Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 26

Mulungu “Wokhululukira”

Mulungu “Wokhululukira”

1-3. (a) Kodi ndi katundu wolemera wotani amene wamasalmo Davide ananyamula, nanga mtima wake wosautsikawo anaukhazika pansi motani? (b) Pamene tachimwa, ndi katundu wanji amene tinganyamule, koma kodi Yehova amatitsimikizira za chiyani?

“MPHULUPULU zanga zapitirira pamutu panga,” analemba motero wamasalmo Davide. “Ndathodwa nazo monga ndi katundu wolemera. Ndafooka ine, ndipo ndachinjizidwa [“ndapsinjika koopsa,” NW].” (Salmo 38:4, 8) Davide anali kudziŵa kuti kukumbukira zolakwa zimene anachita ndi katundu wolemera kwambiri. Koma iye anali wokhoza kukhazika pansi mtima wake wosautsikawo. Anazindikira kuti ngakhale kuti Yehova amadana ndi uchimo, Iye sadana ndi munthu wochimwa amene walapadi moona mtima ndi kusiya njira yake yauchimoyo. Pokhala ndi chikhulupiriro chonse kuti Yehova ndi wofunitsitsa kuchitira chifundo anthu olapa, Davide anati: “Inu, Ambuye, ndinu . . . wokhululukira.”—Salmo 86:5.

2 Pamene tachita tchimo, ifenso tinganyamule katundu wolemera wa chikumbumtima chopwetekedwa. Kumva chisoni kotereku n’kwabwino. Kungatichititse kuchita zinthu zofunikira kuti tikonze zimene talakwa. Komabe, pali ngozi yakuti tikhoza kupsinjika ndi malingaliro akuti ndife olakwa. Mtima wathu womwe umadzitsutsa ungaumirire kunena kuti Yehova sadzatikhululukira ngakhale titalapa chotani. Ngati malingaliro akuti ndife olakwa ‘atimiza,’ Satana angayese kutichititsa kuti tingosiyiratu kutumikira Mulungu, kapena kuti tiziona ngati Yehova amationa kukhala achabechabe ndi osayenera kumutumikira.—2 Akorinto 2:5-11.

3 Kodi ndi mmenedi Yehova amationera? Ayi, sationa choncho. Kukhululukira ena ndi mbali ya chikondi chachikulu cha Yehova. Iye amatitsimikizira m’Mawu ake kuti pamene tilapa zenizeni kuchokera pansi pamtima, amakhala wofunitsitsa kutikhululukira. (Miyambo 28:13) Kuti tipeŵe kulingalira kuti Yehova sangatikhululukire, tiyeni tione chifukwa chake ndiponso mmene iye amakhululukirira anthu.

 Chifukwa Chomwe Yehova Alili “Wokhululukira”

4. Kodi Yehova amakumbukiranji za chibadwa chathu, ndipo zimenezi zimakhudza motani mmene amachitira zinthu ndi ife anthu?

4 Yehova amadziŵa zimene sitingathe kuchita. “Adziŵa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi,” limatero Salmo 103:14. Saiwala kuti tinapangidwa ndi fumbi, ndipo ndife opanda mphamvu, kapena kuti ofooka, chifukwa cha kupanda ungwiro. Mawu akuti amadziŵa “mapangidwe athu” akutikumbutsa kuti Baibulo limafananitsa Yehova ndi woumba mbiya, ndipo ife anthu timafanizidwa ndi zinthu zadothi zimene woumbayo amaumba. * (Yeremiya 18:2-6) Woumba Wamkuluyo amasintha kachitidwe kake ka zinthu ndi ife anthu mogwirizana ndi kufooka kwathu popeza kuti tinabadwa ochimwa, ndiponso mogwirizana ndi mmene timalabadirira kapenanso kulephera kulabadira iye akamatitsogolera.

