Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 27

“Ubwino Wake ndi Waukulu Ndithu”

“Ubwino Wake ndi Waukulu Ndithu”

1, 2. Kodi ubwino wa Mulungu umafika mpaka pati, nanga Baibulo limatsindikanji za khalidwe limeneli?

ALI pa dzuŵa lomwe likuloŵa, anthu angapo amene akhala akugwirizana kwanthaŵi yaitali akudya chakudya panja. Akuseka ndi kumacheza pamene akusangalala ndi malo amene akhalapowo. Kwinakwake kutali, mlimi akuyang’ana minda yake mosangalala chifukwa mvula yayamba kugwa pa mbewu zake zomwe zafota ndi dzuŵa. Kwinanso, mwamuna ndi mkazi wake akusangalala poona mwana wawo akuyamba kudamphira.

2 Kaya akudziŵa kapena sakudziŵa, anthu onsewo akupindula ndi chinthu chimodzi—ubwino, kapena kuti ukoma, wa Yehova Mulungu. Anthu ena opembedza amanena mobwerezabwereza kuti “Mulungu ndi wabwino.” Baibulo limatsindika kwambiri nkhaniyi. Limati: “Ukoma [“ubwino,” NW] wake ndi waukulu ndithu!” (Zekariya 9:17) Koma zikuoneka kuti ndi anthu ochepa chabe amene lerolino amadziŵa zimene mawu amenewo amatanthauza. Kodi ubwino wa Yehova Mulungu umaphatikizapo chiyani makamaka, nanga khalidwe la Mulungu limeneli limam’khudza motani aliyense wa ife?

Mbali Yapadera Yosonyeza Chikondi cha Mulungu

3, 4. Kodi ubwino n’chiyani, nanga n’chifukwa chiyani tinganene momveka kuti ubwino wa Yehova ndiwo kusonyeza chikondi chake?

3 M’zinenero zambiri za masiku ano, mawu akuti “ubwino” amangowagwiritsa ntchito pa zilizonse. Komabe, monga mmene asonyezedwera m’Baibulo, ubwino, kapena ukoma, si mawu oti amanenedwa pa chilichonse. Amanena makamaka za kukhala ndi makhalidwe apamwamba. Motero tikhoza kunena kuti ubwino unamuloŵerera Yehova. Makhalidwe ake onse—kuphatikizapo mphamvu zake, chilungamo chake, ndi nzeru zake—ndi abwino pa kalikonse. Komabe, tingafotokoze momveka kuti ubwino umasonyeza chikondi cha Yehova. Chifukwa chiyani?

 4 Ubwino ndi khalidwe limene limasonyezedwa pochitira ena zinthu. Mtumwi Paulo anaonetsa kuti kwa anthu, khalidweli n’lokondweretsa kwambiri kuposa kukhala wolungama. (Aroma 5:7) Munthu wolungama amangotsatira mokhulupirika zimene lamulo limanena, koma munthu wabwino amachita zoposa pamenepo. Amayamba ndiye kuchitapo kanthu pa zinthu mwa kufunafuna mwachangu njira zothandizira ena. Monga mmene tionere, Yehova alitu wabwino m’lingaliro limeneli. N’zachionekere kuti ubwino woterowo umabwera chifukwa cha chikondi chosefukira cha Yehova.

5-7. N’chifukwa chiyani Yesu anakana kutchedwa kuti “Mphunzitsi wabwino,” ndipo zimenezi zinatsimikizira choonadi chofunika chiti?

5 Yehova alinso wabwino mwapadera. Yesu atatsala pang’ono kufa, anakumana ndi munthu wina yemwe amafuna kumufunsa funso. Munthuyo anatchula Yesu kuti “Mphunzitsi wabwino.” Yesu anayankha kuti: “Unditcha Ine wabwino bwanji? Palibe wabwino koma mmodzi, ndiye Mulungu.” (Marko 10:17, 18) Mungadabwe kwambiri ndi yankholi. N’chifukwa chiyani Yesu anakonza zonena za munthuyo? Kodi Yesu sanalidi “Mphunzitsi wabwino”?

