Pitani ku nkhani yake

Pitani ku menyu yachiwiri

Pitani ku mitu ya nkhani

Mboni za Yehova

Chichewa

Yandikirani kwa Yehova

 MUTU 23

“Anayamba iye Kutikonda”

“Anayamba iye Kutikonda”

1-3. Kodi ndi zochitika zina ziti zimene zinasiyanitsa imfa ya Yesu ndi imfa ina iliyonse m’mbiri ya anthu?

TSIKU linalake m’nyengo ya ngululu zaka pafupifupi 2,000 zapitazo, munthu wosalakwa anazengedwa mlandu, anamuuza kuti anali wolakwa pa milandu imene sanapalamule n’komwe, ndipo kenako anamuzunza mpaka kufa. Sanali munthu woyamba kuphedwa mwankhanza ndi mopanda chilungamo m’mbiri ya anthu; komanso n’zachisoni kuti sanali munthu womaliza. Komatu, imfa yake inali yosiyana ndi imfa zina zonse.

2 Pamene munthuyo anali kuvutika m’maola omalizira ndi osautsa amenewo a moyo wake, kumwamba kunaonetsa kuti panali kuchitika chinthu chofunika kwambiri. Ngakhale kuti panthaŵiyo n’kuti dzuŵa lili pamutu, mwadzidzidzi padzikolo panagwa mdima. Wolemba mbiri wina anati patsikulo “dzuŵa linada.” (Luka 23:44, 45) Ndiyeno, munthuyu atangotsala pang’ono kufa ananena mawu osaiwalika aŵa: “Kwatha [“chakwaniritsidwa,” NW].” Inde, imfa yake inakwaniritsa chinthu chofunika kwambiri. Nsembe imene iye anapereka inali chochitika chosonyeza chikondi chachikulu koposa chimene munthu wina aliyense anasonyezapo.—Yohane 15:13; 19:30.

3 Inde, munthu ameneyo anali Yesu Kristu. Anthu ambiri amadziŵa bwino mmene anavutikira ndiponso mmene anafera pa tsiku lamdimalo la Nisani 14, mu 33 C.E. Komabe, nthaŵi zambiri anthu amanyalanyaza mfundo yofunika zedi. Ngakhale kuti Yesu anavutika kwambiri, munthu wina anavutika kwambiri kuposa iye. Ndipo pa tsikulo munthu wina anapereka nsembe yaikulu kwambiri kuposa ya Yesu—chochitika chosonyeza chikondi chachikulu koposa chimene wina aliyense m’chilengedwe chonse anasonyezapo. Kodi chinali chochitika chotani? Yankho lake likutipatsa mawu oyenera kuyambira nkhani yofunika kwambiri pa zonse: chikondi cha Yehova.

Chochitika Chachikulu Kwambiri Chosonyeza Chikondi

4. Kodi msilikali wachiroma anadziŵa bwanji kuti Yesu sanali munthu wamba, nanga msilikaliyo ananenanji?

4 Mtsogoleri wa gulu la asilikali a Roma yemwe anali kuyang’anira  kuphedwa kwa Yesu anazizwa ndi mdima umene unachitika Yesu asanafe ndiponso chivomezi champhamvu chimene chinatsatira kufa kwake. “Indedi Uyo ndiye Mwana wa Mulungu,” iye ananena choncho. (Mateyu 27:54) N’zachionekere kuti Yesu sanali munthu wamba. Msilikaliyo anapha nawo Mwana wobadwa yekha wa Mulungu Wam’mwambamwamba! Koma kodi Mwana ameneyu anali wofunika motani kwa Atate wake?