5. Kodi buku la Aroma limalongosola motani mmene uchimo wagwirira anthu zolimba?

5 Yehova amazindikira kuti uchimo uli ndi mphamvu kwambiri. Mawu ake amalongosola uchimo monga chinthu champhamvu kwabasi chimene chagwira anthu zolimba. Kodi uchimowo wawagwira mwamphamvu chotani anthu? Mtumwi Paulo anafotokoza m’buku la Aroma kuti: ‘Tagwidwa ndi uchimo,’ monga mmene asilikali amalamuliridwira ndi mtsogoleri wawo (Aroma 3:9); monga mfumu, uchimo ‘wachita ufumu’ pa anthu (Aroma 5:21); ‘ukukhalabe’ nafe (Aroma 7:17, 20); “lamulo” lake limagwira ntchito nthaŵi zonse mwa ife, kuyesa kulamulira zochita zathu. (Aroma 7:23, 25) Komatu ndiye uchimo wagwira matupi athu opanda ungwiroŵa mwamphamvu zedi!—Aroma 7:21, 24.

6, 7. (a) Kodi Yehova amawaona motani anthu a mitima yolapa amene amafunafuna chifundo chake? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti ngakhale tizichimwa Mulungu ndi wachifundo adzatikhululukira?

6 Motero Yehova amadziŵa kuti sitingathe kumumvera popanda kuphonyetsako kenakake, ngakhale titachita khama motani kuti timumvere pa kalikonse. Mwachikondi amatitsimikizira kuti pamene tifunafuna chifundo chake tili ndi mtima wolapa,  iye adzatikhululukira. Salmo 51:17 limati: “Nsembe za Mulungu ndizo mzimu wosweka; inu, Mulungu, simudzaupeputsa mtima wosweka ndi wolapa [“woswanyika,” NW].” Yehova sadzakana, kapena kuti sadzapitikitsa, munthu wa mtima “wosweka ndi woswanyika” chifukwa cha kulemera kwa malingaliro akuti ndi wolakwa.

7 Komabe, kodi zimenezi zikutanthauza kuti popeza tinabadwa ndi uchimo tikhoza kumachimwa, tikuganiza kuti Mulungu ndi wachifundo adzatikhululukira? Ndithudi ayi! Yehova sachita zinthu mongotengeka maganizo. Chifundo chake chili m’polekezera. Sadzakhululukira amene amaumirira kuchita tchimo mwadala, ndipo sasonyeza kulapa. (Ahebri 10:26) Komabe, amakhala wokonzeka kukhululukira amene wamuona kuti ali ndi mtima wolapa. Tsopano tiyeni tione mawu ena omveka bwino kwambiri amene anagwiritsidwa ntchito m’Baibulo polongosola mbali yabwino kwambiriyi ya chikondi cha Yehova.

Kodi Yehova Amakhululukira Mpaka Pati?

8. Kodi tingati n’chiyani chimene Yehova amachita pamene watikhululukira machimo athu, ndipo zimenezi zimatipatsa chidaliro chotani?

8 Davide atalapa ananena mawu aŵa: ‘Ndinavomera choipa changa kwa Inu; ndipo mphulupulu yanga sindinaibisa. . . . Ndipo munakhululukira choipa cha kulakwa kwanga.’ (Salmo 32:5) Mawu akuti “munakhululukira” atembenuzidwa kuchokera ku mawu achihebri amene makamaka amatanthauza kuti “kunyamula” kapena “kutenga.” Mmene agwiritsidwira ntchito pa lembali akusonyeza kuchotsa “cholakwa, tchimo, kapena choipa.” Motero tingati Yehova ananyamula machimo a Davide n’kuwachotsa. Mosakayikira izi zinachepetsa malingaliro amene Davide anali nawo odziona kuti anali wolakwa. (Salmo 32:3) Ifenso tingakhale n’chidaliro chonse mwa Mulungu yemwe amachotsa machimo a anthu ofuna kuti awakhululukire chifukwa cha kukhulupirira kwawo nsembe ya dipo ya Yesu.—Mateyu 20:28.

9. Kodi Yehova amaika machimo athu kutali motani ndi ifeyo?

9 Davide anagwiritsanso ntchito mawu ena omveka bwino polongosola kukhululukira kwa Yehova, anati: ‘Monga kum’maŵa kutanimpha ndi kumadzulo, momwemo anatisiyanitsira kutali zolakwa zathu.’ (Salmo 103:12) Kodi kum’maŵa n’kotalikirana  motani ndi kumadzulo? Nthaŵi zonse kum’maŵa kumatalikirana kwambiri zedi ndi kumadzulo; mbali ziŵirizi sizingakumane. Katswiri wina wa Baibulo anati mawu ameneŵa amatanthauza kuti “kutali zedi; kutali kosayerekezeka.” Mawu a Davide ouziridwa ndi Mulungu amatiuza kuti pamene Yehova watikhululukira, amaika machimo athu kutali zedi ndi ifeyo.

