1-3. (a) Kodi n’chiyani chinachititsa Yesu kufuna kukhala monga Atate wake? (b) Kodi tiphunzira mbali ziti za chikondi cha Yesu?

KODI munaonapo mwana wamng’ono akuyeserera kukhala ngati atate wake? Mwanayo angatsanzire mmene atate wake amayendera, amalankhulira, kapena mmene amachitira zinthu zina. M’kupita kwa nthaŵi, mwanayo angatengere ngakhale makhalidwe abwino ndiponso zinthu zauzimu zimene atate wake amakonda. Inde, mwana akamakonda atate wake amene amamukonda ndiponso akamachita nawo kaso zimamuchititsa kufuna kukhala monga iwowo.

2 Nanga bwanji ubale wa Yesu ndi Atate wake wakumwamba? Panthaŵi ina Yesu anati: “Ndikonda Atate.” (Yohane 14:31) Palibe wina amene angakonde Yehova kwambiri kuposa Mwana ameneyu, yemwe anali ndi Atatewo kwa nthaŵi yaitali zolengedwa zina zonse zisanakhaleko. Chikondi chimenecho chinachititsa Mwana wodzipereka ameneyu kufuna kukhala monga Atate wake.—Yohane 14:9.

3 M’mitu ya koyambiriraku ya buku lino, tafotokoza mmene Yesu anatsanzirira bwino kwambiri mphamvu, chilungamo, ndi nzeru za Yehova. Komano, kodi Yesu anaonetsa motani kuti anali ndi chikondi chonga cha Atate wake? Tiyeni tiphunzire mbali zitatu za chikondi cha Yesu—mtima wodzipereka umene anali nawo, chifundo chake chachikulu, ndi kukhala wofunitsitsa kukhululukira ena.

“Palibe Munthu Ali Nacho Chikondi Choposa Ichi”

4. Kodi Yesu anapereka chitsanzo chachikulu kwambiri chotani cha munthu wachikondi chodzimana?

4 Yesu anapereka chitsanzo chapadera kwambiri cha chikondi chodzimana. Kudzimana kumafuna kuti munthu akhale wopanda dyera mwa kusamalira kaye zosoŵa za ena ndi nkhaŵa zawo asanasamalire zake. Kodi Yesu anaonetsa motani chikondi choterocho? Iye mwini anafotokoza kuti: “Palibe munthu ali nacho  chikondi choposa ichi, chakuti munthu ataya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake.” (Yohane 15:13) Mofunitsitsa Yesu anapereka moyo wake wangwiro m’malo mwathu. Ichi chinali chikondi chachikulu kwambiri kuposa chimene munthu wina aliyense anaonetsapo. Koma Yesu anasonyezanso chikondi chodzimana m’njira zinanso.

5. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anadzipereka mwachikondi pochoka kumwamba?

5 Mwana wobadwa yekha wa Mulungu asanakhale munthu padziko lapansi, anali ndi udindo wapadera komanso wapamwamba kwambiri kumwamba. Anali kuyanjana kwambiri ndi Yehova limodzinso ndi zolengedwa zauzimu miyandamiyanda. Ngakhale kuti anali pabwino chonchi, Mwana wokondedwa ameneyu “anadzikhuthula yekha, natenga maonekedwe a kapolo, nakhala m’mafanizidwe a anthu.” (Afilipi 2:7) Mofunitsitsa anabwera kudzakhala limodzi ndi anthu ochimwa m’dziko lino ‘logona mwa woipayo.’ (1 Yohane 5:19) Mwana wa Mulungu anadziperekatu kwambiri, kodi sindicho chikondi chimenechi?

6, 7. (a) Kodi Yesu anasonyeza chikondi chodzimana m’njira zotani pochita utumiki wake padziko lapansi? (b) Kodi ndi chitsanzo chotani cha chikondi chopanda dyera chimene chili pa Yohane 19:25-27?

