Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 MUTU 12

“Kodi Chilipo Chosalungama ndi Mulungu?”

“Kodi Chilipo Chosalungama ndi Mulungu?”

1. Kodi zochitika zopanda chilungamo zingatikhudze motani?

MKAZI wokalamba wamasiye amubera ndalama zimene anali kusunga. Kholo louma mtima lathaŵa khanda lake lobadwa kumene. Mwamuna wina waikidwa m’ndende chifukwa cha mlandu woti sanapalamule ndiye. Kodi mukumva bwanji ndi zochitika zimenezi? Mwinamwake chilichonse chakunyansani, ndipo m’pomveka kutero. Anthufe timasiyanitsa mofulumira chinthu chabwino ndi choipa. Ngati pachitika zopanda chilungamo, timakalipa kwambiri. Timafuna kuti amene wavutikayo apatsidwe chipukuta misozi ndipo wolakwayo alangidwe. Ngati zimenezi sizikuchitika, timadabwa kuti: ‘Kodi Mulungu amaona zimene zikuchitikazi? N’chifukwa chiyani sachitapo kanthu?’

2. Kodi Habakuku anatani ataona kuti chilungamo chikusoŵeka, nanga n’chifukwa chiyani Yehova sanamudzudzule nazo zimenezi?

2 Mu mbiri yonse ya anthu, atumiki okhulupirika a Yehova akhala akufunsa mafunso ngati amenewo. Mwachitsanzo, mneneri Habakuku anapemphera kwa Mulungu kuti: “N’chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zopanda chilungamo zoopsa chonchi? N’chifukwa chiyani mukulola chiwawa, kusayeruzika, upandu, ndi nkhanza kufalikira ponseponse?” (Habakuku 1:3, Contemporary English Version) Yehova sanadzudzule Habakuku chifukwa chomufunsa moona mtima, popeza Iye ndiye amene anapatsa anthu malingaliro ozindikira chimene chili cholungama. Inde, Yehova anatipatsa mtima woti pang’ono pokha tiziganiza za chilungamo chimene iye amachiganizira kwambiri.

Yehova Amadana ndi Kupanda Chilungamo

3. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova amadziŵa bwino kwambiri za zochitika zopanda chilungamo kuposa mmene ife timadziŵira?

3 Yehova amadziŵa zochitika zonse zopanda chilungamo.  Amaona zimene zikuchitika. Baibulo limatiuza kuti m’masiku a Nowa, “anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu pa dziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yawo zinali zoipabe zokhazokha.” (Genesis 6:5) Talingalirani zimene mawuŵa akutanthauza. Nthaŵi zambiri, ife anthu timazindikira zinthu zopanda chilungamo kuchokera pa zochitika zoŵerengeka zimene tazimvapo kapena zimene zatichitikira ife eni. Mosiyana nafe, Yehova akudziŵa za kupanda chilungamo kochitika pa dziko lonse. Amaona zinthu zosalungama zonse! Kuposa pamenepo, iye angazindikire zimene zili mu mtima mwa munthu; ndiko kuti kulingalira kolakwika kumene kumayambitsa zochitika zosalungama.—Yeremiya 17:10.

4, 5. (a) Kodi Baibulo limasonyeza motani kuti Yehova amasamalira anthu amene anzawo sanawachitire zachilungamo? (b) Kodi Yehova mwiniyo wakhudzidwa motani ndi zinthu zosalungama?

4 Koma Yehova sikuti amangozindikira zinthu zopanda chilungamo osachitapo kalikonse. Amasamaliranso anthu amene avutika ndi kupanda chilungamoko. Pamene mitundu ya adani inachitira nkhanza anthu ake, Yehova anamva chisoni ndi “kubuula kwawo chifukwa cha iwo akuwapsinja ndi kuwatsendereza.” (Oweruza 2:18) Mwinamwake mwaonapo kuti anthu ena akamaona mobwerezabwereza zinthu zosalungama, samveranso chisoni anthu omwe akuvutikawo. Yehova sachita zimenezo! Waona zinthu zonse zosalungama kwa zaka ngati 6,000, komatu iye amadana nazobe, sanasinthe. Ndipo Baibulo limatitsimikizira kuti zinthu ngati “lilime lonama,” “manja akupha anthu osachimwa,” ndi “mboni yonama yonong’ona mabodza” zimamunyansa Yehova.—Miyambo 6:16-19.