6 N’zachionekere kuti munthuyo ananena kuti “Mphunzitsi wabwino” popereka ulemu wachiphamaso. Modzichepetsa Yesu anapereka ulemerero woterowo kwa Atate wake wakumwamba, yemwe ndi wabwino kwambiri pa kalikonse. (Miyambo 11:2) Komanso Yesu anali kutsimikizira choonadi chofunika zedi. Yehova yekha ndiye muyezo wa chimene chili chabwino. Ndiye yekha amene ali ndi ulamuliro posankha chimene chili chabwino ndi chimene chili choipa. Adamu ndi Hava, mwa kudya mopanduka zipatso za mtengo wodziŵitsa zabwino ndi zoipa, analakalaka atatenga ulamuliro umenewo. Koma mosiyana nawo, Yesu anadzichepetsa n’kusiya nkhani ya kuika miyezo ya zinthu m’manja mwa Atate wake.

7 Ndiponso, Yesu anali kudziŵa kuti chilichonse chimene chili chabwinodi chimachokera kwa Yehova. Ndi iyeyo amene amapereka “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro.” (Yakobo 1:17) Tiyeni tione mmene kuwoloŵa manja kwa Yehova kumasonyezera kuti ndi wabwino.

 Umboni Wakuti Yehova Ndi Wabwino Kwambiri

8. Kodi Yehova wachitira motani zabwino anthu onse?

8 Aliyense amene wakhalako ndi moyo wapindula ndi ubwino wa Yehova. Salmo 145:9 limati: ‘Yehova achitira chokoma onse.’ Kodi tili ndi zitsanzo ziti za zinthu zabwino zimene amachitira aliyense? Baibulo limati: “Sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.” (Machitidwe 14:17) Kodi munadyapo chakudya chokoma n’kumachita kubwekera? Kukanakhala kuti Yehova, ndi ubwino wake, sanakonze dziko lapansili lokhala ndi madzi opanda mchere amene amazungulira nthaŵi zonse, ndiponso chikhala kuti sanapange “nyengo za zipatso” zopereka chakudya chochuluka, bwenzi kulibe zakudya. Yehova wachitira aliyense zabwino zimenezi, osati amene amamukonda okha. Yesu anati: “Iye amakwezera dzuŵa lake pa oipa ndi pa  abwino, namavumbitsira mvula pa olungama ndi pa osalungama.”—Mateyu 5:45.

Yehova ‘amakupatsani zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso’

9. Kodi chipatso cha apulo chimapereka motani chitsanzo cha ubwino wa Yehova?

9 Chifukwa chakuti nthaŵi zonse timakhala ndi dzuŵa, mvula, ndiponso nyengo za zipatso, ambiri amaziona mopepuka zinthu zochuluka zimene Yehova waunjikira anthu mowoloŵa manjazi. Mwachitsanzo, lingalirani chipatso cha apulo. Chimenechi n’chipatso chosasoŵa m’madera onse ofunda a dziko lapansi. Komatu, n’chipatso chokongola, chokoma kudya, ndipo chili ndi madzi ambiri otsitsimula komanso zinthu zomanga thupi. Kodi mumadziŵa kuti padziko lonse lapansi pali mitundu pafupifupi 7,500 ya maapulo, okhala ndi maonekedwe osiyanasiyana, ena ofiira ena ooneka agolide ena achikasu enanso  obiriŵira, ndiponso ndi osiyanasiyana kukula kwake, kuyambira pa okulirapo kuposa pa nthudza mpaka kufika pa akuluakulu ngati manyumwa? Mukatenga njere yaing’ono ya apulo m’dzanja lanu, imangokhala ngati palibe chimene mwagwira. Koma njere imeneyo ikamera, imakula n’kukhala umodzi wa mitengo yosangalatsa kwambiri, “mtengo wa apulo.” (Nyimbo ya Solomo 2:3, NW) Chaka chilichonse m’ngululu, mtengo wa apulo umachita maluŵa okongola, ndipo pofika mu mphakasa umabereka zipatso. Chaka chilichonse mtengo wa apulo umabereka zipatso zokwanira kudzaza makatoni 20, katoni iliyonse yolemera makilogalamu 19—ndipo umabereka chonchi kwa zaka 75!