6 M’nthaŵi yonse ya utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu anadzipereka mwachikondi m’njira zosiyanasiyana. Analibe dyera m’pang’onong’ono pomwe. Malingaliro ake onse anali pa utumiki wake moti sanalakelake kukhala ndi zinthu zabwino zimene anthu amakonda kukhala nazo. “Ankhandwe ali nazo nkhwimba zawo, ndi mbalame za m’mlengalenga zisa zawo,” iye anatero, “koma Mwana wa munthu alibe potsamira mutu wake.” (Mateyu 8:20) Pokhala kalipentala waluso, Yesu akanatha kupatula nthaŵi yake n’kumanga nyumba yabwino kwambiri yoti azikhalamo, kapena kupanga zinthu zamatabwa zokongola monga mipando ndi matebulo kuti agulitse n’kupeza ndalama zambiri. Koma iye sanagwiritse ntchito luso lake kuti adziunjikire katundu.

7 Chitsanzo chogwira mtima kwambiri cha chikondi chodzimana cha Yesu chili pa Yohane 19:25-27. Talingalirani zinthu zambirimbiri zimene Yesu anali kulingalira mu mtima mwake  masana pa tsiku limene anafa. Pamene anali kuvutika pa mtengo, anali kudera nkhaŵa ophunzira ake, ntchito yolalikira, ndiponso makamaka kukhulupirika kwake ndi momwe kukhudzire dzina la Atate wake. Inde, tsogolo lonse la anthu linali kudalira pa iye! Komatu atatsala pang’ono kufa, Yesu anasonyeza kuti analinso kudera nkhaŵa amayi wake, Mariya, omwe panthaŵiyi ayenera kuti anali amasiye. Yesu anapempha mtumwi Yohane kusamalira Mariya monga mayi wake enieni a Yohaneyo, ndipo kenako mtumwiyo anamutenga Mariya n’kupita naye kunyumba kwake. Motero Yesu anapanga makonzedwe oti amayi wake azisamaliridwa mwakuthupi ndi mwauzimu. Koma ndiyetu anaonetsadi chikondi chopanda dyera ngakhale pang’ono!

‘Anagwidwa Chifundo’

8. Kodi mawu achigiriki amene Baibulo limagwiritsa ntchito polongosola chifundo cha Yesu amatanthauzanji?

8 Mofanana ndi Atate wake, Yesu anali wachifundo. Malemba amafotokoza Yesu monga munthu amene anali kuchita zonse zimene akanatha kuti athandize ovutika chifukwa zinali kumukhudza. Polongosola chifundo cha Yesu, Baibulo limagwiritsa ntchito mawu achigiriki amene amatembenuzidwa kuti ‘anagwidwa chifundo.’ Katswiri wina wa Baibulo anati: “Mawuŵa amalongosola . . . maganizo amene amachititsa munthu kuchita zinthu kuchokera pansi pamtima. Ndiwo mawu achigiriki amene amatsindikadi kwambiri kuti munthu ndi wachifundo.” Taonani zochitika zina zimene zinachititsa Yesu kugwidwa chifundo zedi moti anachitapo kanthu.

9, 10. (a) Kodi n’zochitika zotani zimene zinachititsa Yesu ndi atumwi ake kufunafuna malo a phee? (b) Pamene anthu analepheretsa Yesu kukhala payekha, kodi Yesu anachitanji, ndipo n’chifukwa chiyani?

9 Anathandiza pa zofunika zauzimu. Nkhani yopezeka pa Marko 6:30-34 imaonetsa chifukwa chachikulu chimene Yesu anali kuchitira chifundo. M’maganizo mwanu taonani zimene zinali kuchitika. Atumwi anali osangalala kwambiri chifukwa anali atangomaliza kumene kulalikira m’madera ambiri. Anapitanso kwa Yesu ndi kumufotokozera mokondwera zonse zimene anaziona ndi kuzimva. Komano panabwera anthu ambiri moti  Yesu ndi atumwi ake analibe mpata woti adye. Pokhala munthu watcheru nthaŵi zonse, Yesu anazindikira kuti atumwiwo atopa. “Idzani inu nokha padera ku malo achipululu, mupumule kamphindi,” anawauza tero. Atakwera ngalawa anawoloka Nyanja ya Galileya cha kunsonga yake ya kumpoto kupita ku malo a phee. Koma khamu lija linawaona pochoka. Enanso anamva za nkhaniyi. Onseŵa anathamanga m’gombe la kumpoto n’kukafika mbali ina ya nyanjayo ngalawayo isanafike!