5 Talingaliraninso mmene Yehova anadzudzulira mwamphamvu atsogoleri opanda chilungamo a Israyeli. “Simuyenera kodi kudziŵa chiweruzo?” anauza mneneri wake kuti awafunse motero. Atafotokoza momveka bwino mmene amuna achinyengoŵa anali kugwiritsira ntchito molakwa mphamvu zawo, Yehova ananena zimene zidzawachitikira kuti: “Adzafuulira kwa Yehova, koma sadzawayankha; inde, adzawabisira  nkhope yake nthaŵi yomweyo, monga momwe anaipsa machitidwe awo.” (Mika 3:1-4) Yehova amadanatu kwambiri ndi zinthu zopanda chilungamo! Ee, iye mwini zakhala zikumuchitikirapo! Satana wakhala akunyoza Yehova kwa zaka masauzande ambiri popanda chifukwa. (Miyambo 27:11) Ndiponso, Yehova anakhudzidwa mtima ndi chochitika choopsa kwambiri cha kupanda chilungamo pamene Mwana wake, yemwe ‘sanachite tchimo,’ anaphedwa monga munthu wopanduka. (1 Petro 2:22; Yesaya 53:9) Ndithudi, Yehova amazindikira kuti anthu ena akuvutika ndi kupanda chilungamo ndipo amawasamalira.

6. Kodi tingafune kuchita zinthu motani pamene zinthu zosalungama zikutichitikira, nanga n’chifukwa chiyani?

6 Komano, n’kwachibadwa kufuna kuchita zinthu mwamphamvu pamene tiona zosalungama, kapena pamene ifeyo tavutika chifukwa ena achita zinthu mokondera. Tinapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, ndipo kupanda chilungamo ndi kosiyana kwambiri ndi zonse zimene Yehova amaimira. (Genesis 1:27) Nangano n’chifukwa chiyani Mulungu amalola zinthu zopanda chilungamo?

Nkhani ya Ulamuliro wa Mulungu

7. Longosolani mmene ulamuliro wa Yehova unatsutsidwira.

7 Yankho la funsoli n’logwirizana ndi nkhani ya ulamuliro. Monga taonera, Mlengi ali ndi ufulu wolamulira dziko lapansi ndi onse okhalamo. (Salmo 24:1; Chivumbulutso 4:11) Komabe, koyambirira kwa mbiri ya anthu ulamuliro wa Yehova unatsutsidwa. Kodi zimenezi zinachitika motani? Yehova analamula mwamuna woyambayo, Adamu, kuti asadye zipatso za mtengo winawake wa m’munda umene unali mudzi wake wa Paradaiso. Nanga ngati akanapanda kumvera? Mulungu anamuuza kuti: “Udzafa ndithu.” (Genesis 2:17) Lamulo la Mulungu silinamuvutitse Adamu ngakhalenso mkazi wake, Hava. Komabe, Satana anakhutiritsa Hava maganizo kuti Mulungu anali kuwaletsa zinthu monyanyira. Nanga bwanji ngati Hava akanadya zipatso za mtengowo? Satana anauza Hava mosabisa mawu, kuti: ‘Kufa simudzafai; chifukwa adziŵa Mulungu  kuti tsiku limene mukadya umenewo, adzatseguka maso anu, ndipo mudzakhala ngati Mulungu, wakudziŵa zabwino ndi zoipa.’—Genesis 3:1-5.

8. (a) Kodi Satana anali kutanthauza chiyani ndi mawu amene anauza Hava? (b) Kodi n’chiyani chimene Satana anatsutsa pa ulamuliro wa Mulungu?

8 Ndi mawu ameneŵa, Satana sanangotanthauza kuti Yehova anabisira Hava zinthu zimene anafunika kuzidziŵa, koma anatanthauzanso kuti Yehova ananamiza Hava. Satana anasamala kwambiri kuti asatsutse kuti Mulungu ndi wolamulira. Koma anatsutsa zakuti ulamuliro wa Mulungu ndi woyenera ndiponso ndi wachilungamo. M’mawu ena, iye ananena kuti Yehova sanali kulamulira mwachilungamo ndiponso m’njira yokomera anthu Ake.

9. (a) Kwa Adamu ndi Hava, kodi n’chiyani chinali chotsatirapo cha kusamvera, nanga ndi mafunso ofunika otani amene anabuka? (b) N’chifukwa chiyani Yehova sanangowononga opandukawo?