5. Kodi nthaŵi yochuluka kwabasi imene Yehova ndi Mwana wake anathera limodzi kumwamba tingaifanizire motani?

5 Baibulo limati Yesu ndiye “wobadwa woyamba wa chilengedwe chonse.” (Akolose 1:15) Tangoganizani, Mwana wa Yehova anali ndi moyo chilengedwe chonse chooneka chisanakhalepo. Ndiye kuti Atate anali limodzi ndi Mwanayu kwa utali wotani? Asayansi ena amayerekezera kuti chilengedwechi chakhala chilipo kwa zaka mabiliyoni 13. Kodi mungathe n’komwe kuona nthaŵi yochuluka imeneyo m’maganizo mwanu? Pothandiza anthu kumvetsetsa zaka zimene chilengedwe chakhalapo monga momwe amanenera asayansi, m’nyumba ina yosonyezeramo zinthu zakuthambo muli mzere wautali mamita 110, wosonyeza nthaŵi imene zinthu zinachitikira. Alendo akamayenda ndi mzerewo, phazi lililonse limene amaponda limaimira zaka 75 miliyoni zimene chilengedwechi chakhala chilipo. Kumapeto kwa mzerewo, mbiri yonse ya anthu ikuimiridwa ndi kamzere kamodzi kakakulu ngati tsitsi la munthu! Komatu, ngakhale zimenezi zitakhala zolondola, mzere wonsewo si wautali mokwanira kuimira nthaŵi yonse imene Mwana wa Yehova wakhala ndi moyo. Kodi iye anali kuchitanji panthaŵi yonseyo?

6. (a) Kodi Mwana wa Yehova anali kuchita chiyani asanakhale munthu? (b) Kodi pali chomangira chamtundu wotani pakati pa Yehova ndi Mwana wake?

6 Mwanayu anali wokondwa kukhala “mmisiri” wa Atate wake. (Miyambo 8:30) Baibulo limati: “Kopanda [Mwanayo] sikunalengedwa kanthu kalikonse kolengedwa.” (Yohane 1:3) Motero Yehova ndi Mwana wake anagwirira ntchito limodzi kuti zinthu zina zonse zikhaleko. Analitu kusangalala kwambiri! Ambiri angavomereze kuti kholo limakondana kwambiri ndi mwana wake. Ndipo chikondi “ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.” (Akolose 3:14) Choncho, ndani wa ife amene angamvetsetse mphamvu zimene zili mu chomangira chimene chakhalapo kwa zaka zambirimbiri zonsezo? N’zachionekere kuti pakati pa Yehova Mulungu ndi Mwana wake pali chomangira cha chikondi champhamvu kwambiri  kuposa chilichonse chimene chinapangidwapo chomwe chimawagwirizanitsa.

7. Yesu atabatizidwa, kodi Yehova anasonyeza motani mmene anali kuonera Mwana wake?

7 Komabe, Atate anatumiza Mwana wake kudziko lapansi kuti akabadwe monga munthu wakhanda. Izi zinatanthauza kuti Yehova akhala zaka zochuluka wosayanjana ndi Mwana wake wokondedwa kumwamba. Ali kumwambako, anali kuyang’ana mwachidwi kwambiri pamene Yesu anali kukula nakhala munthu wangwiro. Ali ndi zaka pafupifupi 30, Yesu anabatizidwa. Sitifunika kuchita kulota kuti Yehova anamuona bwanji. Atate analankhula okha kuchokera kumwamba kuti: “Uyu ndiye Mwana wanga wokondedwa, mwa iyeyu ndikondwera.” (Mateyu 3:17) Atate wake ayenera kuti anasangalalatu kwambiri ataona kuti Yesu wachita mokhulupirika zonse zimene zinaloseredwa, ndiponso zonse zimene anapemphedwa kuchita.—Yohane 5:36; 17:4.

8, 9. (a) Kodi ndi zinthu zotani zimene zinachitikira Yesu pa Nisani 14, mu 33 C.E., ndipo Atate wake wakumwamba zinawakhudza motani? (b) Kodi n’chifukwa chiyani Yehova analola Mwana wake kuti avutike ndi kufa?