Kanjere kakang’ono aka kamamera n’kukhala mtengo umene ungadyetse ndi kusangalatsa anthu kwa zaka zambiri

10, 11. Kodi kukhoza kwathu kuzindikira zinthu zosiyanasiyana kumasonyeza motani ubwino wa Mulungu?

10 Chifukwa cha ubwino wake umene sukutha, Yehova anatipatsa thupi ‘lopangidwa modabwitsa,’ lomwe limatha kuzindikira ntchito za Mulungu ndi kusangalala nazo. (Salmo 139:14) Taganiziraninso zochitika zija tinalongosola m’ndime yoyamba ya mutu uno. Kodi ndi zinthu ziti zimene zimasangalatsa kuziona panthaŵi ngati zimenezi? Kumwetulira kwa mwana yemwe wasangalala. Kugwa kwa mvula m’minda. Maonekedwe osiyanasiyana a dzuŵa pamene likuloŵa. Diso la munthu linapangidwa kuti lizizindikira maonekedwe a zinthu opitirira pa mitundu 300,000. Ndipo makutu athu amamva mokoma kwambiri mawu omveka mosiyanasiyana, kudutsa kwa mphepo m’mitengo, ngakhalenso kuseka kwa mwana wophunzira kuyenda. Kodi n’chifukwa chiyani timatha kusangalala ndi zinthu zimene timaonazo ndiponso mawu amene timamvawo? Baibulo limati: “Khutu lakumva, ndi diso lopenya, Yehova anapanga onse aŵiriwo.” (Miyambo 20:12) Komatu izi ndi ziwalo ziŵiri zokha mwa ziwalo zimene timagwiritsa ntchito pozindikira zinthu.

11 Kumva fungo ndi umboni wina wa ubwino wa Yehova. Mphuno ya munthu ikhoza kusiyanitsa fungo la mitundu pafupifupi 10,000. Taganizirani za mitundu yochepa iyi: fungo limene mumalimva akamaphika chakudya chapamtima panu, la maluŵa, la masamba amene athothoka, la kautsi kamene kakuchokera pamoto wonyeka bwino. Thupi lathu limazindikiranso kuti lakhudza kapena lakhudzidwa ndi kanthu kenakake. Izi zimatithandiza  kumva kamphepo kayeziyezi kakutiwomba kumaso, kumva kuti wokondedwa wathu watikumbatira mwachikondi, ngakhalenso kusangalala titagwira chipatso chosalala bwino. Mutaluma chipatsocho, mumazindikira kukoma kwake. Mumachita kukandira kunkhongo m’kamwa mwanu muli tseketseke ndi makomedwe osiyanasiyana a chipatsocho. Ndithudi, tili ndi zifukwa zomveka zofuulira kwa Yehova kuti: “Ha! Kukoma [“ubwino,” NW] kwanu ndiko kwakukulu nanga, kumene munasungira iwo akuopa Inu.” (Salmo 31:19) Komabe, kodi ndi motani mmene Yehova ‘wasungira’ ubwino anthu amene amamuopa?

Zabwino Zopindulitsa Kwamuyaya

12. Kodi ndi zinthu ziti zimene Yehova amatipatsa zomwe zili zofunika kwambiri, ndipo n’chifukwa chiyani?

12 Yesu anati: “Kwalembedwa, Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.” (Mateyu 4:4) Ndithudi, tingapindule kwambiri ndi zinthu zauzimu zimene Yehova amatipatsa kuposa ndi mmene tingapindulire ndi zakuthupi, chifukwa zauzimu zimapereka moyo wosatha. M’Mutu 8 wa buku lino, tinaona kuti m’masiku otsiriza ano Yehova wagwiritsa ntchito mphamvu zake zobwezeretsa zinthu pokhazikitsa paradaiso wauzimu. Mbali yaikulu ya paradaiso ameneyo ndiyo chakudya chauzimu chochuluka.