“Zoipa zanu . . . zidzayera ngati matalala”

10. Yehova akatikhululukira machimo athu, n’chifukwa chiyani sitifunika kumva kuti ndife othimbirira ndi machimo amenewo kwa moyo wathu wonse?

10 Kodi munayesapo kuchotsa zothimbirira pa chovala chowala? Mwinamwake zothimbirirazo sizinachoke ngakhale kuti munayesetsa kwambiri. Taonani mmene Yehova analongosolera mmene amakhululukirira anthu: ‘Ngakhale zoipa zanu zili zofiira, zidzayera ngati matalala; ngakhale zili zofiira ngati kapezi, zidzakhala ngati ubweya wa nkhosa, woti mbu.’ (Yesaya 1:18) Mawu akuti “zofiira” pa lembali akunena za zinthu zofiira kwambiri. * Zinthu zonikidwa ndi “kapezi” zinali kuonekera  kwambiri. (Nahumu 2:3) Sitingathe kuchotsa kuthimbirira kwathu ndi uchimo mwa zoyesayesa zathu zokha. Koma Yehova akhoza kutenga machimo amene ali ngati ofiira ndiponso amene ali ngati kapezi n’kuwayeretsa monga matalala kapena ubweya wa nkhosa wosanika. Yehova akatikhululukira machimo athu, sitifunikanso kumva kuti ndife othimbirira ndi machimo amenewo kwa moyo wathu wonse.

11. Kodi Yehova amaponya machimo athu kumbuyo kwake m’lingaliro lotani?

11 M’nyimbo yoyamikira yotenga mtima imene Hezekiya anapeka atamuchiritsa matenda amene akanafa nawo, Hezekiya anati kwa Yehova: ‘Mwaponya m’mbuyo mwanu machimo anga onse.’ (Yesaya 38:17) M’lembali Yehova akusonyezedwa kuti amatenga machimo a munthu wolakwa yemwe walapa ndi kuwaponya kumbuyo Kwake kumene Iye sawaonanso kaya kuwalingaliranso. Malinga n’kunena kwa buku lina, lingaliro lomwe lili pa lembali linganenedwe m’mawu akuti: “Mwachititsa [machimo anga] kukhala ngati sanachitike.” Kodi zimenezi sizokhazika mtima pansi zedi?

12. Kodi mneneri Mika anasonyeza motani kuti pamene Yehova watikhululukira, amachotsa machimo athu kwa nthaŵi zonse?

12 Mu lonjezo la kubwezeretsa, mneneri Mika anaonetsa kuti anali kukhulupirira kuti Yehova adzakhululukira anthu ake olapa pamene anati: ‘Ndani Mulungu wofanana ndi Inu, . . . wakupitirira zolakwa za otsala a choloŵa chake? . . . Ndipo mudzataya zochimwa zawo zonse m’nyanja yakuya.’ (Mika 7:18, 19) Lingalirani zimene mawu amenewo anatanthauza kwa anthu amene anali kukhala m’nthaŵi za m’Baibulo. Kodi panali mwayi uliwonse wovuula chinthu chimene chinaponyedwa “m’nyanja yakuya”? Motero mawu a Mika akusonyeza kuti pamene Yehova watikhululukira, amachotsa machimo athu kwa nthaŵi zonse.