8 Komabe, kodi Yehova anamva bwanji pa Nisani 14, mu 33 C.E.? Kodi iye anamva bwanji pamene Yesu anali kuperekedwa kwa adani ake ndiyeno n’kumangidwa ndi gulu la anthu usiku? Pamene Yesu anamuthaŵa mabwenzi ake, ndiyeno n’kumazengedwa mlandu mosemphana ndi malamulo? Pamene anali kumunyoza, kumuthira malovu, ndi kumubwanyula? Pamene anali kumukwapula, kumsana kwake n’kulembekalembeka? Pamene anali kumukhomerera manja ndi miyendo ku mtengo, namusiya ali pachikike anthu n’kumamunenera zoipa? Kodi Atate anamva bwanji pamene Mwana wawo wokondedwa anawalirira pophupha ndi ululu? Kodi Yehova anamva bwanji pamene Yesu anatsirizika, ndipo kwanthaŵi yoyamba kuchokera pamene zolengedwa zonse zinayamba kukhalako, Mwana Wake wokondedwa kunalibeko?—Mateyu 26:14-16, 46, 47, 56, 59, 67; 27:38-44, 46; Yohane 19:1.

“Mulungu . . . anapatsa Mwana wake wobadwa yekha”

9 Timasoŵa chonena. Popeza kuti Yehova amakhudzika ndi zochitika, mawu athu amapereŵera kutalitali kulongosola ululu umene anavutika nawo pa imfa ya Mwana wake. Zimene tingathe kulongosola ndizo cholinga cha Yehova polola kuti zichitike. N’chifukwa chiyani Atate analola kuvutika moteromo? Pa Yohane 3:16, Yehova anaulula chinthu chofunika kwambiri. Vesi la m’Baibulo limeneli  n’lofunika kwabasi moti ena amati mumatha kuonamo Uthenga Wabwino wonse m’vesili. Lembali limati: “Mulungu anakonda dziko lapansi kotero, kuti anapatsa Mwana wake wobadwa yekha, kuti yense wakukhulupirira Iye asatayike, koma akhale nawo moyo wosatha.” Choncho cholinga cha Yehova chinagona pa chikondi. Mphatso imene Yehova anapereka, kutumiza Mwana wake kuti adzavutike n’kutifera, inali chochitika chosonyeza chikondi choposa china chilichonse.

Tanthauzo la Chikondi cha Mulungu

10. Kodi anthu amafunika chiyani pamoyo wawo, nanga n’chiyani chachitikira tanthauzo la mawu akuti “chikondi”?

10 Kodi mawu akuti “chikondi” ameneŵa amatanthauzanji? Ena afotokoza kuti chikondi n’chofunika chachikulu kwambiri pamoyo wa anthu. Kuchokera pa kubadwa mpaka pakufa, anthu amafunafuna chikondi, amakhala okondwa chifukwa cha kusangalatsa kwake, komanso amawonda ndi kufa chifukwa chosoŵa chikondi. Ngakhale zili choncho, n’zodabwitsa kwambiri kuti chikondi n’chovuta kuchitanthauzira. N’zoona kuti anthu amalankhula zambiri za chikondi. Nthaŵi zonse pakutuluka mabuku, nyimbo, ndi ndakatulo za chikondi. Zotsatira zake nthaŵi zambiri sizipereka bwinobwino tanthauzo la mawuŵa. Kungoti mawu ameneŵa amagwiritsidwa ntchito kwambiri moti tanthauzo lake lenileni limaoneka kuti silingadziŵike.

11, 12. (a) Kodi n’kuti kumene tingaphunzire zambiri zokhudza chikondi, ndipo n’chifukwa chiyani tingaziphunzire mmenemo? (b) Kodi ndi mitundu iti ya chikondi imene inali kutchulidwa m’Chigiriki chakale, ndipo ndi mawu ati a “chikondi” amene amagwiritsidwa ntchito nthaŵi zambiri mu Malemba Achigiriki Achikristu? (Onaninso mawu a m’munsi.) (c) Kodi a·ga′pe n’chiyani?