13, 14. (a) Kodi n’chiyani chimene mneneri Ezekieli anaona m’masomphenya, ndipo zikutanthauzanji lerolino kwa ife? (b) Kodi ndi mphatso zauzimu zopatsa moyo zotani zimene Yehova amapereka kwa atumiki ake okhulupirika?

13 Mu ulosi umodzi mwa maulosi akuluakulu a m’Baibulo onena za kubwezeretsa, mneneri Ezekieli anaona masomphenya a kachisi wobwezeretsedwa ndi waulemerero. Madzi anali kuyenda kuchokera ku kachisiyo, ndipo anali kumka nachuluka mpaka unakhala “mtsinje” waukulu zedi. Mtsinjewo unali kubweretsa madalitso kulikonse kumene unadutsa. M’magombe ake munamera mitengo imene inali ndi zakudya komanso inali kuchiritsa anthu. Ndipo mtsinjewo unachititsa Nyanja Yakufa, yomwe inali yamchere zedi komanso yopanda zamoyo, kukhala ndi zamoyo ndi kutinso anthu ayambe kusodzamo. (Ezekieli 47:1-12) Koma kodi zonsezi zinatanthauzanji?

 14 Masomphenyaŵa anatanthauza kuti Yehova adzabwezeretsa makonzedwe ake a kulambira koyera. Kachisi yemwe anaona Ezekieli anaimira zimenezi. Mofanana ndi mtsinje wa m’masomphenya uja, Mulungu anali kudzakonzera anthu ake zinthu zowapatsa moyo zochuluka nthaŵi zonse. Kuchokera pa kubwezeretsedwa kwa kulambira koyera m’chaka cha 1919, Yehova wapatsa anthu ake mphatso zopatsa moyo. Motani? Anthu mamiliyoni ambirimbiri alandira choonadi chofunika kwambiri mothandizidwa ndi mabaibulo, mabuku ofotokoza za m’Baibulo, misonkhano ing’onoing’ono ndiponso ikuluikulu. Kupyolera m’njira zimenezi, Yehova waphunzitsa anthu ake za mphatso yofunika kwambiri pa zonse imene wapatsa anthu kuti akhale ndi moyo—nsembe ya dipo ya Kristu. Anthu onse amene amakondadi Mulungu ndi kumuopa amatha kukhala ndi mbiri yabwino kwa Yehova ndiponso amatha kukhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha chifukwa cha mphatsoyi. * Motero, m’masiku onse otsiriza ano, pamene dzikoli likuvutika ndi njala yauzimu, anthu a Yehova akhala akusangalala ndi phwando lauzimu.—Yesaya 65:13.

15. Kodi mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu ubwino wa Yehova udzayenda kufika kwa anthu okhulupirika m’lingaliro lotani?

15 Koma mtsinje umene Ezekieli anaona m’masomphenya sudzasiya kuyenda pakutha kwa dongosolo lino lakale la zinthu. Udzayenda kwambiri mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Kristu. Panthaŵiyo, kudzera mwa Ufumu Waumesiya, Yehova adzagwiritsa ntchito mtengo wonse wa nsembe ya Yesu, ndipo pang’onopang’ono adzachititsa anthu kukhala angwiro. Zikadzatero tidzasangalalatu kwambiri ndi ubwino wa Yehova!

Mbali Zinanso za Ubwino wa Yehova

16. Kodi Baibulo limaonetsa motani kuti mu ubwino wa Yehova mulinso makhalidwe ena, nanga ena mwa ameneŵa ndi ati?

16 Ubwino wa Yehova umaphatikizapo zambiri kuposa pa kungokhala wowoloŵa manja. Mulungu anauza Mose kuti: “Ndidzapititsa ukoma [“ubwino,” NW] wanga wonse pamaso pako,  ndipo ndidzatchula dzina la Yehova pamaso pako.” Kenako nkhaniyi imati: “Yehova anapita pamaso pake, nafuula, Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi.” (Eksodo 33:19; 34:6) Choncho ndiye kuti mu ubwino wa Yehova muli makhalidwe enanso angapo apamwamba. Tiyeni tionepo aŵiri okha mwa ameneŵa.