10 Kodi Yesu anakhumudwa nazo kuti amulepheretsa kukhala payekha? Ayi ndithu. Anakhudzika mtima ataona kuti anthuŵa, omwe analipo masauzande ambirimbiri, akumudikirira. Marko analemba kuti: ‘Anaona khamu lalikulu la anthu, nagwidwa chifundo ndi iwo, chifukwa anali ngati nkhosa zopanda mbusa; ndipo anayamba kuwaphunzitsa zinthu zambiri.’ Yesu anaona anthu ameneŵa monga anthu ofuna zinthu zauzimu. Anali monga nkhosa zimene zinali kusokera popanda wozithandiza; zopanda mbusa wozitsogolera kapena kuziteteza. Yesu anali kudziŵa kuti atsogoleri achipembedzo ouma mtima, omwe anali kuyenera kukhala abusa osamalira bwino, anali kunyalanyaza anthu wamba. (Yohane 7:47-49) Anamvera chisoni anthuwo motero anayamba kuwaphunzitsa “za Ufumu wa Mulungu.” (Luka 9:11) Taonani kuti Yesu anachitira chifundo anthuwo asanaone n’komwe zimene iwo adzachita akawaphunzitsa. M’mawu ena tinganene kuti, sanakhale ndi mtima wachifundo chifukwa chophunzitsa anthuwo, koma kuti mtima wachifundo ndiwo unamuchititsa kuti awaphunzitse.

‘Anatansa dzanja namukhudza iye’

11, 12. (a) Kodi anthu akhate anali kuwaona motani m’nthaŵi za m’Baibulo, koma kodi Yesu anachitanji pamene anakumana ndi munthu wina “wodzala ndi khate”? (b) Kodi wakhate amene Yesu anamukhudza n’kutheka kuti anamva bwanji, nanga zimene zinachitikira dokotala wina zikutipatsa chitsanzo motani pa nkhaniyi?

11 Anathandiza ovutika. Anthu odwala matenda osiyanasiyana ankadziŵa kuti Yesu ndi wachifundo, motero sanali kutalikirana naye. Izi zinaoneka bwino zedi pamene munthu wina “wodzala ndi khate” anafika kwa Yesu, gulu la anthu likutsatira Yesuyo. (Luka 5:12) M’nthaŵi za m’Baibulo, anthu akhate anali kuwaika kwaokha kuti asapatsire anzawo matenda awowo. (Numeri 5:1-4) Komabe m’kupita kwa nthaŵi, atsogoleri achirabi  analimbikitsa anthu kusachitira chifundo akhate, ndipo anapanga malamulo awoawo owapondereza. * Koma taonani mmene Yesu anachitira ndi wakhateyo: “Ndipo anadza kwa Iye wodwala khate, namupempha Iye, namugwadira, ndi kunena ndi Iye, Ngati mufuna mukhoza kundikonza. Ndipo Yesu anagwidwa chifundo, natansa dzanja namukhudza iye, nanena naye, Ndifuna; khala wokonzedwa. Ndipo pomwepo khate linamuchoka.” (Marko 1:40-42) Yesu anali kudziŵa kuti wakhateyo sanali wololedwa kupezeka pa gulupo. Komatu m’malo momuuza kuti achokepo, Yesu anamva chisoni kwambiri moti anachita chinthu chosayembekezereka. Yesu anakhudza wakhateyo!

12 Kodi muganiza kuti wakhateyo anamva bwanji Yesu atamukhudza? Kuti tifanizire bwino, talingalirani izi. Dokotala wina wa anthu akhate, Dr. Paul Brand, anafotokoza za wakhate amene anamuchiritsa ku India. Pamene anali kumupima, dokotalayo anakoloweka dzanja lake m’khosi mwa wakhateyo ndi kumufotokozera, kudzera mwa munthu wina womasulira, mankhwala amene wodwalayo adzafunika kulandira. Mwadzidzidzi, wakhateyo anayamba kulira. “Kodi ndanena zolakwika?” dokotalayo anafunsa motero. Munthu womasulirayo anafunsa mnyamatayo m’chinenero chake, ndiyeno anayankha dokotalayo kuti: “Ayi, a dokotala. Akuti akulira chifukwa chakuti munamukoloweka dzanja m’khosi. Akuti palibe munthu wamukhudzapo kwa zaka zambiri kufikira pamene wabwera kunomu.” Kwa wakhate amene anakumana ndi Yesu uja, kumukhudza kunatanthauza zazikulu. Atangokhudzidwa kamodzi kokhako basi, matenda amene anamuchititsa kukhala wosafunika pagulu anatheratu!