11 Komabe, Baibulo limaphunzitsa momveka bwino nkhani ya chikondi. Buku lomwe analemba Vine lotchedwa kuti Expository Dictionary of New Testament Words limanena kuti: “Chikondi chikhoza kudziŵika ndi zomwe chimachititsa kuchitika basi.” Nkhani za m’Baibulo zonena za zochita za Yehova zimatiphunzitsa zambiri zokhudza chikondi chake—chiyanjo chokoma mtima chimene ali nacho pa zolengedwa zake. Mwachitsanzo, n’chiyaninso chingaonetse bwino kwambiri khalidwe limeneli kuposa zomwe Yehova mwiniyo anachita posonyeza chikondi m’chochitika chapamwamba kwambiri chomwe tafotokoza chija? M’mitu ikubwerayi, tiona zitsanzo zina zambiri za Yehova akusonyeza chikondi.  Ndiponso, tingadziŵe zochuluka kuchokera m’mawu oyambirira a “chikondi” omwe anagwiritsidwa ntchito m’Baibulo. M’Chigiriki chakale munali mawu anayi onena za “chikondi.” * Mwa mawu ameneŵa, mawu amene amagwiritsidwa ntchito nthaŵi zambiri m’Malemba Achigiriki Achikristu ndi akuti a·ga′pe. Buku lina lotanthauzira mawu a m’Baibulo limati ameneŵa ndi “mawu amphamvu kwambiri onena za chikondi omwe munthu angawalingalire.” Chifukwa chiyani?

12 Mawu akuti a·ga′pe amanena za chikondi chimene munthu amasonyeza chifukwa cholingalira mfundo za makhalidwe abwino. Motero si kungochitira munthu wina zinthu motengeka mtima ndi zimene wanena kapena wachita. Chimaloŵetsamo zambiri, ndipo chimayamba ndi kuganizira ena kwambiri ndi kuwachitira zinthu mokonzekera. Koposa zonse, chikondi cha a·ga′pe n’chopanda dyera m’pang’onong’ono pomwe. Mwachitsanzo, taonaninso Yohane 3:16. Kodi “dziko lapansi” limene Mulungu analikonda kwambiri moti anapereka Mwana wake wobadwa yekha kaamba ka ilo ndi liti? Ndi dziko la anthu amene akhoza kuwomboledwa. Ameneŵa akuphatikizapo anthu ochuluka amene akuyenda njira zauchimo. Kodi Yehova amakonda munthu aliyense monga bwenzi lake, mofanana ndi mmene anakondera Abrahamu? (Yakobo 2:23) Ayi, koma mwachikondi Yehova amachitira zabwino aliyense, ngakhale pamene afunika kuchita zochuluka. Akufuna anthu onse atalapa ndi kusintha njira zawo. (2 Petro 3:9) Ambiri amatero. Ameneŵa iye amawalandira mwachimwemwe monga mabwenzi ake.

13, 14. Kodi n’chiyani chikusonyeza kuti nthaŵi zambiri chikondi cha a·ga′pe chimaphatikizapo kuyanjana ndi ena mwaubwenzi?

13 Komabe anthu ena ali ndi malingaliro olakwika okhudza a·ga′pe. Amaganiza kuti n’chikondi chimene anthu amangokhala nacho m’maganizo, koma osati kuti chimachititsa munthu kukhala waubwenzi. Komatu zoona zake n’zakuti chikondi cha a·ga′pe kaŵirikaŵiri chimaphatikizapo kukhala mwaubwenzi ndi  ena. Mwachitsanzo, pamene Yohane analemba kuti, “Atate akonda Mwana,” anagwiritsa ntchito mawu ochokera ku mawu akuti a·ga′pe. (Yohane 3:35) Kodi Atatewo amakonda Mwana koma wosasangalatsidwa naye? Onani kuti pa Yohane 5:20 Yesu ananena mawu amodzimodziŵa akuti, “Atate akonda Mwana,” komatu anagwiritsa ntchito mawu ochokera ku mawu akuti phi·le′o. Motero chikondi cha Yehova nthaŵi zambiri chimaphatikizapo kuyanjana ndi wina mwaubwenzi. Komabe, sasonyeza chikondi chifukwa chongotengeka maganizo. Nthaŵi zonse chimatsogoleredwa ndi mfundo zake zanzeru ndi zolungama za makhalidwe abwino.