17. Kodi chisomo n’chiyani, nanga Yehova wachisonyeza motani kwa anthu wamba opanda ungwiro?

17 “Wachisomo.” Khalidweli limatiuza zambiri za mmene Yehova amachitira zinthu ndi zolengedwa zake. M’malo mokhala waukali, wosakondweretsedwa ndi ena, kapena wopondereza, monga mmene zimakhalira nthaŵi zambiri ndi anthu audindo, Yehova ndi wodekha ndiponso wokoma mtima. Mwachitsanzo, Yehova anauza Abramu kuti: “Chonde, tukula maso ako, nuyang’ane kuchokera pamene ulilipo, kumpoto ndi kum’mwera ndi kum’maŵa ndi kumadzulo.” (Genesis 13:14, NW) M’mabaibulo ambiri palembali palibe mawu akuti “chonde.” Koma akatswiri a Baibulo amati m’Chihebri choyambiriracho mawu a mu lembali anali ndi liwu limene limasintha chiganizochi kuti chimveke monga kupempha mwaulemu m’malo momveka monga kulamula. Palinso malemba ena omveka mofanana ndi limeneli. (Genesis 31:12; Ezekieli 8:5) Tangoganizirani, Wolamulira wa chilengedwe chonse akulankhula mwaulemu kwa anthu wamba! M’dziko limene anthu ambiri amachita zinthu mwaukali, mwankhanza, ndiponso mwachipongwe, n’zolimbikitsatu kwambiri kumasinkhasinkha kuti Mulungu wathu, Yehova, ndi wachisomo.

18. Kodi Yehova ndi “wachoonadi” m’lingaliro lotani, nanga n’chifukwa chiyani mawu amenewo ali okhazika mtima pansi?

18 “Wachoonadi.” Masiku ano anthu ambiri ali ndi chizoloŵezi cha kusaona mtima. Koma Baibulo limatikumbutsa kuti: “Mulungu sindiye munthu, kuti aname.” (Numeri 23:19) Ndipo Tito 1:2 amati ‘Mulungu sanganame.’ Iye ndi wabwino kwambiri moti sangachite zimenezo. Motero malonjezo a Yehova ndi odalirika kwambiri; ndipo mawu ake ndi otsimikizika nthaŵi zonse kuti adzakwaniritsidwa. Yehova akutchedwatu kuti “Mulungu wa choonadi.” (Salmo 31:5) Sikuti amangopeŵa kunena zabodza,  komanso amapereka choonadi chochuluka. Sabisa zinthu, kapenanso kuzichita mwachinsinsi. Koma ndi nzeru zosaneneka zimene ali nazo, amaunikira mosaumira atumiki ake okhulupirika. * Ndiponso amawaphunzitsa momwe ayenera kukhalira mogwirizana ndi choonadi chimene amawapatsa kotero kuti ‘aziyendabe m’choonadi.’ (3 Yohane 3) Kodi ubwino wa Yehova uyenera kutikhudza motani aliyense payekha?

‘Sangalalani ndi Ubwino wa Yehova’

19, 20. (a) Kodi Satana anachepetsa motani chidaliro cha Hava m’zinthu zabwino zimene Yehova amachita, ndipo n’chiyani chinatsatirapo? (b) Kodi ubwino wa Yehova uyenera kutikhudza motani, ndipo n’chifukwa chiyani?