13. Kodi mawu a Yesu akuti “mutikhululukire mangaŵa athu” amatanthauzanji?

13 Yesu anagwiritsa ntchito zomwe zimachitika pakati pa munthu wokongoza anzake zinthu ndi yemwe amakongolayo kuti apereke fanizo la kukhululukira kwa Yehova. Yesu anatilimbikitsa kupemphera kuti: ‘Mutikhululukire mangaŵa athu.’ (Mateyu 6:12) Motero Yesu anafananitsa machimo ndi mangaŵa, kapena kuti ngongole. (Luka 11:4) Tikachita tchimo timakhala ndi “ngongole”  yoti tipereke kwa Yehova. Buku lina limati mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “mutikhululukire” amatanthauza kuti: “Kusiya, kapena kuleka, ngongole mwa kusailonjerera.” M’lingaliro limeneli, pamene Yehova watikhululukira, amapha ngongole imene tikanafunika kulipira. Zimenezi zikuyeneratu kulimbikitsa ochimwa amene alapa. Yehova sadzalonjerera ngongole imene anapha!—Salmo 32:1, 2.

14. Kodi mawu akuti “afafanizidwe machimo anu” amatipatsa chithunzi chotani m’maganizo?

14 Kukhululukira kwa Yehova kukufotokozedwanso pa Machitidwe 3:19 kuti: ‘Chifukwa chake lapani, bwererani kuti afafanizidwe machimo anu.’ Mawu akuti “afafanizidwe” atembenuzidwa ku mawu achigiriki amene angatanthauze kuti “kupukuta, . . . kufufuta kapena kuwononga.” Malinga n’kunena kwa akatswiri ena a Baibulo, mawuŵa amaphiphiritsira kufufuta zimene munthu analemba. Kodi zimenezi zinkatheka bwanji? Inki imene anali kulembera kaŵirikaŵiri m’masiku akale anali kuipanga posakaniza mkala, manthova a mitengo, ndi madzi. Akangotha kulemba ndi inki yoteroyo, munthu ankatha kutenga chinkhupule chonyowa n’kufufuta zimene analembazo. Pamenepatu tikuona chithunzi chokongola kwambiri cha chifundo cha Yehova. Iye akatikhululukira machimo athu, zimakhala ngati kuti watenga chinkhupule n’kufufuta machimowo.

Yehova amafuna kuti tidziŵe kuti ndi “wokhululukira”

15. Kodi Yehova akufuna kuti tidziŵe chiyani za iye?

15 Pamene tisinkhasinkha pa mafanizo a mawu osiyanasiyana ameneŵa, kodi sizachionekere kuti Yehova amafuna kuti tidziŵe kuti iye ndi wokonzekadi kutikhululukira machimo athu malinga ngati tili olapadi? Tisalingalire kuti m’tsogolo adzationanso monga ochimwa pa machimo omwewo. Zimenezi zikusonyezedwa bwino m’mfundo inanso imene Baibulo limanena yokhudza chifundo chachikulu cha Yehova, yakuti: Pamene wakhululukira munthu, amaiwala.

“Sindidzakumbukira Tchimo Lawo”

16, 17. Pamene Baibulo limanena kuti Yehova amaiwala machimo athu, kodi limatanthauzanji, ndipo n’chifukwa chiyani mukuyankha choncho?

16 Yehova analonjeza izi kwa awo okhala m’pangano latsopano: “Ndidzakhululukira mphulupulu yawo, ndipo sindidzakumbukira  tchimo lawo.” (Yeremiya 31:34) Kodi zikutanthauza kuti Yehova akakhululuka sathanso kukumbukira machimo? Zimenezi sizingachitike. Baibulo limatiuza machimo amene anachita anthu ambiri omwe Yehova anawakhululukira, kuphatikizapo Davide. (2 Samueli 11:1-17; 12:13) Ndithudi Yehova akudziŵabe zolakwa zimene iwo anachita. Nkhani zonena za machimo awo, kulapa kwawo ndiponso mmene Mulungu anawakhululukirira, zinasungidwa kuti tipindule nazo. (Aroma 15:4) Nangano Baibulo limatanthauzanji pamene limati Yehova ‘sakumbukira’ machimo a anthu amene wawakhululukira?