13, 14. (a) Kodi pamene Yesu amayandikira mzinda wa Nayini anakumana ndi anthu akupita kuti, nanga n’chiyani chinachititsa zimenezi kukhala zomvetsa chisoni kwambiri? (b) Kodi chifundo cha Yesu chinamuchititsa kuchitira mkazi wamasiye wa ku Nayini chiyani?

 13 Anathetsa chisoni. Zinali kumukhudza mtima kwambiri Yesu akaona anthu ena ali achisoni. Mwachitsanzo, talingalirani nkhani yomwe ili pa Luka 7:11-15. Inachitika pamene Yesu anayandikira mzinda wa ku Galileya wotchedwa Nayini, chapakatikati pa utumiki wake. Atafika pafupi ndi chipata cha mzindawo, anakumana ndi anthu akukaika maliro. Maliro ake anali omvetsa chisoni kwambiri. Womwalirayo anali mnyamata yemwe anali mwana yekhayo wa mkazi wina wamasiye. Mkaziyu ayenera kuti nthaŵi ina m’mbuyomo analinso ndi anthu atanyamula mtembo chomwechi kupita kumanda, kukaika maliro a mwamuna wake. Tsopano akukaika mwana wake, yemwe mwinamwake anali yekhayo amene anali kumuthandiza. N’kutheka kuti m’khamu limene linali kuperekeza malirowo munalinso olira ena apadera amene anali kubuma ndiponso oimba omwe anali kuimba nyimbo zachisoni. (Yeremiya 9:17, 18; Mateyu 9:23) Komabe, Yesu anali kupenyetsetsa amayi wake a womwalirayo, omwe anali n’chisoni chachikulu ndipo mosakayikira anali kuyenda pafupi ndi chithatha chimene ananyamulirapo mtembo wa mwana wawoyo.

14 Yesu ‘anagwidwa chifundo’ ndi mayi wofedwayo. Ndi mawu olimbikitsa, anamuuza kuti: “Usalire.” Popanda womupempha, anayandikira chithatha ndi kuchikhudza. Onyamula chithathacho anaima, ndipo mwina gulu lonselo linaimanso. Yesu analankhula ndi mawu a mphamvu bwino kwa thupi lopanda moyolo kuti: “Mnyamata iwe, ndinena ndi iwe, Tauka.” Kenako n’chiyani chinachitika? “Wakufayo anakhala tsonga, nayamba kulankhula” ndiye ngati kuti amudzutsa ku tulo tofa nato! Ndiyeno pakubwera mawu olimbikitsa kwambiri akuti: “Ndipo [Yesu] anamupereka kwa amake.”

15. (a) Nkhani za m’Baibulo zonena za Yesu atagwidwa chifundo zimasonyeza kugwirizana kotani pakati pa kukhala wachifundo ndi kuchitapo kanthu pothandiza? (b) Kodi Yesu tingamutsanzire motani pankhaniyi?