19 Pamene Satana anayesa Hava m’munda wa Edene, mochenjera kwambiri anayamba ndi kuchepetsa chidaliro cha mkaziyo chakuti Yehova amachita zabwino. Yehova anali atauza Adamu kuti: “Mitengo yonse ya m’munda udyeko.” Mwa mitengo yonse zikwizikwi imene inali m’mundawo, Yehova analetsa mtengo umodzi wokha. Komatu, taonani mmene Satana anafunsira Hava funso lake loyamba: “Eya! kodi anatitu Mulungu, Usadye mitengo yonse ya m’mundamu?” (Genesis 2:9, 16; 3:1) Satana anapotoza mawu a Yehova pofuna kuchititsa Hava kuganiza kuti Yehova sanali kumupatsa chinthu chinachake chabwino. Mwachisoni, zochita zakezo zinagwiradi ntchito. Hava, mofanana ndi amuna ndi akazi ambiri pambuyo pake, anayamba kukayikira za ubwino wa Mulungu, yemwe anali atamupatsa chilichonse chimene anali nacho.

20 Tikudziŵa kuti kukayikira koteroko kunabweretsa chisoni chosaneneka ndiponso mavuto adzaoneni. Motero tiyeni tilabadire mawu aŵa opezeka pa Yeremiya 31:12, NW: “Iwo . . . adzasangalala ndi ubwino wa Yehova.” Zinthu zabwino zimene Yehova amatichitira zikuyeneradi kutichititsa kukhala achimwemwe zedi. Sitiyenera kukayikira zolinga za Mulungu wathu yemwe ndi wodzala ubwino. Tingamudalire ndi mtima wonse chifukwa anthu amene amamukonda amawafunira zabwino zokhazokha.

21, 22. (a) Kodi ndi njira zina ziti zimene mungakonde kutsatira polabadira ubwino wa Yehova? (b) Kodi m’mutu wotsatira tikambirana khalidwe liti, nanga limasiyana motani ndi ubwino?

 21 Ndiponso, timasangalala pamene tikhala ndi mpata wolankhula ndi ena za ubwino wa Mulungu. Salmo 145:7 limanena za anthu a Yehova kuti: “Adzabukitsa chikumbukiro cha ubwino wanu waukulu.” Tsiku lililonse limene tili ndi moyo, timapindula ndi ubwino wa Yehova m’njira inayake. Bwanji osakonza zoti tsiku lililonse muzithokoza Yehova pa zinthu zabwino zimene wakuchitirani, pozitchula mwachindunji? Kulingalira khalidwe limeneli, kuthokoza Yehova chifukwa cha khalidweli, ndiponso kuuza ena za khalidwe limeneli, zidzatithandiza kutsanzira Mulungu wathu wabwinoyu. Ndipo pamene tifunafuna njira zochitira zabwino, monga amachitira Yehova, tidzamuyandikira kwambiri iyeyo. Mtumwi Yohane wokalambayo analemba kuti: “Wokondedwa, usatsanza chili choipa komatu chimene chili chokoma. Iye wakuchita chokoma achokera kwa Mulungu.”—3 Yohane 11.

22 Palinso makhalidwe ena amene amayendera limodzi ndi ubwino wa Yehova. Mwachitsanzo, Mulungu ndi “wa ukoma mtima wochuluka,” kapena kuti ali ndi chikondi chokhulupirika. (Eksodo 34:6) Khalidwe limeneli, mosiyana ndi ubwino, Yehova salisonyeza kwa aliyense, koma amalisonyeza makamaka kwa atumiki ake okhulupirika. M’mutu wotsatira, tiphunzira mmene amachitira zimenezi.

^ ndime 14 Dipo ndi chitsanzo chachikulu pa zonse cha ubwino wa Yehova. Pa zolengedwa zauzimu zonse mamiliyoni ambirimbiri zimene akanasankhapo, Yehova anasankha Mwana wake wokondedwa ndiponso wobadwa yekha kuti adzatifere.

^ ndime 18 Moyenerera Baibulo limagwirizanitsa choonadi ndi kuunika. Wamasalmo anaimba kuti: “Tumizirani kuunika kwanu ndi choonadi chanu.” (Salmo 43:3) Yehova amapereka kuunika kwauzimu kwakukulu kwa awo amene amafuna kuti iye awaphunzitse, kapena kuti awaunikire.—2 Akorinto 4:6; 1 Yohane 1:5.