17 Mawu achihebri otembenuzidwa kuti ‘kumbukira’ amatanthauza zambiri osati kungokumbukira chabe zinthu zakale. Buku lakuti Theological Wordbook of the Old Testament limati amaphatikizapo “lingaliro linanso la kuchitapo kanthu moyenerera.”  Choncho ndi lingaliro limeneli, ‘kukumbukira’ machimo kukuphatikizapo kuchitapo kanthu pa ochimwawo. (Hoseya 9:9) Koma pamene Mulungu akuti “sindidzakumbukira tchimo lawo,” akutitsimikizira kuti iye akakhululukira ochimwa amene alapa, ndiye kuti sadzawalanganso panthaŵi ina m’tsogolo chifukwa cha machimo omwewo. (Ezekieli 18:21, 22) Motero Yehova amaiwala m’lingaliro lakuti sakumbutsa machimo athu nthaŵi ndi nthaŵi n’cholinga chakuti azingotitsutsa kapena kumangotilanga. Kodi sizokhazika mtima pansi kudziŵa kuti Mulungu wathu amatikhululukira ndiponso amaiwalako?

Nanga Bwanji Zotsatira Zake?

18. N’chifukwa chiyani kukhululukidwa machimo sikutanthauza kuti wochimwa amene walapayo wamasulidwa ku zotsatirapo zonse za zochita zake zoipa?

18 Kodi kukhululuka kwa Yehova kumatanthauza kuti wochimwa yemwe walapa amamasulidwa ku zotsatirapo zonse za zochita zake zoipa? Ayi si choncho. Sitingachite tchimo n’kumayembekezera kuti palibe chitichitikire. Paulo analemba kuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta.” (Agalatiya 6:7) Tingakumane ndi mavuto ena chifukwa cha zochita zathu. Zimenezi sizikutanthauza kuti Yehova akatikhululukira pambuyo pake amatibweretsera mavuto. Pamene mavuto abwera, Mkristu sayenera kulingalira kuti, ‘Mwina Yehova akundilanga chifukwa cha machimo anga akale.’ (Yakobo 1:13) Komanso, Yehova satitchinjiriza ku zilizonse zobwera chifukwa cha zochita zathu zolakwika. Kutha kwa banja, mimba yosafunika, matenda opatsirana mwa kugonana, anthu kuleka kukudalira kapena kukupatsa ulemu—zonsezi zingakhale zotsatirapo zomvetsa chisoni ndiponso zosapeŵeka za kuchita tchimo. Kumbukirani kuti ngakhale pamene Yehova anakhululukira Davide machimo ake okhudzana ndi Bateseba ndi Uriya, sanamuteteze ku zochitika zowononga zimene zinatsatirapo.—2 Samueli 12:9-12.

19-21. (a) Kodi lamulo lolembedwa pa Levitiko 6:1-7 linali lothandiza motani kwa wolakwiridwa ndiponso wolakwira mnzake? (b) Ngati anthu ena asautsidwa ndi machimo athu, kodi Yehova amasangalala pamene tichita chiyani?

19 Machimo athu angakhalenso ndi zotsatirapo zina, makamaka ngati zimene tinachitazo zavutitsanso anthu ena. Mwachitsanzo, lingalirani nkhani yopezeka mu Levitiko chaputala 6.  M’chaputala chimenechi, Chilamulo cha Mose chikulongosola zimene ziyenera kuchitika pamene munthu wachita cholakwa chachikulu cholanda katundu wa Mwisrayeli mnzake pomulanda mwachifwamba, kumuopseza, kapena mwachinyengo. Ndiyeno wochimwayo poyamba angakane kuti sanalakwe, mwinanso mpaka kufika pochita kulumbira zabodza. Nkhaniyi ndi yakuti munthu mmodzi akutsutsana ndi munthu wina. Komabe, m’kupita kwa nthaŵi wolakwayo akuvutika ndi chikumbumtima n’kuvomera tchimo lake. Kuti Mulungu amukhululukire anali kufunika kuchita zinthu zinanso zitatu: kubwezera zimene anatenga, kupereka faindi kwa mwini katunduyo yokwanira pa magawo 20 a magawo 100 alionse a zimene anabazo, ndi kupereka nkhosa yamphongo yoti ikhale nsembe yopalamula. Ndiyeno lamulo lake limati: “Wansembeyo amuchitire chomutetezera pamaso pa Yehova, ndipo adzakhululukidwa.”—Levitiko 6:1-7.