14 Monga taonera, makhalidwe onse a Yehova ndi apamwamba, angwiro, ndipo ndi osangalatsa. Koma chikondi ndi khalidwe losangalatsa kwambiri kuposa ena onse. Palibe chimene chimatiyandikizitsa kwambiri kwa Yehova mofanana ndi chikondi. N’zokondweretsa kuti chikondi ndilonso khalidwe lake lalikulu pa onse. Kodi tikudziŵa bwanji zimenezi?

“Mulungu Ndiye Chikondi”

15. Kodi ndi mawu otani amene Baibulo limanena okhudza khalidwe la Yehova la chikondi, nanga mawuŵa ndi apadera motani? (Onaninso mawu a m’munsi.)

15 Baibulo limanena chinachake chokhudza chikondi chimene silinena mokhudzana ndi makhalidwe ena ofunika kwambiri a Yehova. Malemba sanena kuti Mulungu ndiye mphamvu kapena kuti Mulungu ndiye chilungamo kapenanso kuti Mulungu ndiye nzeru. Iye ali ndi makhalidwe amenewo, ndiye gwero lake lenileni la makhalidwewo, ndipo sitingamuyerekezere n’komwe ndi makhalidwe onse atatuwo. Komabe, pa khalidwe lachinayi pakutchulidwa chinachake chofunika kwambiri kuti: “Mulungu ndiye chikondi.” * (1 Yohane 4:8) Kodi zimenezi zimatanthauzanji?

16-18. (a) N’chifukwa chiyani Baibulo limanena kuti “Mulungu ndiye chikondi”? (b) Pa zolengedwa zonse za padziko lapansi, n’chifukwa chiyani munthu ndiye chizindikiro choyenera cha chikondi cha Yehova?

16 Kunena kuti “Mulungu ndiye chikondi” si kungonena kuti ichi  n’chofanana ndi ichi, monga ngati kunena kuti “Mulungu ndi wofanana ndi chikondi.” Tikhoza kulakwitsa ngati titasintha mawuwo n’kunena kuti “chikondi ndicho Mulungu.” Yehova sali khalidwe losakhudzika, iye ndi weniweni. Ndi munthu yemwe ali ndi malingaliro ndi makhalidwe osiyanasiyana kuphatikiza pa chikondi. Komatu, chikondi chinamuloŵerera kwambiri Yehova. Motero buku lina ponena za vesili limati: “Chikondi ndicho chikhalidwe chake cha Mulungu.” Tingaganizire nkhaniyi mwa njira iyi: Mphamvu za Yehova zimamutheketsa kuchita zinthu. Chilungamo chake ndi nzeru zake zimasonyeza mmene ati azichitire. Koma chikondi cha Yehova chimamulimbikitsa kuchita zinthuzo. Ndipo nthaŵi zonse pamakhala pali chikondi akamagwiritsa ntchito makhalidwe ake enawo.

17 Kaŵirikaŵiri ena amati Yehova ndiye chitsanzo chenicheni cha chikondi. Motero, ngati tikufuna kuphunzira chikondi chomangika pa mfundo za makhalidwe abwino, tifunika kuphunzira za Yehova. Inde, tikhoza kuonanso anthu a khalidwe labwinoli. Koma n’chifukwa chiyani ali ndi khalidwe limeneli? Panthaŵi imene anali kulenga zinthu, Yehova analankhula mawu aŵa, mwachionekere kwa Mwana wake: “Tipange munthu m’chifanizo chathu, monga mwa chikhalidwe chathu.” (Genesis 1:26) Pa zolengedwa zonse za padziko lapansili, ndi amuna ndi akazi okha amene angasankhe kuti azikonda ena ndipo mwakutero n’kutsanzira Atate wawo wakumwamba. Kumbukirani kuti Yehova anasankha zolengedwa zosiyanasiyana kuimira makhalidwe ake ofunika kwambiri. Komatu, Yehova anasankha cholengedwa chake chapamwamba kwambiri padziko lapansi, munthu, kuimira khalidwe Lake lalikulu la chikondi.—Ezekieli 1:10.

