kuti ndi woweruza wopanda nsangala ndi woumirira pa chinthu chimodzimodzi yemwe amangosangalala ndi kuweruza olakwa. M’malo mwake tizimuganizira monga Atate wachikondi ndi wotsimikiza mtima pochita zinthu, yemwe nthaŵi zonse amachita ndi ana ake m’njira yabwino koposa. Pokhala Atate wolungama, Yehova amakhala wolimba mtima pa cholungama kwinaku akuchitira chifundo ana ake a padziko lapansi omwe amafuna kuti awathandize ndi kuwakhululukira.—Salmo 103:10, 13.

22. Chifukwa cha chilungamo chake, kodi Yehova wakonza kuti tithe kukhala ndi chiyembekezo chotani, nanga n’chifukwa chiyani amachita nafe mwa njira yotereyi?

22 Tikuthokoza kwambiri kuti Mulungu sasonyeza chilungamo chake mwakungopereka chiweruzo pa olakwa! Chifukwa cha chilungamo chake, Yehova wakonza kuti tithe kukhala ndi chiyembekezo chosangalatsa kwabasi—kukhala ndi moyo wangwiro, wosatha m’dziko limene ‘mudzakhalitsa chilungamo.’ (2 Petro 3:13) Mulungu wathu amachita nafe moteremu chifukwa chakuti chilungamo chake chimamuchititsa kufunafuna njira zopulumutsira anthu m’malo mowatsutsa. Ndithudi, kumvetsetsa mmene chilungamo cha Yehova chilili kumatithandiza kuyandikana naye! M’machaputala otsatiraŵa, tiphunzira mwatsatanetsatane mmene Yehova amasonyezera khalidwe labwino kwambiri limeneli.

^ ndime 20 N’zochititsa chidwi kuti Yehova anadziyerekeza ndi mkango popereka chiweruzo kwa Israyeli wosakhulupirika.—Yeremiya 25:38; Hoseya 5:14.

Mafunso Owasinkhasinkha