20 Mulungu anawapatsa lamulo limeneli mwa chifundo chake. Linali kuthandiza woberedwa, yemwe katundu wake anali kubwezedwa ndipo mosakayikira anali kumva bwino mumtima mwake pamene pamapeto pake wopalamulayo anavomereza tchimo lake. Panthaŵi yofananayo, lamuloli linali kuthandiza munthu yemwe chikumbumtima chake chinafika pomuchititsa kuvomereza kulakwa kwake ndi kukonza cholakwacho. Zoonadi, ngati iye akanakana kuchita zimenezi, Mulungu sakanamukhululukira.

21 Ngakhale kuti sitikuyendera Chilamulo cha Mose, Chilamulo chimenecho chimatithandiza kuzindikira malingaliro a Yehova, kuphatikizapo zimene iye amaganiza pa nkhani ya kukhululuka. (Akolose 2:13, 14) Ngati machimo athu asautsa anthu ena, Mulungu amasangalala pamene tichita zimene tingathe kuti tikonze zolakwazo. (Mateyu 5:23, 24) Zimenezi zingaphatikizepo kuvomereza tchimo lathu, kuvomera kuti tinalakwa, ndipo ngakhale kupepesa wovutitsidwayo. Ndiyeno tingachonderere Yehova pamaziko a nsembe ya Yesu, n’kumamva kuti tikutsimikiziridwa kuti Mulungu watikhululukira.—Ahebri 10:21, 22.

22. Kodi n’chiyani chingabwere limodzi ndi kutikhululukira kwa Yehova?

22 Mofanana ndi kholo lililonse lachikondi, potikhululukira  Yehova angatipatsenso chilango. (Miyambo 3:11, 12) Mkristu wolapa angataye mwayi umene anali nawo wokhala mkulu, mtumiki wotumikira, kapena mlaliki wanthaŵi zonse. Zingakhale zopweteka kwambiri kuti kwa kanthaŵi sadzakhala ndi maudindo amene anali kuwakonda. Komabe, chilango chotero sichitanthauza kuti Yehova sanatikhululukire. Tiyenera kukumbukira kuti chilango chimene Yehova amatipatsa ndi umboni wakuti amatikonda. Kulandira ndi kugwiritsa ntchito chilangocho kumatipindulitsa.—Ahebri 12:5-11.

23. N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti Yehova sangatichitire chifundo, nanga n’chifukwa chiyani tiyenera kutsanzira kukhululuka kwa Yehova?

23 N’zotsitsimula bwanji kudziŵa kuti Mulungu wathu ndi “wokhululukira”! Ngakhale kuti tinachitapo zolakwa, tisaganize kuti Yehova sangatichitire chifundo. Ngati tilapa zenizeni, tichita zinthu zofunikira kuti tikonze zolakwazo, ndi kupemphera mochokera pansi pa mtima kuti atikhululukire pa maziko a mwazi wokhetsedwa wa Yesu, tingakhale ndi chidaliro chonse kuti Yehova adzatikhululukira. (1 Yohane 1:9) Tiyeni titsanzire kukhululuka kwa Yehova pa zimene timachita ndi anthu anzathu. Inde, ngati Yehova amene sachimwa amatikhululukira mwachikondi kwambiri, kodi ife anthu ochimwafe sitifunika kuyesetsa kuti tizikhululukirana?

^ ndime 4 Mawu achihebri otembenuzidwa kuti “mapangidwe athu” amagwiritsidwanso ntchito pa zinthu zadothi zimene woumba mbiya amapanga.—Yesaya 29:16.

^ ndime 10 Katswiri wina wa Baibulo anati maonekedwe ofiira otchulidwa pano sanali kusuluka. Maonekedwe ameneŵa sanali kuchoka ngakhale chinthu chikhale pa mame, pa mvula, chichapidwe, kayanso achigwiritse ntchito kwa nthaŵi yaitali.

Onaninso

GALAMUKANI!

Kodi Mungatani Kuti Muzikhululukirana?

N’chifukwa chiyani kukhululukirana sikophweka? Werengani nkhani kuti muone mmene Baibulo lingakuthandizireni.

KUYANKHA MAFUNSO A M’BAIBULO

Kodi Mulungu Angandithandize Ndikapemphera?

Kodi Mulungu zimam’khudza tikamavutika?