18 Pamene timakonda ena mopanda dyera ndi molingalira mfundo za makhalidwe abwino, timasonyeza khalidwe lalikulu la Yehova. N’zofanana ndi mmene mtumwi Yohane analembera kuti: “Tikonda ife, chifukwa anayamba Iye kutikonda.” (1 Yohane 4:19) Koma kodi Yehova anayamba iye kutikonda m’njira zotani?

Yehova Ndiye Anayamba Kuchitapo Kanthu

19. N’chifukwa chiyani tinganene kuti chikondi chinali chofunika kwambiri pa ntchito ya kulenga ya Yehova?

19 Chikondi sichinayambe lero. Ndi iko komwe, n’chiyani chinachititsa Yehova kuyamba kulenga zinthu? Sikuti anali kusungulumwa  ndiye amafuna wokhala naye. Yehova ndi wokwanira payekha ndipo ali ndi zonse, moti safunika kanthu kena kamene angamupatse winawake. Koma chikondi chake, khalidwe lolimbikitsa kuchitira ena zinthu, chinamulimbikitsa kupatsa moyo zolengedwa zanzeru zomwe zingayamikire mphatso yoteroyo, kuti zisangalale nawo. “Woyamba wa chilengo cha Mulungu” anali Mwana wake wobadwa yekha. (Chivumbulutso 3:14) Ndiyeno Yehova anagwiritsa ntchito Mmisiri ameneyu polenga zinthu zina zonse, kuyambira ndi angelo. (Yobu 38:4, 7; Akolose 1:16) Pokhala zinapatsidwa ufulu, nzeru, ndi malingaliro, mizimu yamphamvu imeneyi inali ndi mwayi woti iyo ikonde ena—kukondana yokhayokha, komanso kuposa pamenepo, kukonda Yehova Mulungu. (2 Akorinto 3:17) Motero iwo anakonda ena chifukwa iwowo ndiwo anayamba kukondedwa.

20, 21. Kodi Adamu ndi Hava anali ndi umboni wotani wakuti Yehova anali kuwakonda, komabe kodi iwo anachitaponji?

20 Ndi mmenenso zinalili ndi anthu. Kuyambira pachiyambi, Adamu ndi Hava anakutidwa ndi chikondi. Kulikonse kumene anali kuyang’ana m’mudzi wawo wa Paradaiso mu Edene, anali kuona umboni wakuti Atate amawakonda. Taonani zimene Baibulo limanena: “Yehova Mulungu anabzala m’munda ku Edene chakummaŵa; momwemo ndipo adaika munthu adamuumbayo.” (Genesis 2:8) Kodi munayamba mwapezekako m’munda kapena paki yokongola kwambiri? N’chiyani chinakusangalatsani kwambiri? Kodi kunali kuwala kumene munali kukuonera m’masamba muli pamthunzi malo ena ake a phee? Kodi kunali kukongola kochititsa chidwi kwa maluŵa osiyanasiyana? Kodi linali phokoso lomvekera pansipansi la kuyenda kwa madzi mu mtsinje, kapena kulira kwa mbalame ndi tizilombo tina? Nanga bwanji fungo la mitengo, zipatso, ndi maluŵa? Mulimonse mmene zinalili, lerolino palibe paki imene tingaiyerekezere ndi Edene. Chifukwa chiyani?