15 Kodi nkhani zimenezi zikutiphunzitsa chiyani? Onani kuti m’nkhani iliyonse kukhala wachifundo kukuyendera limodzi ndi kuchitapo kanthu. Nthaŵi zonse Yesu akaona ena akuvutika anali kuwamvera chisoni, ndipo akagwidwa chifundo moteromo  anali kuchitapo kanthu. Kodi tingatsatire motani chitsanzo chake? Monga Akristu, tili ndi udindo wolalikira uthenga wabwino ndi kupanga ophunzira. Timachita zimenezi makamaka chifukwa chokonda Mulungu. Koma tizikumbukira kuti imeneyi ndi ntchito imene imafunanso kukhala wachifundo. Pamene timvera anthu chisoni monga anachitira Yesu, mitima yathu idzatilimbikitsa kuchita zonse zimene tingathe kuchita kuti tiuze ena uthenga wabwino. (Mateyu 22:37-39) Bwanji nanga za kuchitira chifundo okhulupirira anzathu amene akuvutika kapena amene ali n’chisoni? Ife sitingachiritse matenda mozizwitsa kapenanso kuukitsa akufa. Komabe, tingasonyeze chifundo mwa kuyamba ifeyo kudera nkhaŵa anthu ena kapena kuwapatsa thandizo limene likufunika.—Aefeso 4:32.

“Atate, Muwakhululukire Iwo”

16. Kodi zinaoneka motani kuti Yesu anali wofunitsitsa kukhululukira ena ngakhale pamene anali pa mtengo wozunzirapo?

16 Yesu anaonetsanso bwino kwambiri chikondi cha Atate wake m’njira ina yofunika zedi; anali “wokhululukira.” (Salmo 86:5) Ngakhale pamene anali pamtengo wozunzirapo iye anasonyeza kuti anali wofunitsitsa kukhululukira ena. Atakakamizika kufa imfa yochititsa manyazi, manja ndi mapazi ake zitakhomedwa misomali, kodi Yesu analankhula zotani? Kodi anapempha Yehova kuti alange amene anali kumuphawo? Ayi sanatero. Mwa mawu omalizira amene Yesu analankhula, ena anali akuti: “Atate, muwakhululukire iwo, pakuti sadziŵa chimene achita.”—Luka 23:34. *

17-19. Kodi Yesu anasonyeza m’njira zotani kuti anakhululukira mtumwi Petro chifukwa chomukana katatu?

17 Mwinamwake chitsanzo chogwira mtima kwambiri cha mmene Yesu analili wokhululukira ena tingachione pa zimene  anachitira mtumwi Petro. Sitingakayikire kuti Petro anali kumukonda kwambiri Yesu. Pa Nisani 14, usiku womaliza womwe Yesu anali ndi moyo, Petro anamuuza kuti: “Ambuye, ndilipo ndikapite ndi Inu kundende ndi kuimfa.” Komatu patangotha maola oŵerengeka chabe, Petro anakana maulendo atatu kuti amam’dziŵa Yesu! Baibulo limatiuza zimene zinachitika pamene Petro anali kum’kana kachitatu, limati: “Ambuye anapotoloka, nayang’ana Petro.” Atavutika ndi kukula kwa tchimo lake, Petro “anatuluka, nalira misozi ndi kuwawa mtima.” Pambuyo pake Yesu atamwalira tsikulo, n’kutheka kuti mtumwiyo anali kukayikira kuti, ‘Kodi Ambuye wanga anandikhululukira?’—Luka 22:33, 61, 62.

18 Petro sanadikire nthaŵi yaitali kuti apeze yankho. Yesu anaukitsidwa pa Nisani 16 m’maŵa, ndipo zikuoneka kuti tsiku lomwelo anakachezera Petro. (Luka 24:34; 1 Akorinto 15:4-8) N’chifukwa chiyani Yesu anali n’chidwi chapadera mwa mtumwi yemwe anamukana kwamtu wa galu? N’kutheka kuti Yesu anali kufuna kutsimikizira Petro yemwe anali atalapa kuti Ambuye wake anali kumukondabe ndi kumuyamikira. Koma Yesu anachitanso zina kuti amukhazike mtima pansi Petro.