9 Ndiyeno, onse aŵiri, Adamu ndi Hava, sanamvere Yehova mwa kudya zipatso za mtengo woletsedwawo. Chifukwa cha kusamverako, anafunika kulandira chilango cha imfa, monga mmene Mulungu ananenera. Bodza la Satana linadzutsa mafunso ofunika kwambiri. Kodi Yehova alidi ndi ufulu wolamulira anthu, kapena anthu ayenera kudzilamulira okha? Kodi Yehova amalamulira m’njira yabwino kwambiri kuposa njira ina iliyonse? Yehova akanatha kugwiritsa ntchito mphamvu zake zosanenekazo kuti awononge opandukawo panthaŵi yomweyo. Koma mafunso amene anabukawo anakhudza ulamuliro wa Mulungu, osati mphamvu zake. Motero kuchotsa Adamu, Hava, ndi Satana, sikukanatsimikizira kuti Mulungu amalamulira molungama. M’malo mwake, kukanawonjezera kukayikira kalamuliridwe kake. Njira yokha yotsimikizira ngati anthu angathe kudzilamulira bwino lomwe popanda Mulungu, ndiyo kulola kuti papite nthaŵi yaitali anthuwo akuyesa kuchita zimenezo.

10. Kodi zochitika za m’mbiri zasonyeza chiyani pankhani ya ulamuliro wa anthu?

10 Kodi n’chiyani chaoneka m’kupita kwa nthaŵi? Kwa zaka masauzande ambiri, anthu ayesapo mitundu yambirimbiri  ya maboma, kuphatikizapo boma lolamulidwa ndi munthu mmodzi, boma la demokalase, boma la sosholizimu, ndi boma la chikomyunizimu. Zotsatira za maboma onsewo zikunenedwa m’mawu achidule ndi osapita m’mbali aŵa a m’Baibulo: “Wina apweteka mnzake pomulamulira.” (Mlaliki 8:9) Mneneri Yeremiya anali ndi zifukwa zomveka ponena kuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu sili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.”—Yeremiya 10:23.

11. N’chifukwa chiyani Yehova analola kuti anthu akumane ndi mavuto?

11 Yehova anadziŵa kuchokera pachiyambi pomwe kuti anthu adzakhala ndi mavuto ambiri podzilamulira. Kodi ndiye kuti iye anasoŵa chilungamo polola kuti mavutowo achitikebe basi? Ayi, sanasoŵe chilungamo. Tiyeni tifanizire motere: Tinene kuti muli ndi mwana amene akufunika opaleshoni kuti achire matenda oti angathe kufa nawo. Mukuzindikira kuti mwana wanu adzavutika ndi opaleshoniyo, ndipo zimenezi zikukumvetsani chisoni kwambiri. Ndiponso mukudziŵa kuti zimenezi zidzathandiza mwana wanu kukhala ndi moyo wabwino m’tsogolo. Mofananamo, Mulungu anadziŵa, ndiponso ananeneratu, kuti anthu adzamva kupweteka ndipo adzavutika chifukwa chowalola kuti adzilamulire. (Genesis 3:16-19) Koma anadziŵanso kuti iwo angakhale ndi mpumulo weniweni ndi wokhalitsa ngati atalola kuti anthu onse aone zotsatira zoipa za kupanduka. Mwa njirayi, nkhani ya ulamuliro wa Mulungu ingathetsedwe yonse mpaka kalekale.

Nkhani ya Kukhulupirika kwa Anthu

12. Monga ikusonyezera nkhani ya Yobu, kodi Satana anawaneneza zotani anthu?

12 Pali mbali inanso pa nkhaniyi. Mwa kukayikira ulamuliro wa Mulungu ngati uli woyenera ndi wolungama, Satana sanangonena bodza lokhudza ulamuliro wa Yehova; ananenanso bodza lokhudza kukhulupirika kwa atumiki a Mulungu. Mwachitsanzo, taonani zimene Satana anauza Yehova za  munthu wolungama uja Yobu: “Kodi simunamutchinga iye ndi nyumba yake, ndi zake zonse, pomuzinga ponse? Ntchito ya manja ake mwaidalitsa, ndi zoŵeta zake zachuluka m’dziko. Koma mutambasule dzanja lanu ndi kumukhudzira zake zonse, ndipo adzakuchitirani mwano pankhope panu.”—Yobu 1:10, 11.

