Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 CHIGAWO CHACHIŴIRI

‘Wokonda Chilungamo’

‘Wokonda Chilungamo’

Masiku ano, kulikonse padziko lapansili kukuchitika zinthu zopanda chilungamo, ndipo anthu ambiri amanena molakwa kuti Mulungu ndiye akuzichititsa. Komatu, Baibulo limatiphunzitsa choonadi chosangalatsa kwambiri pankhaniyi. Limati: “Yehova akonda chiweruzo [“chilungamo,” NW].” (Salmo 37:28) M’chigawo chino tiphunzira mmene iye wasonyezera kuti mawu amenewo ndi oona, zomwe zimapatsa anthu onse chiyembekezo chabwino.

M'CHIGAWO ICHI

MUTU 11

Njira Zake Zonse Ndi Chilungamo

N’chifukwa chiyani khalidwe la Mulungu la chilungamo lili lochititsa chidwi kwambiri?

MUTU 12

“Kodi Chilipo Chosalungama ndi Mulungu?”

Ngati Mulungu amadana ndi zopanda chilungamo, n’chifukwa chiyani padzikoli pali zinthu zopanda chilungamo zambiri?

MUTU 13

“Malamulo a Yehova Ali Angwiro”

Kodi malamulo angalimbikitse bwanji chikondi?

MUTU 14

Yehova Alinganiza “Dipo la Anthu Ambiri”

Chiphunzitso chosavuta kumva koma chofunika chingakuthandizeni kuyandikira Mulungu.

MUTU 15

Yesu Akhazikitsa Chilungamo M’dziko Lapansi

Kodi Yesu analimbikitsa bwanji chilungamo m’mbuyomu? Kodi akuchirimbikitsa bwanji masiku ano? Ndipo adzachita bwanji zimenezi m’tsogolo?

MUTU 16

‘Chitani Cholungama’ Poyenda ndi Mulungu

N’chifukwa chiyani Yesu anachenjeza kuti: “Musaweruze, kuti mungaweruzidwe.”?