21 Yehova mwiniyo ndiye anabzala munda umenewo! Uyenera kuti unali wokongola mosaneneka. Munali mtengo uliwonse wosangalatsa kuuona ndiponso wa zipatso zokoma. M’mundawo munali madzi okwanira, malo ambiri, ndipo munali nyama zosiyanasiyana. Adamu ndi Hava anali ndi chilichonse chowapangitsa kukhala achimwemwe ndi okhutira, kuphatikizapo ntchito yopindulitsa ndiponso wokhala naye wabwino kwambiri. Yehova ndiye anayamba kuwakonda, ndipo iwo anali ndi zifukwa zomveka  zomukonderanso. Komatu, analephera kuchita zimenezi. M’malo moti mwachikondi amvere Atate wawo wakumwamba, anamupandukira mwadyera.—Genesis, chaputala 2.

22. Kodi zimene anachita Yehova ndi kupanduka kwa mu Edene zimasonyeza motani kuti chikondi chake ndi chokhulupirika?

22 Zimenezi ziyenera kuti zinamupweteka kwambiri Yehova. Koma kodi kupandukaku kunaipitsa mtima wake wachikondiwo? Ayi! “Chifundo chake [kapena kuti, “chikondi chake chokhulupirika,” NW, mawu a m’munsi] n’chosatha.” (Salmo 136:1) Motero, mofulumira anakhala n’cholinga chowombola ana a mitima yowongoka a Adamu ndi Hava, ndipo anapanga makonzedwe a zimenezi. Monga taonera, zimene anapanga zinaphatikizapo nsembe ya dipo ya Mwana wake wokondedwa yomwe Atate inawatengera zambiri.—1 Yohane 4:10.

23. Kodi tinganene kuti Yehova ndi “Mulungu wachimwemwe” pa chifukwa chimodzi chiti, ndipo ndi funso lofunika kwambiri liti limene liyankhidwe m’mutu wotsatira?

23 Inde, kuchokera pachiyambi Yehova wakhala akuyamba ndiye kuchitapo kanthu posonyeza anthu chikondi. “Anayamba Iye kutikonda” m’njira zosaŵerengeka. Chikondi chimachititsa anthu kukhala ogwirizana ndi osangalala, motero n’zosadabwitsa kuti Yehova akutchedwa kuti “Mulungu wachimwemwe.” (1 Timoteo 1:11, NW) Komabe, pali funso lofunika kwambiri. Kodi Yehova amatikondadi monga munthu payekha? Mutu wotsatira uyankha funso limeneli.

^ ndime 11 Mawu akuti phi·le′o, amene amanena za kukonda munthu amene umagwirizana naye kapena mbale wako, amagwiritsidwa ntchito kaŵirikaŵiri m’Malemba Achigiriki Achikristu. Mawu ofanana ndi akuti stor·ge′, kapena kuti kukonda anthu a m’banja lako, anagwiritsidwa ntchito pa 2 Timoteo 3:3 posonyeza kuti chikondi choterocho chidzazilala kwambiri m’masiku otsiriza. Mawu ena akuti e′ros, kapena kuti chikondi cha pakati pa mwamuna ndi mkazi, sanagwiritsidwepo ntchito mu Malemba Achigiriki Achikristu, ngakhale kuti mtundu umenewo wachikondi umafotokozedwa m’Baibulo.—Miyambo 5:15-20.

^ ndime 15 Mawu ena m’Malemba analembedwa mofanana ndi ameneŵa. Mwachitsanzo, timaŵerenga kuti “Mulungu ndiye kuunika” ndiponso kuti “Mulungu . . . ndiye moto wonyeketsa.” (1 Yohane 1:5; Ahebri 12:29) Koma mawuŵa tiyenera kuwamva monga mafanizo, chifukwa akufananitsa Yehova ndi zinthu zooneka. Yehova ali ngati kuunika, chifukwa ndi woyera ndi wolungama. Mwa iye mulibe “mdima,” kapena chodetsa. Ndipo tingamufanizire ndi moto chifukwa chakuti amagwiritsa ntchito mphamvu zake zowononga.