13. Kodi Satana anali kutanthauzanji mwa zimene ananeneza Yobu, nanga zikukhudza motani anthu onse?

13 Satana ananena kuti Yehova anali kugwiritsa ntchito mphamvu Zake zoteteza pogula kukhulupirika kwa Yobu. Ndiyeno zimenezi zinatanthauza kuti Yobu anali wokhulupirika mwa chiphamaso chabe, ndipo anali kungolambira Mulungu chifukwa cha zimene anali kumupatsa. Satana anati Yobu akhoza kutukwana Mlengi wake ngati Mulungu atati asamudalitse. Satana anali kudziŵa kuti Yobu anali wapadera pokhala “wangwiro ndi woongoka, wakuopa Mulungu ndi kupeŵa zoipa.” * Tsopano, ngati Satana akanathetsa kukhulupirika kwa Yobu, kodi sakanathetsanso kukhulupirika kwa anthu ena onse? Motero Satana anali kwenikweni kukayikira kukhulupirika kwa anthu onse amene amafuna kutumikira Mulungu. Ndipotu poonetsa kuti nkhaniyo ikukhudza anthu onse, Satana anauza Yehova kuti: ‘Munthu [osati Yobu yekha] adzapereka zonse ali nazo kuwombola moyo wake.’—Yobu 1:8; 2:4.

14. Kodi zochitika za m’mbiri zasonyeza chiyani za zimene Satana ananeneza anthu?

14 Zochitika za m’mbiri zasonyeza kuti anthu ochuluka, mofanana ndi Yobu, akhalabe okhulupirika kwa Yehova pamene anali kukumana ndi ziyeso. Zimenezi n’zosiyana kwambiri ndi zimene ananena Satana. Moyo wawo wokhulupirika wakondweretsa mtima wa Yehova, ndipo zachititsa Yehova kuyankha zimene Satana anali kutonza modzitukumula kuti anthu adzasiya kutumikira Mulungu pamene ali m’mavuto. (Ahebri 11:4-38) Inde, anthu a mitima yabwino akana kulozetsa nkhongo  zawo kwa Mulungu. Ngakhale pamene athedwa nzeru ndi zochitika zovuta kwambiri, adalira kwambiri Yehova kuti awapatse mphamvu kuti athe kupirira.—2 Akorinto 4:7-10.

15. Ndi funso lotani limene lingabuke lokhudza ziweruzo za Mulungu zakale ndiponso zam’tsogolo muno?

15 Komatu, kusonyeza chilungamo kwa Yehova kumakhudzanso nkhani zina kuwonjezera pa nkhani ya ulamuliro ndi nkhani ya kukhulupirika kwa anthu. Baibulo limatiuza nkhani za mmene Yehova anaweruzira anthu ena ake ngakhalenso mitundu yathunthu. Lilinso ndi maulosi a ziweruzo zimene adzapereka m’tsogolo muno. Kodi tingatsimikize chifukwa cha chiyani kuti Yehova wakhala akupereka ziweruzo zake molungama ndi kuti adzaziperekabe molungama?

Chifukwa Chomwe Chilungamo cha Mulungu Chilili Chapamwamba

Yehova ‘sadzawononga olungama pamodzi ndi oipa’

16, 17. Kodi ndi zitsanzo zotani zimene zikusonyeza kuti anthu amaona zinthu mopereŵera pa nkhani ya chilungamo chenicheni?

16 Ponena za Yehova, tinganenedi kuti: “Njira zake zonse ndi chiweruzo [chilungamo].” (Deuteronomo 32:4) Palibe munthu aliyense amene angadzinenerere kuti mmenemu ndimo mmene iyeyo alili, chifukwa kaŵirikaŵiri kaonedwe kathu ka zinthu kopereŵera kamatilepheretsa kuzindikira chimene chili choyenera. Mwachitsanzo, talingalirani za Abrahamu. Anachonderera Yehova kuti asawononge Sodomu, ngakhale kuti kuipa kunali ponseponse m’mudziwo. Anafunsa Yehova kuti: “Kodi mudzawononga olungama pamodzi ndi oipa?” (Genesis 18:23-33) Inde, yankho lake linali lakuti ayi. Yehova ‘anavumbitsa miyala ya sulfure ndi moto’ pa Sodomu panthaŵi yoti Loti wolungamayo ndi ana ake akazi afika bwinobwino ku mudzi wotchedwa Zoari. (Genesis 19:22-24) Mosiyana ndi Abrahamu, Yona “anapsa mtima” pamene Mulungu anachitira chifundo anthu a ku Nineve. Popeza kuti Yona anali atalengeza kale kuti iwo awonongedwa, akanasangalala kuwaona akufafanizidwa, mosasamala kanthu kuti analapa ndi mtima wonse.—Yona 3:10–4:1.