19 Nthaŵi ina izi zitachitika, Yesu anaonekera kwa ophunzira ku Nyanja ya Galileya. Panthaŵiyi, Yesu anafunsa Petro katatu (yemwe anakana Ambuye wake katatu) ngati Petroyo anali kumukonda. Atafunsidwa kachitatu, Petro anayankha kuti: “Ambuye, mudziŵa Inu zonse; muzindikira kuti ndikukondani Inu.” Ndithudi, Yesu yemwe ankatha kudziŵa za mumtima mwa munthu, anali kudziŵa bwino kuti Petro anali kumukonda. Komatu Yesu anapatsa Petro mwayi wotsimikizira chikondi chake. Ndiponso, Yesu anatuma Petro kuti ‘adyetse’ ndi ‘kuŵeta’ “ana a nkhosa” ake. (Yohane 21:15-17) M’mbuyomo, Petro anapatsidwa ntchito yolalikira. (Luka 5:10) Koma tsopano, posonyeza kumudalira mwapadera, Yesu anamupatsa udindo wina waukulu kwambiri, udindo wosamalira amene adzakhale otsatira a Kristu. Patapita nthaŵi yochepa, Yesu anapatsa Petro gawo lofunika kwambiri pa ntchito ya ophunzira. (Machitidwe 2:1-41) Petro ayeneratu kuti anali womasuka kwambiri podziŵa kuti Yesu anamukhululukira ndiponso kuti anali kumukhulupirirabe!

 Kodi ‘Mumazindikira Chikondi cha Kristu’?

20, 21. Kodi ndi motani mmene ‘tingazindikirire chikondi cha Kristu’ mokwanira bwino?

20 Ndithudi, Mawu a Yehova amalongosola bwino kwambiri chikondi cha Kristu. Koma kodi tiyenera kuchitapo chiyani pa chikondi cha Yesu? Baibulo limatilimbikitsa “kuzindikira chikondi cha Kristu, chakuposa mazindikiridwe.” (Aefeso 3:19) Monga mmene taonera, nkhani za moyo wa Yesu ndi utumiki wake mu Mauthenga Abwino zimatiphunzitsa zambiri za chikondi cha Kristu. Komabe, “kuzindikira chikondi cha Kristu” mokwanira bwino kumafuna zambiri osati kungophunzira nkhani zokhudza iye zimene Baibulo limanena.

21 Mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “kuzindikira” amatanthauza kuti kudziŵa “mwa zochita, kupyolera mu zimene zikukuchitikira.” Tikakhala n’chikondi monga analili Yesu—kudzipereka mopanda dyera kuti tithandize ena, kuwachitira chifundo pamene akusoŵeka zinthu zina, kuwakhululukira kuchokera pansi pamtima—m’pamene tidzamvetsetsadi maganizo ake. M’njira imeneyi, ‘timazindikira chikondi cha Kristu chakuposa mazindikiridwe’ mwa zimene zikutichitikira. Ndipo tisaiwale kuti pamene tifanana kwambiri ndi Kristu, m’pamenenso timayandikana zedi ndi yemwe Yesu anamutsanzira bwino kwambiri, Mulungu wathu wachikondi, Yehova.

^ ndime 11 Malamulo a arabi anali kunena kuti munthu sayenera kutalikirana ndi wakhate mochepera pa mikono inayi (pafupifupi mamita 1.8). Koma ngati mphepo inali kuwomba, wakhate anafunika kutalikirana ndi anthu ena mikono yosachepera pa 100 (pafupifupi mamita 45). Buku lakuti Midrash Rabbah limanena za rabi wina yemwe anali kubisala akaona akhate, ndi winanso amene anali kupitikitsa akhate powagenda miyala. Motero anthu akhate anali kudziŵa bwino mmene zimapwetekera, ena akakukana komanso ukamaganiza kuti ena amakunyoza ndi kutinso sakufuna.

^ ndime 16 Mbali yoyambirira ya Luka 23:34 mulibe m’mipukutu ina ya malemba apamanja akale. Koma chifukwa chakuti mawu ameneŵa amapezeka m’mipukutu ina yambiri yodziŵika bwino ya malemba apamanja, anaikidwa mu mabaibulo ambiri kuphatikizapo la New World Translation. Mwachionekere Yesu anali kulankhula za asilikali a Roma amene anamupachika. Iwo sanadziŵe zimene anali kuchita popeza kuti sanali kudziŵa bwinobwino kuti Yesu anali yani kwenikweni. Komabe atsogoleri achipembedzo amene anamuphetsa anali ndi mlandu waukulu chifukwa anali kudziŵa zomwe anali kuchita ndipo anachita mwakaduka. Ambiri a iwo ndi oti sanakhululukidwe.—Yohane 11:45-53.