17 Yehova anatsimikizira Abrahamu kuti Iye akamapereka  chiweruzo sikuti amangowononga anthu oipa, koma amapulumutsanso olungama. Pa chochitika chinacho, Yona anafunika kuphunzira kuti Yehova ndi wachifundo. Ngati oipa asintha njira zawo, iye ndi wokonzeka ‘kukhululukira.’ (Salmo 86:5) Mosiyana ndi anthu ena amene amaopa kuwalanda malo, Yehova sapereka chiweruzo chokhwima kungoti adziŵike kuti ali ndi mphamvu. Ndiponso saleka kuchitira anthu chifundo poopa kuti ena amuona ngati wofooka. Iye amasonyeza chifundo nthaŵi zonse pakakhala chifukwa chosonyezera chifundocho.—Yesaya 55:7; Ezekieli 18:23.

18. Sonyezani kuchokera mu Baibulo kuti Yehova sangochita zinthu motengeka ndi malingaliro chabe.

18 Komabe, anthu sangamate Yehova phula m’maso mwa kungosonyeza malingaliro awo. Pamene anthu ake analoŵerera mu kulambira mafano, Yehova analengeza mwamphamvu kuti: ‘Ndidzakuweruza monga mwa njira zako, ndipo ndidzakubwezera zonyansa zako zonse. Ndipo diso langa silidzakulekerera, sindidzachita chifundo, koma ndidzakubwezera njira zako.’ (Ezekieli 7:3, 4) Motero pamene anthu aumirira pa zochita zawo, Yehova amawaweruza moyenerera. Koma amaweruza mogwirizana ndi umboni womveka. Choncho, pamene anamva “kulira” kwakukulu kokhudza Sodomu ndi Gomora, Yehova anati: “Ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira.” (Genesis 18:20, 21) Tikuthokozatu kwambiri kuti Yehova ndi wosiyana ndi anthu ambiri amene amangothamangira kuweruza asanamve mfundo zonse! Ndithudi, Yehova ali monga momwe Baibulo limamulongosolera kuti ndi “Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo.”—Deuteronomo 32:4.

Dalirani Chilungamo cha Yehova

19. Kodi tingachitenji ngati tili ndi mafunso othetsa nzeru okhudza mmene Yehova amasonyezera chilungamo chake?

19 Baibulo siliyankha funso lililonse lokhudza zimene Yehova anachita m’mbuyomo; sililongosolanso mwatsatanetsatane zinthu zonse zimene Yehova adzachita poweruza anthu ndi magulu a anthu m’tsogolomu. Pamene nkhani zina kapena maulosi ena a m’Baibulo atithetsa nzeru chifukwa sanalembedwe  mwatsatanetsatane chomwecho, tingaonetse kukhulupirika kofanana ndi kumene anasonyeza mneneri Mika, yemwe analemba kuti: “Ndidzadikira Mulungu wa chipulumutso changa.”—Mika 7:7.

20, 21. N’chifukwa chiyani tingakhale ndi chidaliro chakuti Yehova nthaŵi zonse adzachita cholungama?

20 Tingakhale n’chidaliro chakuti mu chochitika chilichonse Yehova adzachita cholungama. Ngakhale pamene zikuoneka kuti anthu akunyalanyaza zinthu zopanda chilungamo, Yehova akulonjeza kuti: “Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera.” (Aroma 12:19) Ngati tikhala ndi mtima wodikira, nafenso tidzakhala ndi chikhulupiriro cholimba ngati chimene anali nacho mtumwi Paulo, yemwe anati: “Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Musatero ayi.”—Aroma 9:14.

21 Pakali pano, tikukhala mu “nthaŵi zoŵaŵitsa” zomwe ndi zovuta. (2 Timoteo 3:1) Kupanda chilungamo ndi “nsautso” zachititsa nkhanza zosaneneka. (Mlaliki 4:1) Komabe, Yehova sanasinthe. Iye amadanabe ndi kupanda chilungamo, ndipo amasamalira kwambiri anthu amene amavutika nako. Ngati tikhalabe okhulupirika kwa Yehova ndi ku ulamuliro wake, adzatipatsa mphamvu zoti tithe kupirira mpaka pa nthaŵi yoikika pamene adzachotsa kupanda chilungamo konse mu ulamuliro wa Ufumu wake.—1 Petro 5:6, 7.

^ ndime 13 Ponena za Yobu, Yehova anati: “Palibe wina wonga iye m’dzikomo.” (Yobu 1:8) Ndiye kuti Yobu ayenera kuti anali ndi moyo Yosefe atafa kale komanso Mose asanasankhidwe kukhala mtsogoleri wa Israyeli. Choncho, panthaŵi imeneyo kunali kolondola kunena kuti panalibe yemwe anali wokhulupirika monga Yobu.